Macitidwe a Atumwi
4 Pamene Petulo ndi Yohane anali kukamba ndi anthu aja, ansembe, kapitawo wa pakacisi, komanso Asaduki anabwela kwa iwo. 2 Iwo anali okwiya cifukwa atumwiwo anali kuphunzitsa anthu komanso kulengeza poyela kuti Yesu anauka kwa akufa. 3 Conco anawagwila n’kuwaponya* m’ndende mpaka tsiku lotsatila cifukwa kunali kutada kale. 4 Koma ambili amene anamvetsela zimene iwo anakamba anakhulupilila, ndipo ciwelengelo ca amuna cinali pafupifupi 5,000.
5 Tsiku lotsatila, olamulila, akulu, ndi alembi anasonkhana pamodzi ku Yerusalemu. 6 Kunalinso Anasi wansembe wamkulu, Kayafa, Yohane, Alekizanda, ndi onse amene anali acibale a wansembe wamkuluyo. 7 Iwo anaimika Petulo ndi Yohane pakati pawo n’kuyamba kuwafunsa kuti: “Kodi mphamvu zocita izi mwazitenga kuti, kapena mwacita izi m’dzina la ndani?” 8 Ndiyeno Petulo atadzazidwa ndi mzimu woyela, anawauza kuti:
“Inu olamulila anthu komanso akulu, 9 ngati mukutifunsa mafunso lelo za cabwino cimene tacitila munthu wolemalayu, ndipo mufuna kudziwa amene wapangitsa munthu uyu kucila, 10 zidziwike kwa nonsenu komanso kwa Aisiraeli onse, kuti m’dzina la Yesu Khristu Mnazareti amene inu munamuphela pamtengo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kupitila mwa iyeyo munthu amene waimilila patsogolo panu wakhala bwinobwino. 11 Yesu ameneyu ndi ‘mwala umene inu omanga munauona kuti ndi wopanda nchito, umene wakhala mwala wapakona* wofunika kwambili.’ 12 Kuwonjezela apo, palibe wina aliyense amene angapeleke cipulumutso, cifukwa palibe dzina lina padziko lapansi limene lapelekedwa kwa anthu limene lingatipulumutse.”
13 Iwo ataona mmene Petulo ndi Yohane anali kulankhulila molimba mtima, podziwanso kuti anali osaphunzila* komanso anali anthu wamba, anadabwa kwambili. Ndipo anazindikila kuti iwo anali kuyenda ndi Yesu. 14 Iwo ataona munthu amene anacilitsidwayo ataimilila nawo pamodzi, anasowa cokamba. 15 Conco anawalamula kuti atuluke mu holo ya Bungwe Lalikulu la Ayuda,* kenako anayamba kukambilana 16 kuti: “Kodi ticite nawo ciyani amuna amenewa? Cifukwa kukamba zoona, iwo acita cozizwitsa* cacikulu cimene cadziwika kwa anthu onse okhala mu Yerusalemu. Ndipo sitingatsutse zimenezo. 17 Conco kuti nkhaniyi isapitilize kufalikila pakati pa anthu, tiyeni tiwaopseze ndi kuwauza kuti asalankhulenso ndi wina aliyense m’dzina limeneli.”
18 Pambuyo pake, anawaitana n’kuwalamula kuti asakambenso kalikonse kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu. 19 Koma Petulo ndi Yohane anawauza kuti: “Weluzani nokha ngati n’koyenela pamaso pa Mulungu kumvela inu m’malo mwa Mulungu. 20 Koma ife sitingaleke kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” 21 Conco atawaopsezanso, anawamasula, popeza kuti sanapeze cifukwa ciliconse cowapatsila cilango. Komanso anaopa anthu cifukwa onse anali kutamanda Mulungu pa zimene zinacitikazo. 22 Munthuyo amene anacilitsidwa mozizwitsa anali ndi zaka zoposa 40.
23 Atamasulidwa, iwo anapita kwa okhulupilila anzawo n’kuwafotokozela zimene ansembe aakulu ndi akulu anawauza. 24 Atamva izi, onse anafuula kwa Mulungu kuti:
“Ambuye Wamkulukulu, inu ndinu munapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo. 25 Ndipo mwa mzimu woyela inu munalankhula kudzela mwa kholo lathu Davide mtumiki wanu kuti, ‘N’cifukwa ciyani anthu a m’maiko osiyanasiyana anakwiya? Komanso n’cifukwa ciyani anthu amitundu yosiyanasiyana anasinkhasinkha zinthu zopanda pake? 26 Mafumu a padziko lapansi anaimilila pamalo awo, ndipo olamulila anasonkhana pamodzi mogwilizana pofuna kulimbana ndi Yehova komanso wodzozedwa wake.’* 27 Pakuti Herode, Pontiyo Pilato, kuphatikizapo anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana pamodzi mumzinda uno kuti alimbane ndi mtumiki wanu woyela Yesu, amene inu munamudzoza. 28 Iwo anasonkhana pamodzi kuti acite zimene inu munakambilatu. Mwa mphamvu yanu, munapangitsa kuti izi zicitike mogwilizana ndi cifunilo canu. 29 . Tsopano Yehova, mvelani mmene akutiopsezela, ndipo thandizani ife akapolo anu kuti tipitilize kulankhula mawu anu molimba mtima. 30 Pitilizani kutambasula dzanja lanu kuti anthu acilitsidwe, ndiponso kuti zizindikilo ndi zodabwitsa zicitike kudzela m’dzina la Yesu mtumiki wanu woyela.”
31 Iwo atapemphela mocondelela,* malo amene anasonkhanapo anagwedezeka, ndiyeno aliyense wa iwo anadzazidwa ndi mzimu woyela ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.
32 Kuwonjezela apo, khamu la anthu amene anakhulupilila linali ndi maganizo ofanana,* ndipo palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anakamba kuti zinthu zimene anali nazo zinali zake yekha, koma zonse zimene anali nazo zinali zawo onse. 33 Ndipo atumwiwo anapitiliza kucitila umboni mwamphamvu kwambili za kuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo Mulungu anawaonetsa cisomo onsewo. 34 Kukamba zoona, pakati pawo panalibe aliyense amene anali kusowa kanthu, cifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba anali kuzigulitsa n’kubweletsa ndalamazo. 35 Ndipo iwo anali kupeleka ndalamazo kwa atumwi. Kenako ndalamazo zinali kupelekedwa kwa aliyense malinga ndi zosowa zake. 36 Conco Yosefe, amene atumwiwo anamupatsanso dzina lakuti Baranaba (limene limatanthauza “Mwana wa Citonthozo”), amenenso anali Mlevi mbadwa ya ku Kupuro, 37 anali ndi munda. Iye anaugulitsa mundawo n’kubweletsa ndalama zake, kenako anazipeleka kwa atumwi.