Wolembedwa na Mateyo
17 Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo na m’bale wake Yohane, n’kukwela nawo m’phili lalitali kwaokha-okha. 2 Kumeneko, iye anasandulika pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuŵa, ndipo zovala zake zakunja zinawala kwambili.* 3 Kenako ophunzilawo anaona Mose na Eliya akulankhula na Yesu. 4 Tsopano Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, zili bwino kuti ife tizikhala pom’pano. Ngati mufuna ningakhome matenti atatu pano. Ina yanu, ina ya Mose, komanso ina ya Eliya.” 5 Mawu ake akali m’kamwa, mtambo wowala unawaphimba. Kenako kunamveka mawu ocokela mu mtambomo akuti: “Uyu ni Mwana wanga wokondedwa amene nimakondwela naye. Muzimumvela.” 6 Ophunzilawo atamva mawu amenewa, anagwada n’kuŵelama mpaka nkhope zawo pansi, ndipo anacita mantha kwambili. 7 Kenako Yesu anawayandikila n’kuwagwila, ndipo anati: “Ŵelamukani. Musaope.” 8 Ataŵelamuka sanaone aliyense koma Yesu yekha. 9 Pamene anali kutsika m’philimo Yesu anawalamula kuti: “Musauzeko aliyense za masomphenyawa mpaka Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa.”
10 Koma ophunzilawo anamufunsa kuti: “Nanga n’cifukwa ciyani alembi amakamba kuti, Eliya ayenela kubwela coyamba?” 11 Poyankha Yesu anati: “Eliya akubweladi, ndipo adzabwezeletsa zinthu zonse. 12 Komabe, nikukuuzani kuti Eliya anabwela kale ndipo iwo sanamuzindikile, koma anamucita ciliconse cimene anali kufuna. Mofananamo, iwo adzazunza Mwana wa munthu.” 13 Pamenepo ophunzilawo anazindikila kuti anali kukamba nawo za Yohane M’batizi.
14 Iwo atafika kufupi na khamu la anthu, mwamuna wina anayandikila Yesu n’kumugwadila, ndipo anati: 15 “Ambuye, mucitileni cifundo mwana wanga wamwamuna, cifukwa ni wakhunyu ndipo akudwala kwambili. Nthawi zambili iye amagwela pa moto komanso pa madzi. 16 N’nabwela naye kwa ophunzila anu, koma alephela kumucilitsa.” 17 Yesu anayankha kuti: “Inu m’badwo wopanda cikhulupililo komanso wopotoka maganizo, kodi nikhalabe nanu mpaka liti? Kodi nikupilileni mpaka liti? Mubweletseni kuno.” 18 Ndiyeno Yesu anadzudzula ciŵandaco, ndipo cinatuluka mwa mnyamatayo moti anacila nthawi yomweyo. 19 Pambuyo pake ophunzilawo anapita kwa Yesu mwamseli n’kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ife tinalephela kutulutsa ciŵanda cija?” 20 Iye anati: “Cifukwa ca kucepa kwa cikhulupililo canu. Pakuti ndithu nikukuuzani kuti, mutakhala na cikhulupililo ngakhale cocepa ngati kanjele ka mpilu, mudzatha kuuza phili ili kuti, ‘coka pano upite apo,’ ndipo lidzacokadi. Palibe cimene cidzakhala cosatheka kwa inu.” 21 ——
22 Iwo atasonkhana ku Galileya Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzapelekedwa m’manja mwa anthu. 23 Anthuwo adzamupha ndipo pa tsiku lacitatu adzaukitsidwa.” Ophunzila ake atamva zimenezi, anamva cisoni kwambili.
24 Atafika ku Kaperenao, anthu okhometsa msonkho wa madalakima aŵili anafika kwa Petulo n’kumufunsa kuti: “Kodi mphunzitsi wanu amakhoma msonkho wa madalakima aŵili?” 25 Iye anayankha kuti: “Inde.” Ndiyeno Petulo analoŵa m’nyumba, koma iye asanakambe ciliconse, Yesu anamufunsa kuti: “Simoni uganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko amalandila misonkho kwa ndani? Kwa ana awo kapena kwa anthu ena?” 26 Atayankha kuti: “Kwa anthu ena,” Yesu anakamba kuti: “Ndiye kuti anawo sayenela kukhoma msonkho. 27 Koma kuti tisawakhumudwitse, pita ku nyanja ukaponye mbedza pamadzi. Nsomba yoyamba imene ukakole ukaitenge n’kuikanula kukamwa. Ndipo m’kamwamo ukapezamo ndalama ya siliva. Ukaitenge ukakhomele msonkho wanga na wako.”