-
Mvelani Mawu a YehovaNsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2019 | March
-
-
“MUZIMUMVELA”
7. Malinga na Mateyu 17:1-5, ni pa cocitika cina citi pamene Yehova anakamba kucokela kumwamba? Nanga anakamba ciani?
7 Ŵelengani Mateyu 17:1-5. Pa cocitika caciŵili pamene Yehova anakamba kucokela kumwamba, ni panthawi imene Yesu “anasandulika.” Tsiku lina Yesu anatenga Petulo, Yakobo, na Yohane n’kukwela nawo m’phili lalitali. Ali kumeneko, anaona masomphenya ocititsa cidwi. Nkhope ya Yesu na malaya ake zinawala kwambili. Kenako panaonekela anthu ena aŵili, Mose na Eliya. Iwo anayamba kukambilana na Yesu za imfa yake na kuukitsidwa kwake. Atumwiwo anali “atatopa ndi tulo,” koma atagalamuka anaona masomphenya ocititsa cidwi amenewa. (Luka 9:29-32) Ndiyeno, mtambo woyela unawaphimba. Kenako anamvela mawu a Mulungu kucokela mumtambowo. Mofanana na pa ubatizo wa Yesu, panthawiyi Yehova anakambanso mawu oonetsa kuti amakonda Mwana wake na kukondwela naye. Anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwela naye.” Koma panthawiyi, Yehova anawonjezela mawu akuti: “Muzimumvela.”
-
-
Mvelani Mawu a YehovaNsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2019 | March
-
-
9. Ni malangizo othandiza ati amene Yesu anapatsa ophunzila ake?
9 “Muzimumvela.” Pamene Yehova anakamba mawu amenewa, anaonetselatu kuti amafuna kuti tizimvela mawu a Mwana wake. Kodi Yesu anakamba ciani pamene anali padziko lapansi? Anakamba zinthu zambili zofunika kuzimvela. Mwacitsanzo, mwacikondi anaphunzitsa otsatila ake mmene angalalikilile uthenga wabwino, komanso anawakumbutsa mobweleza-bweleza kuti afunika kukhala maso. (Mat. 24:42; 28:19, 20) Cinanso, anawalangiza kuti afunika ‘kuyesetsa mwamphamvu kuloŵa pakhomo lopapatiza,’ ndiponso anawalimbikitsa kuti sayenela kubwelela m’mbuyo. (Luka 13:24) Kuwonjezela apo, Yesu anauzanso otsatila ake kuti afunika kukondana wina na mnzake, kukhalabe ogwilizana, na kusunga malamulo ake. (Yoh. 15:10, 12, 13) Ndithudi, malangizo amenewa anali othandiza kwambili kwa atumwi ake! Ndipo malangizowa ni ofunikanso kwambili kwa ife monga mmene analili pa nthawi imene Yesu anawapeleka.
-