LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • nwt Maliko 1:1-16:8
  • Maliko

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Maliko
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Maliko

UTHENGA WABWINO WOLEMBEDWA NA MALIKO

1 Ciyambi ca uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, 2 monga zinalembedwela m’buku la mneneli Yesaya kuti: “(Taona! Nikutumiza mthenga wanga patsogolo pako,* amene adzakukonzela njila.) 3 Winawake akufuula m’cipululu kuti: ‘Konzani njila ya Yehova! Wongolani misewu yake.’” 4 Yohane M’batizi anali ku cipululu, ndipo anali kulalikila kuti anthu ayenela kubatizika monga cizindikilo ca kulapa kuti macimo awo akhululukidwe. 5 Anthu a mu Yudeya yense na onse a mu Yerusalemu anali kupita kwa iye. Iye anali kuwabatiza* mu Mtsinje wa Yorodani, ndipo iwo anali kuulula macimo awo poyela. 6 Yohane anali kuvala covala ca ubweya wa ngamila na lamba wacikumba m’ciuno mwake. Ndipo anali kudya dzombe na uci. 7 Iye anali kulalikila kuti: “Winawake wamphamvu kuposa ine akubwela m’mbuyo mwanga, ndipo ine sindine woyenela kuŵelama na kumasula nthambo za nsapato zake. 8 Ine nakubatizani na madzi, koma iye adzakubatizani na mzimu woyela.”

9 M’masiku amenewo, Yesu anabwela kucokela ku Nazareti wa ku Galileya, ndipo anabatizidwa na Yohane mu Yorodani. 10 Yesu atangovuuka m’madzimo, anaona kumwamba kukutseguka komanso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzatela pa iye. 11 Ndipo kumwamba kunamveka mawu akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondeka, nimakondwela nawe.”

12 Nthawi yomweyo mzimuwo unamulimbikitsa kupita ku cipululu. 13 Conco anakhalabe ku cipululuko masiku 40, ndipo anali kuyesedwa na Satana. Kumeneko kunalinso nyama za kuchile, koma angelo anali kumutumikila.

14 Tsopano Yohane atamangidwa, Yesu anapita ku Galileya kukalalikila uthenga wabwino wa Mulungu. 15 Anali kulalikila kuti: “Nthawi yoikidwilatu ija yakwana, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikila. Lapani ndipo khulupililani uthenga wabwino.”

16 Iye akuyenda m’mbali mwa Nyanja ya Galileya, anaona Simoni na m’bale wake Andireya akuponya maukonde awo panyanja popeza anali asodzi. 17 Conco Yesu anawauza kuti: “Nitsatileni, ndipo ine nidzakusandutsani asodzi a anthu.” 18 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatila. 19 Atapita patsogolo pang’ono, anaona Yakobo mwana wa Zebedayo na m’bale wake Yohane, akusoka maukonde awo m’bwato, 20 ndipo nthawi yomweyo anawaitana. Pamenepo iwo anasiya tate wawo Zebedayo m’bwatomo pamodzi na aganyu n’kumutsatila. 21 Iwo anapita ku Kaperenao.

Tsiku la Sabata litangoyamba, Yesu anapita kukaloŵa m’sunagoge n’kuyamba kuphunzitsa. 22 Ndipo iwo anadabwa kwambili na kaphunzitsidwe kake, cifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu wa ulamulilo, osati monga alembi. 23 Pa nthawiyo, m’sunagogemo munali mwamuna wina wogwidwa na mzimu wonyansa. Mwamunayo anafuula kuti: 24 “Mufuna ciyani kwa ife, inu Yesu Mnazareti? Kodi mwabwela kudzatiwononga? Ine nikudziŵa bwino kuti ndinu Woyela wa Mulungu!” 25 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala cete, tuluka mwa iye!” 26 Kenako mzimu wonyansawo unacititsa munthuyo kupalapata, ndipo unakuwa mwamphamvu n’kutuluka mwa iye. 27 Anthu onsewo anadabwa kwambili moti anayamba kukambilana, amvekele: “N’ciyani cimeneci? N’ciphunzitso catsopano! Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu, ndipo ikumumvela.” 28 Conco mbili yokamba za iye inawanda mofulumila m’madela onse a cigawo ca Galileya.

29 Kenako, anatuluka m’sunagogemo n’kupita kunyumba kwa Simoni na Andireya, ali pamodzi na Yakobo na Yohane. 30 Pa nthawiyo, apongozi aakazi a Simoni anali gone cifukwa codwala malungo, ndipo mwamsanga iwo anamufotokozela za mayiyo. 31 Yesu anapita pomwe panali mayiyo, ndipo anamugwila dzanja n’kumuutsa. Pamenepo malungowo anathelatu, moti mayiyo anayamba kuwakonzela cakudya.

32 Madzulo dzuŵa litaloŵa, anthu anayamba kumubweletsela odwala onse komanso ogwidwa na ziŵanda. 33 Ndipo anthu onse a mu mzindawo anasonkhana pakhomo la nyumbayo. 34 Zitatelo, iye anacilitsa anthu ambili odwala matenda osiyana-siyana, ndiponso anatulutsa ziŵanda zambili. Koma sanalole kuti ziŵandazo zilankhule, cifukwa zinali kumudziŵa kuti ni Khristu.*

35 M’mamaŵa kukali mdima, iye anauka n’kupita panja kwayekha. Kumeneko anayamba kupemphela. 36 Koma Simoni na amene anali naye anayamba kumufunafuna. 37 Atamupeza anamuuza kuti: “Aliyense akukufunafunani.” 38 Koma iye anawauza kuti: “Tiyeni tipite kwina, ku midzi yapafupi kuti nikalalikilenso kumeneko, cifukwa n’cimene n’nabwelela.” 39 Ndipo anapita kukalalikila m’masunagoge awo m’cigawo conse ca Galileya,·komanso anali kutulutsa ziŵanda.

40 Kumeneko kunabwelanso munthu wina wakhate. Iye anagwada n’kuyamba kumucondelela kuti: “Ngati mufuna munganiyeletse.” 41 Pamenepo Yesu anamva cifundo kwambili, ndipo anatambasula dzanja lake n’kumukhudza. Kenako anati: “Nifuna! Khala woyela.” 42 Nthawi yomweyo khate lake linathelatu moti anakhala woyela. 43 Kenako anamuuza kuti azipita na kumupatsa malangizo amphamvu 44 akuti: “Samala kuti usauzeko aliyense zimenezi. Koma pita ukadzionetse kwa wansembe, ndipo kaamba ka kuyeletsedwa kwako ukapeleke zinthu zimene Mose analamula kuti ukhale umboni kwa iwo.” 45 Koma munthuyo atacoka, anayamba kuilengeza kwambili nkhaniyo na kuifalitsa m’madela ambili. Kaamba ka ici, Yesu sanathenso kuloŵa mu mzinda uliwonse moonekela, koma anali kukhala kunja kumalo opanda anthu. Ngakhale n’telo, anthu anali kubwelabe kwa iye kucokela ku mbali zonse.

2 Koma patapita masiku angapo, iye analoŵanso mu mzinda wa Kaperenao, ndipo anthu anamva kuti ali kunyumba. 2 Conco, anthu ambili anasonkhana m’nyumbamo, moti munalibiletu malo ngakhale pafupi na khomo. Kenako iye anayamba kuwauza uthenga wabwino. 3 Ndiyeno anthu anamubweletsela munthu wofa ziwalo, atanyamulidwa na amuna anayi. 4 Koma iwo sanakwanitse kufikitsa munthuyo pomwe panali Yesu cifukwa ca kuculuka kwa anthu. Conco, anakasula mtenje pamwamba pa malo pomwe panali Yesu, n’kupanga cibowo. Kenako analoŵetselapo macila amene panagona munthu wofa ziwalo uja. 5 Yesu ataona cikhulupililo cawo, anauza wofa ziwaloyo kuti: “Mwanawe, macimo ako akhululukidwa.” 6 Ena mwa alembi anali khale pomwepo, ndipo mu mtima anali kunena kuti: 7 “N’cifukwa ciyani munthu uyu akulankhula conci? Akunyoza Mulungu. Ndani wina angakhululukile munthu macimo kupatulapo Mulungu?” 8 Koma mwa mzimu wake, nthawi yomweyo Yesu anazindikila zimene iwo anali kuganiza m’mitima yawo. Conco anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukuganiza zimenezi m’mitima yanu? 9 Kodi capafupi n’citi, kuuza munthu wofa ziwaloyu kuti, ‘Macimo ako akhululukidwa,’ kapena kukamba kuti, ‘Nyamuka, tenga macila ako uyambe kuyenda’? 10 Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa munthu ali na mphamvu zokhululukila anthu macimo pa dziko lapansi—” Iye anauza wofa ziwaloyo kuti: 11 “Nikukuuza kuti, Nyamuka, nyamula macila akowa, pita ku nyumba kwanu.” 12 Pamenepo munthuyo ananyamuka, ndipo nthawi yomweyo ananyamula macila ake n’kuyamba kuyenda onse akuona. Conco anthu onsewo anadabwa kwambili, ndipo anatamanda Mulungu n’kumati: “Zotelezi sitinazionepo.”

13 Kenako iye anapitanso m’mbali mwa nyanja, ndipo khamu lonse la anthu linali kupitabe kwa iye. Ndiyeno anayamba kuwaphunzitsa. 14 Pamene iye anali kudutsa, anaona Levi mwana wa Alifeyo atakhala pansi mu ofesi yokhomelamo misonkho. Ndipo anamuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” Nthawi yomweyo iye ananyamuka na kumutsatila. 15 Patapita nthawi, Yesu anali kudya m’nyumba ya Levi, ndipo okhometsa misonkho ambili komanso ocimwa anali kudya naye pamodzi na ophunzila ake, cifukwa ambili mwa iwo anali kumutsatila. 16 Koma alembi a Afarisi ataona kuti iye akudya na anthu ocimwa komanso okhometsa misonkho, anayamba kufunsa ophunzila ake kuti: “Kodi munthu ameneyu amadya na okhometsa misonkho komanso ocimwa?” 17 Yesu atamva zimenezi anawauza kuti: “Anthu olimba safunikila dokotala, koma odwala ndiwo amamufunikila. Ine n’nabwela kudzaitana anthu ocimwa, osati olungama.”

18 Ophunzila a Yohane komanso Afarisi anali kusala kudya. Conco iwo anabwela kwa Yesu n’kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ife ophunzila a Yohane komanso ophunzila a Afarisi timasala kudya, koma ophunzila anu sasala kudya?” 19 Yesu anawayankha kuti: “Mkwati akakhala pamodzi na anzake, anzakewo sasala kudya, amatelo kodi? Pa nthawi yonse imene mkwatiyo ali nawo limodzi, iwo sangasale kudya. 20 Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzacotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsikulo adzasala kudya. 21 Palibe munthu amene amasokelela cigamba ca nsalu yatsopano pa covala cakunja cakale. Akatelo, cigamba catsopanoco cimaguza covala cakaleco, ndipo pong’ambikapo pamakula kwambili. 22 Komanso palibe amene amathila vinyo watsopano m’matumba acikumba akale. Akatelo matumba a vinyowo amaphulika, ndipo vinyoyo amatayika, matumbawo n’kuwonongeka. Koma vinyo watsopano amamuthila m’matumba acikumba atsopano.”

23 Pamene iye anali kudutsa m’minda ya tiligu pa Sabata, ophunzila ake anayamba kuthyola ngala za tiligu pamene anali kuyenda. 24 Conco Afarisi anamufunsa kuti: “Onani! N’cifukwa ciyani akucita zosaloleka pa Sabata?” 25 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunaŵelengepo zimene Davide anacita cakudya citamuthela, komanso pamene iye na amuna amene anali naye anamva njala? 26 Nkhani yokamba za Abiyatara wansembe wamkulu, imakamba kuti Davide analoŵa m’nyumba ya Mulungu n’kudya mkate wa cionetselo, ndipo mitanda ina ya mkatewo anapatsako ena mwa amuna amene anali naye. Koma mwalamulo, palibe amene anali kuloledwa kudya mkatewo kupatulapo ansembe.” 27 Kenako Yesu anawauza kuti: “Sabata linakhalapo cifukwa ca munthu, osati munthu kukhalapo cifukwa ca Sabata. 28 Conco Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”

3 Pa nthawi inanso Yesu analoŵa m’sunagoge, ndipo m’sunagogemo munali munthu wina wopuwala* dzanja. 2 Conco Afarisi anali kumuyang’anitsitsa kuti aone ngati angacilitse munthuyo pa Sabata. Colinga cawo cinali cakuti amuimbe mlandu. 3 Ndiyeno Yesu anauza munthu wopuwala* dzanjayo kuti: “Nyamuka bwela apa pakati.” 4 Kenako anawafunsa kuti: “Kodi cololeka n’citi pa Sabata, kucita cabwino kapena coipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anangokhala cete. 5 Yesu anawayang’ana mokwiya ndipo anamva cisoni kwambili poona kuuma mitima kwawo. Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhala bwino. 6 Zitatelo Afarisiwo anatuluka, ndipo nthawi yomweyo anayamba kukambilana na acipani ca Herode zakuti amuphe.

7 Koma Yesu anacoka n’kupita ku nyanja pamodzi na ophunzila ake, ndipo khamu lalikulu la anthu ocokela ku Galileya komanso ku Yudeya linamutsatila. 8 Ngakhalenso anthu ambili ocokela ku Yerusalemu, ku Idumeya, ku tsidya lina la Yorodani komanso kumadela a Turo na Sidoni, anabwela kwa iye atamva zinthu zambili zimene anali kucita. 9 Ndipo iye anauza ophunzila ake kuti amubweletsele bwato laling’ono loti akwelemo kuti khamulo lisam’panikize. 10 Cifukwa cakuti anacilitsa anthu ambili, onse amene anali na matenda aakulu, anamuunjilila kuti angomukhudza. 11 Ngakhale mizimu yonyansa ikamuona inali kudzigwetsa pansi n’kufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” 12 Koma mobweleza-bweleza iye anali kuilamula mwamphamvu kuti isamuulule.

