Kwa Afilipi
1 Ine Paulo limodzi ndi Timoteyo, akapolo a Khristu Yesu, ndikulembela oyela onse amene ali mu mgwilizano ndi Khristu Yesu ku Filipi, komanso oyang’anila ndi atumiki othandiza.
2 Cisomo komanso mtendele zocokela kwa Mulungu Atate wathu komanso kwa Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.
3 Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukila za inu. 4 Ndimacita zimenezi m’pemphelo langa lililonse lopembedzela limene ndimapeleka mosangalala cifukwa ca nonsenu. 5 Ndimamuyamika cifukwa ca thandizo lanu* pa nchito yolengeza uthenga wabwino, kuyambila pa tsiku loyamba mpaka pano. 6 Sindikukaikila kuti amene anayambitsa nchito yabwino kwa inu adzaipitiliza n’kuitsilizitsa mpaka tsiku la Khristu Yesu litafika. 7 M’poyenela kwa ine kuti ndiganizile nonsenu mwa njila imeneyi, cifukwa ndinu a pamtima panga. Ndipo munandithandiza pa nthawi imene ndinamangidwa maunyolo m’ndende, komanso poteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo nchito yolengeza uthenga wabwino. Inu limodzi ndi ine tinapindula ndi cisomo ca Mulungu.
8 Ndipo Mulungu angandicitile umboni kuti ndikufunitsitsa kukuonani nonsenu, komanso kuti ndili ndi cikondi cacikulu pa inu ngati cimene Khristu Yesu ali naco. 9 Ine ndikupitiliza kupemphela kuti cikondi canu cizipita cikukulila-kulila, limodzi ndi cidziwitso colongosoka, komanso luso lanu lozindikila zinthu. 10 Ndiponso kuti muzitsimikizila ndi kusankha zinthu zomwe ndi zofunika kwambili n’colinga coti mukhale opanda colakwa ndi osakhumudwitsa ena mpaka tsiku la Khristu. 11 Mucite zimenezi kutinso mudzazidwe ndi zipatso zolungama mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti Mulungu alemekezeke komanso kuti atamandike.
12 Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti zimene zandicitikila, zathandiza kuti uthenga wabwino ufalikile, 13 moti Asilikali onse Oteteza Mfumu ndi anthu ena onse amva kuti ndamangidwa cifukwa ca Khristu. 14 Ndipo abale ambili amene akutumikila Ambuye alimba mtima cifukwa ca kumangidwa kwanga, ndiponso akupitiliza kuonetsa kulimba mtima mwa kulankhula mau a Mulungu mopanda mantha.
15 N’zoona kuti ena akulalikila za Khristu cifukwa akundicitila kaduka ndi kupikisana nane. Koma ena akulalikila ndi colinga cabwino. 16 Amene akulalikila ndi colinga cabwinowa, akufalitsa uthenga wonena za Khristu cifukwa ca cikondi, popeza akudziwa kuti ndinasankhidwa kuti nditeteze uthenga wabwino. 17 Koma enawo akucita zimenezo cifukwa ca mtima wokonda mikangano, osati ndi colinga cabwino. Iwo akungofuna kundiyambitsila mabvuto m’ndende muno. 18 Ndiye kodi pakhala zotsatilapo zotani? Uthenga wokhudza Khristu ukufalitsidwabe, kaya mwaciphamaso kapena m’coonadi. Ndipo ine ndikusangalala cifukwa ca zimenezi. Ndipo ndipitilizabe kusangalala 19 cifukwa ndikudziwa kuti zimenezi zidzacititsa kuti ndipulumutsidwe cifukwa ca mapemphelo anu opembedzela, komanso ndi thandizo la mzimu wa Yesu Khristu. 20 Izi n’zogwilizana ndi zimene ndikuyembekezela mwacidwi, ndiponso ciyembekezo canga cakuti sindidzacititsidwa manyazi mwa njila iliyonse. Koma kuti mwa ufulu wanga wonse wa kulankhula, Khristu alemekezedwe tsopano kudzela mwa ine,* ngati mmene zakhala zikucitikila m’mbuyo monsemu, kaya ndikhala ndi moyo kapena ndimwalila.
21 Cifukwa kwa ine, ndikakhala ndi moyo, ndikhalila moyo Khristu, ndipo ndikamwalila ndipindula. 22 Tsopano ngati ndipitiliza kukhala ndi moyo m’thupi langali, nchito ya manja anga idzaonjezeka, koma coti ndisankhe pamenepa sindikamba. 23 Ndikulephela kusankha pa zinthu ziwilizi, cifukwa ndikulakalaka nditamasulidwa n’kukakhala ndi Khristu, zimene kunena zoona ndi zabwino kwambili. 24 Komabe, ndi bwino kuti ndipitilize kukhala ndi moyo m’thupi langali cifukwa ca inu. 25 Conco, popeza kuti ndine wotsimikiza za zimenezi, ndikudziwa kuti ndipitiliza kukhala ndi moyo komanso kukhala ndi nonsenu kuti mupite patsogolo, komanso kuti musangalale cifukwa ca cikhulupililo canu. 26 Inde, kuti ndikadzabwelanso kwa inu cimwemwe canu cidzasefukile cifukwa ndinu otsatila a Khristu Yesu.
27 Koma cimene ndikungofuna n’cakuti makhalidwe anu akhale ogwilizana* ndi uthenga wabwino wa Khristu, kuti kaya ndabwela kudzakuonani kapena pamene ine kulibe, ndizimva mbili yakuti mukupitilizabe kukhala ogwilizana.* Ndipo ndi mtima umodzi, mukuyesetsa mogwilizana kuti mupitilize kukhulupilila uthenga wabwino. 28 Komanso simukucita mantha m’njila iliyonse ndi okutsutsani. Umenewu ndi umboni wakuti iwo adzaonongedwa, koma kwa inu, ndi umboni wakuti mudzapulumuka, ndipo umboni umenewu ndi wocokela kwa Mulungu. 29 Zili conco cifukwa inu munapatsidwa mwai, osati wokhulupilila Khristu cabe, koma womubvutikila. 30 N’cifukwa cake inunso mukukumana ndi mabvuto ofanana ndi amene ndinakumana nao, amene panopa mukumva kuti ndikukumana naobe.