Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
2 Tsopano m’masiku amenewo, Kaisara Augasito anapeleka lamulo lakuti anthu onse m’dzikolo akalembetse m’kaundula. 2 (Kulembetsa koyamba kumeneko kunacitika pamene Kureniyo anali bwanamkumbwa wa Siriya.) 3 Ndipo anthu onse anapita kukalembetsa, aliyense ku mzinda wakwawo. 4 Nayenso Yosefe anacoka ku Galileya mu mzinda wa Nazareti n’kupita ku Yudeya, ku mzinda wa Davide wochedwa Betelehemu, cifukwa iye anali wa m’banja la Davide komanso wa fuko limenelo. 5 Anapita kukalembetsa pamodzi ndi Mariya amene anakwatilana naye mwa pangano lawo. Ndipo panthawiyi n’kuti Mariya atatsala pang’ono kubeleka. 6 Ali komweko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe. 7 Iye anabeleka mwana wake woyamba wamwamuna, ndipo anamukulunga m’nsalu n’kumugoneka modyelamo ziweto, cifukwa sanapeze malo m’nyumba ya alendo.
8 M’dela limenelo munalinso abusa amene anali kugona panja kumalo odyetsela ziweto, ndipo anali kuyang’anila nkhosa zawo usiku wonse. 9 Mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova anaimilila pafupi nawo, ndipo ulemelelo wa Yehova unawala pa malopo, moti iwo anacita mantha kwambili. 10 Koma mngeloyo anawauza kuti: “Musaope ayi. Ine ndabwela kudzalengeza uthenga wabwino kwa inu, uthenga wa cimwemwe cacikulu cimene anthu onse adzakhala naco. 11 Pakuti lelo, mu mzinda wa Davide mwabadwa mpulumutsi wanu, amene ndi Khristu Ambuye. 12 Ndipo ndikupatsani cizindikilo ici: Kumeneko mukapeza mwana wakhanda wokulunga m’nsalu atamugoneka m’codyela ziweto.” 13 Mwadzidzidzi, panaonekanso khamu lalikulu la angelo akumwamba, lili pamodzi ndi mngeloyo. Iwo anali kutamanda Mulungu n’kumati: 14 “Ulemelelo kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo padziko lapansi pano mtendele kwa anthu amene Mulungu amakondwela nawo.”
15 Ndiyeno angelowo atacoka n’kubwelela kumwamba, abusawo anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu tikaone zimene zacitika, zimene Yehova watidziwitsa.” 16 Iwo anapita mofulumila, ndipo anakapeza Mariya ndi Yosefe, komanso mwana wakhandayo atam’goneka modyelamo ziweto. 17 Ataona zimenezi, iwo anafotokoza uthenga umene anauzidwa, wokhudza mwana wamng’onoyo. 18 Ndipo onse amene anamva, anadabwa kwambili ndi zimene abusawo anawauza. 19 Koma Mariya anasunga mawu onsewa ndi kuganizila tanthauzo la zimenezi mumtima mwake. 20 Ndiyeno abusawo anabwelela akulemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zonse zimene anamva ndi kuona, mogwilizana ndi zimene anauzidwa.
21 Pambuyo pa masiku 8, nthawi ya mdulidwe wa mwanayo itakwana, anamupatsa dzina lakuti Yesu. Ili ndi dzina limene mngelo uja anamupatsa, Mariya asanakhale ndi pathupi.
22 Komanso nthawi yowayeletsa itakwana malinga ndi Cilamulo ca Mose, anapita naye ku Yerusalemu kukamupeleka kwa Yehova. 23 Izi zinali zogwilizana ndi zimene zinalembedwa m’Cilamulo ca Yehova kuti: “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa* adzakhala woyela kwa Yehova.” 24 Ndipo iwo anapeleka nsembe malinga ndi zimene Cilamulo ca Yehova cimanena kuti: “Njiwa ziwili kapena ana a nkhunda awili.”