13 Yesu anakwela m’phili n’kuitana anthu amene anali kuwafuna, ndipo iwo anapita kwa iye. 14 Ndiyeno anapanga* gulu la anthu 12, amenenso anawacha atumwi. Anthu amenewa anali oti aziyenda naye komanso kuti aziwatuma kukalalikila 15 na kuwapatsa mphamvu zotulutsa ziŵanda.

16 Ndipo pa gulu la anthu 12 amenewo panali Simoni, amene anamupatsanso dzina lakuti Petulo, 17 Yakobo mwana wa Zebedayo na Yohane m’bale wake wa Yakobo (Aŵiliŵa anawapatsanso dzina lakuti Bowanege, kutanthauza “Ana a Bingu”), 18 Andireya, Filipo, Batulomeyo, Mateyo, Thomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni Kananiya,* 19 komanso Yudasi Isikariyoti amene pambuyo pake anapeleka Yesu.

Ndiyeno iye ataloŵa m’nyumba, 20 khamu la anthu linasonkhananso, moti iwo sanathe ngakhale kudya cakudya. 21 Koma acibale ake atamva nkhaniyi, anapita kukamugwila, cifukwa anali kunena kuti: “Ameneyu wafuntha.” 22 Komanso, alembi amene anacokela ku Yerusalemu anali kunena kuti: “Ali na Belezebule* ndipo amatulutsa ziŵanda na mphamvu za wolamulila ziŵanda.” 23 Conco atawaitana anayamba kulankhula nawo mwa mafanizo kuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24 Ngati ufumu wagaŵikana, ufumuwo sukhalitsa; 25 ndipo ngati nyumba yagaŵikana, nyumbayo singalimbe. 26 Mofanana na zimenezi, ngati Satana wadziukila yekha, ndipo wagaŵikana, iye sangakhalitse koma amenewo adzakhala mapeto ake. 27 Kukamba zoona, palibe aliyense angaloŵe m’nyumba ya munthu wamphamvu kuti amubele katundu, asanayambe wam’manga munthu wamphamvuyo. Akamumanga m’pamene angathe kutenga zinthu m’nyumbamo. 28 Ndithu nikukuuzani kuti, ana a anthu adzakhululukidwa zinthu zonse, kaya anacita macimo otani komanso kaya analankhula mawu onyoza otani. 29 Koma aliyense wonyoza mzimu woyela sadzakhululukidwa kwamuyaya.” 30 Iye anakamba izi cifukwa iwo anali kumunena kuti: “Ali na mzimu wonyansa.”

31 Tsopano amayi ake na abale ake anabwela n’kuimilila panja. Kenako anatuma winawake kuti akamuitane. 32 Panali khamu la anthu limene linakhala pansi momuzungulila, ndipo iwo anamuuza kuti: “Mayi anu na abale anu ali panja ndipo akukufunani.” 33 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi mayi anga na abale anga ndani?” 34 Ndiyeno anayang’ana anthu amene anakhala pansi momuzungulila aja n’kunena kuti: “Ona! Awa ndiwo amayi anga na abale anga! 35 Aliyense wocita cifunilo ca Mulungu ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga, komanso mayi anga.”

4 Yesu anayambanso kuphunzitsa m’mbali mwa nyanja, ndipo cikhamu ca anthu cinasonkhana pafupi na iye. Conco iye anakwela m’bwato n’kukhala m’bwatomo capatali pang’ono na anthuwo. Koma khamu lonse la anthulo linali m’mbali mwa nyanjayo. 2 Iye anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili mwa mafanizo, ndipo powaphunzitsa anawauza kuti: 3 “Tamvelani! Munthu wina anapita kukafesa mbewu. 4 Pamene anali kufesa mbewuzo, zina zinagwela m’mbali mwa msewu, ndipo mbalame zinabwela n’kuzidya. 5 Zina zinagwela pa miyala pomwe panalibe dothi lokwanila, ndipo zinamela mwamsanga cifukwa nthaka inali yosazama. 6 Koma dzuŵa litatentha zinaŵauka, ndipo zinafota cifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwela pa minga, ndipo mingazo zitakula zinalepheletsa mbewuzo kukula moti sizinabale cipatso ciliconse. 8 Koma mbewu zina zinagwela pa nthaka yabwino, ndipo zitamela n’kukula, zinayamba kubala zipatso. Mbewu zina zinabala zipatso 30, zina 60, ndipo zina 100.” 9 Kenako anawonjezela kuti: “Amene ali na matu akumva, amve.”

10 Tsopano pamene Yesu anali payekha, anthu amene anali naye komanso atumwi 12 aja anayamba kumufunsa za mafanizowo. 11 Iye anawauza kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi womvetsa cinsinsi copatulika ca Ufumu wa Mulungu. Koma kwa aja amene ali kunja zinthu zonse zimakambidwa mwa mafanizo, 12 kuti kuyang’ana aziyang’ana ndithu, koma osaona. Kumva azimva ndithu koma osamvetsa tanthauzo lake, komanso kuti asatembenuke n’kukhululukidwa.” 13 Anawauzanso kuti: “Ngati fanizoli simukulimvetsa, ndiye kodi mudzamvetsa bwanji mafanizo ena onse?

14 “Wofesa amafesa mawu. 15 Cotelo mbewu zimene zimagwela m’mbali mwa msewu ni mawu amene amafesedwa mwa anthu omwe amati akangomva mawuwo, Satana amabwela n’kucotsa mawu amene afesedwa mwa iwo. 16 Mofananamo, mbewu zimene zafesedwa pa miyala ni mawu amene amafesedwa mwa anthu amene akangomva mawuwo amawalandila mwacimwemwe. 17 Ngakhale n’telo, mawuwo sazika mizu mwa iwo. Koma anthuwo amapitiliza kwa kanthawi. Ndiyeno cisautso kapena mazunzo akangobwela cifukwa ca mawuwo, iwo amapunthwa. 18 Palinso mbewu zina zimene zimafesedwa pa minga. Mbewu zimenezi ni anthu amene amamva mawu, 19 koma nkhawa za nthawi ino* na cinyengo camphamvu ca cuma komanso kulakalaka zinthu zina zonse, zimaloŵa m’mitima yawo na kulepheletsa mawuwo kukula ndipo sabala zipatso. 20 Cothela, mbewu zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino ni anthu amene amamva mawu na kuwalandila bwino, ndipo amabala zipatso wina 30, wina 60, ndiponso wina 100.”

21 Iye anawauzanso kuti: “Nyale saibwinikila na thadza* kapena kuiika kunsi kwa bedi, amatelo kodi? Kodi saiika pa coikapo nyale? 22 Pakuti palibe cobisika cimene sicidzaululika. Ndipo palibe cobisidwa mosamala kwambili cimene sicidzaonekela poyela. 23 Amene ali na matu akumva, amve.”

24 Anawauzanso kuti: “Mvetselani mosamala zimene mukumva. Muyeso umene mukupimila ena inunso adzakupimilani womwewo. Inde adzakuwonjezelani zoculuka. 25 Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zoculuka, koma aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo.”

26 Iye anapitiliza kukamba kuti: “Ufumu wa Mulungu uli monga mmene munthu amamwazila mbewu pa nthaka. 27 Iye amagona usiku ndipo kukaca amauka. Mbewuzo zimamela na kukula, koma iye sadziŵa mmene izi zimacitikila. 28 Pang’ono-pang’ono, nthakayo payokha imabala zipatso. Umene umayamba ni mmela, kenako ngala, pothela pake maso okhwima m’ngalamo. 29 Koma mbewuzo zikangoti zaca, iye amazimweta na cikwakwa cifukwa nthawi yokolola yakwana.”

30 Ndiyeno anapitiliza kuwauza kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyelekezele na ciyani, kapena tingaufotokoze na fanizo lotani? 31 Uli ngati kanjele ka mpilu kamene pa nthawi yofesa kamakhala kakang’ono kwambili kuposa njele zonse pa dziko lapansi. 32 Koma kakafesedwa kamamela na kukula kwambili kuposa mbewu zina zonse za kudimba. Ndipo kamapanga nthambi zikulu-zikulu, moti mbalame za mumlengalenga zimapeza malo okhala mu mthunzi wake.”

33 Iye analankhula nawo mogwilitsa nchito mafanizo ambili otelo malinga na zimene akanakwanitsa kumvetsa. 34 Ndithudi, sanalankhule nawo popanda fanizo, koma kumbali iye anali kuwafotokozela zinthu zonse ophunzila ake.

35 Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzila ake kuti: “Tiyeni tiwolokele ku tsidya lina la nyanja.” 36 Conco atauza khamu la anthulo kuti lizipita, ophunzilawo anamutenga n’kupita naye m’bwato, mmene analilimo. Pafupi na bwatolo, panalinso mabwato ena. 37 Ndiyeno kunayamba cimphepo camphamvu camkuntho, ndipo mafunde anali kuwomba bwatolo moti linatsala pang’ono kumila. 38 Koma iye anali gone kumbuyo m’bwatomo atasamila pilo. Conco anamuutsa na kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi sizikukukhudzani kuti tikufa?” 39 Pamenepo ananyamuka na kudzudzula mphepoyo, n’kuuza nyanjayo kuti: “Cete! Khala bata!” Mphepoyo inaleka, ndipo panakhala bata lalikulu. 40 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukucita mantha conci? Kodi mulibiletu cikhulupililo mpaka pano?” 41 Koma iwo anacita mantha kwambili, ndipo anayamba kufunsana, amvekele: “Kodi ameneyu ndani makamaka? Ngakhale mphepo na nyanja zikumumvela!”

5 Ndiyeno iwo anafika ku tsidya lina la nyanja m’cigawo ca Agerasa. 2 Yesu atangotsika m’bwato anakumana na munthu wina wogwidwa na mzimu wonyansa akucokela ku manda.* 3 Iye anali kukonda kukhala ku mandako. Kumbuyo konseko, panalibe aliyense amene anakwanitsa kumumanga ngakhale na cheni koma iye osadula. 4 Nthawi zambili anali kumumanga m’matangadza komanso na macheni. Koma anali kudula macheniwo na kuthyola matangadzawo, moti panalibe aliyense amene anali na mphamvu zomugonjetsa. 5 Nthawi zonse usana na usiku anali kufuula ali ku manda komanso m’mapili, ndipo anali kudziceka-ceka na miyala. 6 Koma ataona Yesu capatali anamuthamangila na kumuŵelamila. 7 Ndiyeno anafuula mwamphamvu, amvekele: “Mufuna ciyani kwa ine, inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wapamwambamwamba? Nikukulumbilitsani pali Mulungu kuti musanizunze ayi.” 8 Anafuula motelo cifukwa Yesu anali kuuza mzimuwo kuti: “Tuluka mwa munthuyu iwe mzimu wonyansa.” 9 Koma Yesu anafunsa mzimuwo kuti: “Dzina lako ndani?” Mzimuwo unayankha kuti: “Dzina langa ndine Khamu, cifukwa ndife ambili.” 10 Ndipo unapitiliza kucondelela Yesu kuti asatumize mizimuyo kutali na delalo.

11 Pa nthawiyi, nkhumba zambili zinali kudya kumeneko m’mbali mwa phili. 12 Conco mizimuyo inamucondelela kuti: “Mutitumize m’nkhumba izo, tikaloŵe mmenemo.” 13 Ndipo anailola. Pamenepo mizimu yonyansa ija inatuluka n’kupita kukaloŵa m‘nkhumbazo, ndipo nkhumbazo zinathamangila ku phompho mpaka kukagwela m’nyanja. Nkhumbazo zinalipo pafupifupi 2,000, ndipo zinamila m’nyanjamo. 14 Oŵetela nkhumbazo anathaŵa n’kukafotokozela anthu mu mzinda na m’midzi, ndipo anthuwo anabwela kudzaona zimene zinacitika. 15 Conco anafika kwa Yesu, ndipo anaona munthu amene anali wogwidwa na ciŵanda uja, amene poyamba anali na khamu la mizimu yonyansa. Iwo atamuona ali khale komanso atavala, ndiponso maganizo ake ali bwino-bwino, anacita mantha. 16 Komanso amene anaona zimene zinacitikazo, anafotokozela anthuwo zimene zinacitikila munthu wogwidwa na ziŵandayo, ndiponso nkhumba zija. 17 Cotelo anthuwo anayamba kumucondelela Yesu kuti acoke m’dela lawo.

18 Tsopano pamene Yesu anali kukwela bwato, munthu amene anali wogwidwa na ziŵanda uja anayamba kumucondelela kuti apite naye. 19 Koma Yesu sanamulole. M’malo mwake anamuuza kuti: “Pita ku nyumba ya acibale ako, ndipo ukawauze zonse zimene Yehova wakucitila, komanso cifundo cimene wakuonetsa.” 20 Cotelo munthu uja anapita, ndipo anayamba kufalitsa mu Dekapoli* zonse zimene Yesu anamucitila, ndipo anthu onse anadabwa kwambili.

21 Yesu atawolokelanso ku tsidya lina la nyanja pa bwato, khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye, apo n’kuti iye ali m’mbali mwa nyanjayo. 22 Mmodzi wa atsogoleli a sunagoge dzina lake Yairo anabwela. Ataona Yesu anagwada pa mapazi ake. 23 Kenako iye anamucondelela mobweleza-bweleza kuti: “Mwana wanga wamkazi wamng’ono akudwala kwakaya-kaya.* Conde tiyeni mukaike manja anu pa iye kuti acile n’kukhala na moyo.” 24 Pamenepo Yesu anapita naye, ndipo khamu lalikulu la anthu linali kumutsatila na kumupanikiza.

25 Lomba panali mayi wina amene anali kudwala matenda otaya magazi kwa zaka 12. 26 Madokotala ambili anamucititsa kuti avutike ngako.* Iye anawononga cuma cake conse koma osacila. M’malo mwake, matendawo anali kungokulila-kulila. 27 Atamva mbili ya Yesu, analoŵa m’gulu la anthu n’kupita kumbuyo kwake. Kenako anagwila covala cake cakunja, 28 cifukwa mu mtima anali kunena kuti: “Nikangogwila covala cake cakunja nicila ndithu.” 29 Nthawi yomweyo analeka kutaya magazi, ndipo anamva m’thupi mwake kuti wacila matenda ake aakuluwo.

