Kwa Aroma
12 Conco abale, ndikukucondelelani mwa cifundo cacikulu ca Mulungu kuti mupeleke matupi anu monga nsembe yamoyo, yoyela, komanso yovomelezeka kwa Mulungu, umene ndi utumiki wopatulika pogwilitsa nchito luso lanu la kuganiza. 2 Lekani kutengela* nzelu za nthawi ino,* koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka, ndi cangwilo.
3 Cifukwa ca cisomo cimene Mulungu anandicitila, ndikuuza aliyense pakati panu kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza mwanzelu mogwilizana ndi cikhulupililo cimene Mulungu wamupatsa.* 4 Thupi limakhala ndi ziwalo zambili, koma ziwalo zonsezo sizigwila nchito yofanana. 5 Conco ifenso ngakhale kuti tili ambili, ndife thupi limodzi mwa Khristu, ndipo ndife ziwalo zolumikizana. 6 Tili ndi mphatso zosiyanasiyana zimene Mulungu anatipatsa mwa cisomo cake. Conco kaya tili ndi mphatso ya kulosela, tiyeni tilosele mogwilizana ndi cikhulupililo cathu. 7 Kaya tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni ticite utumiki umenewo. Amene amaphunzitsa, aike mtima wake pa kuphunzitsako. 8 Amene amalimbikitsa, azilimbikitsa ndithu. Wogawila* azigawila mowolowa manja. Wotsogolela azitsogolela mwakhama. Ndipo amene amacitila ena cifundo, azitelo mokondwela.*
9 Cikondi canu cisakhale caciphamaso. Nyansidwani nazo zoipa, ndipo yesetsani kucita zabwino. 10 Poonetsa cikondi kwa abale, khalani ndi cikondi ceniceni. Pa nkhani yocitilana ulemu, inu mukhale woyamba. 11 Gwilani nchito molimbika,* ndipo musakhale alesi.* Yakani ndi mzimu. Tumikilani Yehova monga akapolo. 12 Muzikondwela cifukwa ca ciyembekezo. Muzipilila masautso. Limbikilani kupemphela. 13 Gawanani ndi oyelawo malinga ndi zimene akusowa. Khalani oceleza. 14 Pitilizani kudalitsa amene akukuzunzani. Adalitseni, m’malo mowatembelela. 15 Sangalalani ndi amene akusangalala, ndipo lilani ndi amene akulila. 16 Onani ena monga mmene inu mumadzionela. Musamaganize modzikuza,* koma khalani odzicepetsa. Musamadzione ngati anzelu.
17 Musabwezele coipa pa coipa kwa munthu wina aliyense. Ganizilani zimene anthu onse amaona kuti ndi zabwino. 18 Ngati nʼkotheka, yesetsani mmene mungathele kukhala mwamtendele ndi anthu onse. 19 Okondedwa, musamabwezele coipa, koma siyilani malo mkwiyo wa Mulungu. Pakuti Malemba amati: “‘Kubwezela ndi kwanga, ndidzabwezela ndine,’ watelo Yehova.” 20 Koma “ngati mdani wako ali ndi njala, m’patse cakudya. Ngati ali ndi ludzu, m’patse madzi akumwa. Pakuti ukacita zimenezi udzamuunjikila makala a moto pa mutu pake.”* 21 Musalole kuti coipa cikugonjetseni, koma pitilizani kugonjetsa coipa pocita cabwino.