25 Ndiyeno mu Yerusalemu, munali munthu wina dzina lake Simiyoni. Mwamunayu anali wolungama komanso wodzipeleka kwa Mulungu. Iye anali kuyembekezela nthawi ya kutonthozedwa kwa Isiraeli, ndipo mzimu woyela unali pa iye. 26 Kuwonjezela apo, Mulungu anamuululila mwa mzimu woyela kuti sadzafa kufikila ataona Khristu wa Yehova. 27 Tsopano motsogoleledwa ndi mzimu, iye anapita ku kacisi. Ndiyeno pamene makolo a mwana wa mng’onoyo, Yesu, anabwela naye kuti amucitile zimene Cilamulo cinali kunena, 28 iye ananyamula mwanayo m’manja mwake ndi kutamanda Mulungu kuti: 29 “Tsopano Ambuye Wamkulukulu, mukulola kapolo wanu kupita mumtendele pakuti mwakwanilitsa lonjezo lanu, 30 cifukwa maso anga aona njila yanu ya cipulumutso 31 imene mwakonza pamaso pa anthu a mitundu yonse, 32 kuunika kocotsa nsalu yophimba mitundu ya anthu kuti isamaone, komanso ulemelelo wa anthu anu Aisiraeli.” 33 Ndiyeno tate ndi mayi a mwanayo anali kungodabwa ndi zimene zinali kunenedwa zokhudza mwanayo. 34 Komanso Simiyoni anawadalitsa ndipo anauza Mariya, mayi wa mwanayo kuti “Tamvela! Mwana uyu waikidwa kuti ambili mu Isiraeli agwe kapena kuimililanso, komanso kuti akhale cizindikilo cimene anthu angacitsutse 35 (inde, lupanga lalitali lidzakulasa), kuti zimene zili m’mitima ya anthu ambili zionekele poyela.”
36 Tsopano kunali mneneli wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuweli wa fuko la Aseri. Mayi ameneyu anali wokalamba, ndipo atakwatilana ndi mwamuna wake,* anakhala m’cikwati zaka 7 zokha, 37 koma tsopano iye anali mkazi wamasiye wa zaka 84. Mayiyu sanali kuphonya pa kacisi. Anali kucita utumiki wopatulika usana ndi usiku ndi kusala kudya komanso kupeleka mapemphelo ocondelela. 38 Mu ola limenelo, iye anabwela pafupi ndi iwo, ndi kuyamba kuyamika Mulungu komanso kulankhula zokhudza mwanayo kwa onse amene anali kuyembekezela cipulumutso ca Yerusalemu.
39 Conco iwo atacita zonse malinga ndi Cilamulo ca Yehova, anabwelela ku Galileya ku mzinda wawo wa Nazareti. 40 Mwana wamng’onoyo anapitiliza kukula komanso kukhala wamphamvu. Nzelu zake zinali kuwonjezeka, ndipo Mulungu anapitiliza kukondwela naye.
41 Makolo ake anali ndi cizolowezi copita ku Yerusalemu caka ndi caka, ku cikondwelelo ca Pasika. 42 Ndipo iye ali ndi zaka 12, anapita naye ku cikondweleloco mwacizolowezi cawo. 43 Masiku a cikondweleloco atatha komanso pamene anali kubwelela, mnyamatayo Yesu anatsalila ku Yerusalemu, ndipo makolo ake sanadziwe zimenezo. 44 Iwo anaganiza kuti iye ali nawo pamodzi pa gulu la anthu a pa ulendowo, moti anayenda mtunda wa tsiku limodzi. Ndiyeno anayamba kumufunafuna pakati pa acibale awo ndi anzawo. 45 Koma cifukwa sanamupeze, anabwelela ku Yerusalemu, ndipo anamufunafuna mwakhama. 46 Patapita masiku atatu, anamupeza m’kacisi atakhala pakati pa aphunzitsi, ndipo anali kuwamvetsela ndi kuwafunsa mafunso. 47 Koma onse amene anali kumumvetsela, anadabwa kwambili ndi luso lake lomvetsa zinthu komanso mayankho ake. 48 Makolo ake atamuona, anadabwa kwambili. Ndipo mayi ake anamufunsa kuti: “Mwanawe, n’cifukwa ciyani wativutitsa conci? Ine ndi atate akowa tinada nkhawa kwambili, ndipo tinali kukufunafuna.” 49 Koma iye anawayankha kuti: “N’cifukwa ciyani munali kundifunafuna? Kodi simudziwa kuti ndiyenela kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?” 50 Koma iwo sanamvetse zimene iye anali kuwauza.
51 Kenako iye anabwelela nawo ku Nazareti, ndipo anapitiliza kuwamvela.* Komanso mayi ake anasunga mawu onsewa mosamala mumtima mwawo. 52 Nzelu za Yesu zinapitiliza kuwonjezeka, komanso anali kukula mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiliza kukondwela naye.