30 Nthawi yomweyo Yesu anadziŵa kuti mphamvu yatuluka mwa iye, ndipo anaceuka m’gululo n’kufunsa kuti: “Ndani wagwila malaya anga akunja?” 31 Koma ophunzila ake anamuyankha kuti: “Inu mukuona kuti gulu lonseli likukupanikizani, ndiye mukufunsilanji kuti, ‘Ndani wanigwila?’” 32 Koma iye anali kuyang’ana-yang’ana kuti aone amene wacita zimenezi. 33 Mayiyo podziŵa zimene zamucitikila, anacita mantha n’kuyamba kunjenjemela. Ndipo anapita kwa Yesu n’kugwada pamaso pake, n’kumuuza zoona zonse. 34 Kenako iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele, ndipo matenda ako aakuluwo atheletu.”

35 Ali mkati molankhula, amuna ena ocokela ku nyumba ya mtsogoleli uja wa sunagoge anabwela na kumuuza kuti: “Mwana wanu wamwalila! Mulekeni Mphunzitsiyu osamuvutitsa.” 36 Koma Yesu atamva zimene iwo anali kukamba, anauza mtsogoleli wa sunagogeyo kuti: “Usacite mantha, ungokhala na cikhulupililo.” 37 Koma pa nthawiyi sanalolenso aliyense kumutsatila kupatulapo Petulo, Yakobo, na Yohane m’bale wake wa Yakobo.

38 Conco anafika ku nyumba ya mtsogoleli uja wa sunagoge, ndipo anamva ciphokoso ca anthu akulila na kubuma* kwambili. 39 Yesu ataloŵa anawauza kuti: “N’cifukwa ciyani mukulila na kubuma motele? Mwanayu sanamwalile koma wagona.” 40 Anthuwo atamva zimenezi anayamba kumuseka monyodola. Koma atawatulutsa onse, anatenga tate na mayi a mwanayo komanso anthu amene anali naye, n’kuloŵa kumene kunali mwanayo. 41 Kenako, anagwila dzanja la mwanayo n’kumuuza kuti: “Talita kumi,” mawu amene akamasulidwa amatanthauza kuti: “Kamtsikanawe, nikukuuza kuti, uka!” 42 Ndipo nthawi yomweyo, mtsikanayo anauka n’kuyamba kuyenda. (Mtsikanayo anali na zaka 12.) Pamenepo anthuwo anakondwela ngako. 43 Koma mobweleza-bweleza anawalamula* kuti asauzeko ena zimenezo. Kenako anawauza kuti amupatse cakudya mwanayo.

6 Ndiyeno anacoka kumeneko n’kufika ku dela lakwawo, ndipo ophunzila ake anamutsatila. 2 Tsiku la Sabata litafika, iye anayamba kuphunzitsa m’sunagoge. Ndipo anthu amene anali kumumvetsela anadabwa kwambili n’kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti zinthu zimenezi? N’cifukwa ciyani anapatsidwa nzelu zimenezi komanso kuti azicita nchito zamphamvu ngati izi? 3 Kodi ameneyu si kalipentala, mwana wa Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Yudasi na Simoni? Kodi alongo ake sitili nawo konkuno?” Conco anayamba kupunthwa cifukwa ca iye. 4 Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneli salemekezedwa kwawo, ngakhale na acibale ake kapena pa nyumba pake, koma kwina.” 5 Conco iye sanacite nchito zamphamvu zambili kumeneko. Koma anangoika manja ake pa odwala ocepa na kuwacilitsa. 6 Ndithudi, iye anadabwa ataona kusoŵa cikhulupililo kwawo. Cotelo anazungulila m’midzi yapafupi na kumaphunzitsa anthu.

7 Tsopano anaitana ophunzila ake 12 aja n’kuyamba kuwatuma aŵili-aŵili, ndipo anawapatsa ulamulilo pa mizimu yonyansa. 8 Komanso anawalamula kuti asanyamule ciliconse pa ulendowo kupatulapo ndodo. Anawalamulanso kuti asanyamule mkate, cola ca zakudya, kapena ndalama* m’zikwama zawo. 9 Anawauza kuti avale nsapato koma asavale zovala ziŵili.* 10 Anawauzanso kuti: “Nthawi zonse mukaloŵa m’nyumba, muzikhala mmenemo mpaka nthawi yocoka kumeneko. 11 Ndipo kulikonse kumene sadzakulandilani kapena kukumvetselani, pocoka kumeneko muzikutumula fumbi ku mapazi anu kuti ukhale umboni kwa iwo.” 12 Kenako anapita kukalalikila kuti anthu alape, 13 ndipo anatulutsa ziŵanda zambili, komanso anapaka mafuta anthu ambili odwala na kuwacilitsa.

14 Mfumu Herode inamva zimenezi cifukwa dzina la Yesu linachuka kwambili, ndipo anthu anali kunena kuti: “Yohane M’batizi waukitsidwa kwa akufa. Ndiye cifukwa cake akucita nchito zamphamvu.” 15 Koma ena anali kukamba kuti: “Ni Eliya.” Ndipo enanso anali kunena kuti: “Ni mneneli monga analili aneneli akale.” 16 Koma Herode atamva zimenezi anati: “Ndithudi ameneyu ni Yohane uja amene n’namudula mutu. Iye waukitsidwadi.” 17 Popeza Herode ndiye anatuma anthu kukam’gwila Yohane, kumumanga, na kukamuponya m’ndende cifukwa ca Herodiya mkazi wa Filipo m’bale wake, popeza Herodeyo anali atamukwatila. 18 Pakuti Yohane anali kuuza Herode kuti: “N’kosaloleka kuti inu mukwatile mkazi wa m’bale wanu.” 19 Conco Herodiya anamusungila cakukhosi, ndipo anali kufuna kumupha, koma sanathe kucita zimenezo. 20 Herode anali kumuopa Yohane cifukwa anali kudziŵa kuti ni munthu wolungama komanso woyela, ndipo iye anali kum’teteza. Nthawi zonse akamva zokamba za Yohane anali kuthedwa nzelu, koma anapitiliza kumumvetsela mokondwela.

21 Komabe, tsiku lakuti Herodiya akwanilitse zolinga zake linafika. Tsikulo linali lokumbukila kubadwa kwa Herode. Ndipo Herodeyo anaitana nduna zake, akulu-akulu a asilikali na anthu ochuka kwambili a mu Galileya kuti adzadye naye cakudya camadzulo. 22 Ndipo mwana wamkazi wa Herodiya analoŵa n’kuyamba kuvina cakuti anakondweletsa Herode na amene anali kudya naye. Ndiyeno mfumuyo inauza mtsikanayo kuti: “Pempha ciliconse cimene ukufuna, ndipo nikupatsa.” 23 Iye anacita kulumbila kuti: “Ciliconse cimene unipemphe nikupatsa, ngakhale hafu ya ufumu wanga.” 24 Conco mtsikanayo anatuluka n’kukafunsa mayi ake kuti: “Nikapemphe ciyani?” Mayiyo anati: “Kapemphe mutu wa Yohane M’batizi.” 25 Nthawi yomweyo anathamangila kwa mfumuyo n’kupempha kuti: “Nifuna munipatse mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.” 26 Ngakhale kuti mfumu inamva cisoni kwambili na zimenezi, siinafune kunyalanyaza pempho la mtsikanayo cifukwa ca lumbilo lake komanso alendo ake aja.* 27 Conco nthawi yomweyo mfumu inatumiza msilikali womulonda n’kumulamula kuti abweletse mutu wa Yohane. Pamenepo iye anapita kukamudula mutu m’ndendemo, 28 ndipo anaubweletsa m’mbale. Kenako anaupeleka kwa mtsikanayo, ndipo mtsikanayo anapita kukaupeleka kwa mayi ake. 29 Ophunzila ake atamva zimenezi anabwela kudzatenga mtembo wake n’kukauika m’manda.*

30 Atumwi anasonkhana kwa Yesu n’kumufotokozela zonse zimene iwo anacita na kuphunzitsa. 31 Iye anawauza kuti: “Bwelani kuno, tipite kwatokha kuti mukapumuleko pang’ono.” Pakuti anthu ambili anali kubwela na kupita. Ndipo analibe nthawi yopumula ngakhale yoti adye cakudya. 32 Conco anakwela bwato n’kupita kwaokha ku malo opanda anthu. 33 Koma anthu anawaona akupita ndipo ambili anadziŵa zimenezi. Conco anthu ocokela m’mizinda yonse anathamangila kumeneko wapansi, ndipo anakafika kumaloko iwo asanafike. 34 Yesu atatsika m’bwatomo anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvela cisoni cifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Cotelo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.

35 Madzulo dzuŵa litatsala pang’ono kuloŵa, ophunzila ake anafika kwa iye n’kumuuza kuti: “Kuno tili n’kopanda anthu ndipo nthawi yatha kale. 36 Auzeni anthuwa azipita akaloŵe m’midzi yapafupi na m’madela ozungulila kuti akadzigulile cakudya.” 37 Iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse cakudya.” Pamenepo iwo anafunsa kuti: “Kodi tipite tikagule cakudya ca ndalama zokwana madinari 200 n’kuwapatsa anthuwa kuti adye?” 38 Yesu anawafunsa kuti: “Kodi muli na mitanda ingati ya mkate? Pitani mukaone!” Ataiona anati: “Ilipo isanu na nsomba ziŵili.” 39 Kenako anauza anthu onse kuti akhale m’magulu-magulu pa udzu wobiliŵila. 40 Iwo anakhaladi m’magulu a anthu 100 komanso 50. 41 Atatenga mitanda isanu ija na nsomba ziŵili zija, anayang’ana kumwamba n’kupempha dalitso. Kenako ananyema-nyema mitanda ya mkateyo n’kuyamba kuipeleka kwa ophunzila ake kuti apatse anthuwo. Ndipo anagaŵila anthu onsewo nsomba ziŵilizo. 42 Onse anadya n’kukhuta. 43 Zotsala anazisonkhanitsa ndipo zinadzala matadza 12 osaŵelengelako nsomba. 44 Anthu amene anadya mkatewo analipo amuna 5,000.

45 Ndiyeno mwamsanga Yesu anauza ophunzila ake kuti akwele bwato na kupita ku tsidya lina la nyanja ca ku Betsaida, pamene iye anali kuuza anthu kuti azipita. 46 Koma atalailana nawo anapita ku phili kukapemphela. 47 Mdima utayamba kugwa, bwatolo linali pakati pa nyanja koma iye anali yekha kumtunda. 48 Conco atawaona akupalasa bwatolo movutikila cifukwa colimbana na mphepo yamphamvu, anawalondola akuyenda pa nyanja. Apa n’kuti ni m’matandakuca, pafupifupi nthawi ya ulonda wacinayi.* Koma anali kuyenda monga afuna kuwapitilila. 49 Atamuona akuyenda pa nyanjapo anaganiza kuti ni cipuku, ndipo anafuula mokweza. 50 Pakuti onse atamuona anacita mantha. Koma nthawi yomweyo anawauza kuti: “Limbani mtima! Ndine, musacite mantha.” 51 Kenako iye anakwela m’bwatomo ndipo mphepoyo inaleka. Ataona izi, ophunzilawo anadabwa kwambili, 52 cifukwa sanamvetsetse tanthauzo la cozizwitsa ca mitanda ya mkate ija, ndipo m’mitima yawo zinali kuwavutabe kumvetsa.

53 Atawolokela kumtunda, anafika ku Genesareti n’kuimika bwatolo capafupi. 54 Koma iwo atangotuluka m’bwatomo anthu anamuzindikila Yesu. 55 Anthuwo anathamangila ku madela osiyana-siyana a cigawo conseco, n’kuyamba kunyamula anthu odwala pamacila kupita nawo kumene anamva kuti ndiko kuli Yesu. 56 Ndipo nthawi iliyonse akaloŵa m’mudzi kapena mu mzinda, kapenanso m’dela lina, anthu anali kuika odwala m’misika. Iwo anali kumucondelela kuti angogwilako ulusi wopota wa m’mbali mwa covala cake cakunja. Ndipo onse amene anagwila ulusiwo anacila.

7 Tsopano Afarisi na alembi ena amene anacokela ku Yerusalemu anasonkhana kwa Yesu. 2 Ndipo iwo anaona ena mwa ophunzila ake akudya cakudya na manja odetsedwa, kapena kuti cosasamba m’manja.* 3 (Pakuti Afarisi na Ayuda onse sakudya cakudya asanasambe m’manja kufika mu kakonyokonyo.* Iwo amacita izi potsatila mwambo wa makolo awo akale. 4 Ndipo akacoka ku msika, sakudya cakudya asanasambe. Palinso miyambo ina yambili imene iwo analandila ndipo amaitsatila, monga mwambo woviika makapu m’madzi, mitsuko, na ziwiya zakopa.) 5 Conco Afarisi na alembiwo anamufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ophunzila anu sasunga miyambo ya makolo akale, koma amadya cakudya na manja odetsedwa?” 6 Iye anawauza kuti: “Yesaya analosela molondola za onyenga inu pamene analemba kuti, ‘Anthu awa amanilemekeza na milomo yawo cabe, koma mitima yawo ili kutali na ine. 7 Iwo amanipembedza pacabe cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.’ 8 Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu n’kumamatila miyambo ya anthu.”

