Kwa Aroma
11 Ndiye ndifunse kuti, kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi! Pakuti inenso ndine Mwisiraeli, mbadwa* ya Abulahamu, wocokela mu fuko la Benjamini. 2 Mulungu sanakane anthu ake amene anali oyamba kuwasankha. Kodi simukudziwa zimene lemba lina limakamba zokhudza Eliya, pamene anali kucondelela Mulungu potsutsa Aisiraeli? Lembalo limati: 3 “Yehova, iwo apha aneneli anu ndipo agwetsa maguwa anu a nsembe, moti ndangotsala ndekhandekha. Ndipo tsopano akundifunafuna kuti andiphe.” 4 Koma kodi Mulungu anamuuza ciyani? Anamuuza kuti: “Ine ndasiya anthu 7,000 amene mawondo awo sanagwadilepo Baala.” 5 Conco mofananamo, palipano alipo ena ocepa amene anasankhidwa mwa cisomo. 6 Ndiye ngati anasankhidwa mwa cisomo, ndiye kuti sanasankhidwe cifukwa ca nchito zawo. Ngati si conco, ndiye kuti cisomo sicingakhalenso cisomo.
7 Ndiye tinene ciyani pamenepa? Cinthu cimene Aisiraeli anali kucifunafuna sanacipeze, koma osankhidwawo ndi amene anacipeza. Enawo anaumitsa mitima yawo 8 monga mmene Malemba amakambila kuti: “Mulungu wawapatsa mzimu wa tulo tofa nato, maso osayang’ana, ndi matu osamva mpaka lelo.” 9 Komanso Davide anati: “Thebulo lawo likhale msampha, mbuna, cokhumudwitsa, ndiponso cilango kwa iwo. 10 Maso awo acite mdima kuti asaone, ndipo nthawi zonse cititsani misana yawo kuwelama.”
11 Ndiyeno ndifunse kuti, kodi iwo anapunthwa mpaka kugwelatu? Ayi! Koma cifukwa ca kucimwa kwawo anthu a mitundu ina apeza cipulumutso, ndipo zimenezi zacititsa kuti iwo acite nsanje. 12 Kucimwa kwawo kwabweletsa cuma mʼdziko, ndipo kucepa kwawo kwabweletsa cuma kwa anthu a mitundu ina. Ndiye padzakhala madalitso ambili ciwelengelo cawo cikadzakwanila.
13 Tsopano ndikulankhula ndi inu anthu a mitundu ina. Popeza ndine mtumwi wotumidwa kwa anthu a mitundu ina, ndikulemekeza utumiki wanga, 14 kuti mwina ndingapangitse anthu a mtundu wanga* kucita nsanje nʼkupulumutsapo ena pakati pawo. 15 Pakuti ngati dziko lagwilizanitsidwa ndi Mulungu cifukwa coti iwo anatayidwa, ndiye kuti akadzalandilidwa zidzakhala monga kuti awaukitsa. 16 Komanso, ngati mbali ya mtanda wa mkate imene yapelekedwa nsembe monga cipatso coyambilila ndi yoyela, ndiye kuti mtanda wonse ndi woyelanso. Ndipo ngati muzu ndi woyela, ndiye kuti nthambi nazonso ndi zoyela.
17 Ngati nthambi zina zinadulidwa, ndipo iwe ngakhale kuti ndiwe nthambi ya mtengo wa maolivi wakuchile, unalumikizidwa pakati pa nthambi zotsala, ndipo unayamba kupeza zonse zofunikila kucokela ku muzu wa mtengo wa maolivi umenewo, 18 usayambe kutukumuka ku nthambi zimene zinadulidwazo. Koma ngati utukumuka kwa izo usaiwale kuti si ndiwe amene ukunyamula muzu, koma muzu ndi umene ukukunyamula iwe. 19 Mwina ukunena kuti: “Anadula nthambi zinazi kuti alumikizepo ine.” 20 Zimenezo nʼzoona. Iwo anadulidwa cifukwa ca kusowa cikhulupililo. Koma iwe ukali wolumikizidwa cifukwa ca cikhulupililo. Usadzitukumule, koma ukhale ndi mantha. 21 Cifukwa ngati Mulungu sanalekelele nthambi zacilengedwe, iwenso sadzakulekelela. 22 Conco uziganizila kukoma mtima kwa Mulungu, komanso mkwiyo wake. Amene anagwa anawaonetsa mkwiyo, koma iwe anakuonetsa kukoma mtima. Ukakhalabe woyenelela udzaonetsedwa kukoma mtima kwake. Apo ayi, iwenso udzadulidwa. 23 Ndipo iwonso akayamba kukhala ndi cikhulupililo, adzalumikizidwa, cifukwa Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24 Ngati iwe unadulidwa ku mtengo wa maolivi umene mwacilengedwe umamela m’chile, ndipo mosiyana ndi cilengedwe unalumikizidwa ku mtengo wa maolivi wolimidwa, kodi si capafupi kulumikiza nthambizi ku mtengo wawo umene zinadulidwako?
25 Pakuti sindikufuna kuti mukhale osadziwa cinsinsi copatulilka cimeneci abale, kuopela kuti mungadzione ngati anzelu. Cinsinsico n’cakuti ena mu Isiraeli aumitsa mitima yawo mpaka ciwelengelo conse ca a mitundu ina citakwanila. 26 Mwa njila imeneyi, Aisiraeli onse adzapulumutsidwa mogwilizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Mpulumutsi adzacokela ku Ziyoni, ndipo adzacotsela Yakobo nchito zonse zosalemekeza Mulungu. 27 Ndipo limeneli ndi pangano limene ndidzacite nawo ndikadzawacotsela macimo awo.” 28 N’zoona kuti iwo ndi adani a uthenga wabwino kuti inu zikupindulileni. Koma Mulungu anawasankha ndipo amawakonda cifukwa ca makolo awo akale. 29 Mulungu sadzadziimba mlandu cifukwa ca mphatso zake, ndiponso cifukwa cakuti anawaitana. 30 Inu pa nthawi ina munali osamvela Mulungu, koma tsopano mwaonetsedwa cifundo cifukwa ca kusamvela kwawo. 31 Mulungu wakucitilani cifundo cifukwa ca kusamvela kwa Ayuda. Koma angawacitilenso cifundo mmene anacitila kwa inu. 32 Mulungu walola onse kuti akhale akaidi a kusamvela kuti onsewo awacitile cifundo.
33 Ndithudi, madalitso a Mulungu ndi oculuka kwambili. Nzelu zake nʼzozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambili. Ziweluzo zake ndi zovuta kuzimvetsa, ndipo ndani angatulukile njila zake? 34 “Ndani wafika podziwa maganizo a Yehova, kapena ndani angakhale mlangizi wake?” 35 Kapenanso “ndani anayambilila kumupatsa kanthu, kuti amubwezele?” 36 Cifukwa zinthu zonse zimacokela kwa iye, ndipo ndiye anazipanga ndiponso ndi zake. Ulemelelo upite kwa iye mpaka muyaya. Ameni.