Wolembedwa na Maliko
6 Ndiyeno anacoka kumeneko n’kufika ku dela lakwawo, ndipo ophunzila ake anamutsatila. 2 Tsiku la Sabata litafika, iye anayamba kuphunzitsa m’sunagoge. Ndipo anthu amene anali kumumvetsela anadabwa kwambili n’kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti zinthu zimenezi? N’cifukwa ciyani anapatsidwa nzelu zimenezi komanso kuti azicita nchito zamphamvu ngati izi? 3 Kodi ameneyu si kalipentala, mwana wa Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Yudasi na Simoni? Kodi alongo ake sitili nawo konkuno?” Conco anayamba kupunthwa cifukwa ca iye. 4 Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneli salemekezedwa kwawo, ngakhale na acibale ake kapena pa nyumba pake, koma kwina.” 5 Conco iye sanacite nchito zamphamvu zambili kumeneko. Koma anangoika manja ake pa odwala ocepa na kuwacilitsa. 6 Ndithudi, iye anadabwa ataona kusoŵa cikhulupililo kwawo. Cotelo anazungulila m’midzi yapafupi na kumaphunzitsa anthu.
7 Tsopano anaitana ophunzila ake 12 aja n’kuyamba kuwatuma aŵili-aŵili, ndipo anawapatsa ulamulilo pa mizimu yonyansa. 8 Komanso anawalamula kuti asanyamule ciliconse pa ulendowo kupatulapo ndodo. Anawalamulanso kuti asanyamule mkate, cola ca zakudya, kapena ndalama* m’zikwama zawo. 9 Anawauza kuti avale nsapato koma asavale zovala ziŵili.* 10 Anawauzanso kuti: “Nthawi zonse mukaloŵa m’nyumba, muzikhala mmenemo mpaka nthawi yocoka kumeneko. 11 Ndipo kulikonse kumene sadzakulandilani kapena kukumvetselani, pocoka kumeneko muzikutumula fumbi ku mapazi anu kuti ukhale umboni kwa iwo.” 12 Kenako anapita kukalalikila kuti anthu alape, 13 ndipo anatulutsa ziŵanda zambili, komanso anapaka mafuta anthu ambili odwala na kuwacilitsa.
14 Mfumu Herode inamva zimenezi cifukwa dzina la Yesu linachuka kwambili, ndipo anthu anali kunena kuti: “Yohane M’batizi waukitsidwa kwa akufa. Ndiye cifukwa cake akucita nchito zamphamvu.” 15 Koma ena anali kukamba kuti: “Ni Eliya.” Ndipo enanso anali kunena kuti: “Ni mneneli monga analili aneneli akale.” 16 Koma Herode atamva zimenezi anati: “Ndithudi ameneyu ni Yohane uja amene n’namudula mutu. Iye waukitsidwadi.” 17 Popeza Herode ndiye anatuma anthu kukam’gwila Yohane, kumumanga, na kukamuponya m’ndende cifukwa ca Herodiya mkazi wa Filipo m’bale wake, popeza Herodeyo anali atamukwatila. 18 Pakuti Yohane anali kuuza Herode kuti: “N’kosaloleka kuti inu mukwatile mkazi wa m’bale wanu.” 19 Conco Herodiya anamusungila cakukhosi, ndipo anali kufuna kumupha, koma sanathe kucita zimenezo. 20 Herode anali kumuopa Yohane cifukwa anali kudziŵa kuti ni munthu wolungama komanso woyela, ndipo iye anali kum’teteza. Nthawi zonse akamva zokamba za Yohane anali kuthedwa nzelu, koma anapitiliza kumumvetsela mokondwela.