9 Kuwonjezela apo, iye anawauza kuti: “Mocenjela mumakankhila pambali malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu. 10 Mwa citsanzo, Mose anati, ‘Uzilemekeza atate ako na amayi ako,’ komanso anati, ‘Aliyense wonyoza atate ake kapena amayi ake ayenela kuphedwa.’ 11 Koma inu mumati, ‘Ngati munthu wauza atate ake kapena amayi ake kuti: “Ciliconse cimene nili naco, cimene nikanakuthandizani naco, ni Khobani (kutanthauza mphatso yoyenela kupelekedwa kwa Mulungu),”’ 12 simumulola kucitila atate ake kapena amayi ake ciliconse. 13 Mwa kutelo, mwapangitsa mawu a Mulungu kukhala opanda phindu cifukwa ca miyambo yanu imene munaipeleka kwa anthu. Ndipo mumacita zinthu zambili zotelezi.” 14 Conco ataitananso gulu la anthuwo anawauza kuti: “Nimvetseleni nonsenu, ndipo mumvetsetse tanthauzo lake. 15 Palibe ciliconse cocokela kunja kwa munthu cimene cikaloŵa m’thupi lake cingamudetse. Koma zinthu zimene zimatuluka mwa munthu n’zimene zimamudetsa.” 16* ——

17 Ndiyeno ataloŵa m’nyumba inayake kutali na gulu la anthulo, ophunzila ake anayamba kumufunsa za fanizo lija. 18 Conco anawafunsa kuti: “Kodi inunso simukumvetsa ngati anthu aja? Kodi simukudziŵa kuti palibe ciliconse cocokela kunja kwa munthu cimene cikaloŵa m’thupi mwake cingamudetse? 19 Pakuti siciloŵa mu mtima mwake koma m’mimba, ndipo cimakatuluka ku cimbudzi.” Mwa kukamba zimenezi, Yesu anagamula kuti zakudya zonse n’zoyela. 20 Anakambanso kuti: “Cotuluka mwa munthu n’cimene cimamudetsa. 21 Pakuti mkati, mumtima mwa anthu ni mmene mumatuluka maganizo oipa monga: zaciwelewele,* zakuba, zakupha anthu, 22 zacigololo, dyela, kucita zoipa, cinyengo, khalidwe lotayilila,* diso lakaduka, manyozo, kudzikuza, na kucita zinthu mopanda nzelu. 23 Zinthu zoipa zonsezi zimacokela mumtima mwa munthu ndipo zimamudetsa.”

24 Iye anacoka kumeneko n’kupita kumadela a Turo na Sidoni. Ali kumeneko, analoŵa m’nyumba inayake, ndipo sanafune kuti munthu aliyense adziŵe kuti ali kumeneko. Koma anthu anadziŵabe. 25 Nthawi yomweyo mayi wina amene mwana wake wamng’ono wamkazi anagwidwa na mzimu wonyansa anamva za iye, ndipo anabwela n’kugwada kumapazi ake. 26 Mayiyu anali Mgiriki wacisirofoinike.* Iye anapempha Yesu mobweleza-bweleza kuti atulutse ciŵanda mwa mwana wakeyo. 27 Koma Yesu anamuuza kuti: “Ana ayenela kukhuta coyamba, cifukwa n’kosayenela kutenga cakudya ca ana n’kuponyela tuagalu.” 28 Koma mayiyo anayankha kuti: “N’zoona mbuyanga, koma ngakhale tuagalu tumene tuli pansi pa thebulo tumadya nyenyeswa za anawo.” 29 Pamenepo Yesu anauza mayiyo kuti: “Cifukwa ca zimene wakambazi, pita. Ciŵanda cija catuluka mwa mwana wako.” 30 Conco mayiyo anapita ku nyumba kwake, ndipo anapeza mwana wamng’ono uja ali gone pabedi ciŵanda cija citatuluka.

31 Pamene Yesu anali kubwelela kucokela ku dela la Turo kupita ku Nyanja ya Galileya anapitila m’dela la Sidoni komanso m’cigawo ca Dekapoli.* 32 Kumeneko, anthu anamubweletsela munthu wogontha komanso wosalankhula, ndipo anamucondelela kuti aike dzanja lake pa iye. 33 Ndiyeno anatengela munthuyo pambali capatali na gulu la anthulo. Kenako anapisa zala zake m’matu a munthuyo, ndipo atalavula mata anakhudza lilime la munthuyo. 34 Ndiyeno atayang’ana kumwamba, anafuza mwamphamvu n’kunena kuti: “Efata,” kutanthauza, “Tseguka.” 35 Atakamba izi, makutu ake anatseguka ndipo vuto lake losalankhula linatha, moti anayamba kulankhula bwino-bwino. 36 Ndiyeno anawalamula kuti asauze aliyense zimene zinacitikazo. Koma amati akawalamula mwamphamvu, m’pamenenso anthuwo anali kufalitsa kwambili nkhaniyo. 37 Inde, iwo anazizwa kosaneneka, amvekele: “Wacita zonse bwino-bwino. Akucititsa ngakhale ogontha kumva, na osalankhula kulankhula!”

8 M’masiku amenewo, khamu lalikulu la anthu linasonkhananso, koma linalibe cakudya. Conco Yesu anaitana ophunzila ake n’kuwauza kuti: 2 “Nikuwamvela cifundo anthuwa cifukwa akhala nane masiku atatu, ndipo alibe cakudya. 3 Nikawauza kuti azipita kwawo na njala,* akomoka m’njila, ndipo ena mwa iwo kwawo n’kutali ngako.” 4 Koma ophunzila ake anamuyankha kuti: “Kodi munthu angapeze kuti cakudya cokwanila anthu onsewa kumalo opanda anthu ngati kuno?” 5 Pamenepo iye anawafunsa kuti: “Muli na mitanda ingati ya mkate?” Iwo anati: “Tili nayo 7.” 6 Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako anatenga mitanda 7 ija ya mkate n’kuyamika, pambuyo pake anainyema-nyema n’kuyamba kupatsa ophunzila ake kuti aigaŵile kwa anthuwo. Ndipo iwo anaipeleka kwa anthuwo. 7 Analinso na tunsomba tocepa, ndipo atatudalitsa anauzanso ophunzila ake kuti atugaŵile kwa anthuwo. 8 Conco anadya n’kukhuta, ndipo anasonkhanitsa zotsala zokwana matadza* 7 akulu-akulu. 9 Amene anadya analipo amuna pafupifupi 4,000. Kenako anauza anthuwo kuti azipita.

10 Nthawi yomweyo iye anakwela bwato pamodzi na ophunzila ake n’kupita ku cigawo ca Dalamanuta. 11 Kumeneko, Afarisi anabwela n’kuyamba kukangana naye. Iwo anali kumuumiliza kuti awaonetse cizindikilo cocokela kumwamba pofuna kumuyesa. 12 Conco pomva cisoni iye anafuza mwamphamvu n’kunena kuti: “N’cifukwa ciyani m’badwo uwu ukufuna-funa cizindikilo? Ndithu nikukuuzani, m’badwo uwu sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse.” 13 Atakamba zimenezi, anawasiya n’kukwelanso bwato kupita ku tsidya lina la nyanja.

14 Koma ophunzilawo anaiŵala kunyamula mkate, ndipo analibe cakudya ciliconse m’bwatomo kupatulapo mtanda umodzi wa mkate. 15 Ndipo iye anawacenjeza mosapita m’mbali kuti: “Khalani maso. Ndipo samalani na zofufumitsa za Afarisi komanso zofufumitsa za Herode.” 16 Conco iwo anayamba kukangana pa nkhani yakuti sananyamule mkate. 17 Yesu atadziŵa zimenezi, anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukukangana zakuti mulibe mkate? Kodi mpaka pano simukuzindikila na kumvetsa tanthauzo lake? Kodi mitima yanu ikali yosazindikila? 18 ‘Ngakhale kuti maso muli nawo, kodi simukuona, komanso ngakhale kuti matu muli nawo kodi simukumva?’ Simukukumbukila kodi 19 zimene zinacitika pamene n’nanyema-nyema mitanda isanu ya mkate n’kupatsa amuna 5,000? Kodi zotsala zimene munasonkhanitsa zinakwana matadza angati?” Iwo anayankha kuti: “Matadza 12.” 20 “Nanga pamene n’nanyema-nyema mitanda 7 ya mkate n’kupatsa amuna 4,000, kodi zotsala zimene munasonkhanitsa zinadzala matadza* angati akulu-akulu?” Iwo anamuyankha kuti: “Matadza 7.” 21 Pamenepo iye anawafunsa kuti: “Ndiye kodi simukumvetsabe?”

22 Tsopano anafika ku Betsaida. Kumeneko anthu anamubweletsela munthu wakhungu, ndipo anamucondelela kuti amukhudze munthuyo. 23 Iye anagwila dzanja la munthu wakhunguyo n’kupita naye kunja kwa mudzi. Ndiye atamuthila mata m’maso, anaika manja ake pa iye n’kunena kuti: “Kodi ukuona ciliconse?” 24 Munthuyo anayang’ana kumwamba n’kunena kuti: “Nikuona anthu, koma akuoneka monga mitengo imene ikuyenda.” 25 Iye anagwilanso m’maso mwa munthuyo, ndipo anayamba kuona bwino-bwino. Maso ake anatseguka moti anayamba kuona ciliconse bwino-bwino. 26 Basi anamuuza kuti azipita kunyumba, ndipo anati: “Usaloŵe m’mudzimu.”

27 Lomba Yesu na ophunzila ake ananyamuka kupita ku midzi ya Kaisareya wa ku Filipi. Ali m’njila, anayamba kufunsa ophunzilawo kuti: “Kodi anthu amati ndine ndani?” 28 Iwo anamuyankha kuti: “Amati ndinu Yohane M’batizi. Koma ena amati ndinu Eliya, ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneli.” 29 Ndiyeno anafunsa ophunzilawo kuti: “Nanga inu mumati ndine ndani?” Petulo anamuyankha kuti: “Ndinu Khristu.” 30 Pamenepo anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense za iye. 31 Komanso anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu ayenela kukumana na mavuto ambili ndiponso kukanidwa na akulu, ansembe aakulu komanso alembi, kenako adzaphedwa. Ndipo pambuyo pa masiku atatu adzaukitsidwa. 32 Ndithudi, iye anali kukamba zimenezi poyela. Koma Petulo anamutengela pambali n’kuyamba kumudzudzula. 33 Atamva izi anaceuka n’kuyang’ana ophunzila ake. Kenako anadzudzula Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga Satana! Ndiwe copunthwitsa kwa ine, cifukwa zimene ukuganiza si maganizo a Mulungu koma maganizo a anthu.”

34 Ndiyeno anauza khamu la anthu pamodzi na ophunzila ake kuti abwele kwa iye. Kenako anawauza kuti: “Ngati munthu afuna kunitsatila adzikane yekha, na kunyamula mtengo wake wozunzikilapo* n’kupitiliza kunitsatila. 35 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine komanso cifukwa ca uthenga wabwino, adzaupeza. 36 Kunena zoona, kodi pali phindu lanji munthu kupeza zinthu zonse za m’dzikoli, koma n’kutaya moyo wake? 37 Kapena munthu angapeleke ciyani cosinthanitsa na moyo wake? 38 Pakuti aliyense wocita manyazi na ine komanso na mawu anga mu m’badwo wacigololo* ndiponso wocimwawu, Mwana wa munthu adzacitanso naye manyazi akadzabwela mu ulemelelo wa Atate wake pamodzi na angelo oyela.”

9 Iye anawauzanso kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti pali ena pano amene sadzalaŵa imfa ngakhale pang’ono, mpaka coyamba ataona Ufumu wa Mulungu utayamba kulamulila.” 2 Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo, na Yohane n’kukwela nawo m’phili lalitali kwaokha-okha. Kumeneko, iye anasandulika pamaso pawo. 3 Zovala zake zakunja zinayamba kunyezimila n’kuyela mbee, kuposa mmene wocapa zovala aliyense pa dziko lapansi angaziyeletsele. 4 Komanso Eliya na Mose anaonekela kwa iwo, akulankhula na Yesu. 5 Tsopano Petulo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi,* zili bwino kuti ife tizikhala pompano. Ngati mufuna, ningakhome matenti atatu pano. Ina yanu, ina ya Mose, inanso ya Eliya.” 6 Iye anakamba zimenezi posoŵa cocita, cifukwa onse atatu anacita mantha kwambili. 7 Ndiyeno kunacita mtambo, ndipo unawaphimba. Kenako mu mtambomo munamveka mawu akuti: “Uyu ni Mwana wanga wokondeka. Muzimumvela.” 8 Ndiyeno iwo atayang’ana-yang’ana anangoona kuti palibenso aliyense amene ali nawo, kupatulapo Yesu.

9 Pamene anali kutsika m’philimo, Yesu anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense zimene anaona, mpaka Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa. 10 Iwo anasungadi mawu amenewa mumtima,* koma anali kukambilana tanthauzo la kuuka kwa akufa kumeneku. 11 Ndipo anayamba kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani alembi amakamba kuti Eliya ayenela kubwela coyamba?” 12 Iye anawayankha kuti: “Eliya adzabweladi coyamba ndipo adzabwezeletsa zinthu zonse. Koma n’cifukwa ciyani Malemba amakamba kuti Mwana wa munthu ayenela kukumana na mavuto ambili komanso kucitidwa cipongwe? 13 Koma nikukuuzani kuti Eliya anabwela kale, ndipo anamucita ciliconse cimene anali kufuna monga mmene Malemba amanenela za iye.”

14 Atafika kumene kunali ophunzila ena aja, anaona khamu lalikulu la anthu litawazungulila, ndipo panali alembi amene anali kukangana nawo. 15 Koma anthu onsewo atangomuona anadabwa kwambili, ndipo anam’thamangila kuti akam’patse moni. 16 Conco iye anawafunsa kuti: “Kodi mukukangana nawo ciyani?” 17 Mmodzi m’khamulo anamuyankha nati: “Mphunzitsi, nabweletsa mwana wanga kwa inu, cifukwa ali na mzimu umene umamulepheletsa kulankhula. 18 Nthawi zonse mzimuwo ukamugwila, umamugwetsela pansi. Ndipo amacita thovu kukamwa, n’kumakukuta mano ndipo amafooka. N’napempha ophunzila anu kuti autulutse koma alephela.” 19 Poyankha iye anawauza kuti: “Inu m’badwo wopanda cikhulupililo, nikhalabe nanu mpaka liti? Kodi nikupilileni mpaka liti? M’bweletseni kuno.” 20 Conco anamubweletsa kwa iye. Koma mzimuwo utangoona Yesu, unam’gwetsela pansi mwanayo ndipo anayamba kupalapata. Kenako anayamba kukunkhulika, uku akucita thovu kukamwa. 21 Ndiyeno Yesu anafunsa tate wa mwanayo kuti: “Kodi izi zakhala zikumucitikila kwa nthawi yaitali bwanji?” Tateyo anayankha kuti: “Kuyambila ali wamng’ono, 22 ndipo nthawi zambili umamugwetsela pa moto komanso pa madzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kucitapo kanthu, timveleni cifundo ndipo mutithandize.” 23 Yesu anamuuza kuti: “N’cifukwa ciyani mukukamba kuti, ‘Ngati mungathe’? Zinthu zonse n’zotheka ndithu kwa munthu amene ali na cikhulupililo.” 24 Nthawi yomweyo, tate wa mwanayo anafuula amvekele: “Cikhulupililo nili naco! N’thandizeni kulimbitsa cikhulupililo canga!”

