Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
5 Pa nthawi ina, khamu la anthu linali kupanikizana kuti lipite kwa Yesu kukamvetsela mawu a Mulungu. Apo n’kuti iye waimilila m’mbali mwa nyanja ya Genesareti.* 2 Iye anaona mabwato awili okoceza m’mbali mwa nyanjayo. Koma asodzi anali atatulukamo ndipo anali kutsuka maukonde awo. 3 Atalowa mu imodzi ya mabwatowo, imene inali ya Simoni, anamupempha kuti aikankhile m’nyanja pang’ono. Kenako iye anakhala pansi m’bwatomo n’kuyamba kuphunzitsa khamu la anthulo. 4 Atatsiliza kulankhula, anauza Simoni kuti: “Palasila kozama, ndipo muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” 5 Koma Simoni anayankha kuti: “Mlangizi, tagwila nchito usiku wonse, koma sitinaphe kanthu. Komabe poti ndinu mwakamba, ndiponya maukondewa.” 6 Atacita zimenezi, anapha nsomba zambilimbili, moti maukonde awo anayamba kung’ambika. 7 Conco iwo anakodola anzawo amene anali m’bwato linalo kuti abwele kudzawathandiza. Atafika, anadzaza nsombazo m’mabwato onse awili, moti mabwatowo anayamba kumila. 8 Simoni Petulo ataona izi, anagwada pamaso pa Yesu n’kumuuza kuti: “Ambuye cokani pano pali ine cifukwa ndine munthu wocimwa.” 9 Simoni ndi amene anali naye anadabwa kwambili ndi kuculuka kwa nsomba zimene anaphazo. 10 Nawonso ana a Zebedayo, Yakobo ndi Yohane, amene anali kupha nsomba pamodzi ndi Simoni anadabwa kwambili. Koma Yesu anauza Simoni kuti: “Usacite mantha. Kuyambila lelo, uzisodza anthu amoyo.” 11 Pamenepo iwo anakokela mabwatowo ku mtunda, ndipo anasiya zonse n’kuyamba kum’tsatila.
12 Nthawi ina pamene Yesu anali mu mzinda wina, munthu wina wakhate thupi lonse ataona Yesu, anagwada mpaka nkhope yake pansi, ndipo anamucondelela kuti: “Ambuye, ngati mufuna mungandiyeletse.” 13 Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Ndifuna! Khala woyela.” Nthawi yomweyo, khate lake linathelatu. 14 Ndiyeno analamula munthuyo kuti asauze aliyense. Koma anamuuza kuti: “Pita ukadzionetse kwa wansembe, ndipo kaamba ka kuyeletsedwa kwako, ukapeleke nsembe malinga ndi zimene Mose analamula, kuti ukhale umboni kwa iwo.” 15 Koma mbili yake inapitiliza kufalikila, ndipo makamu a anthu anali kusonkhana pamodzi kuti amumvetsele, ndi kuwacilitsa matenda awo. 16 Komabe, nthawi zambili iye anali kupita ku malo kwayekha kukapemphela.
17 Tsiku lina pamene Yesu anali kuphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi a Cilamulo ocokela m’midzi yosiyanasiyana ku Galileya, Yudeya, ndi Yerusalemu, anabwela n’kudzakhala pansi pamenepo. Ndipo Yehova anapatsa Yesu mphamvu kuti athe kucilitsa. 18 Ndiyeno anthu anamubweletsela munthu wofa ziwalo ali pa macila. Ndipo iwo anali kufunafuna njila yomulowetsela mkati kuti amuike pafupi ndi Yesu. 19 Koma popeza kuti njila sanaipeze yomufikitsila pa iye cifukwa ca kuculuka kwa anthu, iwo anakwela pa mtenje n’kupanga cibowo. Kenako anatsitsa munthuyo ali pa macilawo kudzela pa cibowoco. Anamufikitsa pakati pa anthu amene anali pamaso pa Yesu. 20 Iye ataona cikhulupililo cawo anati: “Bwanawe, macimo ako akhululukidwa.” 21 Ndiyeno alembi ndi Afarisi anayamba kufunsana amvekele: “Ameneyu ndani kuti azinyoza Mulungu conci? Ndaninso wina angakhululukile macimo kupatulapo Mulungu?” 22 Koma Yesu atazindikila maganizo awo, anawafunsa kuti: “Mukuganiza ciyani m’mitima yanu? 23 Kodi capafupi n’citi, kukamba kuti ‘Macimo ako akhululukidwa,’ kapena kukamba kuti, ‘Nyamuka uyambe kuyenda?’ 24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu zokhululukila macimo padziko lapansi—” iye anauza munthu wofa ziwaloyo kuti: “Ndikukuuza kuti, Nyamuka, nyamula macila akowa, pita ku nyumba kwanu.” 25 Pamenepo iye anaimilila iwo akuona, n’kunyamula cimene anagonapo. Basi anapita kwawo akutamanda Mulungu. 26 Onsewo anadabwa kwambili ndipo anayamba kutamanda Mulungu. Iwo anacita mantha kwambili, n’kunena kuti: “Koma lelo taona zinthu zodabwitsa!”
27 Izi zitacitika iye anacoka, ndipo anaona munthu wina wokhometsa misonkho dzina lake Levi, atakhala pansi mu ofesi yokhomelamo misonkho. Ndipo anamuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” 28 Iye anasiya zonse, ndipo ananyamuka n’kuyamba kumutsatila. 29 Ndiyeno Levi anakonzela Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake, ndipo kunali anthu ambili okhometsa misonkho komanso ena amene anali kudya nawo.* 30 Afarisi ndi alembi awo ataona izi, anayamba kung’ung’udza n’kufunsa ophunzila ake kuti: “N’cifukwa ciyani mumadya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa misonkho komanso ocimwa?” 31 Yesu anawayankha kuti: “Anthu athanzi safunikila dokotala, koma odwala ndiwo amamufunikila. 32 Ine ndinabwela kudzaitana anthu ocimwa kuti alape, osati olungama.”
33 Iwo anamuuza kuti: “Ophunzila a Yohane amasala kudya kawilikawili, ndipo amapemphela mopembedzela. Ophunzila a Afarisi nawonso amacita cimodzimodzi. Koma ophunzila anu amadya ndi kumwa.” 34 Yesu anawayankha kuti: “Simungauze anzake a mkwati kuti asale kudya pamene mkwatiyo ali nawo limodzi, mungatelo kodi? 35 Koma masiku adzafika ndithu pamene mkwatiyo adzacotsedwa pakati pawo. Ndipo m’masiku amenewo adzasala kudya.”
36 Komanso anawauza fanizo lakuti: “Palibe amene amadula cigamba catsopano pa covala cakunja catsopano n’kucisokelela pa covala cakale. Akatelo, cigamba catsopanoco cimacoka ndipo cigamba ca nsalu yatsopanoco sicigwilizana ndi covala cakale. 37 Komanso palibe amene amathila vinyo watsopano m’matumba acikumba akale. Akatelo, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba a vinyoyo, ndipo vinyoyo amatayika, komanso matumba a vinyowo amawonongeka. 38 Koma vinyo watsopano ayenela kuthilidwa m’matumba acikumba atsopano. 39 Munthu akamwa vinyo wakale, safunanso kumwa watsopano, cifukwa amakamba kuti, ‘Wakale ndi wokoma kwambili.’”