21 Komabe, tsiku lakuti Herodiya akwanilitse zolinga zake linafika. Tsikulo linali lokumbukila kubadwa kwa Herode. Ndipo Herodeyo anaitana nduna zake, akulu-akulu a asilikali na anthu ochuka kwambili a mu Galileya kuti adzadye naye cakudya camadzulo. 22 Ndipo mwana wamkazi wa Herodiya analoŵa n’kuyamba kuvina cakuti anakondweletsa Herode na amene anali kudya naye. Ndiyeno mfumuyo inauza mtsikanayo kuti: “Pempha ciliconse cimene ukufuna, ndipo nikupatsa.” 23 Iye anacita kulumbila kuti: “Ciliconse cimene unipemphe nikupatsa, ngakhale hafu ya ufumu wanga.” 24 Conco mtsikanayo anatuluka n’kukafunsa mayi ake kuti: “Nikapemphe ciyani?” Mayiyo anati: “Kapemphe mutu wa Yohane M’batizi.” 25 Nthawi yomweyo anathamangila kwa mfumuyo n’kupempha kuti: “Nifuna munipatse mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.” 26 Ngakhale kuti mfumu inamva cisoni kwambili na zimenezi, siinafune kunyalanyaza pempho la mtsikanayo cifukwa ca lumbilo lake komanso alendo ake aja.* 27 Conco nthawi yomweyo mfumu inatumiza msilikali womulonda n’kumulamula kuti abweletse mutu wa Yohane. Pamenepo iye anapita kukamudula mutu m’ndendemo, 28 ndipo anaubweletsa m’mbale. Kenako anaupeleka kwa mtsikanayo, ndipo mtsikanayo anapita kukaupeleka kwa mayi ake. 29 Ophunzila ake atamva zimenezi anabwela kudzatenga mtembo wake n’kukauika m’manda.*
30 Atumwi anasonkhana kwa Yesu n’kumufotokozela zonse zimene iwo anacita na kuphunzitsa. 31 Iye anawauza kuti: “Bwelani kuno, tipite kwatokha kuti mukapumuleko pang’ono.” Pakuti anthu ambili anali kubwela na kupita. Ndipo analibe nthawi yopumula ngakhale yoti adye cakudya. 32 Conco anakwela bwato n’kupita kwaokha ku malo opanda anthu. 33 Koma anthu anawaona akupita ndipo ambili anadziŵa zimenezi. Conco anthu ocokela m’mizinda yonse anathamangila kumeneko wapansi, ndipo anakafika kumaloko iwo asanafike. 34 Yesu atatsika m’bwatomo anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvela cisoni cifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Cotelo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.
35 Madzulo dzuŵa litatsala pang’ono kuloŵa, ophunzila ake anafika kwa iye n’kumuuza kuti: “Kuno tili n’kopanda anthu ndipo nthawi yatha kale. 36 Auzeni anthuwa azipita akaloŵe m’midzi yapafupi na m’madela ozungulila kuti akadzigulile cakudya.” 37 Iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse cakudya.” Pamenepo iwo anafunsa kuti: “Kodi tipite tikagule cakudya ca ndalama zokwana madinari 200 n’kuwapatsa anthuwa kuti adye?” 38 Yesu anawafunsa kuti: “Kodi muli na mitanda ingati ya mkate? Pitani mukaone!” Ataiona anati: “Ilipo isanu na nsomba ziŵili.” 39 Kenako anauza anthu onse kuti akhale m’magulu-magulu pa udzu wobiliŵila. 40 Iwo anakhaladi m’magulu a anthu 100 komanso 50. 41 Atatenga mitanda isanu ija na nsomba ziŵili zija, anayang’ana kumwamba n’kupempha dalitso. Kenako ananyema-nyema mitanda ya mkateyo n’kuyamba kuipeleka kwa ophunzila ake kuti apatse anthuwo. Ndipo anagaŵila anthu onsewo nsomba ziŵilizo. 42 Onse anadya n’kukhuta. 43 Zotsala anazisonkhanitsa ndipo zinadzala matadza 12 osaŵelengelako nsomba. 44 Anthu amene anadya mkatewo analipo amuna 5,000.
45 Ndiyeno mwamsanga Yesu anauza ophunzila ake kuti akwele bwato na kupita ku tsidya lina la nyanja ca ku Betsaida, pamene iye anali kuuza anthu kuti azipita. 46 Koma atalailana nawo anapita ku phili kukapemphela. 47 Mdima utayamba kugwa, bwatolo linali pakati pa nyanja koma iye anali yekha kumtunda. 48 Conco atawaona akupalasa bwatolo movutikila cifukwa colimbana na mphepo yamphamvu, anawalondola akuyenda pa nyanja. Apa n’kuti ni m’matandakuca, pafupifupi nthawi ya ulonda wacinayi.* Koma anali kuyenda monga afuna kuwapitilila. 49 Atamuona akuyenda pa nyanjapo anaganiza kuti ni cipuku, ndipo anafuula mokweza. 50 Pakuti onse atamuona anacita mantha. Koma nthawi yomweyo anawauza kuti: “Limbani mtima! Ndine, musacite mantha.” 51 Kenako iye anakwela m’bwatomo ndipo mphepoyo inaleka. Ataona izi, ophunzilawo anadabwa kwambili, 52 cifukwa sanamvetsetse tanthauzo la cozizwitsa ca mitanda ya mkate ija, ndipo m’mitima yawo zinali kuwavutabe kumvetsa.
53 Atawolokela kumtunda, anafika ku Genesareti n’kuimika bwatolo capafupi. 54 Koma iwo atangotuluka m’bwatomo anthu anamuzindikila Yesu. 55 Anthuwo anathamangila ku madela osiyana-siyana a cigawo conseco, n’kuyamba kunyamula anthu odwala pamacila kupita nawo kumene anamva kuti ndiko kuli Yesu. 56 Ndipo nthawi iliyonse akaloŵa m’mudzi kapena mu mzinda, kapenanso m’dela lina, anthu anali kuika odwala m’misika. Iwo anali kumucondelela kuti angogwilako ulusi wopota wa m’mbali mwa covala cake cakunja. Ndipo onse amene anagwila ulusiwo anacila.