25 Tsopano Yesu poona kuti khamu la anthu likuthamangila kwa iye, anakalipila mzimu wonyansawo nati: “Iwe mzimu wolepheletsa kulankhula komanso wogonthetsa munthu, nikukulamula kuti, tuluka ndipo usadzaloŵenso mwa iye!” 26 Mzimuwo unafuula mokweza na kucititsa mwanayo kupalapata kwambili. Kenako unatuluka. Koma mwanayo anangokhala ngati wafa, moti anthu ambili anali kunena kuti: “Wamwalila!” 27 Koma Yesu anamugwila dzanja mwanayo n’kumuimilitsa, ndipo anaimilila. 28 Ndiyeno ataloŵa m’nyumba, ophunzila ake anamufunsa ali okha kuti: “N’cifukwa ciyani ife tinalephela kutulutsa ciŵanda cija?” 29 Iye anawayankha kuti: “Ciŵanda cotele sicingatuluke popanda pemphelo.”

30 Iwo anacoka kumeneko n’kudutsa m’Galileya. Koma sanafune kuti aliyense adziŵe kumene ali. 31 Pakuti iye anali kuphunzitsa ophunzila ake na kuwauza kuti: “Mwana wa munthu adzapelekedwa m’manja mwa anthu, ndipo iwo adzamupha. Koma ngakhale adzamuphe, iye adzaukitsidwa pambuyo pa masiku atatu.” 32 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la mawu akewo, ndipo anaopa kumufunsa.

33 Ndiyeno anafika ku Kaperenao. Ndipo ali m’nyumba anawafunsa kuti: “Munali kukangana ciyani m’njila?” 34 Koma iwo anangokhala cete, cifukwa m’njila anali kukangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani. 35 Conco anakhala pansi n’kuitana ophunzila ake 12 aja, ndipo anawauza kuti: “Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wothela pa onse komanso mtumiki wa onse.” 36 Kenako anatenga mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo, ndipo anaika manja ake pa mapewa a mwanayo n’kuwauza kuti: 37 “Aliyense wolandila mwana wamng’ono ngati uyu cifukwa ca dzina langa, walandilanso ine. Ndipo aliyense wolandila ine, sanalandile ine nekha, koma walandilanso Iye amene ananituma.”

38 Ndiyeno Yohane anamuuza kuti: “Mphunzitsi, ife tinaona winawake akutulutsa ziŵanda m’dzina lanu, ndipo tamuletsa cifukwa sayenda nafe.” 39 Koma Yesu anati: “Musamuletse, cifukwa palibe aliyense yemwe angacite nchito yamphamvu m’dzina langa, amene mwamsanga angasinthe n’kuyamba kunena zoipa za ine. 40 Cifukwa aliyense amene satsutsana nafe, ali ku mbali yathu. 41 Ndipo aliyense wokupatsani kapu ya madzi kuti mumwe cifukwa cakuti ndinu otsatila a Khristu, ndithu nikukuuzani, iye sadzalephela konse kulandila mphoto yake. 42 Koma aliyense wopunthwitsa mmodzi wa ana aang’ono awa amene ali na cikhulupililo, cingakhale bwino kwambili atam’mangilila cimwala camphelo m’khosi cimene bulu amaguza na kum’ponya m’nyanja.

43 “Ngati dzanja lako limakupunthwitsa, ulidule. Ni bwino kuti ukalandile moyo* ulibe ciwalo cimodzi, kusiyana n’kuti ukapite na manja onse aŵili ku Gehena,* ku moto wosazimitsika. 44* —— 45 Ndipo ngati phazi lako limakupunthwitsa, ulidule. Ni bwino kuti ukalandile moyo uli wolemala, kusiyana n’kuti ukaponyedwe ku Gehena* uli na mapazi onse aŵili. 46* —— 47 Komanso ngati diso lako limakupunthwitsa, ulikolowole. Ni bwino kuti ukaloŵe mu Ufumu wa Mulungu uli na diso limodzi, kusiyana n’kuti ukaponyedwe ku Gehena* uli na maso onse aŵili, 48 kumene mphutsi sizikufa komanso moto suzima.

49 “Monga mmene mcele umathilidwila, aliyense wa anthuwo adzathilidwa moto. 50 Mcele ni wabwino. Koma ngati mcele ungathe mphamvu yake, kodi mphamvuyo mungaibwezeletse na ciyani? Khalani na mcele mwa inu, ndipo sungani mtendele pakati panu.”

10 Yesu atacoka kumeneko, anapita ku madela a ku malile kwa Yudeya, kutsidya lina la Yorodani. Kumeneko, khamu lalikulu la anthu linasonkhananso kwa iye. Ndipo mwa cizoloŵezi cake, iye anayambanso kuwaphunzitsa. 2 Ndiyeno Afarisi anamufikila n’colinga cakuti amuyese. Iwo anamufunsa ngati n’kololeka mwamuna kusudzula mkazi wake. 3 Iye anawafunsa kuti: “Kodi Mose anakulamulani ciyani?” 4 Iwo anati: “Mose analola kuti mwamuna azilembela mkazi wake cikalata ca cisudzulo n’kumuleka.” 5 Koma Yesu anawauza kuti: “Iye anakulembelani lamulo limeneli cifukwa ca unkhutukumve wanu. 6 Komabe, kuyambila pa ciyambi pa cilengedwe, ‘Mulungu anawalenga mwamuna na mkazi. 7 Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya atate ake na amayi ake, 8 ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi.’ Conco iwo salinso aŵili, koma thupi limodzi. 9 Cotelo, cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” 10 Ataloŵanso m’nyumba, ophunzilawo anayamba kumufunsa za nkhaniyi. 11 Iye anawauza kuti: “Aliyense wosudzula mkazi wake n’kukwatila wina, wacita cigololo ndipo akumulakwila mkaziyo. 12 Ndipo ngati mkazi wasudzula mwamuna wake n’kukwatiwa na mwamuna wina, wacita cigololo.”

13 Lomba anthu anayamba kum’bweletsela ana aang’ono kuti awaike manja, koma ophunzila ake anawadzudzula. 14 Yesu ataona izi anakwiya kwambili, ndipo anawauza kuti: “Alekeni anawo abwele kwa ine, musawaletse, cifukwa Ufumu wa Mulungu ni wa anthu amene ali ngati ana amenewa. 15 Ndithu nikukuuzani kuti, aliyense wosalandila Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono, sadzaloŵamo ngakhale pang’ono.” 16 Ndiyeno anakumbatila anawo, kuwaika manja, n’kuyamba kuwadalitsa.

17 Pamene anali kupita, munthu wina anamuthamangila n’kugwada pamaso pake, ndipo anam’funsa kuti: “Mphunzitsi wabwino, kodi niyenela kucita ciyani kuti nikapeze moyo wosatha?” 18 Yesu anamufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ukunichula kuti wabwino? Palibe aliyense wabwino, koma Mulungu yekha. 19 Umadziŵa malamulo akuti: ‘Usaphe munthu, usacite cigololo, usabe, usapeleke umboni wonama, usabe mwacinyengo, ndiponso lakuti uzilemekeza atate ako na amayi ako.’” 20 Munthuyo anayankha kuti: “Mphunzitsi, nakhala nikutsatila malamulo onsewa kuyambila nili mwana.” 21 Yesu anamuyang’ana ndipo anamukonda. Kenako anati, “Cinthu cimodzi cikusoŵeka mwa iwe. Pita ukagulitse zinthu zako, ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatelo udzakhala na cuma kumwamba. Kenako ubwele udzakhale wotsatila wanga.” 22 Koma atamva zimenezi anakhumudwa, ndipo anacoka ali wacisoni cifukwa anali na katundu wambili.

23 Yesu atayang’ana uku na uku, anauza ophunzila ake kuti: “Cidzakhala covuta kwambili anthu a ndalama kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu!” 24 Koma ophunzilawo atamva mawu akewa, anadabwa. Kenako Yesu anati kwa iwo: “Ana inu, cidzakhala covuta kwambili kuti munthu akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu! 25 N’capafupi ngamila kuloŵa pa diso la singano, kusiyana n’kuti munthu wolemela akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” 26 Iwo anadabwa kwambili ndipo anamufunsa* kuti: “Ndiye pali amene angadzapulumuke ngati?” 27 Yesu atawayang’anitsitsa anati: “Kwa anthu n’zosathekadi, koma sizili conco kwa Mulungu, pakuti kwa Mulungu zinthu zonse n’zotheka.” 28 Petulo anayamba kumuuza kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse n’kukutsatilani.” 29 Yesu anati: “Ndithu nikukuuzani, palibe aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, amayi, atate, ana, kapena minda cifukwa ca dzina langa, komanso cifukwa ca uthenga wabwino, 30 amene sadzapeza zoculuka kuŵilikiza maulendo 100 m’nthawi ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana, na minda, pamodzi na mazunzo, ndipo m’nthawi* imene ikubwelayo adzapeza moyo wosatha. 31 Koma ambili amene ni oyamba adzakhala othela, ndipo othela adzakhala oyamba.”

32 Tsopano Yesu na ophunzila ake anali m’njila kupita ku Yerusalemu, ndipo iye anali patsogolo pawo. Ophunzilawo anadabwa kwambili, koma anthu amene anali kumutsatila anayamba kucita mantha. Apanso, Yesu anatengela ophunzila 12 aja pambali, n’kuyamba kuwauza zinthu zimene zinali pafupi kumucitikila. Anati: 33 “Lomba, tikupita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa munthu akapelekedwa kwa ansembe aakulu na alembi. Iwo adzamuweluza kuti aphedwe, komanso adzamupeleka kwa anthu a mitundu ina. 34 Iwo akamucita zacipongwe, akamuthila mata, akamukwapula, na kumupha. Koma pambuyo pa masiku atatu adzaukitsidwa.”

35 Yakobo na Yohane, ana aamuna a Zebedayo anafika kwa iye n’kumuuza kuti: “Mphunzitsi, tifuna muticitile ciliconse cimene tikupempheni.” 36 Iye anawafunsa kuti: “Mufuna nikucitileni ciyani?” 37 Iwo anayankha kuti: “Lolani kuti mmodzi wa ife akakhale ku dzanja lanu lamanja, ndipo wina kumanzele kwanu mu ulemelelo wanu.” 38 Koma Yesu anawauza kuti: “Simudziŵa cimene mukupempha. Kodi mungamwe zimene nikumwa m’kapu iyi, kapena kubatizika na ubatizo umene ine nikubatizika nawo?” 39 Iwo anamuyankha kuti: “Inde tingatelo.” Pamenepo Yesu anawauza kuti: “Za m’kapu zimene ine nikumwa, mudzamwadi. Ndipo mudzabatizikadi na ubatizo umene ine nikubatizika nawo. 40 Koma kusankha munthu wokakhala ku dzanja langa lamanja kapena lamanzele, si udindo wanga. Malo amenewo adzapelekedwa kwa anthu amene anawakonzela malowo.”

41 Ophunzila 10 enawo atamva zimenezi, anamukwiyila kwambili Yakobo na Yohane. 42 Koma Yesu anawaitana n’kuwauza kuti: “Inu mukudziŵa kuti amene amaoneka kuti* akulamulila anthu a mitundu ina amapondeleza anthu awo, ndipo akulu-akulu awo amaonetsa mphamvu zawo pa iwo. 43 Siziyenela kukhala conco pakati panu. Koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. 44 Ndipo aliyense wofuna kukhala woyamba pakati panu, akhale kapolo wa onse. 45 Cifukwa ngakhale Mwana wa munthu sanabwele kudzatumikilidwa, koma kudzatumikila na kudzapeleka moyo wake dipo kuti awombole anthu ambili.”

46 Ndiyeno iwo anafika ku Yeriko. Koma pamene iye na ophunzila ake, komanso gulu lalikulu la anthu, anali kutuluka mu Yeriko, Batimeyu (mwana wa Timeyu), amene anali wopempha-pempha komanso wakhungu, anali atakhala pansi m’mbali mwa msewu. 47 Atamva kuti Yesu Mnazareti ndiye anali kudutsa, anayamba kufuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide, nicitileni cifundo!” 48 Pamenepo anthu ambili anayamba kumudzudzula kuti akhale cete. Koma m’pamene iye anakuwa kwambili, amvekele: “Nicitileni cifundo, inu Mwana wa Davide!” 49 Conco Yesu anaima n’kukamba kuti: “Muitaneni abwele kuno.” Anthuwo anamuitana n’kumuuza kuti: “Limba mtima! Nyamuka, akukuitana.” 50 Iye anangoti covala cake cakunja kuja cii! n’kuimilila mwamsanga kupita kwa Yesu. 51 Ndiyeno Yesu anamufunsa kuti: “Ufuna nikucitile ciyani?” Munthu wakhunguyo anayankha kuti: “Raboni,* nithandizeni niyambe kuona.” 52 Yesu anamuuza kuti: “Pita. Cikhulupililo cako cakucilitsa.” Nthawi yomweyo munthuyo anayamba kuona, ndipo anayamba kumutsatila.

11 Tsopano atayandikila Yerusalemu, anafika pa Phili la Maolivi, kumene kunali Betifage na Betaniya. Ali kumeneko, Yesu anatuma ophunzila ake aŵili 2 n’kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi uwo, ndipo mukangoloŵamo mupeza mwana wa bulu wamphongo amene munthu sanamukwelepo n’kale lonse, atam’mangilila. Mukamumasule n’kumubweletsa kuno. 3 Munthu aliyense akakakufunsani kuti, ‘N’cifukwa ciyani mukucita zimenezi?’ mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna. Ndipo abwela naye akangotsiliza kumuseŵenzetsa.’” 4 Conco anapita ndipo anapezadi mwana wa bulu atamumangilila pakhomo kunja m’mbali mwa njila, ndipo anam’masula. 5 Koma ena amene anaimilila pamenepo anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukum’masula buluyu?” 6 Iwo anawauza zimene Yesu anakamba ndipo anawalola kupita.

