1
Kalata yopita kwa Teofilo (1-4)
Mngelo Gabirieli anenelatu za kubadwa kwa Yohane M’batizi (5-25)
Mngelo Gabirieli anenelatu za kubadwa kwa Yesu (26-38)
Mariya apita kwa Elizabeti (39-45)
Mariya alemekeza Yehova (46-56)
Kubadwa kwa Yohane ndi mmene anamupatsila dzina (57-66)
Ulosi wa Zekariya (67-80)
2
Kubadwa kwa Yesu (1-7)
Angelo aonekela kwa abusa (8-20)
Mdulidwe ndi kuyeletsedwa (21-24)
Simiyoni aona Khristu (25-35)
Anna akamba zokhudza mwanayo (36-38)
Abwelela ku Nazareti (39, 40)
Yesu wa zaka 12 apita ku kacisi (41-52)
3
Ciyambi ca nchito ya Yohane (1, 2)
Yohane alalikila za ubatizo (3-20)
Ubatizo wa Yesu (21, 22)
Mzele wa makolo a Yesu Khristu (23-38)
4
Mdyelekezi ayesa Yesu (1-13)
Yesu ayamba kulalikila ku Galileya (14, 15)
Yesu akanidwa ku Nazareti (16-30)
Zimene zinacitika m’sunagoge ku Kaperenao (31-37)
Apongozi aakazi a Simoni ndi anthu ena acilitsidwa (38-41)
Khamu la anthu lipeza Yesu ku malo opanda anthu (42-44)
5
Akupha nsomba mozizwitsa; ophunzila oyambilila (1-11)
Wakhate acilitsidwa (12-16)
Yesu acilitsa munthu wofa ziwalo (17-26)
Yesu aitana Levi (27-32)
Funso pa nkhani ya kusala kudya (33-39)
6
Yesu, “Mbuye wa Sabata” (1-5)
Munthu wopuwala dzanja acilitsidwa (6-11)
Atumwi 12 (12-16)
Yesu aphunzitsa ndi kucilitsa (17-19)
Anthu acimwemwe komanso anthu atsoka (20-26)
Kukonda adani (27-36)
Lekani kuweluza ena (37-42)
Umadziwika ndi zipatso zake (43-45)
Nyumba yomangidwa bwino; nyumba yopanda maziko (46-49)
7
Cikhulupililo ca kapitawo wa asilikali (1-10)
Yesu acilitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye ku Naini (11-17)
Yohane M’batizi atamandidwa (18-30)
Adzudzula m’badwo wosamvela (31-35)
Mayi wocimwa akhululukidwa (36-50)
8
Azimayi amene anali kutsatila Yesu (1-3)
Fanizo la wofesa mbewu (4-8)
Cifukwa cake Yesu anagwilitsa nchito mafanizo (9, 10)
Afotokoza tanthauzo la fanizo la wofesa mbewu (11-15)
Nyale saibwinikila (16-18)
Amayi ake a Yesu ndi abale ake (19-21)
Yesu aleketsa namondwe (22-25)
Yesu atumiza ziwanda m’nkhumba (26-39)
Mwana wamkazi wa Yairo; mzimayi agwila covala cakunja ca Yesu (40-56)
9
Alangiza atumwi 12 molalikilila (1-6)
Herode adabwa naye kwambili Yesu (7-9)
Yesu adyetsa anthu 5,000 (10-17)
Petulo azindikila kuti Yesu ndi Khristu (18-20)
Yesu anenelatu za imfa yake (21, 22)
Zimene ophunzila oona a Yesu amacita (23-27)
Kusandulika kwa Yesu (28-36)
Kamnyamata kogwidwa ndi ciwanda kacilitsidwa (37-43a)
Kaciwili, Yesu anenelatu za imfa yake (43b-45)
Ophunzila akangana zakuti wamkulu ndani (46-48)
Aliyense amene satsutsana nafe ali ku mbali yathu (49, 50)
Mudzi wina wa Asamariya ukana Yesu (51-56)
Mmene tingatsatilile Yesu (57-62)
10
Yesu atuma ophunzila 70 (1-12)
Tsoka ku mizinda yosalapa (13-16)
Ophunzila 70 abwelako (17-20)
Yesu atamanda Atate ake cifukwa cokonda anthu odzicepetsa (21-24)
Fanizo la Msamariya wacifundo (25-37)
Yesu apita kwa Marita ndi Mariya (38-42)
11
Mmene tingapemphelele (1-13)
Ziwanda zitulutsidwa ndi cala ca Mulungu (14-23)
Mzimu wonyansa ubwelelanso (24-26)
Cimwemwe ceniceni (27, 28)
Cizindikilo ca Yona (29-32)
Nyale ya thupi (33-36)
Tsoka kwa atsogoleli onyenga acipembedzo (37-54)
12
Zofufumitsa za Afarisi (1-3)
Opani Mulungu, osati anthu (4-7)