7 Ndiyeno mwana wa buluyo anabwela naye kwa Yesu. Kenako anayanzika zovala zawo zakunja pa buluyo, ndipo Yesu anakwelapo. 8 Komanso anthu ambili anayanzika zovala zawo zakunja mu msewu, koma ena anali kudula zitsamba m’minda. 9 Ndiponso anthu amene anali patsogolo na pambuyo pake anali kufuula kuti “Mpulumutseni! Wodalitsika ni iye wobwela m’dzina la Yehova! 10 Wodala ni Ufumu wa atate wathu Davide umene ukubwela! Mpulumutseni inu amene muli kumwambamwambako!” 11 Iye ataloŵa mu Yerusalemu anapita kukaloŵa m’kacisi, ndipo anayang’ana-yang’ana zinthu zonse mmenemo. Koma popeza nthawi inali itatha kale, anacoka n’kupita ku Betaniya pamodzi na atumwi ake 12 aja.

12 Tsiku lotsatila pamene anali kucoka ku Betaniya anamva njala. 13 Ali capatali, anaona mtengo wa mkuyu umene unali na masamba, ndipo anapitako kuti akaone ngati angapezemo kanthu. Koma atafika pa mtengowo sanapezemo ciliconse koma masamba okha-okha cifukwa sinali nthawi ya nkhuyu. 14 Conco anauza mtengowo kuti: “Munthu asadzadyenso zipatso zako mpaka kale-kale.” Ndipo ophunzila ake anali kumva.

15 Tsopano iwo anafika ku Yerusalemu. Kumeneko, analoŵa m’kacisi ndipo anayamba kupitikitsila panja anthu omwe anali kugulitsa na kugula zinthu m’kacisimo. Komanso anagudubula matebulo a osintha ndalama na mabenchi a ogulitsa nkhunda. 16 Ndipo sanalole aliyense kupitila pa kacisi atanyamula ciwiya ciliconse. 17 Iye anali kuwaphunzitsa na kuwauza kuti: “Kodi si paja Malemba amanena kuti, ‘Nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphelelamo anthu a mitundu yonse’? Koma inu mwaisandutsa phanga la acifwamba.” 18 Ansembe aakulu na alembi atamva zimenezi, anayamba kufuna-funa njila yomuphela cifukwa iwo anali kumuopa, popeza khamu lonse la anthu linali kudabwa na kaphunzitsidwe kake.

19 Pa tsikulo ca kumadzulo, iwo anatuluka mumzindawo. 20 Koma m’mamaŵa pamene anali kudutsa, anaona kuti mtengo wa mkuyu uja wafota kale na mizu yake yomwe. 21 Petulo ataukumbukila mtengowo, anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi* onani! Mtengo wa mkuyu uja munautembelela wafota.” 22 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Muzikhulupilila Mulungu. 23 Ndithu nikukuuzani kuti ngati aliyense angauze phili ili kuti, ‘Nyamuka ukadziponye m’nyanja,’ ndipo sakayikila mumtima mwake, koma ali na cikhulupililo pa zimene wakamba kuti zidzacitika, zidzacitikadi. 24 Ndiye cifukwa cake nikukuuzani kuti pa zinthu zonse zimene mumapemphela na kupempha, khalani na cikhulupililo ngati kuti mwazilandila kale, ndipo mudzazilandiladi. 25 Komanso mukaimilila kuti mupemphele muzikhululukila aliyense pa ciliconse cimene anakulakwilani, kuti nayenso Atate wanu wa kumwamba akukhululukileni macimo anu.” 26* ——

27 Iwo anafikanso ku Yerusalemu. Ndipo pamene anali kuyenda mu kacisi, ansembe aakulu, alembi, na akulu anafika kwa iye, 28 ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ulamulilo wocita zimenezi munautenga kuti? Nanga ndani anakupatsani ulamulilo wocita zimenezi?” 29 Yesu anawayankha kuti: “Nikufunsani funso limodzi. Muniyankhe, ndipo mukatelo, nikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi. 30 Kodi ubatizo wa Yohane unacokela kumwamba kapena kwa anthu?* Niyankheni.” 31 Conco iwo anayamba kukambilana n’kumati: “Tikanena kuti, ‘Unacokela kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’cifukwa ciyani simunamukhulupilile?’ 32 Koma kodi tinganene kuti, ‘Unacokela kwa anthu’?” Iwo anali kuopa khamu la anthu, cifukwa anthu onsewo anali kukhulupilila kuti Yohane analidi mneneli. 33 Conco pomuyankha Yesu, iwo anati: “Sitidziŵa.” Yesu anati: “Inenso sinikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi.”

12 Ndiyeno anayamba kukamba nawo mwa mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa n’kumanga mpanda kuzungulila mundawo. Ndipo anakumba dzenje lopondelamo mphesa na kumanga nsanja. Kenako anausiya m’manja mwa alimi n’kupita ku dziko lina. 2 Nyengo yokolola itakwana, iye anatuma kapolo wake kwa alimiwo kuti akatengeko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo. 3 Koma iwo anamugwila n’kumumenya, ndipo anamubweza cimanjamanja. 4 Iye anatumanso kapolo wina kwa iwo, ndipo ameneyo anamutema m’mutu na kumucita zacipongwe. 5 Anatumanso wina, ndipo ameneyo anamupha. Komanso anatuma ena ambili, ndipo ena a iwo anawamenya, ena anawapha. 6 Ndiyeno anatsala na mmodzi yekha woti atume, mwana wake wokondeka. Pothela, iye anatuma mwanayo n’kunena kuti, ‘Mwana wangayu akamulemekeza.’ 7 Koma alimiwo anayamba kukambilana kuti, ‘Eya! Uyu ndiye wolandila coloŵa. Bwelani, tiyeni timuphe ndipo coloŵaci cidzakhala cathu.’ 8 Conco iwo anamugwila n’kumupha. Kenako anamutayila kunja kwa munda wa mpesawo. 9 Kodi mwinimundayo adzacita ciyani? Adzabwela n’kupha alimiwo ndipo adzapeleka mundawo kwa ena. 10 Kodi simunaŵelengepo zimene lemba limanena? Paja limati: ‘Mwala umene omanga anaukana, wakhala mwala wa pakona wofunika kwambili.* 11 Umenewu wacokela kwa Yehova, ndipo ni wodabwitsa m’maso mwathu’.”

12 Atamva zimenezi anafuna kumugwila,* cifukwa anadziŵa kuti iye anali kunena za iwo pokamba fanizo limeneli. Koma poopa khamu la anthu, anangomuleka n’kucokapo.

13 Kenako anamutumizila ena mwa Afarisi komanso a cipani ca Herode kuti akamutape m’kamwa. 14 Iwo atafika, anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tidziŵa kuti mumakamba zoona komanso simukondela cifukwa simuyang’ana maonekedwe a anthu, koma mumaphunzitsa njila ya Mulungu m’coonadi. Kodi n’kololeka* kupeleka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi tiyenela kupeleka kapena ayi?” Atazindikila cinyengo cawo, anawauza kuti: “N’cifukwa ciyani mukuniyesa? Bweletsani khobili la Dinari nilione.” 16 Iwo anamubweletsela khobili limodzi, ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi cithunzi ici na mawu awa ni za ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ni za Kaisara.” 17 Ndiyeno Yesu anati: “Pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.” Ndipo anthuwo anadabwa naye kwambili.

18 Tsopano Asaduki amene amati kulibe kuuka kwa akufa anabwela n’kumufunsa kuti: 19 “Mphunzitsi, Mose anatilembela kuti ngati munthu wamwalila n’kusiya mkazi koma sanabeleke naye mwana, m’bale wake wa munthuyo ayenela kukwatila mkazi wamasiyeyo na kumubelekela ana m’bale wake uja. 20 Lomba panali amuna 7 a pacibale. Woyamba anakwatila mkazi, koma anamwalila asanabeleke naye mwana mkaziyo. 21 Waciŵili anamukwatila mkaziyo, koma nayenso anamwalila asanabeleke naye mwana. N’zimenenso zinacitikila mwamuna wacitatu. 22 Ndipo amuna onse 7 anamwalila osabeleka naye mwana. Pothela pake, mkazi uja nayenso anamwalila. 23 Pamene akufa adzauka, kodi mkaziyo adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatilapo?” 24 Yesu anawauza kuti: “Simudziŵa Malemba kapena mphamvu za Mulungu, ndiye cifukwa cake mukuganiza molakwika. 25 Pakuti anthu akadzauka kwa akufa, amuna sadzakwatila ndipo akazi sadzakwatiwa koma adzakhala ngati angelo a kumwamba. 26 Koma pa nkhani yakuti akufa adzauka, kodi simunaŵelenge m’buku la Mose pa nkhani yokamba za citsamba ca minga, kuti Mulungu anamuuza kuti: ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki, komanso Mulungu wa Yakobo’? 27 Iye si Mulungu wa akufa ayi, koma wa anthu amoyo. Maganizo anu ni olakwika kwambili.”

28 Mmodzi wa alembi amene anabwela anawamva akutsutsana. Podziŵa kuti Yesu anawayankha bwino Asadukiwo, iye anamufunsa kuti: “Kodi lamulo loyamba* pa malamulo onse ni liti?” 29 Yesu anamuyankha kuti: “Lamulo loyamba n’lakuti, ‘Mvelani inu Aisiraeli, Yehova Mulungu wathu ni Yehova mmodzi basi. 30 Ndipo uzikonda Yehova Mulungu wako na mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse, na mphamvu zako zonse.’ 31 Laciŵili ni ili, ‘Uzikonda munthu mnzako mmene umadzikondela wekha.’ Palibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” 32 Mlembiyo anamuuza kuti: “Mphunzitsi mwakamba bwino mogwilizana na coonadi, ‘Iye ni mmodzi basi ndipo palibenso wina kupatulapo iye.’ 33 Ndipo kumukonda na mtima wathu wonse, nzelu zathu zonse, na mphamvu zathu zonse komanso kukonda munthu mnzathu mmene timadzikondela n’kofunika kwambili. Zimenezi zimaposa nsembe zonse zonyeketsa zathunthu na nsembe zina.” 34 Yesu ataona kuti mlembiyo wayankha mwanzelu anamuuza kuti: “Suli kutali na Ufumu wa Mulungu.” Ndipo palibe amene analimbanso mtima kumufunsa mafunso.

35 Komabe, pamene Yesu anali kuphunzitsa m’kacisi ananena kuti: “N’cifukwa ciyani alembi amakamba kuti Khristu ni mwana wa Davide? 36 Motsogoleledwa na mzimu woyela, Davide iyemwini anati, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala ku dzanja langa lamanja kufikila n’taika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’ 37 Ngati Davideyo akumucha Ambuye, zitheka bwanji iye kukhala mwana wake?”

Ndipo khamu lalikulu la anthu linali kumumvetsela mokondwela. 38 Pophunzitsa, Yesu anakambanso kuti: “Samalani na alembi amene amafuna kumayendayenda atavala mikanjo, amenenso amafuna kupatsidwa moni m’misika. 39 Iwo amafunanso kukhala pa mipando yakutsogolo* m’masunagoge, komanso pamalo olemekezeka kwambili pa cakudya camadzulo. 40 Amalanda cuma ca akazi* amasiye komanso amapeleka mapemphelo atali-atali pofuna kudzionetsela.* Amenewa adzalandila cilango coŵaŵa* kwambili.”

41 Ndiyeno anakhala pansi atayang’ana kumene kunali coponyamo zopeleka. Iye anayamba kuona mmene gulu la anthu linali kuponyela ndalama mmenemo. Ndipo anthu ambili olemela anali kuponyamo makobili ambili. 42 Kenako kunabwela mkazi wamasiye wosauka n’kuponyamo tumakobili tuŵili tocepa mphamvu kwambili. 43 Conco iye anaitana ophunzila ake n’kuwauza kuti: “Ndithu nikukuuzani, mayi wamasiye wosaukayu waponya zambili kuposa ena onse amene aponya ndalama moponya zopelekamu. 44 Pakuti onsewa aponya zimene atapa pa zoculuka zimene ali nazo, koma mayiyu ngakhale kuti ni wosauka, wapeleka zonse zimene anali nazo, zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”

13 Pamene Yesu anali kutuluka m’kacisi, mmodzi wa ophunzila ake anamuuza kuti: “Mphunzitsi, onani kukongola kwa miyalayi na nyumbazi!” 2 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Kodi waziona nyumba zikulu-zikulu zokongolazi? Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”

3 Atakhala pansi m’Phili la Maolivi, moyang’ana kumene kunali kacisi, Petulo, Yakobo, Yohane, na Andireya anamufunsa mwamseli kuti: 4 “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti? Nanga cizindikilo cakuti zinthu zonsezi zili pafupi kufika kumapeto cidzakhala ciyani?” 5 Conco, Yesu anayamba kuwauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusoceletseni. 6 Ambili adzabwela m’dzina langa n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasoceletsa anthu ambili. 7 Ndiponso mukadzamva phokoso la nkhondo komanso mbili za nkhondo, musadzacite mantha. Zimenezi ziyenela kucitika, koma mapeto adzakhala asanafikebe.

8 “Mtundu udzaukilana na mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana na ufumu wina. Kudzakhala zivomezi m’malo osiyana-siyana, komanso kudzakhala njala. Zinthu zonsezi ni ciyambi ca masautso.*

9 “Koma inu samalani. Anthu adzakupelekani ku makhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge na kukupelekani kwa abwanamkubwa na mafumu cifukwa ca ine, kuti ukhale umboni kwa iwo. 10 Komanso uthenga wabwino uyenela kulalikidwa ku mitundu yonse coyamba. 11 Ndipo akakutengani kuti akakupelekeni, musade nkhawa kuti mukakamba ciyani. Koma mukakambe zilizonse zimene mudzapatsidwa nthawi yomweyo, pakuti amene adzakamba si inuyo ayi, koma mzimu woyela. 12 Komanso munthu adzapeleka m’bale wake kuti aphedwe, tate adzapeleka mwana wake, ndipo ana adzaukila makolo awo n’kuwapeleka kuti aphedwe. 13 Anthu onse adzakudani cifukwa ca dzina langa. Koma amene adzapilile* mpaka pa mapeto adzapulumuka.

14 “Koma mukadzaona cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko citaimilila pa malo amene siciyenela kuima (woŵelenga adzazindikile), pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthaŵila ku mapili. 15 Munthu amene adzakhale pa mtenje asadzatsike kapena kuloŵa m’nyumba mwake kuti akatenge cinthu ciliconse. 16 Ndipo munthu amene adzakhale ku munda, asadzabwelele ku zinthu zimene wasiya kumbuyo kuti akatenge covala cake cakunja. 17 Tsoka kwa akazi apathupi komanso oyamwitsa m’masiku amenewo! 18 Pitilizani kupemphela kuti zimenezi zisadzacitike m’nyengo yozizila, 19 cifukwa masiku amenewo kudzakhala cisautso cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca cilengedwe cimene Mulungu analenga mpaka pa nthawiyo, ndipo sicidzacitikanso. 20 Kukamba zoona, Yehova akanapanda kucepetsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma cifukwa ca osankhidwa amene iye wawasankha, adzacepetsa masikuwo.

21 “Komanso munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena kuti, ‘Onani! Ali uko,’ musakakhulupilile. 22 Pakuti kudzabwela anthu onamizila kukhala Khristu komanso aneneli onyenga, ndipo adzacita zizindikilo na zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, asoceletse osankhidwawo. 23 Conco samalani. Ine nakuuzilantoni zinthu zonse.

24 “Koma m’masiku amenewo cisautsoco cikadzatha, dzuŵa lidzacita mdima, ndipo mwezi sudzawala. 25 Komanso nyenyezi zidzagwa kucokela kumwamba, ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka. 26 Ndiyeno iwo adzaona Mwana wa munthu akubwela m’mitambo, ali na mphamvu zazikulu komanso ulemelelo. 27 Kenako iye adzatumiza angelo ake ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela ku mphepo zinayi, kucokela ku malekezelo a dziko mpaka ku malekezelo a kumwamba.

28 “Tsopano phunzilamponi kanthu pa fanizo ili la mtengo wa mkuyu. Mukangoona kuti nthambi yake yanthete yayamba kuphuka na kutulutsa masamba, mumadziŵa kuti dzinja layandikila. 29 Mofananamo, inunso mukadzaona zinthu zimenezi zikucitika, mukadziŵe kuti iye ali pafupi, pa khomo penipeni. 30 Ndithu nikukuuzani, m’badwo uwu sudzatha wonse mpaka zinthu zonsezi zitacitika. 31 Kumwamba na dziko lapansi zidzacoka, koma mawu anga sadzacoka ayi.

32 “Ponena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene adziŵa, ngakhale angelo kumwamba kapena Mwanayo, koma Atate yekha basi. 33 Khalani maso, khalani chelu, cifukwa nthawi yoikika simukuidziŵa. 34 Zili monga munthu amene anasiya nyumba yake n’kupita ku dziko lina, ndipo anapatsa akapolo ake ulamulilo. Aliyense anamupatsa nchito yake, komanso analamula mlonda wa pakhomo kuti akhalebe maso. 35 Conco khalanibe maso cifukwa simukudziŵa nthawi imene mwininyumba adzabwela, kaya ni madzulo, pakati pa usiku, m’matandakuca* kapena m’mamaŵa, 36 kuti iye akadzabwela modzidzimutsa, asadzakupezeni mutagona. 37 Koma zimene nikukuuzani nikuuza onse kuti: Khalanibe maso.”

14 Tsopano kunali kutatsala masiku aŵili kuti Pasika komanso Cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa zicitike. Ndiyeno ansembe aakulu na alembi anali kufuna-funa njila yakuti amugwile* Yesu mocenjela na kumupha. 2 Koma iwo anali kunena kuti: “Tisakamugwile pa cikondwelelo, cifukwa anthu angadzacite cipolowe.”*

3 Pamene Yesu anali kudya m’nyumba ya Simoni amene anali wakhate ku Betaniya, kunabwela mayi wina atanyamula botolo la mwala wa alabasitala, mmene munali mafuta onunkhila odula kwambili, nado weniweni. Iye anatsegula botolo limenelo mocita kuphwanya, n’kuyamba kuthila mafutawo pa mutu pa Yesu. 4 Ena ataona izi, anayamba kukambilana mokwiya kuti: “N’cifukwa ciyani akuwononga mafuta onunkhilawa? 5 Pakuti mafuta onunkhilawa akanagulitsidwa madinali oposa 300, ndipo ndalamazo zikanapelekedwa kwa osauka!” Iwo anakhumudwa naye kwambili* mayiyo. 6 Koma Yesu anati: “Mulekeni. N’cifukwa ciyani mukumuvutitsa? Zimene iyeyu wanicitila n’zabwino. 7 Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse, ndipo mungawacitile zabwino nthawi iliyonse imene mufuna. Koma ine simudzakhala nane nthawi zonse. 8 Mayiyu wacita zimene angathe. Iye wathililatu mafuta onunkhila pa thupi langa pokonzekela kuikidwa m’manda kwanga. 9 Ndithu nikukuuzani kuti, kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse, anthu azikafotokozanso zimene mayiyu wacita pomukumbukila.”

10 Ndiyeno Yudasi Isikariyoti, mmodzi wa atumwi 12 aja anapita kwa ansembe aakulu kuti akapeleke Yesu kwa iwo. 11 Iwo atamva za nkhaniyo, anakondwela ndipo anamulonjeza kuti adzamupatsa ndalama zasiliva. Conco iye anayamba kufuna-funa mpata wabwino woti amupeleke.

12 Tsopano pa tsiku loyamba la cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa, pamene anali kupeleka nsembe za Pasika, ophunzila ake anamufunsa kuti: “Mufuna tipite kukakukonzelani kuti malo odyelako Pasika?” 13 Pamenepo Yesu anatuma ophunzila ake aŵili n’kuwauza kuti: “Pitani mu mzinda, ndipo mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi adzakumana nanu. Mukamutsatile, 14 ndipo akakaloŵa m’nyumba mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi wakamba kuti: “Kodi cipinda ca alendo cili kuti, cimene ningadyelemo Pasika pamodzi na ophunzila anga?”’ 15 Iye adzakuonetsani cipinda cacikulu cam’mwamba, cokonzedwa bwino. Mukatikonzele Pasika m’cipindaco.” 16 Conco ophunzilawo anapita. Iwo ataloŵa mu mzindawo, zinacitikadi mmene Yesu anawauzila, ndipo anakonza zonse zofunikila za Pasika.

17 Nthawi yamadzulo, Yesu anabwela pamodzi na atumwi ake 12 aja. 18 Ndiyeno pamene iwo anali kudya pathebulo, Yesu anawauza kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti mmodzi wa inu, amene akudya nane pamodzi, anipeleka.” 19 Iwo anayamba kumva cisoni kwambili, ndipo aliyense wa iwo anayamba kumufunsa kuti: “Ndine kapena?” 20 Iye anawauza kuti: “Ni mmodzi wa inu 12, amene akusunsa nane pamodzi m’mbalemu. 21 Pakuti Mwana wa munthu akupita, monga mmene Malemba amakambila za iye. Koma tsoka kwa munthu amene apeleke Mwana wa munthu! Cikanakhala bwino munthu ameneyo akanapanda kubadwa.”

22 Akupitiliza kudya, anatenga mtanda wa mkate, ndipo atayamika anaunyema-nyema n’kuupeleka kwa iwo. Kenako anati: “Aneni, mkate uwu ukuimila thupi langa.” 23 Ndiyeno anatenga kapu n’kuyamika, ndipo anapatsa ophunzila ake moti onse anamwa za m’kapuyo. 24 Kenako anawauza kuti: “Vinyoyu akuimila ‘magazi anga a cipangano,’ amene adzakhetsedwa kaamba ka anthu ambili. 25 Ndithu nikukuuzani, sinidzamwanso cakumwa ciliconse cocokela ku mphesa, kufikila tsiku limene nidzamwa cakumwa catsopano pamodzi na inu mu Ufumu wa Mulungu.” 26 Pa mapeto pake, iwo atatsiliza kuimba nyimbo za citamando,* anapita ku Phili la Maolivi.

27 Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthaŵa n’kunisiya nekha, cifukwa Malemba amanena kuti: ‘Nidzapha m’busa ndipo nkhosa zake zidzamwazikana.’ 28 Koma nikadzaukitsidwa, nidzatsogola kupita ku Galileya inu musanafike kumeneko.” 29 Koma Petulo anamuuza kuti: “Ngakhale ena onsewa atathaŵa n’kukusiyani, ine sinidzathaŵa.” 30 Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Ndithu nikukuuza kuti lelo, inde, usiku wa lelo, tambala asanalile kaŵili, iwe unikana katatu.” 31 Koma iye anapitiliza kunena kuti: “Ngati n’kufa tifela pamodzi, ndipo siningakukaneni ngakhale pang’ono.” Komanso ophunzila ena onsewo anayamba kukamba cimodzimodzi.

32 Ndiyeno iwo anafika pa malo ochedwa Getsemani, ndipo Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Khalani pansi pompano, ine nipita kukapemphela.” 33 Popita kumeneko anatenga Petulo, Yakobo, na Yohane, ndipo iye anayamba kumva cisoni na kuvutika kwambili mumtima. 34 Ndiyeno anawauza kuti: “Nili na cisoni* cofa naco. Khalani pano ndipo mukhalebe maso.” 35 Atapitako patsogolo pang’ono, anagwada pansi n’kuyamba kupemphela kuti ngati n’kotheka ola limenelo limupitilile. 36 Kenako anati: “Abba,* Atate, zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Nicotseleni kapuyi, osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.” 37 Atabwelela anawapeza akugona, ndipo anafunsa Petulo kuti: “Simoni, n’cifukwa ciyani ukugona? Kodi unalibe mphamvu zokhalabe maso kwa ola limodzi? 38 Khalanibe maso, ndipo pitilizani kupemphela kuti musaloŵe m’mayeselo. Zoona, mzimu ni wofunitsitsa,* koma thupi n’lofooka.” 39 Ndipo anapitanso kukapemphela, akubweleza zinthu zimodzimodzi. 40 Atabwelelanso anawapeza akugona, cifukwa zikope zawo zinali zitalemela. Ndipo iwo anasoŵa comuyankha. 41 Anabwelelanso kacitatu, ndipo anawauza kuti: “Zoona pa nthawi ngati ino mukugona na kupumula! Basi kwatha! Ola lija lafika! Onani! Mwana wa munthu akupelekedwa m’manja mwa anthu ocimwa. 42 Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wonipeleka uja ali pafupi.”

43 Nthawi yomweyo ali mkati molankhula, Yudasi mmodzi wa atumwi 12 aja anafika pamodzi na khamu la anthu lotumidwa na ansembe aakulu, alembi, komanso akulu. Anthuwo anali atanyamula malupanga na nkholi. 44 Pa nthawiyo, womupelekayo anali atawapatsa cizindikilo cakuti: “Amene nikam’psompsone, ni ameneyo. Mukamugwile n’kupita naye ndipo musakamutaye.” 45 Ndiyeno Yudasi analunjika pamene panali Yesu. Atafika pa iye ananena kuti, “Mphunzitsi!”* Kenako anam’psompsona mwacikondi. 46 Conco anthuwo anamugwila na kumumanga. 47 Koma wina mwa amene anaimilila naye pafupi, anasolola lupanga lake n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kumudula khutu. 48 Koma Yesu anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mwabwela kudzanigwila mutanyamula malupanga na nkholi, ngati kuti mukubwela kudzagwila wacifwamba? 49 Tsiku lililonse n’nali kukhala nanu m’kacisi n’kumaphunzitsa, koma simunanigwile. Koma izi zacitika kuti Malemba akwanilitsidwe.”

50 Ndiyeno ophunzila ake onse anang’ondoka n’kuthaŵa kumusiya yekha. 51 Koma mnyamata wina amene anangofunda nsalu yabwino pathupi lake lamalisece, anayamba kumutsatila capafupi. Ndipo anthuwo anayesa kumugwila, 52 koma iye anasiya nsalu yake ija kumbuyo n’kuthaŵa ali malisece.*

53 Tsopano anthu anatenga Yesu n’kupita naye kwa mkulu wa ansembe, ndipo ansembe aakulu onse, akulu, komanso alembi anasonkhana. 54 Koma Petulo anamutsatila capatali ndithu mpaka kukafika m’bwalo la ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Iye anakhala pansi pamodzi na anchito a m’nyumbamo, ndipo anali kuwotha moto wa lawilawi. 55 Pa nthawiyo, ansembe aakulu komanso onse m’Khoti Yaikulu ya Ayuda* anali kufuna-funa umboni kuti amunamizile mlandu Yesu, n’colinga cakuti amuphe. Koma sanapeze umboni uliwonse. 56 Anthu ambili anali kupeleka maumboni abodza kuti amunamizile. Koma maumboni awo anali kutsutsana. 57 Komanso anthu ena anali kuimilila n’kumapeleka umboni wabodza kuti: 58 “Tinamumva uyu akunena kuti, ‘Nidzagwetsa kacisi uyu amene anamangidwa na manja, ndipo m’masiku atatu nidzamanganso wina osati womangidwa na manja.’” 59 Koma ngakhale pa mfundo zimenezi, umboni wawo unali kutsutsana.

60 Ndiyeno mkulu wa ansembe anaimilila pakati pawo n’kufunsa Yesu kuti: “Kodi suyankha ciliconse? Ukutipo ciyani pa zimene anthu awa akukuneneza?” 61 Koma iye anangokhala cete, ndipo sanayankhe ciliconse. Mkulu wa ansembeyo anayamba kumufunsanso kuti: “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?” 62 Yesu anayankha kuti: “Ndinedi, ndipo mudzaona Mwana wa munthu atakhala ku dzanja lamanja lamphamvu komanso akubwela na mitambo.” 63 Atamva zimenezi, mkulu wa ansembeyo anang’amba zovala zake n’kunena kuti: “Kodi apa n’kufunanso umboni wina? 64 Mwadzimvela nokha kuti akunyoza Mulungu. Ndiye mukutipo bwanji?”* Onse anakamba kuti iye ayenela kuphedwa ndithu. 65 Ndipo ena anayamba kumuthila mata, kumuphimba kumaso, na kumumenya makofi n’kumanena kuti: “Lotela!” Atamuwaza mbama kumaso, asilikali a pa khoti anamutenga.