Kuvomeleza kuti ndife ophunzila a Khristu (8-12)
Fanizo la munthu wacuma wopusa (13-21)
Lekani kuda nkhawa (22-34)
Kukhala maso (35-40)
Woyang’anila wokhulupilika komanso woyang’anila wosakhulupilika (41-48)
Osati mtendele, koma magawano (49-53)
Kufunika kodziwa tanthauzo la zimene zikucitika (54-56)
Kuthetsa mikangano (57-59)
13
Lapani, apo ayi muwonongedwa (1-5)
Fanizo la mtengo wamkuyu wosabala zipatso (6-9)
Mzimayi wopindika msana acilitsidwa pa Sabata (10-17)
Fanizo la kanjele ka mpilu komanso la zofufumitsa (18-21)
Khama n’lofunika kuti tilowe pa khomo lopanikiza (22-30)
Herode achulidwa kuti “nkhandwe” (31-33)
Yesu adandaula za Yerusalemu (34, 35)
14
Mwamuna wina wodwala matenda otupikana acilitsidwa pa Sabata (1-6)
Khalani mlendo wodzicepetsa (7-11)
Muziitana anthu amene sangakubwezeleni (12-14)
Fanizo la anthu amene anakana kupita ku phwando (15-24)
Zofunika kucita kuti munthu akhale wophunzila (25-33)
Mcele umene watha mphamvu (34, 35)
15
Fanizo la nkhosa yosecela (1-7)
Fanizo la khobili lotayika (8-10)
Fanizo la mwana wolowelela (11-32)
16
Fanizo la woyang’anila nyumba wosalungama (1-13)
Cilamulo komanso Ufumu wa Mulungu (14-18)
Fanizo la munthu wolemela ndi Lazaro (19-31)
17
Kupunthwa, kukhululukila, ndi cikhulupililo (1-6)
Akapolo opanda pake (7-10)
Anthu 10 akhate acilitsidwa (11-19)
Kubwela kwa Ufumu wa Mulungu (20-37)
18
Fanizo la mkazi wamasiye wolimbikila (1-8)
Mfarisi ndi wokhometsa misonkho (9-14)
Yesu ndi ana aang’ono (15-17)
Funso la wolamulila wacuma (18-30)
Yesu anenelatunso za imfa yake (31-34)
Munthu wakhungu wopemphapempha ayamba kuona (35-43)
19
Yesu apita kwa Zakeyo (1-10)
Fanizo la ndalama 10 za mina (11-27)
Yesu atamandidwa polowa mu Yerusalemu (28-40)
Yesu alilila Yerusalemu (41-44)
Yesu ayeletsa kacisi (45-48)
20
Anthu akayikila mphamvu za Yesu (1-8)
Fanizo la alimi akupha (9-19)
Mulungu ndi Kaisara (20-26)
Funso pa nkhani ya kuuka kwa akufa (27-40)
Kodi Khristu ndi mwana wa Davide? (41-44)
Acenjeza anthu kuti asamale ndi alembi (45-47)
21
Tumakobili tuwili twa mkazi wamasiye wosauka (1-4)
CIZINDIKILO CA ZIMENE ZIKUBWELA (5-36)
Nkhondo, zivomezi zamphamvu, milili, ndi njala (10, 11)
Yerusalemu adzazungulilidwa ndi magulu a asilikali (20)
Nthawi zoikika za anthu a mitundu (24)
Kubwela kwa Mwana wa Munthu (27)
Fanizo la mtengo wamkuyu (29-33)
Khalanibe maso (34-36)
Yesu aphunzitsa m’kacisi (37, 38)
22
Ansembe akonza ciwembu ca kupha Yesu (1-6)
Kukonzekela Pasika wothela (7-13)
Kukhazikitsidwa kwa Mgonelo wa Ambuye (14-20)
“Wondipeleka uja ali nane pathebulo pano” (21-23)
Akangana kwambili zakuti wamkulu ndani (24-27)
Cipangano ca Yesu ca Ufumu (28-30)
Yesu akambilatu zakuti Petulo adzamukana (31-34)
Kufunika kokhala okonzeka; malupanga awili (35-38)
Pemphelo la Yesu pa Phili la Maolivi (39-46)
Yesu agwidwa (47-53)
Petulo akana Yesu (54-62)
Yesu acitidwa zacipongwe (63-65)
Azengedwa mlandu ku Khoti Yaikulu ya Ayuda (66-71)
23
Yesu aonekela pamaso pa Pilato ndi Herode (1-25)
Yesu ndi zigawenga ziwili apacikidwa pa mitengo (26-43)
Imfa ya Yesu (44-49)
Yesu aikidwa m’manda (50-56)
24
Yesu aukitsidwa (1-12)
Pa msewu wopita ku Emau (13-35)
Yesu aonekela kwa ophunzila (36-49)
Yesu akwela kumwamba (50-53)