66 Tsopano Petulo ali khale m’bwalo lija, kunabwela mmodzi wa atsikana anchito a mkulu wa ansembe. 67 Iye ataona Petulo akuwotha moto, anamuyang’anitsitsa n’kunena kuti: “Inunso munali na Yesu uja Mnazareti.” 68 Koma iye anakana kuti: “Ine sinim’dziŵa, ndipo sinikumvetsa zimene ukukamba.” Kenako anatuluka panja n’kupita ku geti.* 69 Kumeneko, mtsikana wanchito uja anamuona, ndipo anayambanso kuuza amene anaimilila capafupi kuti: “Bambo awa nawonso ni mmodzi wa iwo.” 70 Petulo anakananso. Ndipo patapita kanthawi pang’ono, amene anaimilila capafupi anayambanso kumuuza kuti: “Mosakayikila, ndiwe mmodzi wa iwo, komanso ndiwe Mgalileya.” 71 Koma apa lomba, anayamba kukana* na kulumbila kuti: “Nati munthu uyu amene mukunena sinimudziŵa iyayi!” 72 Nthawi yomweyo, tambala analila kaciŵili, ndipo Petulo anakumbukila mawu a Yesu aja akuti: “Iwe unikana katatu tambala asanalile kaŵili.” Ndipo iye anamva cisoni kwambili n’kuyamba kulila.

15 M’mamaŵa matandakuca, ansembe aakulu pamodzi na akulu komanso alembi, inde Khoti Yaikulu yonse ya Ayuda,* anasonkhana pamodzi kuti akambilane zoti amucite Yesu. Iwo anamumanga na kupita naye kukam’peleka kwa Pilato. 2 Conco Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Mwanena nokha.” 3 Koma ansembe aakulu anali kumuneneza zinthu zambili. 4 Lomba Pilato anamufunsanso kuti: “Kodi suyankha ciliconse? Ona kuculuka kwa milandu imene akukuneneza.” 5 Koma Yesu sanayankhenso ciliconse, moti Pilato anadabwa kwambili.

6 Pa cikondwelelo ciliconse, Pilato anali kumasula mkaidi mmodzi amene anthu apempha. 7 Pa nthawiyo, munthu wina dzina lake Baraba anali m’ndende pamodzi na ena oukila boma. Ndipo panthawi imene iwo anali kuukila boma, anapha anthu. 8 Conco khamu la anthu linafika n’kuyamba kumupempha mogwilizana na zimene Pilato anali kukonda kuwacitila. 9 Iye anawayankha kuti: “Kodi mufuna nikumasulileni Mfumu ya Ayuda?” 10 Pakuti Pilato anali kudziŵa kuti ansembe aakulu anamupeleka cifukwa ca kaduka. 11 Koma ansembe aakulu anasonkhezela khamu la anthulo kuti iye amasule Baraba m’malo mwa Yesu. 12 Poyankha, Pilato anawafunsanso kuti: “Nanga nicite naye ciyani munthu amene mumamucha Mfumu ya Ayuda?” 13 Iwo anafuulanso mwamphamvu kuti: “Apacikidwe!”* 14 Koma Pilato anawafunsanso kuti: “Cifukwa ciyani? Walakwanji?” Koma m’pamene anthuwo anafuula mwamphamvu kuti: “Apacikidwe ndithu!”* 15 Conco Pilato pofuna kukwanilitsa zofuna za anthuwo anawamasulila Baraba, ndipo analamula kuti Yesu akwapulidwe. Kenako anamupeleka m’manja mwawo kuti akaphedwe pa mtengo.

16 Tsopano asilikali anamutenga Yesu n’kupita naye ku bwalo la pa nyumba ya bwanamkubwa, ndipo anasonkhanitsa asilikali onse. 17 Iwo anamuveka cinsalu camtundu wapepo, ndipo analuka cisoti cacifumu ca minga n’kumuveka. 18 Ndiyeno anthu anayamba kumukuwilila kuti: “Moni,* inu Mfumu ya Ayuda!” 19 Komanso iwo anali kumumenya pamutu na bango na kumuthila mata, ndipo anali kugwada n’kumuŵelamila. 20 Pambuyo pomucita zacipongwezo, anamuvula cinsalu camtundu wapepo cija n’kumuveka zovala zake zakunja. Ndipo anapita naye kukamukhomelela pamtengo. 21 Komanso iwo analamula munthu wina wa ku Kurene dzina lake Simoni, amene anali kudutsa kucokela ku dela la kumidzi kuti anyamule mtengo wa Yesu wozunzikilapo.* Munthu ameneyo anali tate wa Alekizanda komanso Rufasi.

22 Conco iwo anapita naye ku malo ochedwa Gologota. Liwuli likamasulidwa limatanthauza “Malo a Cigoba.” 23 Kumeneko anamupatsa vinyo wosakaniza na mule, koma iye anakana. 24 Iwo anamukhomelela pa mtengo, ndipo anagaŵana zovala zake zakunja mwa kucita maele kuti adziŵe covala cimene aliyense wa iwo angatenge. 25 Pamene anam’khomelela pa mtengo n’kuti nthawi ili ca m’ma 9 kololo m’maŵa.* 26 Ndipo mawu oonetsa mlandu umene anam’patsa anawalemba kuti: “Mfumu ya Ayuda.” 27 Ndiponso pambali pake panapacikidwa acifwamba aŵili pa mitengo, mmodzi ku dzanja lake lamanja, wina kumanzele kwake. 28* —— 29 Ndipo anthu opita m’njila anali kumunena monyoza n’kumapukusa mitu yawo. Iwo anali kunena kuti: “Aha! Iwe amene unali kunena kuti ukhoza kugwetsa kacisi n’kumumanganso m’masiku atatu, 30 dzipulumutse mwa kutsika pa mtengo wozunzikilapowo.”* 31 Nawonso ansembe aakulu pamodzi na alembi anali kumunyodola pakati pawo n’kumanena kuti: “Anali kupulumutsa ena, koma cam’kanga kuti adzipulumutse yekha! 32 Tsopano Khristu Mfumu ya Isiraeli, itsike pa mtengo wozunzikilapowo,* kuti tione na kuikhulupilila.” Nawonso amene anapacikidwa pa mitengo pambali pake anali kumunyoza.

33 Pamene nthawi inakwana 12 koloko masana,* m’dziko lonselo munagwa mdima mpaka ca m’ma 3 koloko masana.* 34 Ndipo m’ma 3 koloko momwemo, Yesu anafuula mokweza kuti: “Eli, Eli, lama sabakitani?” Mawuwa akamasulidwa amatanthauza kuti “Mulungu wanga, Mulungu wanga, n’cifukwa ciyani mwanilekelela?” 35 Ena mwa amene anaimilila pamenepo atamumva, anayamba kunena kuti: “Mwamva! Akuitana Eliya.” 36 Ndiyeno munthu wina anathamanga n’kukaviika cinkhupule mu vinyo wowawasa. Kenako anaciika ku bango na kum’patsa kuti amwe. Iye ananena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliyayo abwela kudzamutsitsa.” 37 Koma Yesu anafuula mokweza, kenako anatsilizika.* 38 Ndipo cinsalu cochinga ca m’nyumba yopatulika cinang’ambika pakati, kucokela pamwamba mpaka pansi. 39 Tsopano kapitawo wa asilikali amene anaimilila pafupi mopenyana na Yesu ataona zimene zinacitika pamene iye anali kutsilizika, anati: “Munthu ameneyu analidi Mwana wa Mulungu.”

40 Panalinso azimayi amene anali kuona capatali. Ena a iwo anali Mariya Mmagadala, Mariya mayi wa Yakobo Wamng’ono na Yose, komanso Salome, 41 amene anali kumutsatila na kum’tumikila pamene anali ku Galileya. Komanso panali azimayi ena ambili amene anabwela naye ku Yerusalemu.

42 Tsopano popeza nthawi inali kale madzulo, komanso linali tsiku la Cikonzekelo, kutanthauza tsiku lakuti maŵa lake ni Sabata, 43 kunabwela Yosefe wa ku Arimateya, munthu wochuka m’Khoti Yaikulu ya Ayuda. Nayenso anali kuyembekeza Ufumu wa Mulungu. Iye analimba mtima n’kupita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. 44 Koma Pilato anakayikila ngati Yesu anali atamwalila kale. Conco iye anaitana kapitawo wa asilikali kuti amufunse ngati Yesu anali atamwaliladi kale. 45 Conco Pilato atatsimikizila kucokela kwa kapitawo wa asilikaliyo kuti Yesu wamwaliladi, anapeleka mtembowo kwa Yosefe. 46 Yosefe anagula nsalu yabwino kwambili, ndipo atatsitsa mtembo wa Yesu, anaukulunga m’nsaluyo n’kukauika m’manda* amene anali atagobedwa m’thanthwe. Kenako anakunkhunizilapo cimwala pa khomo la mandawo. 47 Koma Mariya Mmagadala na Mariya mayi a Yose, anapitiliza kuyang’ana pamene anamuika.

16 Tsiku la Sabata litatha, Mariya Mmagadala, Mariya mayi ake a Yakobo, na Salome anagula zonunkhilitsa kuti apite ku manda kukapaka mtembo wa Yesu. 2 Ndipo m’mamaŵa pa tsiku loyamba la mlunguwo dzuŵa litatuluka, iwo anafika ku mandako.* 3 Anali kufunsana kuti: “Ndani atikunkhunizile cimwala kucicotsa pa khomo la manda?” 4 Koma atayang’ana pa khomo la mandawo, anaona kuti cimwala cija cakunkhunizidwa kale ngakhale kuti cinali cacikulu kwambili. 5 Ataloŵa m’mandamo, anaona mnyamata wovala mkanjo woyela atakhala pansi ku dzanja lamanja, ndipo iwo anadabwa kwambili. 6 Iye anawauza kuti: “Musadabwe. Nidziŵa kuti mukufuna-funa Yesu Mnazareti amene anaphedwa pa mtengo. Iye anaukitsidwa ndipo sali muno. Onani, apa m’pamene anamuika. 7 Koma pitani mukauze ophunzila ake na Petulo kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona kumeneko monga anakuuzilani.’” 8 Atatuluka m’mandamo, anathaŵa akunjenjemela komanso ali odabwa kwambili. Ndipo sanauze aliyense zimene zinacitikazo cifukwa anali na mantha kwambili.*

Mawu ake enieni, “pamaso pako.”

Kapena kuti, “kuwaviika; kuwamiza.”

Kamasulidwe kena, “zinali kumudziŵa kuti ndani?”

Kapena kuti, “wolemala.”

Kapena kuti, “wolemala.”

Kapena kuti, “anasankha.”

Kapena kuti, “wokangalika.”

Dzina lina la Satana.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “thadza lopimila.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “Cigawo ca Mizinda 10.”

Kapena kuti, “watsala pangʼono kufa.”

Kapena kuti, “anamucititsa kuti amve zoŵaŵa zambili.”

Kutanthauza, “kulila kwa gulu la anthu pa malilo.”

Kapena kuti, “anawalamula mwamphamvu.”

Mawu ake enieni, “kopa.”

Kapena kuti, “covala cina.”

Kapena kuti, “komanso aja amene anali kudya naye pathebulo.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Nthawiyi inali kuyamba ca m’ma 3 koloko usiku mpaka dzuŵa litatuluka ca m’ma 6 koloko.

Kutanthauza, kusayeletsedwa motsatila mwambo.

Ena amati, “kasukusuku.”

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

Mu Cigiriki ni por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “khalidwe lopanda manyazi.” Mu Cigiriki a·sel′gei·a.

Cioneka kuti mayiyu anabadwila ku Foinike.

Kapena kuti, “Cigawo ca Mizinda 10.”

Kapena kuti, “asanadye.”

Kapena kuti, “matadza onyamulilamo zinthu.”

Kapena kuti, “matadza onyamulilamo zinthu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “wosakhulupilika.”

Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ni dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.

Kamasulidwe kena, “Iwo sanauzeko aliyense nkhaniyo.”

Onani mawu a m’munsi pa Mateyo 18:8.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kamasulidwe kena, “anauzana.”

Kapena kuti, “ndipo pa nyengo imene ikubwelayo.”

Kapena kuti, “amene amadziŵika kuti.”

Kutanthauza “Mphunzitsi.”

Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ni dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

Kapena kuti, “kapena unayambitsidwa na anthu?”

Mawu ake enieni, “mutu wa kona.”

Kapena kuti, “kumumanga.”

Kapena kuti, “n’coyenela.”

Kapena kuti, “lofunika kwambili.”

Kapena kuti, “yabwino kwambili.”

Mawu ake enieni, “Amadya nyumba za akazi.”

Kapena kuti, “mwaciphamaso.”

Kapena kuti, “colema.”

Mawu ake enieni, “zoŵaŵa za pobeleka.”

Kapena kuti, “amene wapilila.”

Mawu ake eni-eni, “tambala akulila.”

Kapena kuti, “amumange.”

Kapena kuti, “zaciwawa.”

Kapena kuti, “Iwo analankhula naye mokwiya; iwo anam’kalipila.”

Kapena kuti, “nyimbo zauzimu; masalimo.”

Kapena kuti, “Moyo wanga uli na cisoni.”

Liwu la Ciheberi kapena Ciaramu lotanthauza “Atate,” kapena “Ababa.”

Kapena kuti, “mzimu ufuna.”

Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ni dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.

Kapena kuti, “ali wosavala mokwanila; ali na covala camkati cabe.”

Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”

Kapena kuti, “Muganiza bwanji?”

Kapena kuti, “ku kanyumba ka pageti.”

Mawu ake enieni, “kudzitembelela.”

Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”

Kapena kuti, “Aphedwe mwa kumupacika pa mtengo!”

Kapena kuti, “Aphedwe mwa kumupacika pa mtengo!”

Kapena kuti, “Mutamandike.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “pafupifupi ola lacitatu.”

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu ake enieni, “ola la 6.”

Mawu ake enieni, “ola la 9.”

Kapena kuti, “anapuma kothela.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Malinga na mipukutu yoyambilila yodalilika, Uthenga Wabwino wa Maliko umatha na mawu a pa vesi 8.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani