LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • nwt Macitidwe 1:1-28:31
  • Macitidwe

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Macitidwe
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Macitidwe

MACITIDWE A ATUMWI

1 A Teofilo, m’buku loyamba, ndinalemba zonse zimene Yesu anacita ndi kuphunzitsa 2 mpaka tsiku limene iye anatengedwa kupita kumwamba, pambuyo pakuti wapeleka malangizo kupyolela mwa mzimu woyela kwa atumwi amene anasankha. 3 Yesu atazunzika mpaka imfa, anaonekela kwa iwo ali wamoyo mwa kugwilitsa nchito maumboni okhutilitsa. Kwa masiku 40, iye anaonekela kwa iwo nthawi zambili, ndipo anali kukamba nawo za Ufumu wa Mulungu. 4 Pa nthawi imene anasonkhana nawo pamodzi, anawalangiza kuti: “Musacoke mu Yerusalemu, koma pitilizani kuyembekezela lonjezo la Atate limene munamva kwa ine. 5 Cifukwa Yohane anali kubatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyela pasanapite masiku ambili.”

6 Conco atasonkhana pamodzi, anamufunsa kuti: “Ambuye kodi mubwezeletsa ufumu kwa Aisiraeli pa nthawi ino?” 7 Iye anawayankha kuti: “Si kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo imene Atate asankha mu ulamulilo wawo. 8 Mzimu woyela ukadzafika pa inu, mudzalandila mphamvu, ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezelo* a dziko lapansi.” 9 Atatsiliza kukamba zimenezi, anatengedwa kupita kumwamba iwo akuona, ndipo mtambo unamuphimba cakuti sanathenso kumuona. 10 Ndipo pamene iwo anali kuyang’anitsitsa kumwamba pomwe iye anali kupita, mwadzidzidzi amuna awili ovala zoyela anaimilila pambali pawo. 11 Amunawo anati: “Amuna inu a mu Galileya, n’cifukwa ciyani mwangoimilila n’kumayang’ana kumwamba? Yesu amene watengedwa pakati panu kupita kumwamba, adzabwela mofanana ndi mmene mwamuonela akupita kumwamba.”

12 Ndiyeno iwo anabwelela ku Yerusalemu kucoka kuphili lochedwa Phili la Maolivi limene linali pafupi ndi Yerusalemu, pa mtunda wa pafupifupi kilomita imodzi* kucokela ku Yerusalemu. 13 Iwo atafika kumeneko, anapita m’cipinda cam’mwamba mmene anali kukhala. Mmenemo munali Petulo, Yohane, Yakobo, Andireya, Filipo, Tomasi, Batolomeyo, Mateyo, Yakobo mwana wa Alifeyo, Simoni wochedwanso kuti wakhama, komanso Yudasi mwana wa Yakobo. 14 Onsewa mogwilizana anali kulimbikila kupemphela pamodzi ndi Mariya mayi ake a Yesu, azimayi ena, komanso abale ake a Yesu.

15 M’masiku amenewo, Petulo anaimilila pakati pa abalewo (ciwelengelo* ca anthu onse cinali pafupifupi 120) ndipo anati: 16 “Amuna inu, abale, kunali kofunikila kuti lemba likwanilitsidwe limene mzimu woyela unanenelatu kudzela mwa Davide za Yudasi, amene anatsogolela anthu kuti agwile Yesu. 17 Iye anali pakati pathu, ndipo anatengako mbali pa utumiki umenewu. 18 (Munthu ameneyu, anagula munda ndi malipilo a nchito zosalungama. Iye anagwa camutu, ndipo thupi lake linaphulika* moti matumbo ake anakhutuka. 19 Nkhani imeneyi inadziwika kwa anthu onse okhala mu Yerusalemu, moti m’cinenelo cawo mundawo anaucha kuti A·kel′da·ma, kutanthauza “Munda wa Magazi.”) 20 Pakuti m’buku la Masalimo analembamo kuti, ‘Malo ake okhala akhale matongwe, ndipo pasapezeke aliyense wokhalapo,’ ndiponso kuti ‘Udindo wake monga woyang’anila, munthu wina autenge.’ 21 Conco m’pofunika kuti iye alowedwe m’malo ndi mmodzi wa amuna amene anali kuyenda nafe pa nthawi yonse imene Ambuye Yesu anali kucita utumiki wawo pakati pathu. 22 Munthu ameneyo, akhale amene anali kuyenda nafe kuyambila pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane, mpaka tsiku limene anatengedwa pakati pathu kupita kumwamba. Munthuyo ayenela kukhala mboni ya kuukitsidwa kwake pamodzi ndi ife.”

23 Conco, panachulidwa amuna awili, Yosefe wochedwa Barasaba amene analinso kuchedwa kuti Yusito, ndi Matiya. 24 Ndiyeno anapemphela kuti: “Inu Yehova, mumadziwa mitima ya anthu onse, tionetseni amene mwasankha pakati pa amuna awiliwa 25 kuti atenge malo a utumikiwu ndi kukhala mtumwi, zimene Yudasi anasiya n’kuyenda njila zake.” 26 Conco iwo anacita maele, ndipo maelewo anagwela Matiya. Cotelo iye anawonjezedwa pa atumwi 11 aja.

2 Tsopano patsiku la cikondwelelo ca Pentekosite, onse anasonkhana pamalo amodzi. 2 Mwadzidzidzi, kumwamba kunamveka phokoso monga la mkokomo wa mphepo yamphamvu. Phokoso lake linadzaza nyumba yonse imene iwo analimo. 3 Ndiyeno iwo anaona malawi a moto ooneka ngati malilime ndipo anagawikana n’kukhala pa aliyense wa iwo limodzi limodzi. 4 Onse anadzazidwa ndi mzimu woyela, ndipo anayamba kukamba zinenelo zosiyanasiyana,* monga mmene mzimuwo unawacititsila kulankhula.

5 Panthawiyo, Ayuda oopa Mulungu ocokela m’mitundu yonse pa dziko lapansi, anali kukhala ku Yerusalemu. 6 Conco phokosolo litamveka, khamu la anthu linasonkhana, ndipo anadabwa kwambili cifukwa aliyense wa iwo anawamva akulankhula m’cinenelo cake. 7 Iwo anadabwa kwambili cakuti anayamba kufunsana kuti: “Taonani, anthu onsewa amene akulankhula ndi Agalileya, si conco? 8 Nanga zikutheka bwanji kuti aliyense wa ife azimva cinenelo cake?* 9 Pakati pathu pali Apati, Amedi, Aelamu, anthu ocokela ku Mesopotamiya, ku Yudeya, ku Kapadokiya, ku Ponto, ndi ku cigawo ca Asia. 10 Palinso anthu ocokela ku Fulugiya, Pamfuliya, ku Iguputo, ndi kumadela a ku Libiya, amene ali pafupi ndi Kurene. Ndipo palinso alendo ocokela ku Roma ndi Ayuda, komanso anthu otembenukila ku Ciyuda, 11 Akerete, komanso a Arabu. Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu m’zinenelo zathu.” 12 Inde, onsewa anadabwa kwambili ndipo anathedwa nzelu, moti anali kufunsana kuti: “Kodi zocitika izi zikutanthauza ciyani?” 13 Koma ena anali kuwaseka ndipo anali kukamba kuti: “Amenewa aledzela ndi vinyo watsopano.”

14 Koma Petulo anaimilila pamodzi ndi atumwi 11 aja, n’kulankhula nawo mokweza mawu kuti: “Anthu inu a ku Yudeya, komanso onse okhala ku Yerusalemu, dziwani izi ndipo mvetselani mosamala mawu anga. 15 Anthu awa sanaledzele monga mmene mukuganizila, cifukwa apa ndi m’mawa ndipo nthawi ili ca m’ma 9 koloko.* 16 Koma zimene zacitikazi n’zimene mneneli Yoweli ananenelatu kuti: 17 ‘Mulungu anati, “Ndipo m’masiku otsiliza, ndidzapungulila mzimu wanga pa camoyo ciliconse, ndipo ana anu aamuna komanso ana anu aakazi adzalosela. Anyamata anu adzaona masomphenya, ndipo amuna okalamba adzalota maloto. 18 Ndidzapungulilanso mzimu wanga ngakhale pa akapolo anga aamuna ndi akapolo anga aakazi m’masiku amenewo, ndipo iwo adzalosela. 19 Ndidzacita zodabwitsa* kumwamba, komanso zizindikilo pa dziko lapansi. Padzakhala magazi, moto, ndi utsi watolotolo. 20 Dzuwa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi, tsiku lalikulu komanso laulemelelo la Yehova lisanafike. 21 Ndipo aliyense woitanila pa dzina la Yehova adzapulumuka.”’

22 “Amuna inu a mu Isiraeli, mvelani mawu awa: Yesu Mnazareti, ndi munthu amene Mulungu anakuonetsani poyela kudzela mu nchito za mphamvu, zodabwitsa, ndi zizindikilo zimene Mulungu anacita pakati panu kupitila mwa iye, monga mmene inu mukudziwila. 23 Mulungu anadziwilatu pasadakhale kuti Yesu adzapelekedwa. Conco, cinali cifunilo cake. Inu munamukhomelela pamtengo pogwilitsa nchito anthu osamvela malamulo, ndipo munamupha. 24 Koma Mulungu anamuukitsa pomumasula ku zowawa* za imfa cifukwa zinali zosatheka kuti imfa imugwile mwamphamvu. 25 Pakuti Davide anakamba za iye kuti: ‘Nthawi zonse ndimaika Yehova patsogolo panga,* cifukwa iye ali kudzanja langa lamanja kuti ndisagwedezeke. 26 Pa cifukwa cimeneci, mtima wanga unasangalala ndipo n’nalankhula mokondwela kwambili. Ndiponso ine ndidzakhala ndi ciyembekezo, 27 cifukwa simudzandisiya m’Manda,* kapena kulola kuti thupi la munthu wokhulupilika kwa inu liwole. 28 Mwandidziwitsa njila za moyo, ndipo ndikakhala nanu pafupi* mudzacititsa kuti ndisangalale kwambili.’

29 “Amuna inu, abale, ndiloleni ndilankhule mwaufulu za kholo lathu Davide. Iye anamwalila ndi kuikidwa m’manda, ndipo manda ake tili nawo mpaka lelo. 30 Popeza iye anali mneneli, ndipo anali kudziwa kuti Mulungu anamulonjeza mwakucita kulumbila kuti pa mpando wake wacifumu adzaikapo mmodzi wa mbadwa zake, 31 anaonelatu pasadakhale ndipo anakambilatu za kuuka kwa Khristu kuti sadzasiyidwa m’Manda,* ndipo thupi lake silidzawola. 32 Mulungu anaukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife tonse ndife mboni za nkhani imeneyi. 33 Conco, cifukwa cakuti iye anakwezedwa n’kukhala kudzanja lamanja la Mulungu ndipo analandila mzimu woyela umene Atate analonjeza, iye ndiye watipatsa* mzimu woyela malinga ndi zimene mukuona ndi kumva. 34 Davide sanapite kumwamba, koma iyeyo anati, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 35 kufikila n’taika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’ 36 Conco nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu kuti Yesu ameneyu, amene inu munamuphela pamtengo, Mulungu anamuika kukhala Ambuye komanso Khristu.”

37 Anthuwo atamva mawu amenewo anakhudzika mtima kwambili* moti anafunsa Petulo ndi atumwi ena onse kuti: “Amuna inu, abale, ndiye ticite ciyani?” 38 Petulo anawayankha kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu kuti macimo anu akhululukidwe. Mukacita izi, mudzalandila mphatso ya mzimu woyela kwaulele. 39 Cifukwa lonjezoli lipita kwa inu, kwa ana anu, komanso kwa anthu onse okhala kutali, onse amene Yehova Mulungu wathu angawaitane.” 40 Ndi mawu enanso ambili, Petulo anacitila umboni mokwanila, komanso anapitiliza kuwadandaulila kuti: “Dzipulumutseni ku m’badwo uwu wa maganizo opotoka.” 41 Cotelo amene analandila mawu ake mokondwela anabatizidwa. Moti pa tsikulo, anthu amene anawonjezekawo anali pafupifupi 3,000. 42 Iwo anapitiliza kutsatila zimene atumwi anali kuphunzitsa, ndipo anali kucezela pamodzi,* kudyela pamodzi, komanso kupemphela.

43 Anthu onse anayamba kucita mantha, ndipo atumwi anayamba kucita zodabwitsa ndi zizindikilo zambili. 44 Onse amene anakhala okhulupilila anali kukhala pamodzi ndipo anali kugawana zonse zimene anali nazo. 45 Iwo anali kugulitsa malo ndi zinthu zina zimene anali nazo, ndipo ndalama zake anali kugawila onse malinga ndi zosowa zawo. 46 Tsiku lililonse anali kusonkhana m’kacisi mogwilizana. Iwo anali kudyela pamodzi cakudya m’nyumba zawo. Ndipo anali kugawana cakudya cawo mokondwela kwambili komanso ndi mtima wonse. 47 Analinso kutamanda Mulungu ndipo anthu onse anali kuwakonda. Panthawi imodzimodzi, Yehova tsiku lililonse anapitiliza kuwonjezela anthu amene anali kuwapulumutsa.

3 Tsopano Petulo ndi Yohane anali kupita kukalowa m’kacisi pa nthawi yopemphela. Nthawiyo inali 3 koloko masana.* 2 Ndiyeno panali mwamuna wina amene anabadwa wolemala. Tsiku lililonse, anali kumuika pafupi ndi khomo la kacisi lochedwa Geti Yokongola, kuti azipempha mphatso zacifundo kwa amene anali kulowa m’kacisi. 3 Iye ataona kuti Petulo ndi Yohane akufuna kulowa m’kacisimo, anayamba kuwapempha mphatso zacifundo. 4 Koma Petulo pamodzi ndi Yohane anamuyang’anitsitsa, ndipo anamuuza kuti: “Tiyang’ane.” 5 Conco munthuyo anawayang’anitsitsa, akuyembekezela kuti iwo amupatsa kenakake. 6 Koma Petulo anati: “Ine ndilibe siliva ndi golide, koma ndikupatsa cimene ndili naco. M’dzina la Yesu Khristu Mnazareti, yenda!” 7 Atatelo anamugwila dzanja lamanja n’kumuimilika. Nthawi yomweyo, mapazi ndi miyendo* yake inalimba. 8 Munthuyo analumpha n’kuyamba kuyenda, ndipo analowa nawo m’kacisimo. Iye anali kuyenda ndi kulumpha akutamanda Mulungu. 9 Ndipo anthu onse anamuona akuyenda ndi kutamanda Mulungu. 10 Iwo anamuzindikila kuti ndi munthu uja amene anali kukhala pa geti ya kacisi yochedwa Geti Yokongola, n’kumayembekezela kupatsidwa mphatso zacifundo. Anthuwo anadabwa kwambili, ndipo anakondwela ndi zimene zinacitikila munthuyo.

11 Munthu uja akali wogwililila manja a Petulo ndi Yohane, anthu onse anathamangila kwa iwo ku Khonde la Zipilala la Solomo. Ndipo anthuwo anadabwa kwambili. 12 Petulo ataona izi, anauza anthuwo kuti: “Aisiraeli inu, n’cifukwa ciyani mwadabwa kwambili ndi zimenezi? N’cifukwa ciyani mukutiyang’anitsitsa monga kuti ife tamuyendetsa mwa mphamvu zathu, kapena cifukwa ca kudzipeleka kwathu kwa Mulungu? 13 Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki, komanso wa Yakobo, Mulungu wa makolo athu akale, walemekeza Mtumiki wake Yesu amene inu munamupeleka ndi kumukana pamaso pa Pilato. Ngakhale kuti Pilatoyo anafuna kumumasula. 14 Inde, inu munamukana munthu woyela komanso wolungama ameneyo. Ndipo munapempha kuti iye akumasulileni munthu wopha anthu. 15 Inu munamupha Mtumiki Wamkulu wa moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, ndipo ife ndife mboni za nkhaniyi. 16 Conco kupitila m’dzina lake komanso mwa cikhulupililo cathu m’dzinalo, munthu uyu amene mukumuona ndi kum’dziwa wacilitsidwa. Cikhulupililo cimene tili naco cifukwa ca Yesu, cacititsa kuti munthu uyu acililetu monga mmene nonsenu mukumuonela. 17 Tsopano abale, ndikudziwa kuti munacita zinthu mosazindikila monga mmene olamulila anu nawonso anacitila. 18 Koma mwa njila imeneyi, Mulungu wakwanilitsa zinthu zimene analengezelatu kupitila mwa aneneli onse, kuti Khristu wake adzavutika.

19 “Conco lapani ndi kutembenuka kuti macimo anu afafanizidwe. Mukatelo, nyengo zotsitsimula zocokela kwa Yehova* zidzabwela kwa inu. 20 Ndipo iye adzatumiza Yesu, amene ndi Khristu wosankhidwa cifukwa ca inu. 21 Kumwamba kuyenela kumusunga ameneyu kufikila nthawi ya kubwezeletsa zinthu zonse zimene Mulungu analankhula kudzela mwa aneneli ake oyela akale. 22 Ndipo Mose anati: ‘Yehova Mulungu wanu adzakuutsilani mneneli ngati ine pakati pa abale anu. Mudzamumvele pa zonse zimene adzakuuzani. 23 Ndithudi, aliyense amene sadzamvela Mneneliyo adzawonongedwa kothelatu pakati pa anthu.’ 24 Ndipo aneneli onse kuyambila pa Samueli komanso amene anabwela pambuyo pake, onse amene analosela, anakambanso mosapita m’mbali za masiku amenewa. 25 Inu ndinu ana a aneneliwo, komanso a cipangano cimene Mulungu anacita ndi makolo anu akale. Iye anauza Abulahamu kuti: ‘Kudzela mwa mbadwa* yako, mabanja onse pa dziko lapansi adzadalitsidwa.’ 26 Mulungu atasankha Mtumiki wake, anamutumiza kwa inu coyamba kuti adzakudalitseni mwa kubweza aliyense wa inu kuti aleke nchito zake zoipa.”

4 Pamene Petulo ndi Yohane anali kukamba ndi anthu aja, ansembe, kapitawo wa pakacisi, komanso Asaduki anabwela kwa iwo. 2 Iwo anali okwiya cifukwa atumwiwo anali kuphunzitsa anthu komanso kulengeza poyela kuti Yesu anauka kwa akufa. 3 Conco anawagwila n’kuwaponya* m’ndende mpaka tsiku lotsatila cifukwa kunali kutada kale. 4 Koma ambili amene anamvetsela zimene iwo anakamba anakhulupilila, ndipo ciwelengelo ca amuna cinali pafupifupi 5,000.

5 Tsiku lotsatila, olamulila, akulu, ndi alembi anasonkhana pamodzi ku Yerusalemu. 6 Kunalinso Anasi wansembe wamkulu, Kayafa, Yohane, Alekizanda, ndi onse amene anali acibale a wansembe wamkuluyo. 7 Iwo anaimika Petulo ndi Yohane pakati pawo n’kuyamba kuwafunsa kuti: “Kodi mphamvu zocita izi mwazitenga kuti, kapena mwacita izi m’dzina la ndani?” 8 Ndiyeno Petulo atadzazidwa ndi mzimu woyela, anawauza kuti:

“Inu olamulila anthu komanso akulu, 9 ngati mukutifunsa mafunso lelo za cabwino cimene tacitila munthu wolemalayu, ndipo mufuna kudziwa amene wapangitsa munthu uyu kucila, 10 zidziwike kwa nonsenu komanso kwa Aisiraeli onse, kuti m’dzina la Yesu Khristu Mnazareti amene inu munamuphela pamtengo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kupitila mwa iyeyo munthu amene waimilila patsogolo panu wakhala bwinobwino. 11 Yesu ameneyu ndi ‘mwala umene inu omanga munauona kuti ndi wopanda nchito, umene wakhala mwala wapakona* wofunika kwambili.’ 12 Kuwonjezela apo, palibe wina aliyense amene angapeleke cipulumutso, cifukwa palibe dzina lina padziko lapansi limene lapelekedwa kwa anthu limene lingatipulumutse.”

13 Iwo ataona mmene Petulo ndi Yohane anali kulankhulila molimba mtima, podziwanso kuti anali osaphunzila* komanso anali anthu wamba, anadabwa kwambili. Ndipo anazindikila kuti iwo anali kuyenda ndi Yesu. 14 Iwo ataona munthu amene anacilitsidwayo ataimilila nawo pamodzi, anasowa cokamba. 15 Conco anawalamula kuti atuluke mu holo ya Bungwe Lalikulu la Ayuda,* kenako anayamba kukambilana 16 kuti: “Kodi ticite nawo ciyani amuna amenewa? Cifukwa kukamba zoona, iwo acita cozizwitsa* cacikulu cimene cadziwika kwa anthu onse okhala mu Yerusalemu. Ndipo sitingatsutse zimenezo. 17 Conco kuti nkhaniyi isapitilize kufalikila pakati pa anthu, tiyeni tiwaopseze ndi kuwauza kuti asalankhulenso ndi wina aliyense m’dzina limeneli.”

18 Pambuyo pake, anawaitana n’kuwalamula kuti asakambenso kalikonse kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu. 19 Koma Petulo ndi Yohane anawauza kuti: “Weluzani nokha ngati n’koyenela pamaso pa Mulungu kumvela inu m’malo mwa Mulungu. 20 Koma ife sitingaleke kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” 21 Conco atawaopsezanso, anawamasula, popeza kuti sanapeze cifukwa ciliconse cowapatsila cilango. Komanso anaopa anthu cifukwa onse anali kutamanda Mulungu pa zimene zinacitikazo. 22 Munthuyo amene anacilitsidwa mozizwitsa anali ndi zaka zoposa 40.

23 Atamasulidwa, iwo anapita kwa okhulupilila anzawo n’kuwafotokozela zimene ansembe aakulu ndi akulu anawauza. 24 Atamva izi, onse anafuula kwa Mulungu kuti:

“Ambuye Wamkulukulu, inu ndinu munapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo. 25 Ndipo mwa mzimu woyela inu munalankhula kudzela mwa kholo lathu Davide mtumiki wanu kuti, ‘N’cifukwa ciyani anthu a m’maiko osiyanasiyana anakwiya? Komanso n’cifukwa ciyani anthu amitundu yosiyanasiyana anasinkhasinkha zinthu zopanda pake? 26 Mafumu a padziko lapansi anaimilila pamalo awo, ndipo olamulila anasonkhana pamodzi mogwilizana pofuna kulimbana ndi Yehova komanso wodzozedwa wake.’* 27 Pakuti Herode, Pontiyo Pilato, kuphatikizapo anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana pamodzi mumzinda uno kuti alimbane ndi mtumiki wanu woyela Yesu, amene inu munamudzoza. 28 Iwo anasonkhana pamodzi kuti acite zimene inu munakambilatu. Mwa mphamvu yanu, munapangitsa kuti izi zicitike mogwilizana ndi cifunilo canu. 29  Tsopano Yehova, mvelani mmene akutiopsezela, ndipo thandizani ife akapolo anu kuti tipitilize kulankhula mawu anu molimba mtima. 30 Pitilizani kutambasula dzanja lanu kuti anthu acilitsidwe, ndiponso kuti zizindikilo ndi zodabwitsa zicitike kudzela m’dzina la Yesu mtumiki wanu woyela.”

31 Iwo atapemphela mocondelela,* malo amene anasonkhanapo anagwedezeka, ndiyeno aliyense wa iwo anadzazidwa ndi mzimu woyela ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.

32 Kuwonjezela apo, khamu la anthu amene anakhulupilila linali ndi maganizo ofanana,* ndipo palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anakamba kuti zinthu zimene anali nazo zinali zake yekha, koma zonse zimene anali nazo zinali zawo onse. 33 Ndipo atumwiwo anapitiliza kucitila umboni mwamphamvu kwambili za kuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo Mulungu anawaonetsa cisomo onsewo. 34 Kukamba zoona, pakati pawo panalibe aliyense amene anali kusowa kanthu, cifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba anali kuzigulitsa n’kubweletsa ndalamazo. 35 Ndipo iwo anali kupeleka ndalamazo kwa atumwi. Kenako ndalamazo zinali kupelekedwa kwa aliyense malinga ndi zosowa zake. 36 Conco Yosefe, amene atumwiwo anamupatsanso dzina lakuti Baranaba (limene limatanthauza “Mwana wa Citonthozo”), amenenso anali Mlevi mbadwa ya ku Kupuro, 37 anali ndi munda. Iye anaugulitsa mundawo n’kubweletsa ndalama zake, kenako anazipeleka kwa atumwi.

5 Tsopano munthu wina, dzina lake Hananiya, ndi mkazi wake Safira, anagulitsa munda wawo. 2 Koma mwamseli iye anacotsapo ndalama zina ndipo mkazi wake anadziwa. Ndalama zotsalazo anazipeleka kwa atumwi. 3 Koma Petulo anati: “Hananiya, n’cifukwa ciyani Satana wakulimbitsa mtima kuti unamize mzimu woyela n’kubisa ndalama zina za mundawo? 4 Mundawo usanaugulitse, kodi sunali wako? Ndipo utaugulitsa, ndalama zake sukanacita nazo zimene unali kufuna? N’cifukwa ciyani unaganiza zocita zimenezi mumtima mwako? Sunanamize anthu koma wanamiza Mulungu.” 5 Hananiya atamva mawu amenewa anangoti pansi khu! n’kumwalila. Ndipo onse amene anamva za nkhaniyi anacita mantha kwambili. 6 Ndiyeno anyamata anabwela n’kukulunga thupi lake mu nsalu kenako anatuluka naye n’kukamuika m’manda.

7 Ndiyeno patapita maola pafupifupi atatu mkazi wake analowa ndipo sanadziwe zimene zinacitika. 8 Petulo anamufunsa kuti: “Ndiuze, kodi ndalama zonse zimene awilinu munagulitsa munda uja ndi izi?” Iye anati: “Inde, ndi zimenezi.” 9 Kenako Petulo anamufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani inu awili munagwilizana zakuti muyese mzimu wa Yehova? Taona, mapazi a anthu amene aika mwamuna wako m’manda ali pakhomo. Iwenso akunyamula n’kutuluka nawe.” 10 Nthawi yomweyo iye anangoti pansi khu! kumapazi a Petulo n’kufa. Pamene anyamata aja amalowa anapeza kuti wafa kale. Iwo anamunyamula n’kutuluka naye, ndipo anapita kukamuika m’manda pafupi ndi mwamuna wake. 11 Conco mpingo wonse komanso anthu onse amene anamva zimenezi, anacita mantha kwambili.

12 Komanso atumwi anapitiliza kucita zizindikilo ndi zodabwitsa zambili pakati pa anthu. Ndipo onse okhulupilila anali kusonkhana pa Khonde la Zipilala la Solomo. 13 Kukamba zoona, panalibe ndi mmodzi yemwe mwa enawo amene analimba mtima kugwilizana ndi ophunzilawo, koma anthu anali kuwatamanda. 14 Kuposa pamenepo, okhulupilila Ambuye anapitiliza kuwonjezeka cifukwa amuna ndi akazi ambili anakhala okhulupilila. 15 Iwo anali kubweletsa anthu odwala m’misewu n’kuwagoneka pa timabedi komanso pa mphasa kuti Petulo akadutsa, cithunzithunzi cake cokha cifike pa ena a iwo. 16 Ndiponso makamu a anthu ocokela ku mizinda yozungulila Yerusalemu anali kupita kumeneko, atanyamula anthu odwala komanso amene anali kuzunzika ndi mizimu yonyansa. Ndipo onsewo anacilitsidwa.

17 Koma mkulu wa ansembe pamodzi ndi onse amene anali naye, amene anali a gulu la mpatuko la Asaduki, anacita nsanje. 18 Conco iwo ananyamuka n’kugwila* atumwiwo, ndipo anawaponya m’ndende ya mumzindawo. 19 Koma usiku, mngelo wa Yehova anatsegula zitseko za ndendeyo n’kuwatulutsa, ndipo anawauza kuti: 20 “Pitani mukaimilile m’kacisi, ndipo mupitilize kuuza anthu zokhudza moyo umene ukubwelawo.” 21 Atamva zimenezi, iwo analowa m’kacisi m’mamawa kwambili n’kuyamba kuphunzitsa.

Tsopano mkulu wa ansembe ndi onse amene anali nawo atafika, anasonkhanitsa a m’Bungwe Lalikulu la Ayuda* komanso akulu onse a Aisiraeli. Kenako anatuma alonda a ku ndende kuti akatenge atumwiwo n’kuwabweletsa kwa iwo. 22 Koma alondawo atafika kumeneko sanawapeze m’ndendemo. Conco iwo anabwelela kuti akawafotokozele zimenezi. 23 Iwo anati: “Ife tapeza kuti ndende ndi yokhoma ndiponso ndi yotetezedwa bwino, ndipo alonda anali cilili m’makomo. Koma titatsegula tapeza kuti mkati mulibe aliyense.” 24 Akapitawo a pakacisi komanso ansembe aakulu atamva zimenezi anathedwa nzelu, cifukwa sanadziwe kuti nkhaniyi idzatha bwanji. 25 Koma kunabwela munthu wina, ndipo anawauza kuti: “Anthu inu! Amuna aja amene munawaika m’ndende ali m’kacisi aimilila mmenemo ndipo akuphunzitsa anthu.” 26 Ndiyeno kapitawo wa pakacisi uja ndi alonda ake anapita kukawatenga. Koma osati mwaciwawa cifukwa iwo anali kuopa kuti anthu angawaponye miyala.

27 Conco anawabweletsa n’kuwaimilika pamaso pa Bungwe Lalikulu la Ayuda. Kenako mkulu wa ansembe ananena 28 kuti: “Tinakulamulani mwamphamvu kuti musapitilize kuphunzitsa m’dzina limeneli, koma taonani mwadzaza Yerusalemu yense ndi zimene mukuphunzitsa, ndipo mwatsimikiza mtima kubweletsa magazi a munthu uyu pa ife.” 29 Poyankha, Petulo ndi atumwi enawo anati: “Ife tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila osati anthu. 30 Mulungu wa makolo athu akale anaukitsa Yesu, amene inu munamupha mwa kumupacika pamtengo. 31 Mulungu anamukweza kudzanja lake lamanja monga Mtumiki wake Wamkulu ndi Mpulumutsi, kuti Aisiraeli alape komanso kuti akhululukidwe macimo awo. 32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zimenezi. Mzimu woyela umene Mulungu waupeleka kwa anthu amene amamumvela monga wolamulila wawo, nawonso ndi mboni.”

33 Iwo atamva zimenezi anakwiya* kwambili moti anafuna kuwapha. 34 Koma Mfarisi wina dzina lake Gamaliyeli anaimilila m’Bungwe Lalikulu la Ayuda. Iye anali mphunzitsi wa Cilamulo amene anthu onse anali kumulemekeza, ndipo analamula kuti amunawo atulutsidwe panja kwakanthawi. 35 Kenako anawauza kuti: “Amuna inu Aisiraeli, samalani ndi zimene mukufuna kuwacita anthuwa. 36 Mwacitsanzo, m’masiku akumbuyoku, kunali Teuda amene anadzichukitsa kwambili, ndipo amuna pafupifupi 400 analowa m’gulu lake. Koma iye anaphedwa, ndipo onse amene anali kumutsatila anamwazikana moti sanapezekenso. 37 Pambuyo pake kunabwela Yudasi Mgalileya m’masiku a kalembela. Iye anakopa anthu ambili ndipo anali kumutsatila. Koma nayenso anafa ndipo onse amene anali kumutsatila anamwazikana. 38 Conco malinga ndi mmene zinthu zilili apa, ndikukuuzani kuti musalimbane nawo anthu awa, koma alekeni. Cifukwa ngati pulani yawo kapena nchito yawo ndi yocokela kwa anthu sipita patali. 39 Koma ngati ndi yocokela kwa Mulungu, simungakwanitse kuwaletsa. Cifukwa mukapitiliza mudzapezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.” 40 Iwo anamvela malangizo ake, ndipo anaitana atumwiwo n’kuwakwapula* ndi kuwalamula kuti aleke kulankhula m’dzina la Yesu, ndipo anawamasula.

41 Conco atumwiwo, anacoka pamaso pa Bungwe Lalikulu la Ayuda ali osangalala cifukwa Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucititsidwa manyazi kaamba ka dzina la Yesu. 42 Ndipo tsiku ndi tsiku iwo anapitiliza kuphunzitsa mwakhama m’kacisi komanso kunyumba ndi nyumba, ndipo anali kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu Yesu.

6 Tsopano m’masiku amenewo pamene ophunzila anali kuwonjezeka, Ayuda okamba Cigiriki anayamba kudandaula za Ayuda okamba Ciheberi, cifukwa akazi amasiye a Cigiriki anali kunyalanyazidwa pa kagawidwe ka cakudya ca tsiku ndi tsiku. 2 Conco atumwi 12 aja anasonkhanitsa khamu la ophunzila n’kunena kuti: “Sibwino* kuti ife tilekeze kuphunzitsa mawu a Mulungu n’kuyamba kugawa cakudya. 3 Conco abale, sankhani amuna 7 pakati panu a mbili yabwino, odzala ndi mzimu komanso nzelu kuti tiwapatse udindo wosamalila nchitoyi. 4 Koma ife tidzadzipeleka pa kupemphela ndi kuphunzitsa mawu a Mulungu.” 5 Zimene anakamba zinasangalatsa khamu lonse, moti anasankha Sitefano munthu wacikhulupililo colimba, ndiponso wodzala ndi mzimu woyela. Anasankhanso Filipo, Pulokoro, Nikanora, Timoni, Pamenasi, komanso Nikolao wocokela ku Antiokeya, wotembenukila ku Ciyuda. 6 Iwo anawapeleka kwa atumwi, ndipo atumwiwo atawapemphelela anaika manja pa amunawo.

7 Zitatelo, mawu a Mulungu anapitiliza kufalikila, ndipo ciwelengelo ca ophunzila cinali kuwonjezeka kwambili mu Yerusalemu. Ngakhale ansembe ambili anakhala okhulupilila.

8 Tsopano Sitefano wokondedwa ndi Mulungu, komanso amene Mulungu anamupatsa mphamvu, anali kucita zodabwitsa zazikulu ndi zizindikilo pakati pa anthu. 9 Koma amuna ena a gulu lochedwa Sunagoge wa Omasulidwa anabwela pamodzi ndi anthu a ku Kurene, a ku Alekizandiriya, ku Kilikiya komanso ku Asia kudzatsutsana ndi Sitefano. 10 Koma iwo sanathe kulimbana naye cifukwa ca nzelu zake komanso mzimu umene anali nawo polankhula. 11 Zitatelo, iwo ananyengelela mseli anthu kuti anene kuti: “Ife tamumva akulankhula zinthu zonyoza Mose komanso Mulungu.” 12 Iwo anatuntha gulu la anthu, akulu komanso alembi, kuti amugwile modzidzimutsa n’kupita naye ku Bungwe Lalikulu la Ayuda.* 13 Iwo anabweletsa mboni zonama zimene zinakamba kuti: “Munthu uyu akungolankhula zinthu zambili zonyoza malo oyelawa komanso Cilamulo. 14 Mwacitsanzo, tamumva akunena kuti Yesu Mnazareti adzagwetsa malo ano n’kusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”

15 Ndipo anthu onse amene anali m’Bungwe Lalikulu la Ayuda, atamuyang’anitsitsa Sitefano, anaona kuti nkhope yake inali kuoneka ngati ya mngelo.

7 Koma mkulu wa ansembe anafunsa kuti: “Kodi zimenezi n’zoona?” 2 Sitefano anayankha kuti: “Anthu inu, abale anga ndi azibambo anga, tamvelani. Ulemelelo wa Mulungu unaonekela kwa atate wathu Abulahamu pamene anali ku Mesopotamiya asanapite kukakhala ku Harana. 3 Anamuuza kuti: ‘Tuluka m’dziko lako komanso pakati pa abale ako upite kudziko limene ndidzakuonetsa.’ 4 Cotelo iye anatuluka m’dziko la Akasidi n’kukakhala ku Harana. Ndiyeno kumeneko, atate ake atamwalila, Mulungu anamucititsa kuti akhale m’dziko lino limene inu mukukhala. 5 Koma kumeneko sanamupatse colowa ciliconse, ngakhale kamalo kakang’ono. M’malomwake, anamulonjeza kuti adzamupatsa dzikolo kuti likhale colowa cake, komanso ca mbadwa* zake, ngakhale kuti panthawiyo analibe mwana. 6 Komanso Mulungu anamuuza kuti mbadwa* zake zidzakhala alendo m’dziko la eni, ndipo anthu adzawapanga kukhala akapolo ndi kuwazunza* kwa zaka 400. 7 Mulungu anati, ‘Mtundu umene udzawasunga ngati akapolo, ine ndidzauweluza. Ndipo pambuyo pa zimenezi, iwo adzamasulidwa n’kudzanditumikila pamalo ano.’

8 “Anamupatsanso cipangano ca mdulidwe. Kenako anabeleka Isaki, ndipo anamucita mdulidwe pa tsiku la 8. Isaki nayenso anabeleka* Yakobo, ndipo Yakobo anabeleka mitu ya mabanja 12. 9 Mitu ya mabanja imeneyo inamucitila nsanje Yosefe, ndipo inamugulitsa ku Iguputo. Koma Mulungu anali naye, 10 ndipo anamupulumutsa m’masautso ake onse. Komanso anali kumukonda, ndipo anam’patsa nzelu pamaso pa Farao mfumu ya Iguputo. Farao ameneyo, anasankha Yosefe kuti aziyang’anila Iguputo ndi nyumba yake yonse. 11 Koma ku Iguputo ndi ku Kanani kunagwa njala yaikulu moti kunali mavuto aakulu. Ndipo makolo athu akale amenewo sanali kukwanitsa kupeza cakudya. 12 Koma Yakobo anamva kuti ku Iguputo kuli cakudya, ndipo anatuma makolo athu kwa nthawi yoyamba. 13 Paulendo waciwili, Yosefe anadziulula kwa abale ake, ndipo makolo ake ndi abale ake a Yosefe anadziwika kwa Farao. 14 Conco Yosefe anatumiza uthenga woitana Yakobo atate ake ndi abale ake onse. Ndipo onse pamodzi anali anthu 75. 15 Ndiyeno Yakobo anapita ku Iguputo, ndipo anafela kumeneko. Nawonso makolo athu akale anafela kumeneko. 16 Kenako, mafupa awo anatengedwa n’kupita nawo ku Sekemu kumene anaikidwa m’manda, amene Abulahamu anagula ndi ndalama zasiliva kwa ana a Hamori ku Sekemu.

17 “Pamene nthawi inali kuyandikila yakuti lonjezo limene Mulungu anauza Abulahamu likwanilitsidwe, anthuwo anaculuka kwambili ku Iguputo. 18 Kenako mfumu ina inayamba kulamulila Iguputo, mfumuyo sinali kumudziwa Yosefe. 19 Mfumu imeneyo inawacenjelela anthu a mtundu wathu, ndipo inakakamiza makolo athu amenewo kusiya makanda awo kuti asakhale ndi moyo. 20 Panthawiyo Mose anabadwa, ndipo anali wokongola m’maso mwa Mulungu. Iye analeledwa m’nyumba ya atate ake kwa miyezi itatu. 21 Koma pamene anamusiya yekha, mwana wamkazi wa Farao anamutenga n’kuyamba kumulela ngati mwana wake. 22 Conco Mose anaphunzitsidwa nzelu zonse za Aiguputo. Ndiponso anali wamphamvu m’zokamba komanso m’zocita zake.

23 “Tsopano iye atakwanitsa zaka 40, anaganiza zopita kukaona* abale ake, ana a Isiraeli. 24 Mose ataona Mwisiraeli akuzunzidwa, anamuteteza ndipo anabwezela mwa kupha Mwiguputo amene anali kuzunza Mwisiraeliyo. 25 Mose anali kuganiza kuti abale ake adzazindikila kuti Mulungu akuwapulumutsa kudzela m’dzanja lake. Koma iwo sanazindikile zimenezo. 26 Tsiku lotsatila iye anaonekela kwa iwo pamene anali kumenyana. Ndipo anayesa kuwayanjanitsa mwa mtendele n’kuwauza kuti, ‘Amuna inu m’pacibale. N’cifukwa ciyani mukuzunzana?’ 27 Koma amene anali kuzunza mnzakeyo anakankha Mose n’kunena kuti: ‘Ndani anakuika kukhala wolamulila komanso woweluza wathu? 28 Kodi ukufuna kundipha mmene unaphela Mwiguputo uja dzulo?’ 29 Iye atamva izi, anathawa n‘kupita kukakhala mlendo m’dziko la Midiyani. Kumeneko anabeleka ana aamuna awili.

30 “Patapita zaka 40, mngelo anaonekela kwa iye m’cipululu ku Phili la Sinai, m’citsamba caminga coyaka moto walawilawi. 31 Mose ataona zimenezi anadabwa kwambili. Koma pamene anali kuyandikila kuti ayang’anitsitse, pa citsambaco panamveka mawu a Yehova akuti: 32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki komanso wa Yakobo.’ Conco Mose anayamba kunjenjemela, ndipo sanapitilize kuyang’anitsitsa pa citsambaco. 33 Yehova anamuuza kuti: ‘Vula nsapato kumapazi ako, cifukwa malo amene waimapowa ndi oyela. 34 Ine ndaona kupondelezedwa kwa anthu anga ku Iguputo. Ndamva kubuula kwawo, ndipo ndatsika kudzawapulumutsa. Tsopano tamvela, ndikutuma ku Iguputo.’ 35 Mose ameneyo ndi uja amene iwo anamukana n’kunena kuti, ‘Ndani anakuika kukhala wolamulila komanso woweluza?’ Ameneyo ndi amene Mulungu anamutuma monga wolamulila komanso wowaombola kudzela mwa mngelo amene anaonekela kwa iye m’citsamba caminga. 36 Munthu ameneyu anawatsogolela n’kutuluka nawo, ndipo anacita zodabwitsa komanso zizindikilo ku Iguputo, pa Nyanja Yofiila ndiponso m’cipululu kwa zaka 40.

37 “Uyu ndi Mose amene anauza ana Aisiraeli kuti: ‘Mulungu adzakuutsilani mneneli ngati ine pakati pa abale anu.’ 38 Ameneyu ndi amene anali pakati pa Aisiraeli m’cipululu pamodzi ndi mngelo amene analankhula naye, komanso makolo athu pa Phili la Sinai. Iye analandila mawu a Mulungu amoyo n’kutipatsa. 39 Makolo athu anakana kumumvela. Koma anamukankhila kumbali ndipo m’mitima yawo anabwelela ku Iguputo. 40 Iwo anauza Aroni kuti: ‘Tipangile milungu ititsogolele cifukwa sitidziwa zimene zacitikila Mose amene anatitsogolela pocoka m’dziko la Iguputo.’ 41 Conco m’masiku amenewo iwo anapanga fano la mwana wa ng’ombe. Atatelo, anabweletsa nsembe n’kuzipeleka kwa fanolo, ndipo anayamba kusangalala ndi nchito ya manja awo. 42 Conco Mulungu anawasiya kuti atumikile zakumwamba* monga mmene zinalembedwela m’buku la Aneneli kuti: ‘Inu nyumba ya Isiraeli kodi munali kupeleka nsembe ndi zopeleka zina kwa ine kwa zaka 40 m’cipululu? 43 Inuyo munali kunyamula cihema ca Moloki ndi nyenyezi ya mulungu wochedwa Refani, mafano amene munapanga kuti muziwalambila. Conco ndidzakupitikitsilani kutali kupitilila ku Babulo.’

44 “Makolo athu akale anali ndi cihema ca umboni m’cipululu. Cihemaci cinali kuonetsa kuti Mulungu ali nawo. Mulungu anauza Mose kuti acipange, ndipo anacipanga mogwilizana ndi pulani imene Mulungu anamuonetsa. 45 Makolo athu analandila cihemaci kucokela kwa makolo awo, ndipo analowa naco pamodzi ndi Yoswa m’dziko limene linali la anthu a mitundu ina. Anthu amenewa Mulungu anawapitikitsa pamaso pa makolo athu. Ndipo cihemaco cinakhalapobe mpaka m’masiku a Davide. 46 Mulungu anamukomela mtima Davide, ndipo iye anapempha kuti apatsidwe mwayi wakuti amange nyumba yoti Mulungu wa Yakobo azikhalamo. 47 Koma Solomo ndi amene anamangila Mulungu nyumba. 48 Komabe, Wam’mwambamwamba sakhala m’nyumba zopangidwa ndi manja, malinga ndi mmene mneneli anakambila kuti: 49 ‘Yehova anakamba kuti, Kumwamba ndiko mpando wanga wacifumu, ndipo dziko lapansi ndi copondapo mapazi anga. Kodi nyumba imene mufuna kundimangila idzakhala yotani? Nanga malo anga opumulilako ali kuti? 50 Kodi dzanja langa si limene linapanga zinthu zonsezi?’

51 “Anthu okanga inu, komanso osacita mdulidwe wamumtima ndi wam’makutu. Nthawi zonse mumatsutsa mzimu woyela, mumacita zinthu monga mmene makolo anu anali kucitila. 52 Kodi ndi mneneli uti amene makolo anu sanazunze? Iwo anapha aja amene anali kulengezelatu za kubwela kwa wolungamayo, amene inu munamupeleka ndi kumupha. 53 Mulungu anagwilitsa nchito angelo kuti akupatseni Cilamulo, koma inu simunacitsatile.”

54 Iwo atamva zimenezi anakwiya* kwambili m’mitima yawo, ndipo anayamba kumukukutila mano. 55 Koma iye atadzazidwa ndi mzimu woyela, anayang’ana kumwamba n’kuona ulemelelo wa Mulungu, ndiponso Yesu ataimilila kudzanja lamanja la Mulungu. 56 Ndipo iye anati: “Taonani! Ndikuona kumwamba kwatseguka, ndipo Mwana wa munthu waimilila kudzanja la manja la Mulungu.” 57 Iwo atamva zimenezi anafuula kwambili, ndipo anatseka matu awo ndi manja. Kenako onse anathamangila pa iye. 58 Atamutulutsila kunja kwa mzinda anayamba kumuponya miyala. Ndipo mboni zija zinaika zovala zawo zakunja ku mapazi a mnyamata wina dzina lake Saulo. 59 Pamene anthuwo anali kumuponya miyala, Sitefano anacondelela kuti: “Ambuye Yesu, landilani mzimu wanga.” 60 Kenako anagwada n’kufuula ndi mawu amphamvu kuti: “Yehova, musawaimbe mlandu wa chimoli.” Atakamba zimenezi, anafa.*

8 Saulo anavomeleza zakuti Sitefano aphedwe.

Pa tsiku limenelo, mpingo umene unali ku Yerusalemu unayamba kuzunzidwa koopsa. Ndipo ophunzila onse anamwazikana n’kupita ku zigawo za ku Yudeya ndi Samariya, kupatulapo atumwi. 2 Koma anthu oopa Mulungu ananyamula mtembo wa Sitefano n’kukauika m’manda, ndipo anamulila kwambili. 3 Saulo anayamba kuzunza mpingo mwankhanza. Iye anali kulowa m’nyumba ndi nyumba kumatulutsa panja amuna ndi akazi, kenako n’kukawaponya m’ndende.

4 Komabe, anthu aja amene anamwazikana anapitiliza kulalikila uthenga wabwino wa mawu a Mulungu kumene anapita. 5 Tsopano Filipo anapita ku mzinda* wa Samariya, ndipo anayamba kulalikila za Khristu kwa anthu a kumeneko. 6 Khamu la anthu linali kumvetsela zimene Filipo anali kukamba. Onse pamodzi anali kumvetsela ndi kuona zizindikilo zimene iye anali kucita. 7 Pakuti ambili a iwo anali ndi mizimu yonyansa, ndipo mizimuyo inali kufuula mwamphamvu n’kutuluka. Komanso anthu ambili ofa ziwalo ndi olemala anali kucilitsidwa. 8 Conco anthu a mumzindawo anakondwela kwambili.

9 Ndiyeno mumzindawo munali munthu wina dzina lake Simoni. Izi zisanacitike, iye anali kucita zamatsenga ndiponso zodabwitsa kwa anthu a ku Samariya. Iye anali kudzitama kuti ndi munthu wamphamvu. 10 Anthu onse, kuyambila wamng’ono mpaka wamkulu, anali kucita naye cidwi n’kumanena kuti: “Munthu uyu ali ndi mphamvu yaikulu yocokela kwa Mulungu.” 11 Conco iwo anali kucita naye cidwi cifukwa anawadabwitsa kwa nthawi yaitali ndi zamatsenga zake. 12 Koma pamene anthuwo anakhulupilila Filipo, yemwe anali kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndiponso wokamba za dzina la Yesu Khristu, amuna ndi akazi omwe anali kubatizika. 13 Nayenso Simoni anakhala wokhulupilila, ndipo atabatizika, anapitiliza kutsatila Filipo. Iye anali kudabwa poona zizindikilo* ndi nchito zazikulu zamphamvu zimene zinali kucitika.

14 Pamene atumwi ku Yerusalemu anamva kuti anthu a ku Samariya alandila mawu a Mulungu, anawatumizila Petulo ndi Yohane. 15 Iwo anapita kumeneko ndipo anawapemphelela kuti alandile mzimu woyela. 16 Cifukwa pa nthawiyi, mzimu woyela unali usanafike pa aliyense wa iwo, koma anali atangobatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu. 17 Ndiyeno atumwiwo anaika manja awo pamitu ya anthuwo, ndipo iwo anayamba kulandila mzimu woyela.

18 Simoni ataona kuti anthu akulandila mzimu woyela atumwiwo akawaika manja pamutu, anafuna kuwapatsa ndalama. 19 Iye anati: “Inenso ndipatsenkoni mphamvu kuti ndikaika manja anga pamutu pa munthu azilandila mzimu woyela.” 20 Koma Petulo anamuuza kuti: “Siliva wako uwonongeke naye pamodzi, cifukwa ukuganiza kuti ungagule mphatso yaulele ya Mulungu ndi ndalama. 21 Nchitoyi sikukhudza, ndipo ulibepo mbali kapena gawo cifukwa mtima wako si wowongoka pamaso pa Mulungu. 22 Conco lapa coipa cimene wacitaci, ndipo umucondelele Yehova kuti ngati n’kotheka akukhululukile pa maganizo oipa amene ali mumtima mwako. 23 Cifukwa taona kuti ndiwe poizoni wowawa* ndipo ndiwe kapolo wa kupanda cilungamo.” 24 Simoni anawayankha kuti: “Ndipelekeleni pemphelo locondelela kwa Yehova kuti zinthu zimene mwakambazi zisandicitikile.”

25 Conco iwo atatsiliza kucitila umboni mokwanila ndi kulankhula mawu a Yehova, anayamba kubwelela ku Yerusalemu. Pobwelela anali kulengeza uthenga wabwino m’midzi yambili ya Asamariya.

26 Komabe mngelo wa Yehova analankhula ndi Filipo kuti: “Nyamuka upite kum’mwela kumsewu wocokela ku Yerusalemu kupita ku Gaza.” (Msewu umenewu unali wa m’cipululu.) 27 Iye atamva zimenezi, ananyamuka n’kupita, ndipo anakumana ndi nduna ya ku Itiyopiya, munthu wa ulamulilo pansi pa Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Ndunayo ndiyo inali kuyang’anila cuma conse ca mfumukazi imeneyi, ndipo inapita ku Yerusalemu kukalambila Mulungu. 28 Iyo inali kubwelela kwawo ndipo inali khale m’galeta lake ikuwelenga mokweza ulosi wa mneneli Yesaya. 29 Conco mzimu unauza Filipo kuti: “Pita ufike pafupi ndi galetalo.” 30 Filipo anali kuthamanga m’mbali mwa galetalo, ndipo anamumva akuwelenga mokweza ulosi wa mneneli Yesaya. Ndiyeno Filipo anamufunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwelengazo?” 31 Iye anayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulila?” Conco anapempha Filipo kuti akwele ndi kukhala naye m’galetamo. 32 Mawu a m’Malemba amene iye anali kuwelenga anali akuti: “Anapelekedwa kumalo okamuphela ngati nkhosa. Ndipo iye sanatsegule pakamwa pake ngati mwana wa nkhosa amene wangokhala cete pamaso pa womumeta ubweya. 33 Pamene anali kumucititsa manyazi, sanamucitile zinthu mwacilungamo. Kodi ndani amene angafotokoze mwatsatanetsatane m’badwo wa makolo ake? Cifukwa moyo wake wacotsedwa padziko lapansi.”

34 Ndiyeno ndunayo inauza Filipo kuti: “Conde ndiuze, kodi mneneliyu anali kukamba za ndani apa? Anali kukamba za iye mwini kapena za munthu wina?” 35 Filipo anayamba kulankhula. Iye anayambila palembali kumuuza uthenga wabwino wonena za Yesu. 36 Pamene iwo anali kuyenda mumsewumo, anafika pamene panali madzi ambili, ndipo nduna ija inauza Filipo kuti: “Taonani! Madzi si awa, cikundiletsa kubatizika n’ciyani?” 37* —— 38 Zitatelo, iye analamula kuti galetalo liime. Kenako Filipo ndi nduna ija anatsika n’kulowa m’madzimo, ndipo Filipo anaibatiza. 39 Iwo atatuluka m’madzimo, mwamsanga mzimu wa Yehova unatsogolela Filipo kuti acoke kumeneko moti nduna ija sinamuonenso, koma inapitiliza ulendo wake ikusangalala. 40 Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Asidodi, ndipo anayamba kulengeza uthenga wabwino kumizinda yonseyo mpaka anafika ku Kaisareya.

9 Koma Saulo anapitilizabe kuopseza ophunzila a Ambuye, ndipo anali kufunitsitsa kuwapha. Conco iye anapita kwa mkulu wa ansembe 2 kukapempha makalata opita nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti akhale ndi cilolezo cokamanga mwamuna kapena mkazi aliyense amene angapezeke kuti akutsatila Njilayo* n’kubwela naye ku Yerusalemu.

3 Tsopano ali pa ulendo wake umenewo, atatsala pang’ono kufika ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kocokela kumwamba kunamuzungulila. 4 Izi zitacitika, anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti: “Saulo, Saulo, n’cifukwa ciyani ukundizunza?” 5 Saulo anafunsa kuti: “Ambuye, kodi ndinu ndani?” Iye anamuyankha kuti: “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza. 6 Koma nyamuka ulowe mu mzindawo ndipo udzauzidwa zoyenela kucita.” 7 Anthu amene anali naye pa ulendowo anangoima cilili kusowa conena. Iwo anamva ndithu mawuwo koma sanaone aliyense. 8 Ndiyeno Saulo anaimilila, koma ngakhale kuti maso ake anali otseguka, sanali kuona ciliconse. Conco anamugwila dzanja n’kulowa naye mumzinda wa Damasiko. 9 Kwa masiku atatu Saulo sanali kuona, ndipo sanadye kapena kumwa ciliconse.

10 Ku Damasiko kunali wophunzila wina dzina lake Hananiya, ndipo Ambuye anamuuza m’masomphenya kuti: “Hananiya!” Iye anayankha kuti: “Ine pano Ambuye.” 11 Ambuye anamuuza kuti: “Nyamuka upite ku msewu wochedwa Wowongoka. Ukakafika panyumba ya Yudasi, ukafunse za munthu wina dzina lake Saulo wa ku Tariso. Pakuti iye akupemphela. 12 Ndipo m’masomphenya, iye waona munthu wina dzina lake Hananiya akubwela kwa iye n’kumuika manja pamutu kuti ayambenso kuona.” 13 Koma Hananiya anayankha kuti: “Ambuye, ndamva kwa anthu ambili za munthu ameneyu, komanso zoipa zonse zimene anacitila oyela anu ku Yerusalemu. 14 Ndipo anatenga cilolezo kwa ansembe aakulu kuti amange aliyense woitanila pa dzina lanu.” 15 Koma Ambuye anamuuza kuti: “Pita! Cifukwa munthu ameneyu ndi ciwiya cosankhidwa kwa ine kuti cikacitile umboni dzina langa kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu ndi kwa Aisiraeli. 16 Pakuti ndidzamuonetsa bwinobwino mavuto onse amene adzakumana nawo cifukwa ca dzina langa.”

17 Conco Hananiya anapita n’kukalowa m’nyumbamo, ndipo anaika manja ake pa iye n’kunena kuti: “Saulo m’bale wanga, Ambuye Yesu amene anaonekela kwa iwe pa msewu pamene unali kubwela kuno, wandituma kwa iwe kuti uyambenso kuona komanso kuti udzazidwe ndi mzimu woyela.” 18 Nthawi yomweyo m’maso mwake munagwa tinthu tooneka ngati mamba, ndipo anayambanso kuona. Kenako iye anapita kukabatizidwa. 19 Ndiyeno anadya cakudya n’kupeza mphamvu.

Iye anakhala ndi ophunzila ku Damasiko kwa masiku angapo. 20 Posapita nthawi, iye anayamba kulalikila za Yesu m’masunagoge kuti ameneyu ndi Mwana wa Mulungu. 21 Koma onse amene anamumva anadabwa kwambili, ndipo anali kukamba kuti: “Kodi munthu ameneyu si uja amene anazunza koopsa anthu oitanila pa dzina limeneli ku Yerusalemu? Kodi sanabwele kuno n’colinga coti awamange n’kuwapeleka* kwa ansembe aakulu?” 22 Koma Saulo anapitiliza kukhala ndi mphamvu zambili, ndipo anali kuwathetsa nzelu Ayuda okhala ku Damasiko pamene anali kuwatsimikizila momveka bwino kuti Yesu ndi Khristu.

23 Tsopano patapita masiku ambili, Ayudawo anakonza ciwembu cakuti amuphe. 24 Koma Saulo anadziwa za ciwembu cawo. Iwo anali kuyembekezelanso pa mageti a mumzindawo mosamala kwambili usana ndi usiku kuti amuphe ndithu. 25 Conco ophunzila ake anamuika m’dengu n’kumutsitsila kunja usiku kupitila pa cibowo ca mpanda.

26 Atafika ku Yerusalemu, iye anayesetsa kugwilizana ndi ophunzila kumeneko, koma onse anali kumuopa cifukwa sanakhulupilile kuti anakhaladi wophunzila. 27 Conco Baranaba anamuthandiza ndipo anapita naye kwa atumwi. Iye anawafotokozela mwatsatanetsatane mmene Saulo anaonela Ambuye pa msewu pamene analankhula naye, komanso mmene Saulo analankhulila molimba mtima m’dzina la Yesu ku Damasiko. 28 Cotelo iye anakhalabe nawo, ndipo anali kuyenda momasuka mu Yerusalemu, akulankhula molimba mtima m’dzina la Ambuye. 29 Iye anali kulankhula komanso kutsutsana ndi Ayuda olankhula Cigiriki. Iwo anayesayesa kupeza njila yoti amuphele. 30 Abale atadziwa zimenezi, anapita naye ku Kaisareya n’kumutumiza ku Tariso.

31 Ndiyeno, mpingo ku Yudeya konse, Galileya komanso ku Samariya unayamba kukhala pamtendele ndipo unalimba. Cifukwa cakuti mpingo unali kuopa Yehova komanso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyela, mpingowo unapitilizabe kukula.

32 Pamene Petulo anali kuyenda m’cigawo conseco, anafikanso kwa oyela amene anali kukhala ku Luda. 33 Kumeneko anapeza munthu wina dzina lake Eneya. Iye anali kukhala gone pa bedi lake kwa zaka 8 cifukwa anali wakufa ziwalo. 34 Petulo anamuuza kuti: “Eneya, Yesu Khristu akukucilitsa. Uka konza bedi lako.” Ndipo nthawi yomweyo ananyamuka. 35 Pamene anthu onse a ku Luda komanso ku cigawo ca Sharoni anamuona anayamba kukhulupilila Ambuye.

36 Tsopano ku Yopa kunali wophunzila wina dzina lake Tabita, dzinali mu Cigiriki limamasulidwa kuti “Dorika.”* Mayiyu anali kucita zinthu zambili zabwino, ndipo anali kupatsa ena mphatso zambili zacifundo. 37 Koma m’masiku amenewo iye anadwala n’kumwalila. Conco iwo anamusambika n’kumugoneka m’cipinda cam’mwamba. 38 Popeza kuti mzinda wa Luda unali pafupi ndi mzinda wa Yopa, ophunzilawo atamva kuti Petulo ali mumzindawo, anatuma anthu awili n’kukamupempha kuti: “Conde bwelani kuno mwamsanga.” 39 Petulo atamva zimenezi, ananyamuka n’kupita nawo. Ndiyeno iye atafika, iwo anapita naye m’cipinda cam’mwamba cija. Akazi onse amasiye anapita kwa iye akulila, ndipo anali kumuonetsa zovala zambili ndi mikanjo* imene Dorika anawasokela pamene anali nawo. 40 Petulo anauza anthu onse kuti atuluke, kenako anagwada n’kupemphela. Ndiyeno anatembenuka n’kuyang’ana thupilo, ndipo anati: “Tabita, uka!” Ndiyeno mayiyo anatsegula maso ake, ndipo ataona Petulo anauka n’kukhala tsonga. 41 Petulo anamugwila dzanja n’kumuimilika mayiyo. Iye anaitana oyelawo komanso akazi amasiye, ndipo anamupeleka kwa iwo ali wamoyo. 42 Nkhaniyi inamveka mu Yopa monse, ndipo anthu ambili anakhulupilila Ambuye. 43 Petulo anakhalabe ku Yopa kwa masiku angapo. Iye anali kukhala kwa munthu wina wofufuta zikumba dzina lake Simoni.

10 Tsopano ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Koneliyo, kapitawo wa asilikali* a m’gulu la asilikali a ku Italy.* 2 Iye anali kukonda zopemphela, ndipo anali kuopa Mulungu pamodzi ndi onse a m’banja lake. Anali kukondanso kupatsa anthu mphatso zambili zacifundo ndipo anali kupemphela mocondelela nthawi zonse kwa Mulungu. 3 Tsiku lina ca m’ma 3 koloko masana,* anaona mngelo wa Mulungu m’masomphenya akubwela kwa iye n’kunena kuti: “Koneliyo!” 4 Koneliyo anayang’anitsitsa mngeloyo mwamantha ndipo ananena kuti: “Ndili pano Ambuye.” Mngeloyo anati: “Mulungu wamva mapemphelo ako komanso waona mphatso zako zacifundo ndipo akuzikumbukila. 5 Conco tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina dzina lake Simoni, wodziwikanso kuti Petulo. 6 Munthu ameneyu ndi mlendo kunyumba kwa Simoni wofufuta zikumba, amene ali ndi nyumba m’mbali mwa nyanja.” 7 Mngelo amene anali kulankhula naye atangocoka, Koneliyo anaitana atumiki ake awili, komanso msilikali wake wina wokonda kupemphela pakati pa atumiki ake. 8 Iye anawafotokozela zinthu zonse ndi kuwatumiza ku Yopa.

9 Tsiku lotsatila, ulendo wawo uli mkati, komanso atatsala pafupi kufika mumzindawo, Petulo anakwela pamtenje ca m’ma 12 koloko masana* kukapemphela. 10 Koma iye anamva njala kwambili, ndipo anali kufuna kudya. Pamene cakudya cinali kukonzedwa, iye anayamba kuona masomphenya. 11 M’masomphenyawo anaona kumwamba kutatseguka, ndiponso cinthu cinacake cooneka ngati cinsalu cacikulu cikutsika. Cinthuco anacigwila m’makona onse anayi pocitsitsila padziko lapansi. 12 Pa cinthuco panali nyama za mitundu yonse za miyendo inayi, komanso nyama zokwawa za padziko lapansi ndi mbalame za mumlengalenga. 13 Ndiyeno anamva mawu omuuza kuti: “Petulo, nyamuka uphe ndi kudya zinthu zimenezi.” 14 Koma Petulo anati: “Ayi Ambuye, ine sindinadyepo codetsedwa komanso conyansa ciliconse.” 15 Koma anamvanso mawu olankhula ndi iye kaciwili kuti: “Ulekeletu kuchula zinthu zimene Mulungu waziyeletsa kuti ndi zodetsedwa.” 16 Anamvanso mawu kacitatu, ndipo nthawi yomweyo cinthu cooneka ngati cinsalu cija cinatengedwa kupita kumwamba.

17 Petulo ali wodabwa kwambili posamvetsa tanthauzo la masomphenya amene anaonawo, anthu aja amene Koneliyo anatuma anafunsa kumene kuli nyumba ya Simoni ndipo anaimilila pageti. 18 Iwo anafunsa mofuula ngati Simoni wochedwanso Petulo anali mlendo kumeneko. 19 Petulo akuganizila za masomphenyawo, mzimu wa Mulungu unamuuza kuti: “Taona! Amuna atatu akukufuna. 20 Conco nyamuka, tsika upite nawo. Usakayikile ngakhale pang’ono, cifukwa ndine ndawatuma.” 21 Petulo anatsika kukakumana ndi amunawo ndipo anati: “Munthu amene mukumufunayo ndine. Ndingakuthandizeni bwanji?” 22 Iwo anati: “Tatumidwa ndi Koneliyo, mtsogoleli wa asilikali. Iye ndi munthu wolungama komanso woopa Mulungu amene ali ndi mbili yabwino pakati pa mtundu wonse wa Ayuda. Mngelo woyela anamupatsa malangizo ocokela kwa Mulungu kuti atume anthu kudzakutengani kuti mupite kunyumba kwake, akamve zimene inu mukanene.” 23 Conco anawalowetsa m’nyumba ndipo anawasamalila monga alendo ake.

Tsiku lotsatila ananyamuka n’kupita nawo, ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye limodzi. 24 Tsiku lotsatila anafika ku Kaisareya. Koneliyo anali kuwayembekezela, ndipo anali atasonkhanitsa acibale ake ndi mabwenzi ake apamtima. 25 Pamene Petulo anali kulowa, Koneliyo anakumana naye ndipo anagwada pansi kumapazi ake n’kumuwelamila. 26 Koma Petulo anamuimilitsa n’kumuuza kuti: “Nyamuka, inenso ndine munthu ngati iwe.” 27 Kenako, analowa uku akukambilana naye, ndipo anapeza anthu ambili atasonkhana mmenemo. 28 Ndiyeno Petulo anawauza kuti: “Inu mukudziwa bwino kuti sikololeka kuti Myuda aziceza ndi munthu wa mtundu wina, kapena kumuyandikila. Komabe Mulungu wandionetsa kuti sindifunika kuchula munthu aliyense kuti wodetsedwa kapena wonyansa. 29 Ndiye cifukwa cake ndabwela mosanyinyilika nditaitanidwa. Conco ndiuzeni, n’cifukwa ciyani mwandiitana?”

30 Ndiyeno Koneliyo anati: “Masiku anayi apitawa, ndinali kupemphela m’nyumba mwanga ca m’ma 3 koloko masana,* basi ndinangoona munthu wovala zovala zowala ataimilila kutsogolo kwanga, 31 n’kundiuza kuti: ‘Koneliyo, Mulungu wamva pemphelo lako, ndipo waona mphatso zako zacifundo n’kuzikumbukila. 32 Conco tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni wodziwikanso kuti Petulo. Munthuyo ndi mlendo m’nyumba ya Simoni wofufuta zikumba amene amakhala m’mbali mwa nyanja.’ 33 Ndiyeno nthawi yomweyo ndinatuma anthu kuti adzakuitaneni, ndipo mwatikomela mtima n’kubwela. Conco tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Yehova wakulamulani kuti mutiuze.”

34 Petulo atamva izi, anayamba kukamba kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti Mulungu alibe tsankho. 35 Koma munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo, ndi wovomelezeka kwa iye. 36 Mulungu anatumiza mawu kwa Aisiraeli, ndipo analengeza kwa iwo uthenga wabwino wa mtendele kupitila mwa Yesu Khristu. Ameneyu ndi Ambuye wa onse. 37 Inu mukuidziwa nkhani imene inafala kwambili kuyambila ku Galileya mpaka ku Yudeya konse, pambuyo pa ubatizo umene Yohane analalikila. 38 Nkhaniyo inali yokamba za Yesu wa ku Nazareti, amene Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyela ndi kumupatsa mphamvu. Iye anayenda m’dziko lonse, ndipo anali kucita zabwino komanso kucilitsa onse amene anali kusautsidwa ndi Mdyelekezi cifukwa Mulungu anali naye. 39 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zonse zimene iye anacita m’dziko la Ayuda komanso ku Yerusalemu. Koma iwo anamupha mwa kumupacika pamtengo. 40 Mulungu anamuukitsa iyeyo pa tsiku lacitatu, ndipo analola kuti anthu amuone. 41 Sanaonekele kwa anthu onse, koma kwa mboni zimene Mulungu anasankhilatu, ifeyo amene tinadya ndi kumwa naye limodzi ataukitsidwa. 42 Komanso anatilamula kuti tilalikile kwa anthu, ndi kupeleka umboni wokwanila wakuti iyeyu ndi amene Mulungu anamuika kukhala woweluza wa anthu amoyo ndi akufa. 43 Aneneli onse amacitila umboni za iye, kuti aliyense wokhulupilila iye, Mulungu adzamukhululukila macimo kupitila m’dzina lake.”

44 Petulo ali mkati mokamba zimenezi, anthu onse amene anali kumvetsela mawuwo analandila mzimu woyela. 45 Ndipo okhulupilila odulidwa, amene anabwela ndi Petulo anadabwa kwambili cifukwa mphatso yaulele ya mzimu woyela inapelekedwanso* kwa anthu a mitundu ina. 46 Cifukwa anawamva akulankhula zinenelo* zina ndiponso kutamanda Mulungu. Ndiyeno Petulo ananena kuti: 47 “Kodi pali aliyense amene angaletse kuti anthu awa amene alandila mzimu woyela ngati ife asabatizidwe m’madzi?” 48 Atatelo, iye anawalamula kuti abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu. Kenako iwo anamupempha kuti akhalebe nawo kwa masiku angapo.

11 Tsopano atumwi ndi abale amene anali ku Yudeya anamva kuti anthu a mitundu ina nawonso alandila mawu a Mulungu. 2 Conco Petulo atapita ku Yerusalemu, anthu olimbikitsa mdulidwe anayamba kumuimba mlandu.* 3 Anali kumuuza kuti: “Iwe unalowa m’nyumba ya anthu osadulidwa ndipo unadya nawo.” 4 Petulo atamva izi anayamba kuwafotokozela mwatsatanetsatane zimene zinacitika kuti:

5 “Ndinali kupemphela mumzinda wa Yopa ndipo ndinaona masomphenya. M’masomphenyawo ndinaona cinthu cooneka ngati cinsalu cacikulu, cikutsika kucokela kumwamba. Cinthuco anacigwila m’makona ake anayi n’kucitsitsila pamene panali ine. 6 N’taciyang’anitsitsa, ndinaonapo nyama za miyendo inayi za padziko lapansi, nyama zakuchile, nyama zokwawa, komanso mbalame za mumlengalenga. 7 Ndinamvanso mawu ondiuza kuti: ‘Petulo, nyamuka, uphe ndi kudya zinthu zimenezi!’ 8 Koma ine ndinati: ‘Ayi Ambuye, cinthu codetsedwa komanso conyansa sicinalowepo m’kamwa mwanga.’ 9 Kaciwili, ndinamvanso mawu ocokela kumwamba akuti: ‘Ulekeletu kuchula zinthu zimene Mulungu waziyeletsa kuti zodetsedwa.’ 10 Mawuwa anamvekanso kacitatu, ndipo zonse zinatengedwa n’kubwelela kumwamba. 11 Nthawi yomweyo amuna atatu ocokela ku Kaisareya amene anatumidwa kwa ine, anafika panyumba imene tinali kukhala. 12 Kenako mzimu unandiuza kuti ndipite nawo ndisakayikile ngakhale pang’ono. Abale 6 awa anapita nane, ndipo tinakalowa m’nyumba ya munthuyo.

13 “Iye anatifotokozela kuti ali m’nyumba mwake anaona mngelo ataimilila, ndipo anamuuza kuti: ‘Tuma anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni wodziwikanso kuti Petulo. 14 Iye adzakuuza zimene iwe ndi a m’banja lako mungacite kuti mupulumuke.’ 15 Koma nditangoyamba kulankhula, mzimu woyela unafika pa iwo monga unacitila kwa ife poyamba paja. 16 Zitatelo, ndinakumbukila mawu amene Ambuye anali kukonda kukamba akuti: ‘Yohane anali kubatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyela.’ 17 Conco, ngati Mulungu anawapatsa mphatso yaulele imenenso anapeleka kwa ife amene tinakhulupilila mwa Ambuye Yesu Khristu, ndiye ndine ndani kuti ndimuletse Mulungu?”*

18 Iwo atamva zimenezi analeka kumutsutsa,* ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Ndiye kuti Mulungu wapatsanso anthu a mitundu ina mwayi wakuti alape ndi kukapeza moyo.”

19 Anthu amene anabalalika kaamba ka mavuto amene anayamba cifukwa ca zimene zinacitikila Sitefano, anafika mpaka ku Foinike, ku Kupuro, ndi Antiokeya. Koma anali kungolalikila kwa Ayuda okha. 20 Komabe, ena mwa anthu ocokela ku Kupuro ndi Kurene atafika ku Antiokeya anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ambuye Yesu kwa anthu okamba Cigiriki. 21 Kuwonjezela apo, dzanja la Yehova linali nawo, ndipo anthu ambili anakhala okhulupilila, ndiponso anayamba kutsatila Ambuye.

22 Mpingo wa ku Yerusalemu unamva zokhudza anthuwa, ndipo unatumiza Baranaba kuti apite ku Antiokeya. 23 Atafika kumeneko n’kuona cisomo ca Mulungu, anasangalala ndipo anayamba kulimbikitsa onse kuti apitilize kukhala okhulupilika kwa Ambuye ndi mtima wonse. 24 Baranaba anali munthu wabwino wa cikhulupililo colimba, komanso wodzazidwa ndi mzimu woyela. Cifukwa ca zimenezo, khamu la anthu linayamba kukhulupilila Ambuye. 25 Kenako iye anapita ku Tariso kukafunafuna Saulo mosamala. 26 Atamupeza, anapita naye ku Antiokeya. Kwa caka cathunthu, iwo anali kusonkhana ndi mpingo, ndipo anaphunzitsa anthu ambili. Motsogoleledwa ndi Mulungu, ku Antiokeya n’kumene ophunzilawo anayamba kuchedwa Akhristu.

27 M’masiku amenewo, aneneli ocokela ku Yerusalemu anapita ku Antiokeya. 28 Mmodzi wa iwo dzina lake Agabo analosela mothandizidwa ndi mzimu woyela kuti padziko lonse lapansi padzagwa njala yaikulu. Ndipo zimenezi zinadzacitikadi m’nthawi ya Kalaudiyo. 29 Conco ophunzilawo anatsimikiza mtima kutumiza thandizo* kwa abale a ku Yudeya, aliyense malinga n’zimene akanakwanitsa. 30 Iwo anacitadi zimenezo, ndipo anatumiza thandizolo kwa akulu mwa kupatsila Baranaba ndi Saulo.

12 M’masiku amenewo, mfumu Herode anayamba kuzunza anthu ena a mumpingo. 2 Iye anapha Yakobo m’bale wake wa Yohane ndi lupanga. 3 Ataona kuti zimenezo zawasangalatsa Ayuda, anamanganso Petulo. (Anacita zimenezi m’masiku a Mikate Yopanda Cofufumitsa.) 4 Anamugwila n’kumuponya m’ndende, ndipo anamupeleka m’manja mwa magulu anayi a asilikali kuti azimulonda mosinthanasinthana. Gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Colinga cake cinali cakuti amuzenge mlandu pamaso pa anthu pambuyo pa Pasika. 5 Conco Petulo anasungidwa m’ndendemo, koma mpingo unali kumupemphelela kwambili kwa Mulungu.

6 Herode atatsala pang’ono kumutulutsa Petulo kuti akamuzenge mlandu, Petuloyo anali gone usiku umenewo atamangidwa maunyolo awili pakati pa asilikali awili. Ndipo pakhomo panali alonda amene anali kulonda ndendeyo. 7 Koma mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova anaimilila, ndipo m’citolokosimo munawala. Pomuutsa, mngeloyo anagunduza Petulo m’nthiti, nati: “Uka mwamsanga!” Basi maunyolo amene anam’manga nawo anagwa pansi. 8 Mngeloyo anamuuza kuti: “Vala zovala zako ndi nsapato zako.” Iye anavaladi. Pamapeto pake anamuuza kuti: “Vala covala cako cakunja ndipo uzindilondola.” 9 Iye anatuluka ndipo anapitiliza kumulondola, koma sanadziwe kuti zimene zinali kucitika kudzela mwa mngeloyo zinali zenizeni. Anaganiza kuti anali kuona masomphenya. 10 Atapitilila gulu loyamba la asilikali a pageti ndi laciwili, anafika pageti yacitsulo yotulukila popita mumzinda, ndipo inatseguka yokha. Atatuluka anayenda naye msewu umodzi, ndipo mwadzidzidzi mngeloyo anamucokela. 11 Ndiyeno Petulo atazindikila zimene zinali kucitika anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova anatumiza mngelo wake kudzandipulumutsa m’manja mwa Herode, komanso ku zonse zimene Ayuda anali kuyembekezela kuti zicitike.”

12 Atazindikila zimenezi, iye anapita kunyumba ya Mariya, mayi wa Yohane wochedwanso Maliko. Kumeneko anthu ambili anasonkhana ndipo anali kupemphela. 13 Petulo atagogoda pakhomo la geti, mtsikana wanchito dzina lake Roda anabwela kuti aone amene anali kugogoda. 14 Mtsikanayo atazindikila kuti amene anali kulankhula anali Petulo, anakondwela kwambili moti sanatsegule getiyo, koma anathamangila mkati kukafotokoza kuti Petulo ali panja pageti. 15 Iwo anauza mtsikanayo kuti: “Wacita misala iwe!” Koma iye analimbikila kuwauza kuti zimene anali kukamba ndi zoona. Ndiyeno iwo anayamba kunena kuti: “Ndi mngelo wake.” 16 Koma Petulo anapitiliza kugogoda. Iwo atatsegula citseko anaona kuti ndi iyedi, ndipo anadabwa kwambili. 17 Koma iye anawauza anthuwo ndi dzanja lake kuti akhale cete, ndipo anawafotokozela mwatsatanetsatane mmene Yehova anamutulutsila m’ndende. Ndiyeno anati: “Mukauze Yakobo ndi abale ena nkhani imeneyi.” Atanena zimenezi anatuluka n’kupita kumalo ena.

18 Kutaca, asilikali anasokonezeka kwambili posadziwa zimene zacitikila Petulo. 19 Herode anafunafuna Petulo mosamala. Ndipo popeza kuti sanamupeze, anapanikiza alonda ndi mafunso n’kulamula kuti awatenge akawapatse cilango. Kenako Herode anacoka ku Yudeya nʼkupita ku Kaisareya, kumeneko anakhalako kwa kanthawi ndithu.

20 Herode anawakwiyila kwambili anthu a ku Turo ndi Sidoni. Conco iwo mogwilizana anapita kwa iye, ndipo pambuyo ponyengelela Balasito, munthu amene anali kuyang’anila zocitika za panyumba ya mfumu, anapempha mtendele. Anatelo cifukwa dziko lawo linali kudalila cakudya cocokela mʼdziko la mfumuyo. 21 Pa tsiku lina limene anasankha, Herode anavala zovala zacifumu nʼkukhala pampando woweluzila milandu, ndipo anayamba kulankhula ndi anthu. 22 Ndiyeno anthu amene anasonkhanawo anayamba kufuula kuti: “Mawu awa ndi a mulungu osati a munthu!” 23 Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova anamukantha* cifukwa sanalemekeze Mulungu, ndipo anadyedwa ndi mphutsi n’kumwalila.

24 Koma mawu a Yehova anapitiliza kufalikila, ndipo anthu ambili anakhala okhulupilila.

25 Baranaba ndi Saulo atatsiliza nchito yopeleka thandizo ku Yerusalemu, anabwelela. Ndipo popita anatenga Yohane wochedwanso Maliko.

13 Mumpingo wa ku Antiokeya munali aneneli ndi aphunzitsi. Iwo anali Baranaba, Sumiyoni wochedwanso Nigeri, Lukiyo wa ku Kurene, Saulo komanso Manayeni amene anaphunzila pamodzi ndi Herode wolamulila cigawo. 2 Pamene iwo anali kutumikila Yehova* komanso kusala kudya, mzimu woyela unawauza kuti: “Mundipatulile Baranaba ndi Saulo kuti agwile nchito imene ine ndinawaitanila.” 3 Ndiyeno atatsiliza kusala kudya ndi kupemphela, iwo anawagwila pamutu* pawo n’kuwatumiza.

4 Conco amuna amenewa, amene anatumizidwa ndi mzimu woyela, anapita ku Selukeya, ndipo atacoka kumeneko anayenda ulendo wa pamadzi kupita ku Kupuro. 5 Atafika ku Salami anayamba kulalikila mawu a Mulungu mʼmasunagoge a Ayuda. Iwo analinso ndi Yohane amene anali kuwatumikila.*

6 Iwo anayenda pa cisumbu conse ca Kupuro mpaka kukafika ku Pafo. Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Bara-Yesu, amene anali wamatsenga komanso mneneli wabodza. 7 Ameneyu anali pamodzi ndi bwanamkubwa* Serigio Paulo, munthu wanzelu kwambili. Bwanamkubwayu anaitana Baranaba ndi Saulo, cifukwa anali kufunitsitsa kumva mawu a Mulungu. 8 Koma Elima, wamatsenga uja, (cifukwa umu ndi mmene dzina lakeli amalimasulila) anayamba kuwatsutsa. Iye anayesetsa kuti bwanamkubwayo asakhale wokhulupilila. 9 Kenako Saulo, wochedwanso Paulo, atadzazidwa ndi mzimu woyela, anamuyangʼanitsitsa, 10 ndipo anati: “Iwe munthu wodzaza ndi cinyengo camtundu uliwonse ndiponso zoipa, mwana wa Mdyelekezi komanso mdani wa cinthu ciliconse colungama, kodi sudzaleka kupotoza njila za Yehova zowongoka? 11 Tamvela! Dzanja la Yehova lili pa iwe ndipo ukhala wakhungu. Kwakanthawi, sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo anaona nkhungu yamphamvu mʼmaso mwake ndiponso mdima wandiweyani, ndipo anayamba kufunafuna munthu amene angamugwile dzanja ndi kumutsogolela. 12 Bwanamkubwayo ataona zimene zinacitikazi, anakhala wokhulupilila, cifukwa anadabwa kwambili ndi zimene anaphunzila zokhudza Yehova.

13 Kenako Paulo ndi anzake ananyamuka ulendo wa panyanja kucoka ku Pafo, ndipo anakafika ku Pega, ku Pamfuliya. Koma Yohane Maliko anawasiya nʼkubwelela ku Yerusalemu. 14 Koma atacoka ku Pega anakafika ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Kumeneko analowa mʼsunagoge pa tsiku la Sabata ndi kukhala pansi. 15 Atatsiliza kuwelenga Cilamulo ndi zolemba za aneneli pamaso pa anthu, atsogoleli a sunagoge anatumiza mawu kwa iwo kuti: “Abale inu, ngati muli ndi mawu alionse olimbikitsa anthu awa, lankhulani.” 16 Conco Paulo anaimilila ndipo anakweza dzanja lake nʼkunena kuti:

“Anthu inu, Aisiraeli, komanso ena nonsenu oopa Mulungu, tamvelani. 17 Mulungu wa anthu awa Aisiraeli, anasankha makolo athu akale. Iye anapangitsa anthu amenewa kukhala mtundu wamphamvu, pamene anali alendo mʼdziko la Iguputo. Ndipo anawatulutsa mʼdzikolo ndi dzanja lake lamphamvu. 18 Kwa zaka pafupifupi 40, iye anapilila khalidwe lawo mʼcipululu. 19 Atawononga mitundu 7 mʼdziko la Kanani, anapeleka dzikolo kwa Aisiraeli kuti likhale colowa cawo. 20 Zonsezi zinacitika mʼzaka pafupifupi 450.

“Pambuyo pa zimenezi iye anawapatsa oweluza mpaka kudzafika pa nthawi ya mneneli Samueli. 21 Koma pambuyo pake iwo anafuna kukhala ndi mfumu. Ndipo Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini. Iye anakhala mfumu yawo kwa zaka 40. 22 Atamucotsa pa ufumu, anawapatsa Davide kuti akhale mfumu yawo. Iye anamucitila umboni mwa kukamba kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Jese, munthu wapamtima panga. Iyeyu adzacita zonse zimene ndikufuna.’ 23 Mogwilizana ndi lonjezo lake, kucokela pa mbadwa za munthu ameneyu, Mulungu wabweletsa mpulumutsi kwa Isiraeli, amene ndi Yesu. 24 Mpulumutsi ameneyu asanafike, Yohane analalikila kwa anthu onse a ku Isiraeli za ubatizo, ngati cizindikilo ca kulapa. 25 Koma kumapeto kwa utumiki wake, Yohane anali kunena kuti, ‘Kodi mukuganiza kuti ndine ndani? Munthu amene mukuyembekezela si ndine ayi. Koma wina akubwela pambuyo panga, amene ine si ndine woyenela kumasula nsapato zake.’

26 “Anthu inu, abale, inu mbadwa za Abulahamu, komanso anthu amene amaopa Mulungu amene ali pakati panu, mawu a cipulumutso cimeneci atumizidwa kwa ife. 27 Cifukwa anthu a ku Yerusalemu ndi olamulila awo sanamuzindikile ameneyu. Koma pamene anali kumuweluza, anakwanilitsa zimene aneneli anakamba, zimene zimawelengedwa mokweza sabata lililonse. 28 Ngakhale kuti sanapeze cifukwa comuphela, iwo anakakamiza Pilato kuti ameneyu aphedwe. 29 Ndiyeno atakwanilitsa zonse zimene zinalembedwa zokhudza iye, anamutsitsa pamtengo nʼkukamuika mʼmanda.* 30 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. 31 Ndipo kwa masiku ambili anaonekela kwa anthu amene anayenda naye kucoka ku Galileya kupita ku Yerusalemu. Palipano amenewa ndi mboni zake kwa anthu.

32 “Conco tikulengeza kwa inu uthenga wabwino wokamba za lonjezo limene linapelekedwa kwa makolo athu akale. 33 Uthengawo ndi wakuti Mulungu wakwanilitsa zonse zimene anawalonjezazo kwa ife ana awo mwa kuukitsa Yesu, monga zinalembedwa mu salimo laciwili kuti: ‘Iwe ndiwe mwana wanga. Lelo ndakhala tate wako.’ 34 Ndipo mfundo yakuti iye anamuukitsa kwa akufa, ndipo sadzabwelelanso kuthupi limene lingawole, anaifotokoza motele: ‘Ine ndidzakuonetsani cikondi cokhulupilika cimene ndinalonjeza Davide. Ndipo lonjezo limeneli ndi lodalilika.’ 35 Ndipo salimo lina limakambanso kuti, ‘Simudzalola kuti thupi la wokhulupilika kwa inu liwole.’ 36 Davide anacita cifunilo ca Mulungu pa nthawi ya mʼbadwo wake, anamwalila nʼkuikidwa mʼmanda a makolo ake, ndipo thupi lake linawola. 37 Koma amene Mulungu anamuukitsa, thupi lake silinawole.

38 “Tsopano abale anga, dziwani kuti ife tikulalikila kwa inu kuti kupitila mwa ameneyu, macimo akukhululukidwa. 39 Mudziwenso kuti pa zinthu zonse zimene kunali kosatheka kuti muonedwe opanda mlandu kudzela mʼCilamulo ca Mose, aliyense wokhulupilila akuonedwa wopanda mlandu kudzela mwa ameneyu. 40 Conco samalani kuti zimene aneneli analemba zisakucitikileni, zimene zimati: 41 ‘Inu onyoza onani zimene ine ndikucita ndipo mudabwe nazo, kenako mudzatha, cifukwa nchito zimene ndikucita mʼmasiku anu, ndi nchito zimene inu simungazikhulupilile ngakhale wina atakufotokozelani mwatsatanetsatane.’”

42 Tsopano pamene iwo anali kutuluka, anthuwo anawacondelela kuti akawauzenso zinthu zimenezo Sabata lotsatila. 43 Conco msonkhano wamʼsunagoge utatha, Ayuda ndi anthu ambili amene analowa Ciyuda, omwe anali kulambila Mulungu, anatsatila Paulo ndi Baranaba. Ndipo iwo analimbikitsa anthuwo kuti apitilize kukhala oyenela kulandila cisomo ca Mulungu.

44 Sabata lotsatila, pafupifupi mzinda wonse unasonkhana pamodzi kuti umvetsele mawu a Yehova. 45 Ayuda ataona khamu la anthulo, anacita nsanje ndipo anayamba kutsutsa mwamwano zimene Paulo anali kulankhula. 46 Conco Paulo ndi Baranaba anakamba molimba mtima kuti: “Kunali koyenela kuti inu mukhale oyamba kuuzidwa mawu a Mulungu. Koma popeza mukuwakana ndipo mukudziweluza nokha kuti ndinu osayenela moyo wosatha, taonani ife tikupita kwa anthu a mitundu ina. 47 Pakuti Yehova watilamula kuti, ‘Ine ndakupatsani udindo woti mukhale kuwala kwa anthu a mitundu ina, kuti mukhale cipulumutso mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.’”

48 Pamene anthu a mitundu ina anamva izi, anayamba kusangalala ndi kutamanda mawu a Yehova. Anthu onse amene anali ndi maganizo abwino ofunadi moyo wosatha anakhala okhulupilila. 49 Kuwonjezela apo, mawu a Yehova anali kufalitsidwa mʼdziko lonselo. 50 Koma Ayuda anatuntha azimayi ochuka amene anali oopa Mulungu komanso amuna olemekezeka a mumzindawo. Ndipo iwo anacititsa kuti Paulo ndi Baranaba ayambe kuzunzidwa, ndipo anawaponya kunja kwa mzinda wawo. 51 Conco iwo anakutumula fumbi kumapazi awo, kenako anapita ku Ikoniyo. 52 Ndipo ophunzilawo anapitiliza kukhala acimwemwe komanso odzazidwa ndi mzimu woyela.

14 Tsopano Paulo ndi Baranaba ali ku Ikoniyo analowa mu sunagoge wa Ayuda, ndipo analankhula bwino kwambili cakuti Ayuda komanso Agiriki ambili anakhala okhulupilila. 2 Koma Ayuda amene sanakhulupilile anatuntha anthu a mitundu ina ndi kuwasokoneza kuti aukile abalewo. 3 Cotelo kwa nthawi yaitali, analankhula molimba mtima cifukwa ca mphamvu ya Yehova. Iye anacitila umboni mawu a cisomo cake mwa kulola ophunzilawo kucita zizindikilo ndi zodabwitsa. 4 Koma khamu la anthu mu mzindawo linagawikana. Ena anali kumbali ya Ayuda, pamene ena anali kumbali ya atumwi. 5 Ndiyeno anthu a mitundu ina, komanso Ayuda pamodzi ndi olamulila awo, anakonza zakuti awacite cipongwe ndi kuwaponya miyala. 6 Koma atumwiwo anadziwitsidwa, ndipo anathawila mʼmizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi mʼmadela ozungulila. 7 Kumeneko anapitiliza kulengeza uthenga wabwino.

8 Ku Lusitara, kunali munthu wina wolemala miyendo amene anali khale pansi. Munthuyu anabadwa wolemala ndipo anali asanayendepo. 9 Iye anali kumvetsela pamene Paulo anali kulankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa munthuyo, ndipo anaona kuti ali ndi cikhulupililo cakuti angacilitsidwe. 10 Conco Paulo mokweza mawu anati: “Imilila!” Atatelo, munthuyo analumpha nʼkuyamba kuyenda. 11 Khamu la anthu litaona zimene Paulo anacita, linafuula mʼcinenelo ca Cilukaoniya kuti: “Milungu yakhala ngati anthu ndipo yatsikila kwa ife!” 12 Iwo anayamba kuchula Baranaba kuti Zeu, koma Paulo anali kumuchula kuti Heme, cifukwa ndi amene anali kutsogolela polankhula. 13 Ndiyeno wansembe wa Zeu, amene kacisi wake anali pafupi ndi khomo lolowela mumzindawo, anabweletsa ngʼombe zamphongo ndi nkhata zamaluwa pa mageti. Ndipo anafuna kupeleka nsembe pamodzi ndi khamu la anthulo.

14 Koma atumwiwo, Baranaba ndi Paulo, atamva zimenezi anangʼamba zovala zawo nʼkuthamanga kukalowa mʼkhamu la anthulo akufuula kuti: 15 “Anthu inu, n’cifukwa ciyani mukucita zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu. Ife tikulengeza uthenga wabwino kwa inu kuti muleke kucita zinthu zopandapakezi nʼkuyamba kulambila Mulungu wamoyo, amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo. 16 Mʼmibadwo ya mʼmbuyomu iye analola anthu a mitundu yonse kuti aziyenda mʼnjila zawo. 17 Ngakhale n’telo, sanangokhala wopanda umboni wakuti anacita zabwino. Anakupatsani mvula kucokela kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambili. Anadzazanso mitima yanu ndi cakudya komanso cimwemwe.” 18 Ngakhale kuti atumwiwo ananena zimenezi, zinavutabe kuletsa khamu la anthulo kupeleka nsembe kwa iwo.

19 Koma Ayuda obwela kucokela ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo anakopa anthuwo. Conco iwo anaponya miyala Paulo nʼkumuguzila kunja kwa mzinda poganiza kuti wafa. 20 Koma ophunzila atamuzungulila, anauka nʼkulowa mumzinda. Tsiku lotsatila anacoka kupita ku Debe ndi Baranaba. 21 Pambuyo polengeza uthenga wabwino mumzindawu nʼkupanga ophunzila ambili ndithu, iwo anabwelela ku Lusitara, ku Ikoniyo, ndi ku Antiokeya. 22 Kumeneko iwo analimbitsa ophunzila komanso kuwathandiza kuti akhalebe m’cikhulupililo. Anali kuwauza kuti: “Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.” 23 Iwo anasankhanso akulu mumpingo uliwonse, ndipo anapemphela ndi kusala kudya, kenako anawapeleka kwa Yehova Mulungu amene iwo anayamba kumukhulupilila.

24 Ndiyeno anadutsa ku Pisidiya nʼkupita ku Pamfiliya. 25 Ndipo atatsiliza kulalikila mawu a Mulungu ku Pega, anapita ku Ataliya. 26 Pocoka kumeneko anayenda ulendo wa pamadzi kubwelela ku Antiokeya. Kumeneku nʼkumene kumbuyoku abale anawasankha kuti Mulungu awaonetse cisomo nʼcolinga coti agwile nchito, imene tsopano anali ataitsiliza.

27 Iwo atafika kumeneko anasonkhanitsa anthu a mumpingo, ndipo anawafotokozela zinthu zambili zimene Mulungu anacita kudzela mwa iwo. Anawafotokozelanso kuti Mulungu anatsegula khomo kuti anthu a mitundu ina akhale okhulupilila. 28 Conco anakhala ndi ophunzilawo kwa kanthawi ndithu.

15 Ndiyeno amuna ena ocokela ku Yudeya anafika n’kuyamba kuphunzitsa abale kuti: “Ngati simudulidwa mogwilizana ndi mwambo wa Mose, simungapulumuke.” 2 Koma Paulo ndi Baranaba sanagwilizane nazo, ndipo anatsutsana nawo. Conco iwo anasankha Paulo, Baranaba, komanso anthu ena, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu, kuti akawauze za nkhaniyi.*

3 Conco mpingo utawapelekeza, anthu amenewa anapitiliza ndi ulendo wawo kupitila ku Foinike ndi ku Samariya. Kumeneko anawafotokozela mwatsatanetsatane mmene anthu a mitundu ina anatembenukila n’kuyamba kulambila Mulungu. Ndipo abale onse atamva zimenezi anakondwela kwambili. 4 Atafika ku Yerusalemu, mpingo, atumwi, komanso akulu anawalandila ndi manja awili. Ndipo anawafotokozela zinthu zambili zimene Mulungu anacita kudzela mwa iwo. 5 Koma ena amene kale anali m’gulu lampatuko la Afarisi omwe anakhala okhulupilila, anaimilila m’mipando yawo n’kunena kuti: “M’pofunika kuwadula ndi kuwalamula kuti azisunga Cilamulo ca Mose.”

6 Conco atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuti aikambilane nkhaniyo. 7 Pambuyo potsutsana kwambili za nkhaniyo, Petulo anaimilila n’kuwauza kuti: “Anthu inu, abale, mukudziwa bwino kuti kucokela m’masiku oyambilila, Mulungu anandisankha kuti kudzela pakamwa panga, anthu a mitundu ina amve mawu a uthenga wabwino ndi kukhulupilila. 8 Ndipo Mulungu, amene amadziwa za mumtima akucitila umboni mwa kuwapatsa mzimu woyela, mmenenso anacitila kwa ife. 9 Iye sanasiyanitse ngakhale pang’ono pakati pa ife ndi iwo. Koma anayeletsa mitima yawo cifukwa ca cikhulupililo cawo. 10 Ndiye n’cifukwa ciyani inu tsopano mukumuyesa Mulungu ponyamulitsa ophunzila joko imene makolo athu, ngakhale ifeyo, sitinathe kuinyamula? 11 Koma tsopano ife tikhulupilila kuti tidzapulumuka cifukwa ca cisomo ca Ambuye Yesu, mofanananso ndi anthu amenewa.”

12 Atatelo gulu lonse linakhala cete, ndipo anayamba kumvetsela pamene Paulo ndi Baranaba anali kuwafotokozela zizindikilo ndi zodabwitsa zambili zimene Mulungu anacita pakati pa anthu a mitundu ina kudzela mwa iwo. 13 Atatsiliza kulankhula, Yakobo anayankha kuti: “Anthu inu, abale, ndimvetseleni. 14 Sumiyoni wafotokoza bwino kwambili mmene Mulungu anaceukila anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti pakati pawo atengepo anthu ena odziwika ndi dzina lake. 15 Ndipo zimenezi zikugwilizana ndi zimene aneneli analemba kuti: 16 ‘Zinthu zimenezi zikadzatha ine ndidzabwelela ndipo ndidzautsanso tenti* ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso mbali yogumuka ya nyumbayo ndi kuikonzanso. 17 Ndidzacita zimenezi kuti anthu otsalawo afunefune Yehova ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu ochedwa ndi dzina langa, watelo Yehova amene akucita zinthu zimenezi, 18 zomwe anatsimikiza kalekale kuti adzazicita.’ 19 Conco cigamulo canga* n’cakuti, tisawavutitse anthu a mitundu ina amene atembenukila kwa Mulungu. 20 Koma tiwalembele kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,* ciwelewele,* zopotola,* komanso magazi. 21 Pakuti kuyambila kalekale, nthawi zonse anthu akhala akulalikila mu mzinda ndi mzinda mawu ocokela m’mabuku a Mose, cifukwa sabata lililonse mabukuwa amawelengedwa mokweza m’masunagoge.”

22 Ndiyeno atumwi ndi akulu pamodzi ndi mpingo wonse, anagwilizana zakuti amuna amene anasankhidwa pakati pawo, awatumize ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Baranaba. Conco anatumiza Yudasi wochedwanso Barasaba, ndi Sila, amene anali kutsogolela abale. 23 Iwo analemba kalata n’kuwapatsila. Kalatayo inati:

“Ife abale anu atumwi ndi akulu, tikukulembelani inu abale athu ocokela m’mitundu ina, amene muli ku Antiokeya, ku Siriya, ndi ku Kilikiya: Tikuti landilani moni wathu! 24 Tamva kuti ena ocokela pakati pathu akukuvutitsani ndi kukusokonezani mwa zolankhula zawo ngakhale kuti ife sitinawapatse malangizo alionse. 25 Conco tonse tagwilizana kuti tisankhe amuna n’kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi abale athu okondedwa, Baranaba ndi Paulo. 26 Anthu amenewa apeleka miyoyo yawo cifukwa ca dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu. 27 Conco tikutumiza Yudasi ndi Sila, kuti nawonso adzakufotokozeleni zinthu zimodzimodzi ndi mawu apakamwa. 28 Cifukwa mzimu woyela komanso ife taona kuti ndi bwino kuti tisakunyamulitseni mtolo wolemela, kupatulapo zinthu zofunika zokhazi zimene ndi: 29 kupitiliza kupewa zinthu zopelekedwa nsembe ku mafano, magazi, zopotola,* ndi ciwelewele.* Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambili, zinthu zidzakuyendelani bwino. Tikukufunilani zabwino zonse!”*

30 Conco amuna amenewa atanyamuka, anapita ku Antiokeya. Kumeneko anasonkhanitsa gulu lonse la anthu n’kuwapatsa kalatayo. 31 Ataiwelenga, anakondwela ndi mawu acilimbikitso amene analimo. 32 Popeza kuti Yudasi ndi Sila analinso aneneli, anawakambila nkhani zambili abalewo ndipo anawalimbikitsa. 33 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abalewo analailana nawo, ndipo anabwelela kwa amene anawatuma mwamtendele. 34* —— 35 Koma Paulo ndi Baranaba anakhalila ku Antiokeya. Iwo anali kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wa mawu a Yehova pamodzi ndi anthu enanso ambili.

36 Patapita masiku, Paulo anauza Baranaba kuti: “Tiyeni tibwelele tsopano ku mizinda yonse kumene tinalalikila mawu a Yehova kuti tikacezele abale ndi kukawaona kuti ali bwanji.” 37 Baranaba anali kufunitsitsa kuti atenga Yohane, wochedwanso Maliko. 38 Koma Paulo sanafune kumutenga cifukwa ulendo wina Yohane anawasiya ku Pamfuliya, ndipo sanapite nawo ku nchitoyo. 39 Mwa ici, iwo anakangana koopsa mpaka anapatukana. Baranaba anatenga Maliko ndipo anayenda ulendo wa pamadzi kupita ku Kupuro. 40 Koma Paulo anasankha Sila, ndipo abale atamupemphelela Pauloyo kuti Yehova amuonetse cisomo cake, ananyamuka. 41 Iye anapitila ku Siriya ndi ku Kilikiya, ndipo anali kulimbitsa mipingo.

16 Kenako Paulo anafika ku Debe komanso ku Lusitara. Kumeneko kunali wophunzila wina dzina lake Timoteyo, mwana amene mayi ake anali Myuda wokhulupilila, koma atate ake anali Mgiriki. 2 Abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anamucitila umboni wabwino. 3 Paulo anaonetsa kuti akufuna kutenga Timoteyo pa ulendo wake. Conco anamutenga ndi kumucita mdulidwe cifukwa ca Ayuda amene anali kumeneko, popeza onse anali kudziwa kuti atate ake ndi Mgiriki. 4 Pamene anali kupita m’mizinda, anali kupatsa okhulupilila a kumeneko malamulo oyenela kuwatsatila, mogwilizana ndi zimene atumwi komanso akulu ku Yerusalemu anagamula. 5 Conco mipingo inapitiliza kukhala yolimba m’cikhulupililo, ndipo ciwelengelo ca ophunzila cinali kuwonjezeka tsiku lililonse.

6 Kenako iwo anadzela ku Fulugiya komanso m’dziko la Galatiya, cifukwa mzimu woyela unawaletsa kulankhula mawu a Mulungu m’cigawo ca Asia. 7 Ndiyeno atafika ku Musiya anayesetsa kuti apite ku Bituniya, koma mzimu wa Yesu sunawalole. 8 Conco anangodutsamo m’cigawo ca Musiya n’kukafika ku Torowa. 9 Ndiyeno usiku Paulo anaona masomphenya. Anaona munthu wa ku Makedoniya ataimilila akumupempha kuti: “Wolokelani kuno ku Makedoniya mudzatithandize.” 10 Iye atangoona masomphenyawo, tinaganiza zopita ku Makedoniya. Tinali otsimikiza kuti Mulungu ndiye watiitana kuti tikalengeze uthenga wabwino kwa anthu a kumeneko.

11 Conco tinanyamuka ulendo wa panyanja kucoka ku Torowa kupita ku Samatirake. Koma tsiku lotsatila tinapita ku Neapoli. 12 Titacoka kumeneko tinapita ku Filipi, mzinda wolamulidwa ndi Aroma, umenenso ndi wofunika kwambili m’cigawo ca Makedoniya. Tinakhala mumzindawu kwa masiku angapo. 13 Tsiku la Sabata tinatuluka pageti n’kupita m’mbali mwa mtsinje, kumene tinali kuganiza kuti kuli malo opemphelela. Ndipo tinakhala pansi n’kuyamba kulankhula ndi azimayi amene anasonkhana komweko. 14 Pa gulu la azimayiwo panali mayi wina dzina lake Lidiya, ndipo anali kugulitsa zovala za mtundu wapepo. Iye anali wocokela mumzinda wa Tiyatira, ndipo anali wolambila Mulungu. Pamene anali kumvetsela, Yehova anatsegula mtima wake kwambili kuti amvetse zimene Paulo anali kulankhula. 15 Iye ndi a m’banja lake atabatizika, anaticondelela kuti: “Ngati muona kuti ndine wokhulupilika kwa Yehova, tiyeni mukakhale kunyumba kwanga.” Moti anatiumiliza ndithu kuti tipite naye kwawo.

16 Tsopano pamene tinali kupita kumalo opemphelela, tinakumana ndi mtsikana wina wogwidwa ndi mzimu, womwe ndi ciwanda coloseletsa zakutsogolo. Iye anapangitsa mabwana ake kupeza phindu kwambili, cifukwa ca zolosela zake. 17 Mtsikanayu anali kungotsatila Paulo limodzi ndi ife n’kumafuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wapamwambamwamba, ndipo akulengeza kwa inu njila ya cipulumutso.” 18 Iye anacita zimenezi kwa masiku ambili. Pothela pake Paulo anafika potopa nazo, ndipo anaceuka n’kuuza mzimuwo kuti: “Ndikukulamula m’dzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa mtsikanayu.” Ndipo mzimuwo unatuluka nthawi yomweyo.

19 Ndiyeno mabwana ake aja ataona kuti sadzapezanso phindu, anagwila Paulo ndi Sila ndi kuwaguzila mumsika, kubwalo la olamulila. 20 Atafika nawo kwa akuluakulu a zamalamulo, iwo ananena kuti: “Anthu awa akusokoneza kwambili mzinda wathu, ndipo ndi Ayuda. 21 Akufalitsa miyambo imene kwa ife ndi yosaloleka kuitsatila kapena kuicita, cifukwa ndife Aroma.” 22 Kenako gulu lonselo linawaukila atumwiwo. Ndipo akuluakulu a zamalamulowo, anavula atumwiwo zovala mocita kuwang’ambila n’kulamula kuti awakwapule ndi ndodo. 23 Atawakwapula zikoti zambili, anawatsekela m’ndende ndi kulamula woyang’anila ndendeyo kuti aziwalonda mokwana kuti asathawe. 24 Popeza kuti woyang’anila ndendeyo analamulidwa zimenezi, iye anakawatsekela m’cipinda camkati ca ndendeyo ndi kumanga mapazi awo m’matangadza.

25 Koma capakati pa usiku, Paulo ndi Sila anayamba kupemphela ndiponso kutamanda Mulungu mwa kuimba nyimbo, ndipo akaidi ena anali kumvetsela. 26 Mwadzidzidzi panacitika civomezi camphamvu, moti maziko a ndendeyo anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse zinatseguka, ndipo aliyense unyolo wake unamasuka. 27 Woyang’anila ndende uja atauka n’kuona kuti zitseko za ndende n’zotseguka, anasolola lupanga lake kuti adziphe, cifukwa anaganiza kuti akaidiwo athawa. 28 Koma Paulo anafuula kuti: “Usadzivulaze, cifukwa tonse tilipo!” 29 Iye anapempha nyale ndipo anathamangila mkatimo. Akunjenjemela ndi mantha, anagwada pamaso pa Paulo ndi Sila. 30 Kenako anawatulutsa panja n’kunena kuti: “Inu mabwana, ndiyenela kucita ciyani kuti ndipulumuke?” 31 Iwo anati: “Khulupilila Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, pamodzi ndi anthu a m’banja lako.” 32 Ndiyeno anamuuza mawu a Yehova pamodzi ndi onse a m’nyumba yake. 33 Kenako anawatenga usiku womwewo ndi kutsuka mabala awo. Ndiyeno posapita nthawi iye ndi onse a m’banja lake anabatizika. 34 Kenako anawalowetsa m’nyumba mwake n’kuwaikila cakudya pathebulo. Ndipo iye ndi a m’banja lake onse anakondwela kwambili cifukwa anakhulupilila Mulungu.

35 Kutaca m’mawa, akuluakulu a zamalamulo anatumiza asilikali kukauza woyang’anila ndende kuti: “Amasuleni anthu awa.” 36 Woyang’anila ndende uja anauza Paulo uthengawo kuti: “Akuluakulu a zamalamulo atumiza anthu kudzanena kuti awilinu mumasulidwe. Conco tulukani tsopano, ndipo mupite mu mtendele.” 37 Koma Paulo anawauza kuti: “Iwo anatikwapula pamaso pa anthu n’kutiponya m’ndende popanda kutiweluza,* ngakhale kuti ndife Aroma. Koma tsopano akufuna kutitulutsa mobisa? Ayi, sitilola! Auzeni iwo abwele adzatipelekeze potuluka.” 38 Ndiyeno asilikaliwo anapita kukafotokoza zimenezi kwa akuluakulu a zamalamulo aja. Akuluakulu a zamalamulowo atamva kuti anthuwo ndi Aroma anacita mantha kwambili. 39 Conco iwo anabwela n’kuwacondelela, ndipo atawapelekeza powatulutsa anawapempha kuti acoke mumzindawo. 40 Koma atatuluka m’ndendemo anapita kunyumba kwa Lidiya. Iwo ataona abale, anawalimbikitsa, kenako ananyamuka n’kumapita.

17 Kenako iwo anayenda kudutsa ku Amfipoli komanso Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda. 2 Conco Paulo mwacizolowezi cake, analowa m’sunagogemo. Ndipo kwa milungu itatu anali kukambilana nawo kucokela m’Malemba. 3 Iye anafotokoza ndi kuonetsa umboni wolembedwa wowatsimikizila kuti kunali koyenela kuti Khristu avutike, kenako auke. Anali kunena kuti: “Yesu amene ndikumulalikila kwa inu ndiye Khristu.” 4 Zotulukapo zake zinali zakuti, ena mwa iwo anakhala okhulupilila ndipo anagwilizana ndi Paulo ndi Sila. Agiriki ambili opembedza Mulungu komanso azimayi ambili olemekezeka anacitanso cimodzimodzi.

5 Koma Ayuda anacita nsanje, moti anasonkhanitsa anthu ena oipa amene anali kungoyendayenda mu msika. Iwo anapanga gulu laciwawa n’kuyambitsa cipolowe mu mzindamo. Kenako anaphwanya citseko n’kukalowa m’nyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse panja n’kuwapeleka ku gulu la cipolowelo. 6 Atalephela kuwapeza, anatenga Yasoni komanso abale ena n’kuwaguzila kwa olamulila mu mzinda, akufuula kuti: “Anthu awa amene asokoneza* dziko lonse alinso kuno. 7 Ndipo Yasoni wawalandila ngati alendo ake. Anthu onsewa akucita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara. Iwo akunena kuti kulinso mfumu ina dzina lake Yesu.” 8 Iwo atamva izi, khamu lonse komanso olamulila a mu mzindawo anakwiya kwambili. 9 Olamulila a mzindawo analipilitsa Yasoni komanso enawo ndalama.* Kenako anawamasula.

10 Kutangokuda, abale anatulutsa Paulo ndi Sila n’kuwatumiza ku Bereya. Iwo atafika kumeneko analowa mu sunagoge wa Ayuda. 11 Anthu a ku Bereya anali a mtima wofuna kuphunzila kuposa anthu a ku Tesolonika aja. Iwo analandila mawu a Mulungu ndi cidwi cacikulu kwambili, ndipo tsiku lililonse anali kufufuza Malemba mosamala kuti atsimikizile ngati zimene anamva zinalidi zoona. 12 Conco ambili a iwo anakhala okhulupilila, cimodzimodzinso akazi ochuka ambili ndi amuna acigiriki. 13 Koma Ayuda a ku Tesalonika atadziwa kuti Paulo akulengezanso mawu a Mulungu ku Bereya, anapita kumeneko kukatuntha khamu la anthu kuti agwile atumwiwo. 14 Kenako nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo ku nyanja. Koma Sila ndi Timoteyo anatsalila kumeneko. 15 Anthu amene anapelekeza Paulo anafika naye mpaka ku Atene. Koma anabwelela atauzidwa kuti Sila ndi Timoteyo abwele kwa Paulo mwamsanga.

16 Pamene Paulo anali kuwayembekezela ku Atene, cinamuwawa kwambili poona kuti mzindawo ndi wodzala ndi mafano. 17 Conco ali m’sunagoge anayamba kukambilana ndi Ayuda komanso anthu ena olambila Mulungu. Ndipo tsiku lililonse anali kukambilananso ndi anthu amene anali kuwapeza mu msika. 18 Koma ena anzelu za Epikureya ndi Asitoiki anayamba kutsutsana naye. Ena anali kunena kuti: “Kodi munthu wobwetukabwetuka uyu akufuna kutiuza ciyani?” Pamene ena anali kunena kuti: “Ayenela kuti ndi mlaliki wa milungu yacilendo.” Zinali conco cifukwa iye anali kulengeza uthenga wabwino wokamba za Yesu, komanso za kuuka kwa akufa. 19 Conco anamugwila n’kupita naye ku bwalo la Areopagi n’kumuuza kuti: “Kodi ungatifotokozeleko za ciphunzitso catsopano cimene ukuphunzitsaci? 20 Cifukwa ukufotokoza zinthu zimene ndi zacilendo m’makutu mwathu, ndipo tifuna kudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi.” 21 Anthu onse a ku Atene, komanso alendo okhala kumeneko* anali kuthela nthawi yawo yopumula, akufotokoza kapena kumvetsela nkhani zatsopano. 22 Tsopano Paulo anaimilila pakati pa bwalo la Areopagi n’kunena kuti:

“Inu anthu a ku Atene, ndaona kuti pa zinthu zonse mumaopa kwambili milungu* kuposa mmene anthu ena amacitila. 23 Mwacitsanzo, pamene ndinali kudutsa n’kuyang’anitsitsa zinthu zimene mumalambila, ndapezanso guwa la nsembe lolembedwa kuti ‘Kwa Mulungu Wosadziwika.’ Conco ine, ndikulalikila kwa inu za Mulungu wosadziwikayo amene mukumulambila. 24 Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zonse zokhala mmenemo, Mbuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala mu akacisi opangidwa ndi manja. 25 Komanso satumikilidwa ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu, cifukwa iye mwini amapeleka kwa anthu onse moyo, mpweya ndi zinthu zina zonse. 26 Ndipo kucokela mwa munthu mmodzi, anapanga mitundu yonse ya anthu kuti ikhale pa dziko lonse lapansi. Iye anaika nthawi yakuti zinthu zina zizicitika, komanso anaika malile a malo akuti anthu azikhalamo. 27 Anacita zimenezo kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuze ndi kumupezadi, ngakhale kuti iye kwenikweni sali kutali ndi aliyense wa ife. 28 Pakuti cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda, ndipo tilipo ngati mmene andakatulo anu ena ananenela kuti, ‘Pakuti nafenso ndife ana ake.’

29 “Conco, popeza ndife ana a Mulungu, sitiyenela kuganiza kuti Mulunguyo ali ngati golide, siliva, mwala, kapena ciliconse cosemedwa ndi anthu aluso. 30 N’zoona kuti Mulungu ananyalanyaza nthawi imene anthu sanali kudziwa zinthu, koma tsopano akulengeza kwa anthu onse kwina kulikonse kuti alape. 31 Cifukwa wakhazikitsa tsiku limene adzaweluza mwacilungamo dziko lonse lapansi kudzela mwa munthu amene iye wamusankha. Ndipo watsimikizila anthu onse zimenezi mwa kumuukitsa kwa akufa.”

32 Ndiyeno anthuwo atamva za kuuka kwa akufa, ena a iwo anayamba kumunyodola, pamene ena anati: “Tidzakumvetselanso nthawi ina pa nkhaniyi.” 33 Conco Paulo anawasiya. 34 Koma anthu ena anakhala kumbali ya Paulo ndipo anakhala okhulupilila. Ena mwa iwo anali Diyonisiyo, amene anali woweluza m’khoti ya Areopagi, mayi wina dzina lake Damarisi komanso anthu ena.

18 Pambuyo pake Paulo anacoka ku Atene n’kupita ku Korinto. 2 Kumeneko anapeza Myuda wina dzina lake Akula, wa ku Ponto. Iye ndi mkazi wake Purisila, anali atangofika kumene kucokela ku Italy, cifukwa Kalaudiyo anali atalamula kuti Ayuda onse acoke ku Roma. Conco Paulo anapita kunyumba kwawo. 3 Popeza nchito yawo inali yofanana, anakhala kunyumba kwawo. Iwo anali kugwilila nchito pamodzi cifukwa onse anali opanga matenti. 4 Paulo anali kukamba nkhani m’sunagoge sabata lililonse, ndipo anali kukopa Ayuda ndi Agiriki.

5 Tsopano Sila ndi Timoteyo atafika kucokela ku Makedoniya, Paulo anatangwanika kwambili ndi nchito yolalikila mawu a Mulungu. Iye anali kucitila umboni kwa Ayuda ndiponso kuwatsimikizila kuti Yesu ndiye Khristu. 6 Koma iwo atapitiliza kumutsutsa komanso kumunyoza, iye anakutumula zovala zake n’kuwauza kuti: “Magazi anu akhale pa mutu panu. Ine ndilibe mlandu. Kuyambila tsopano ndizipita kwa anthu a mitundu ina.” 7 Conco, iye anacoka kumeneko* n’kupita kunyumba ya munthu wina dzina lake Titiyo Yusito. Iye anali munthu wolambila Mulungu, amene nyumba yake inali moyandikana ndi sunagoge. 8 Kirisipo, mtsogoleli wa sunagoge, anakhala wokhulupilila Ambuye, pamodzi ndi anthu onse a m’banja lake. Anthu ambili a ku Korinto amene anamva uthenga wabwino, anayamba kukhulupilila ndipo anabatizika. 9 Koma usiku Ambuye anauza Paulo m’masomphenya kuti: “Usaope, pitiliza kulankhula. Ndipo usakhale cete, 10 cifukwa ine ndili nawe. Ndipo palibe amene adzakupanda kapena kukucita zacipongwe, popeza ndili ndi anthu ambili mu mzindawu.” 11 Conco anakhala kumeneko caka cimodzi ndi miyezi 6, akuwaphunzitsa mawu a Mulungu.

12 Pamene Galiyo anali bwanamkubwa* wa Akaya, Ayuda anagwilizana zogwila Paulo, ndipo anapita naye ku mpando woweluzila milandu. 13 Kumeneko iwo anati: “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu m’njila yosemphana ndi Cilamulo.” 14 Koma Paulo atangotsala pang’ono kuyamba kulankhula, Galiyo anauza Ayudawo kuti: “Inu Ayuda, cikanakhala colakwa cina kapena mlandu waukulu, ndithu ndikanaleza mtima kukumvetselani. 15 Koma ngati nkhani yake ndi yokhudza mikangano pa mawu, maina ndi cilamulo canu, muthane nazo nokha. Sindikufuna kuti ndikhale woweluza pa nkhani ngati zimenezi.” 16 Atatelo, anauza anthuwo kuti acoke ku mpando woweluzila milanduwo. 17 Zitatelo, onse anagwila Sositeni mtsogoleli wa sunagoge n’kuyamba kumumenya pafupi ndi mpando woweluzila milanduwo. Koma Galiyo sanafune kulowelelapo ngakhale pang’ono pa zinthu zimenezi.

18 Paulo atakhala kumeneko kwa masiku ndithu, analayilana ndi abalewo n’kunyamuka ulendo wa panyanja kupita ku Siriya. Pa ulendowu anapita limodzi ndi Purisila ndi Akula. Paulo ali ku Kenkereya, anameta tsitsi lake cifukwa ca lumbilo limene anacita. 19 Conco iwo anafika ku Efeso, ndipo anasiya anzakewo kumeneko. Koma iye anapita kukalowa m’sunagoge n’kuyamba kukambilana ndi Ayuda. 20 Ngakhale kuti iwo mobwelezabweleza anamupempha kuti akhale nawo kwa masiku ena ambili, iye sanalole. 21 M’malomwake, analayilana nawo n’kuwauza kuti: “Yehova akalola, ndidzabwelanso kudzakuonani.” Kenako ananyamuka ku Efeso n’kuyamba ulendo wa panyanja, 22 ndipo anafika ku Kaisareya. Kenako anapita* kukapeleka moni ku mpingo, ndipo pambuyo pake anapita ku Antiokeya.

23 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, ananyamuka n’kuyamba kuyenda malo osiyanasiyana m’cigawo ca Galatiya ndi Fulugiya, ndipo anali kulimbikitsa ophunzila onse.

24 Tsopano Myuda wina dzina lake Apolo wa ku Alekizandiriya, anafika ku Efeso. Ameneyu anali kulankhula mwaluso komanso anali kudziwa bwino Malemba. 25 Mwamuna ameneyu anaphunzitsidwa* njila ya Yehova. Anali wodzipeleka kwambili cifukwa anali ndi mzimu woyela, ndipo anali kulankhula ndi kuphunzitsa za Yesu molondola. Koma iye anali kudziwa za ubatizo wa Yohane wokha basi. 26 Iye anayamba kulankhula molimba mtima m’sunagoge. Ndiyeno Purisila ndi Akula atamumvetsela, anamutenga n’kumufotokozela njila ya Mulungu molondola. 27 Ndipo popeza kuti Apolo anali kufunitsitsa kupita ku Akaya, abalewo analembela kalata ophunzila kumeneko. Anawalimbikitsa kuti amulandile bwino. Conco iye atafika kumeneko, anawathandiza kwambili anthu amene mwa cisomo ca Mulungu, anakhala okhulupilila. 28 Cifukwa iye anawatsimikizila Ayuda poyela komanso mwamphamvu kuti anali olakwa. Ndipo anagwilitsa nchito Malemba poonetsa kuti Yesu ndiye Khristu.

19 Apolo ali ku Korinto, Paulo anadzela ku madela a kumtunda mpaka anafika ku Efeso. Kumeneko iye anapeza ophunzila ena, 2 ndipo anawafunsa kuti: “Kodi munalandila mzimu woyela mutakhala okhulupilila?” Iwo anamuyankha kuti: “Sitinamvepo kuti kuli mzimu woyela.” 3 Iye anawafunsanso kuti: “Ndiye kodi munabatizidwa ubatizo wotani?” Iwo anayankha kuti: “Ubatizo wa Yohane.” 4 Ndiyeno Paulo anati: “Yohane anali kubatiza anthu ndipo ubatizowo unali cizindikilo cakuti munthu walapa. Anali kuuza anthu kuti akhulupilile amene anali kubwela m’mbuyo mwake, kutanthauza Yesu.” 5 Atamva izi, anthuwo anabatizika m’dzina la Ambuye Yesu. 6 Ndiyeno Paulo ataika manja ake pamutu pawo, iwo analandila mzimu woyela, ndipo anayamba kukamba zinenelo zina komanso kulosela. 7 Onse pamodzi anali amuna pafupifupi 12.

8 Kwa miyezi itatu, Paulo anali kulowa m’sunagoge ndipo anali kulankhula molimba mtima. Kumeneko anali kukamba nkhani ndi kuwafotokozela mfundo zogwila mtima za Ufumu wa Mulungu. 9 Koma ena anakana mwamwano kukhulupilila,* ndipo anali kukamba zinthu zonyoza Njilayo pamaso pa khamu la anthu. Conco iye anacoka n’kucotsanso ophunzila pakati pawo. Ndipo tsiku ndi tsiku anali kukamba nkhani mu holo ya pa sukulu ya Turano. 10 Izi zinacitika kwa zaka ziwili, moti anthu onse okhala m’cigawo ca Asia, anamva mawu a Ambuye, onse Ayuda ndi Agiriki.

11 Ndipo kupitila mwa Paulo, Mulungu anapitiliza kucita zinthu zamphamvu komanso zodabwitsa, 12 cakuti anthu anali kutenga ngakhale tunsalu ndi zovala* zimene zinakhudza thupi la Paulo n’kupita nazo kwa odwala, ndipo matenda awo anali kuthelatu. Mizimu yoipa nayonso inali kutuluka. 13 Koma Ayuda ena amene anali kuyendayenda n’kumatulutsa ziwanda, nawonso anayesa kuchula dzina la Ambuye Yesu pofuna kucilitsa anthu amene anali ndi mizimu yoipa. Iwo anali kunena kuti: “Ndikukulamula m’dzina la Yesu amene Paulo amalalikila za iye.” 14 Tsopano panali ana aamuna 7 a Sikeva, wansembe wamkulu waciyuda, amene anali kucita zimenezi. 15 Koma mzimu woipa unawauza kuti: “Yesu ndimamudziwa, komanso Paulo ndimamudziwa bwino. Nanga inu ndinu ndani?” 16 Ndiyeno munthu uja amene anali ndi mzimu woipa anawalumphila. Analimbana nawo mmodzi mmodzi ndipo anawagonjetsa onsewo, moti anathawa m’nyumbamo ali malisece komanso atavulazidwa. 17 Izi zinadziwika kwa onse, kwa Ayuda ndi Agiriki amene anali kukhala ku Efeso. Onsewo anagwidwa ndi mantha, ndipo dzina la Ambuye Yesu linapitiliza kulemekezedwa. 18 Anthu ambili mwa amene anakhala okhulupilila anali kubwela kudzaulula macimo awo, ndiponso kudzafotokoza poyela zoipa zimene anali kucita. 19 Anthu ambili amene anali kucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo n’kuwatentha anthu onse akuona. Ndipo atawelengetsela mtengo wake, anapeza kuti anali okwana ndalama zasiliva 50,000. 20 Conco mawu a Yehova anapitiliza kufalikila ndipo sanagonjetsedwe.

21 Izi zitacitika, Paulo anatsimikiza mu mtima mwake kuti atadzela ku Makedoniya ndi ku Akaya, apite ku Yerusalemu. Iye anakamba kuti: “Ndikakafika kumeneko, ndidzapitanso ku Roma.” 22 Conco ku Makedoniya anatumizako awili mwa amene anali kumutumikila, iwo anali Timoteyo ndi Erasito. Koma iye anakhalabe m’cigawo ca Asia kwa kanthawi ndithu.

23 Panthawiyo, panali patabuka msokonezo waukulu wokhudza Njila ya Ambuye. 24 Panali munthu wina dzina lake Demetiriyo, wopanga zinthu zasiliva. Amisili anali kupeza phindu kwambili cifukwa ca nchito yake yopanga tuakacisi twasiliva twa Atemi. 25 Demetiriyo anasonkhanitsa amisiliwo, limodzi ndi ena amene anali kugwila nchito ngati zimenezi n’kuwauza kuti: “Anthu inu, mukudziwa kuti timapeza cuma kucokela m’bizinesi imeneyi. 26 Tsopano mukuona ndi kumva mmene Paulo ameneyu wakopela anthu ambili kuti ayambe kukhulupilila zinthu zina. Iye wacita zimenezi osati mu Efeso mokha, koma pafupifupi m’cigawo conse ca Asia. Iye akukamba kuti milungu yopangidwa ndi manja si milungu yeniyeni. 27 Komanso cimene cikuopsa kwambili si kunyozeka kwa bizinesi yathuyi ayi, koma kacisi wa mulungu wamkazi Atemi adzaonedwa wacabecabe. Atemi ameneyu amene amalambilidwa m’cigawo conse ca Asia, komanso kulikonse kumene kuli anthu pa dziko lapansi adzaleka kupatsidwa ulemelelo wake.” 28 Anthuwo atamva zimenezi anakwiya kwambili, ndipo anayamba kufuula kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!”

29 Zitatelo, mu mzindawo munadzala cisokonezo, ndipo anthu onse anathamangila m’bwalo la masewela, n’kukokela Gayo ndi Arisitako m’bwalomo. Gayo ndi Arisitako amene anali kuyenda ndi Paulo kwawo kunali ku Makedoniya. 30 Paulo anali kufuna kulowa mkati m’gulu la anthulo, koma ophunzila sanamulole. 31 Ngakhale ena mwa oyang’anila zikondwelelo ndi masewela, amene anali anzake a Paulo, anatumiza uthenga kumucondelela kuti asaike moyo wake pangozi mwa kulowa m’bwalo la masewelalo. 32 Kukamba zoona, khamu lonse linali litasokonezeka, ena anali kufuula zinthu zina pamene ena zinthu zina. Ndipo ambili a iwo sanadziwe kuti n’cifukwa ciyani anasonkhana kumeneko. 33 Conco anatulutsa Alekizanda m’khamulo ndipo Ayuda anali kumukankhila kutsogolo. Ndiyeno Alekizanda anakweza dzanja lake kuti alankhule podziteteza kwa anthuwo. 34 Koma atazindikila kuti ndi Myuda, anayamba kufuula capamodzi kwa maola pafupifupi awili kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!”

35 Woyang’anila mzindawo atauza khamulo kuti likhale cete anati: “Anthu inu a mu Efeso, kodi pali amene sadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndi umene umayang’anila kacisi wamkulu wa Atemi ndi cifanizilo cimene cinagwa kucokela kumwamba? 36 Popeza palibe amene angatsutse zimenezi, muyenela kudekha, ndipo musacite zinthu mopupuluma. 37 Cifukwa anthu amene mwabweletsa kunowa si akuba akacisi kapena onyoza mulungu wathu wamkaziyo. 38 Conco ngati Demetiriyo ndi amisili awa akuimba mlandu munthu winawake, pali masiku osamalila milandu ndipo abwanamkubwa* alipo. Apite akafole kumeneko. 39 Koma ngati mukufuna zina zoposa pamenepa, cigamulo cake ciyenela kukapelekedwa pa bwalo lovomelezeka. 40 Pakuti zimene zacitikazi n’zoopsa kwambili cifukwa tingaimbidwe nazo mlandu woukila boma. Pakuti palibe cifukwa comveka cimene tingapeleke pa cipolowe cimene cacitikaci.” 41 Atanena zimenezi, anauza anthuwo kuti acoke pamalopo.

20 Cipolowe cija citatha, Paulo anaitanitsa ophunzila, ndipo atawalimbikitsa, analailana nawo. Kenako anayamba ulendo wake wopita ku Makedoniya. 2 Iye atayendayenda m’madela a kumeneko, komanso kulimbikitsa ophunzila ndi mawu ambili, anafika ku Girisi. 3 Anakhala kumeneko miyezi itatu. Koma cifukwa cakuti Ayuda anali atamukonzela ciwembu atatsala pang’ono kuyamba ulendo wa panyanja kupita ku Siriya, iye anaganiza zobwelela n’kudzela ku Makedoniya. 4 Pa ulendowo anali ndi Sopaturo mwana wa Puro wa ku Bereya, Arisitako ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Debe, ndi Timoteyo, komanso Tukiko ndi Terofimo ocokela ku cigawo ca Asia. 5 Amunawo anatsogola ndipo anali kutiyembekezela ku Torowa. 6 Koma masiku a mkate wopanda zofufumitsa atatha, tinanyamuka ulendo wa panyanja wocoka ku Filipi. Ndipo pambuyo pa masiku asanu tinawapeza ku Torowa kumene tinakhalako masiku 7.

7 Pa tsiku loyamba la mlungu, titasonkhana pamodzi kuti tidye cakudya, Paulo anayamba kuwakambila nkhani cifukwa tsiku lotsatila anali kucoka. Ndipo anakamba kwa nthawi yaitali mpaka pakati pa usiku. 8 M’cipinda capamwamba mmene tinali titasonkhanamo munali nyale zambili. 9 Paulo ali mkati mokamba nkhani, mnyamata wina dzina lake Utiko anali khale pawindo ndipo anagona tulo tofa nato. Ali m’tulo telo, anagwa kucoka pa nsanjika yacitatu ya nyumbayo, ndipo anamupeza atafa. 10 Koma Paulo anatsika n’kufika pamene panali mnyamatayo n’kumukumbatila. Kenako anakamba kuti: “Khalani cete, cifukwa tsopano mnyamatayu ali moyo.” 11 Atatelo Paulo anapitanso m’cipinda capamwamba ndipo anatenga cakudya* n’kuyamba kudya. Kenako anapitiliza kukambilana nawo kwa nthawi yaitali mpaka matandakuca. Ndiyeno ananyamuka n’kupita. 12 Conco iwo anatenga mnyamatayo ali wamoyo, ndipo anatonthozedwa kwambili.

13 Tsopano ife tinatsogola kukakwela ngalawa n’kuyamba ulendo wopita ku Aso, koma Paulo anayenda wapansi. Tinamutengela ku Asosi malinga ndi mmene anatilangizila. 14 Conco atatipeza ku Asosi tinamunyamula m’ngalawa n’kupita ku Mitilene. 15 Tsiku lotsatila tinacoka kumeneko, ndipo tinafika pafupi ndi Kiyo. Koma mawa lake tinaima kwa kanthawi ku Samo, ndipo tsiku lotsatila tinafika ku Mileto. 16 Paulo anaganiza zolambalala Efeso, kuti asataye nthawi m’cigawo ca Asia. Iye anali kuthamangila ku Yerusalemu kuti ngati n’kotheka, patsiku la Cikondwelelo ca Pentekosite akakhale kumeneko.

17 Koma ali ku Mileto anatumiza uthenga wakuti akulu a mu mpingo wa ku Efeso abwele. 18 Akuluwo atabwela, iye anawauza kuti: “Inu mukudziwa bwino mmene ndinali kucitila zinthu pakati panu kucokela tsiku loyamba limene ndinafika m’cigawo ca Asia. 19 Ndinatumikila Ambuye modzicepetsa kwambili ngati kapolo, ndi misozi komanso ziyeso zimene ndinakumana nazo cifukwa ca ziwembu za Ayuda. 20 Komabe sindinakubisileni ciliconse cothandiza, ndipo sindinaleke kukuphunzitsani pagulu komanso kunyumba ndi nyumba. 21 Koma ndinacitila umboni mokwanila kwa Ayuda komanso Agiriki kuti alape n’kubwelela kwa Mulungu, komanso kuti ayambe kuika cikhulupililo cawo mwa Ambuye wathu Yesu. 22 Ndipo tsopano ndikupita ku Yerusalemu motsogoleledwa* ndi mzimu ngakhale kuti sindikudziwa zimene zikandicitikile kumeneko. 23 Koma cimene ndikudziwa n’cakuti mu mzinda ndi mzinda, mzimu woyela wakhala ukundicitila umboni mobwelezabweleza kuti ndikuyembekezela kumangidwa komanso masautso. 24 Komabe kwa ine moyo wanga sindikuuona monga wofunika, ndingofuna kuti nditsilize kuthamanga mpikisanowu, komanso nditsilize utumiki umene ndinalandila kwa Ambuye Yesu. Kuti ndicitile umboni za uthenga wabwino wa cisomo ca Mulungu.

25 “Tsopano tamvelani! Ndikudziwa kuti nonsenu amene ndinakulalikilani za Ufumu simudzaonanso nkhope yanga. 26 Conco ine ndakuitanani kuti mukhale mboni lelo, kuti ndilibe mlandu wa magazi a anthu onse. 27 Pakuti ndinakuuzani malangizo* onse a Mulungu. 28 Muzidziyang’anila nokha komanso muyang’anile gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyela unakuikani kuti muziliyang’anila, kuti muwete mpingo wa Mulungu umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweniyo. 29 Ine ndidziwa kuti ndikapita, mimbulu yopondeleza idzabwela pakati panu, ndipo siidzacitila cifundo gulu la nkhosali. 30 Ndipo pakati panu padzakhala anthu ena amene adzayamba kulankhula zinthu zopotoka n’colinga copatutsa ophunzila kuti aziwatsatila.

31 “Conco khalani maso, ndipo musaiwale kuti kwa zaka zitatu, usana ndi usiku, sindinaleke kucenjeza aliyense wa inu ndikukhetsa misozi. 32 Tsopano Mulungu komanso mawu a cisomo cake akutetezeni. Mawuwo angakulimbikitseni ndi kukupatsani colowa pakati pa oyela onse. 33 Sindinakhumbile siliva, golide kapena covala ca munthu. 34 Inu mukudziwa kuti manja awa anagwila nchito kuti ndidzipezele zofunikila komanso za anthu amene ndinali nawo. 35 Ine ndakuonetsani m’zinthu zonse kuti mwa kugwila nchito molimbika mwa njila imeneyi, muyenela kuthandiza anthu ofooka, komanso muzikumbukila mawu a Ambuye Yesu. Iye mwiniyo anati: ‘Kupatsa kumabweletsa cimwemwe cacikulu kuposa kulandila.’”

36 Atakamba izi, iye ndi akulu onsewo anagwada n’kupemphela. 37 Zitatelo, onse analila kwambili, ndipo anakumbatila Paulo ndi kumukising’a* mwacikondi. 38 Iwo anamva cisoni kwambili, makamaka cifukwa ca mawu a Paulo akuti iwo sadzaonanso nkhope yake. Kenako anamupelekeza kukakwela ngalawa.

21 Cifukwa cakuti tinali kusiyana nawo, tinayamba ulendo wathu wa panyanja tili acisoni kwambili. Tinayenda osakoneka mpaka kukafika ku Ko. Tsiku lotsatila tinafika ku Rode, ndipo titacoka kumeneko tinakafika ku Patara. 2 Titapeza ngalawa yopita ku Foinike, tinakwela n’kupita nayo. 3 Cisumbu ca Kupuro citayamba kuonekela, tinapatukila kumanzele* n’kucisiya, ndipo tinalowela ku Siriya. Kenako tinaima ku Turo kuti ngalawayo itsitse katundu. 4 Tinafufuza ophunzila n’kuwapeza, ndipo tinakhala kumeneko masiku 7. Koma iwo atauzilidwa ndi mzimu, anauza Paulo mobwelezabweleza kuti asakapondeko phazi ku Yerusalemu. 5 Conco masiku athu okhala kumeneko atatha, tinanyamuka kuti tipitilize ulendo wathu. Koma abale onse ndi azimayi komanso ana, anatipelekeza mpaka kunja kwa mzindawo. Kumeneko tinagwada m’mbali mwa nyanja n’kupemphela. 6 Kenako tinalailana nawo. Ndiyeno ife tinakwela ngalawa, ndipo iwo anabwelela kunyumba kwawo.

7 Conco tinanyamuka ku Turo pa ngalawa ndipo tinafika ku Tolemayi. Kumeneko tinapeleka moni kwa abale n’kukhala nawo tsiku limodzi. 8 Tsiku lotsatila tinanyamuka n’kufika ku Kaisareya, ndipo tinalowa m’nyumba ya mlaliki wina dzina lake Filipo. Iye anali mmodzi wa amuna 7 aja a mbili yabwino, ndipo tinakhala naye. 9 Munthu ameneyu anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa* amene anali kunenela. 10 Koma titakhala kumeneko kwa masiku ndithu, mneneli wina dzina lake Agabo anabwela kucokela ku Yudeya. 11 Iye anabwela kwa ife n’kutenga lamba wa Paulo ndipo anadzimanga manja ndi miyendo n’kunena kuti: “Mzimu woyela wanena kuti, ‘Mwiniwake wa lambayu, adzamangidwa conci ndi Ayuda ku Yerusalemu, ndipo adzamupeleka m’manja mwa anthu a mitundu ina.’” 12 Titamva zimenezi, ifeyo ndi anthu omwe analipo, tinayamba kumucondelela kuti asapite ku Yerusalemu. 13 Koma Paulo anafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukulila ndiponso mukufuna kundifooketsa? Ndithu ndikukuuzani, ndine wokonzeka osati cabe kumangidwa koma ngakhale kukafa ku Yerusalemu cifukwa ca dzina la Ambuye Yesu.” 14 Titalephela kumusintha maganizo, tinaleka* kumucondelela ndipo tinati: “Cifunilo ca Yehova cicitike.”

15 Pambuyo pake tinakonzekela n’kuuyamba ulendo wopita ku Yerusalemu. 16 Nawonso ophunzila ena a ku Kaisareya anatipelekeza mpaka kukafika kunyumba kwa Mnaso wa ku Kupuro. Munthu ameneyu anali mmodzi wa ophunzila oyambilila. Iye anatilandila monga alendo. 17 Titafika ku Yerusalemu, abale anatilandila mokondwela. 18 Koma tsiku lotsatila Paulo anapita nafe kwa Yakobo, ndipo akulu onse anali komweko. 19 Paulo anapeleka moni kwa iwo, n’kuyamba kuwafotokozela mwatsatanetsatane zimene Mulungu anacita kwa anthu a mitundu ina kudzela mu utumiki wake.

20 Atamva zimenezi, anayamba kutamanda Mulungu, koma anamuuza kuti: “Ona m’bale, pali Ayuda masauzande ambili okhulupilila, ndipo ndi okangalika potsatila Cilamulo. 21 Koma iwo anamva mphekesela zakuti iwe ukuphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa anthu a mitundu ina kuti apatuke pa Cilamulo ca Mose. Akuti ukuwaletsa kucita mdulidwe wa ana awo komanso kutsatila miyambo imene akhala akuitsatila. 22 Ndiye titani pamenepa? Mosakayikila iwo adzamva kuti iwe wabwela. 23 Conco ucite zimene tikuuze. Tili ndi amuna anayi amene anacita mdulidwe. 24 Utenge amuna awa, ndipo ukadziyeletse mwamwambo pamodzi ndi iwo. Uwalipilile zofunikila kuti amete tsitsi lawo. Ukatelo onse adzadziwa kuti mphekesela zimene anamva zokhudza iwe sizinali zoona. Koma adzaona kuti ukucita zinthu mwadongosolo ndiponso kuti ukutsatila Cilamulo. 25 Ponena za okhulupilila ocokela m’mitundu ina, iwo tinawalembela kalata yofotokoza cigamulo cathu cakuti azipewa zinthu zopelekedwa nsembe ku mafano komanso magazi, zopotola* ndiponso ciwelewele.”*

26 Conco tsiku lotsatila Paulo anatenga amunawo, ndipo anadziyeletsa mwamwambo pamodzi ndi iwo. Ndiyeno analowa m’kacisi n’kunena pamene masiku awo a mwambo wa kudziyeletsa adzathela, ndiponso pamene wansembe adzapeleke nsembe ya aliyense wa iwo.

27 Masiku 7 atatsala pang’ono kutha, Ayuda a ku Asia anaona Paulo ali m’kacisi. Iwo anatuntha khamu lonse la anthu kuti ligwile Paulo, ndipo anamugwila. 28 Iwo anali kufuula kuti: “Amuna inu, Aisiraeli, tithandizeni! Uyu ndiye munthu amene amaphunzitsa anthu kulikonse zotsutsana ndi anthu a mtundu wathu, Cilamulo cathu, ndi malo ano. Kuwonjezela apo, walowetsa Agiriki mʼkacisi ndipo waipitsa malo oyelawa.” 29 Anatelo cifukwa anali ataona Paulo ali ndi Telofimo wa ku Efeso mumzindawo, ndiye anaganiza kuti Paulo analowa naye m’kacisi. 30 Conco mumzinda wonsewo munali cipolowe, ndipo anthu anali kuthamangila ku kacisiko. Iwo anagwila Paulo ndi kumuguzila kunja kwa kacisi. Ndipo nthawi yomweyo zitseko zinatsekedwa. 31 Pamene anali kufuna kumupha, uthenga unafika kwa mkulu wa gulu la asilikali kuti mu Yerusalemu monse muli cipwilikiti. 32 Nthawi yomweyo, iye anatenga asilikali ndi atsogoleli awo nʼkuthamangila komweko. Anthuwo ataona mkulu wa asilikali ndi asilikaliwo, analeka kumumenya Paulo.

33 Ndiyeno mkulu wa asilikaliyo anafika pafupi ndi kumugwila ndipo analamula kuti amumange ndi maunyolo awili. Kenako anafunsa anthu kuti iye ndi ndani komanso kuti anacita ciyani. 34 Koma anthu ena m’khamulo anayamba kufuula zinthu zina, enanso zina. Conco atalephela kutolapo mfundo yeniyeni cifukwa ca phokoso, analamula kuti apite naye kumalo okhala asilikali. 35 Koma atafika pa masitepe, asilikaliwo anacita kumunyamula cifukwa ca ciwawa ca khamulo. 36 Pakuti khamu limene linali kuwatsatila linali kufuula kuti: “Aphedwe ameneyo!”

37 Atatsala pang’ono kufika kumalo okhala asilikali, Paulo anafunsa mkulu wa asilikaliwo kuti: “Kodi mungandilole ndilankhule nanu pang’ono?” Mkulu wa asilikaliyo anati: “Kansi umalankhula Cigiriki? 38 Kodi si ndiwe munthu wa ku Iguputo amene kumbuyoku unayambitsa cipolowe coukila boma n’kutsogolela zigawenga 4,000 kupita nazo ku cipululu?” 39 Ndiyeno Paulo anayankha kuti: “Ine ndine Myuda wa ku Tariso ku Kilikiya, nzika ya mzinda wochuka. Conco ndikukupemphani kuti mundilole ndilankhule nawo anthuwa.” 40 Atamulola, Paulo anaimilila pa masitepe ndi kukwezela anthuwo dzanja lake. Onse anakhala cete, ndiyeno analankhula nawo m’Ciheberi kuti:

22 “Amuna inu, abale ndi azitate, imvani mawu anga odziteteza.” 2 Ataona kuti akulankhula nawo m’Ciheberi, onse anangoti zii, ndipo iye anati: 3 “Ine ndine Myuda, wobadwila ku Tariso wa ku Kilikiya, koma ndinaphunzitsidwa ndi Gamaliyeli mu mzinda womwe uno. Anandiphunzitsa kutsatila mwakhama Cilamulo ca makolo athu. Ndinalinso wacangu kwambili potumikila Mulungu, ngati mmene zilili kwa nonsenu lelo. 4 Ndinali kuzunza otsatila Njilayo mpaka ena kuwapha. Ndinali kumanga amuna komanso akazi nʼkuwapeleka ku ndende. 5 Mkulu wa ansembe ndi bungwe lonse la akulu angandicitile umboni. Cifukwa kwa iwo n’kumene ndinatenga makalata ondiloleza kukamanga abale athu ku Damasiko. Ndinanyamuka kuti ndikagwile anthu a kumeneko nʼkuwapeleka ku Yerusalemu ali omangidwa kuti akapatsidwe cilango.

6 “Koma pamene ndinali mʼnjila, nditatsala pangʼono kufika ku Damasiko dzuwa lili pamutu, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kunandiunika. Kuwalaku kunacokela kumwamba ndipo kunandizungulila. 7 Ndiyeno ndinagwa pansi n’kumva mawu akuti: ‘Saulo! Saulo! N’cifukwa ciyani ukundizunza?’ 8 Ine ndinayankha kuti: ‘Ambuye, kodi ndinu ndani?’ Iye anandiuza kuti: ‘Ndine Yesu Mnazareti amene ukumuzunza.’ 9 Anthu amene ndinali nawo anaona kuwalako, koma sanamve mawu a amene anali kulankhula nane. 10 Ndiyeno ine ndinati, ‘Ndicite ciyani Ambuye?’ Ambuyewo anandiuza kuti, ‘Nyamuka upite ku Damasiko. Kumeneko udzauzidwa zonse zimene zakonzedwa kuti ucite.’ 11 Koma popeza sindinali kutha kuona cifukwa ca mphamvu ya kuwalako, anthu amene ndinali nawo anandigwila dzanja mpaka kukafika ku Damasiko.

12 “Ndiyeno munthu wina woopa Mulungu mogwilizana ndi Cilamulo, dzina lake Hananiya, amene anali ndi mbili yabwino pakati pa Ayuda okhala kumeneko, 13 anabwela. Anaima pafupi ndi ine n’kundiuza kuti: ‘Saulo m’bale wanga, yambanso kuona!’ Nthawi yomweyo ndinakweza maso anga n’kumuona. 14 Ndiyeno anandiuza kuti: ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha kuti udziwe cifunilo cake, komanso kuti uone wolungamayo ndi kumva mawu otuluka pakamwa pake. 15 Cifukwa udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zinthu zimene waona ndi kumva. 16 Ndiye n’cifukwa ciyani ukuzengeleza? Nyamuka ubatizike n’kucotsa macimo ako mwa kuitanila pa dzina lake.’

17 “Koma pamene ndinabwelela ku Yerusalemu n’kuyamba kupemphela m’kacisi, ndinaona masomphenya. 18 M’masomphenyawo ndinaona Ambuye akundiuza kuti: ‘Tuluka mwamsanga mu Yerusalemu, cifukwa anthuwo sadzamvela uthenga umene ukulengeza wokhudza ine.’ 19 Ndipo ine ndinati: ‘Ambuye, iwowa akudziwa bwino kuti ndinali kupita m’masunagoge n’kumaika anthu m’ndende, ndi kukwapula amene amakukhulupililani. 20 Pamene Sitefano mboni yanu anali kuphedwa,* ineyo ndinalipo, ndipo ndinavomelezana nazo. Ine ndi amene ndinali kuyang’anila zovala zakunja za anthu amene anali kumupha.’ 21 Koma iye anandiuza kuti: ‘Pita, cifukwa ndidzakutumiza kutali kwa anthu a mitundu ina.’”

22 Iwo anali kumumvetsela mpaka atanena mawu amenewa. Ndiyeno anafuula kuti: “M’cotseni munthu ameneyu pa dziko lapansi! Cifukwa sayenela kukhala ndi moyo!” 23 Popeza anali kufuula komanso kumaponya zovala zawo zakunja ndi fumbi m’mwamba, 24 mkulu wa asilikali analamula kuti Paulo alowe naye kumalo okhala asilikali. Ndipo anati ayenela kumufunsa mafunso kwinaku akum’kwapula kuti adziwe cimene anthu anali kumukuwilila conci. 25 Koma atamugoneka kuti amukwapule, Paulo anafunsa woyang’anila asilikali amene anaima pafupi naye kuti: “Kodi malamulo amakulolani kukwapula nzika ya Roma mlandu wake usanazengedwe?” 26 Mtsogoleli wa asilikaliyo atamva zimenezo, anapita kwa mkulu wa asilikali nʼkumuuza kuti: “Kodi mukufuna kucita ciyani? Pakuti munthuyu ndi nzika ya Roma.” 27 Conco mkulu wa asilikaliyo anayandikila Paulo n’kumufunsa kuti: “Ndiuze, kodi ndiwe nzika ya Roma?” Iye anati: “Inde.” 28 Mkulu wa asilikaliyo anakamba kuti: “Ine ndinagula ufulu wokhala nzika ya Roma ndi ndalama zambili.” Paulo anati: “Koma ine ndinacita kubadwa nawo.”

29 Nthawi yomweyo amuna amene anali kufuna kumufunsa mafunso kwinaku akumukwapula, anamutalamuka. Ndipo mkulu wa asilikaliyo anacita mantha atazindikila kuti munthu amene anamumanga uja ndi nzika ya Roma.

30 Conco tsiku lotsatila, popeza anali kufuna kudziwa cimene Ayuda anali kumuimbila mlandu, anamumasula. Ndiyeno analamula kuti ansembe aakulu komanso onse a m’Bungwe Lalikulu la Ayuda* asonkhane. Kenako anabweletsa Paulo nʼkumuimika pakati pawo.

23 Paulo anayang’anitsitsa Bungwe Lalikulu la Ayuda,* ndipo anati: “Amuna inu, abale, ndacita zinthu popanda cikumbumtima canga kunditsutsa ngakhale pang’ono, pamaso pa Mulungu mpaka lelo.” 2 Atamva izi, Hananiya mkulu wa ansembe analamula anthu amene anaimilila naye pafupi kuti amubwanyule kukamwa. 3 Kenako Paulo anamuuza kuti: “Uona, Mulungu akukantha, cipupa copaka laimu iwe. Wakhala apo kuti undiweluze motsatila Cilamulo, kodi ukuphwanyanso Cilamuloco polamula kuti andimenye?” 4 Amene anaimilila pafupi naye anati: “Kodi ukunyoza mkulu wa ansembe wa Mulungu?” 5 Ndiyeno Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Pakuti Malemba amati, ‘Usanenele zacipongwe wolamulila wa anthu a mtundu wako.’”

6 Lomba Paulo ataona kuti ena a iwo anali Asaduki, koma ena anali Afarisi, anafuula m’Bungwe Lalikulu la Ayuda kuti: “Amuna inu, abale anga, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi. Pano ndikuweluzidwa cifukwa ca ciyembekezo cakuti akufa adzauka.” 7 Cifukwa cakuti anakamba zimenezi, mkangano waukulu unabuka pakati pa Afarisi ndi Asaduki, ndipo gululo linagawikana. 8 Pakuti Asaduki amakamba kuti kulibe ciukitso, komanso kulibe angelo kapena colengedwa cauzimu. Pamene Afarisi amakhulupilila* kuti zonsezi zilipo. 9 Conco panabuka ciphokoso, ndipo alembi ena a m’gulu la Afarisi anaimilila n’kuyamba kutsutsa mwaukali kuti: “Munthu uyu sitinamupeze ndi mlandu wina ulionse, koma ngati mzimu kapena mngelo wakamba naye—.” 10 Mkanganowo utakula kwambili, mkulu wa asilikali anaopa kuti anthuwo adzamukhadzulakhadzula Paulo. Conco analamula asilikali kuti apite akamucotse pa gululo n’kupita naye kumalo okhala asilikali.

11 Koma tsikulo usiku, Ambuye anaimilila pafupi ndi Paulo n’kumuuza kuti: “Limba mtima! Cifukwa wandicitila umboni mokwanila mu Yerusalemu, ndipo uyenela kukandicitilanso umboni ku Roma.”

12 Kutaca, Ayuda anakonza ciwembu ndipo analumbila mocita kudzitembelela kuti sadzadya kapena kumwa kalikonse mpaka atapha Paulo. 13 Panali amuna opitilila 40 amene anakonza ciwembu cocita kulumbilaci. 14 Amunawa anapita kwa ansembe aakulu ndi akulu n’kuwauza kuti: “Ife talumbila mocita kudzitembelela kuti sitidzadya kalikonse mpaka titapha Paulo. 15 Tsopano inu ndi Bungwe Lalikulu la Ayuda muuze mkulu wa asilikali kuti abweletse Paulo kwa inu ngati kuti mukufuna kumvetsa bwino nkhani yake. Koma asanafike, ife tidzakhala okonzeka kumupha.”

16 Koma mwana wamwamuna wa mlongosi wake wa Paulo atamva za ciwembuci, cakuti akamukhalizila panjila, anapita kumalo okhala asilikali kukam’tsina khutu Paulo za ciwembuco. 17 Ndiyeno Paulo anaitana mmodzi wa atsogoleli a asilikali n’kumuuza kuti: “Tengani mnyamatayu mupite naye kwa mkulu wa asilikali, cifukwa ali naye mawu.” 18 Conco anamutenga n’kupita naye kwa mkulu wa asilikali, ndipo anamuuza kuti: “Paulo mkaidi uja anandiitana n’kundipempha kuti ndibweletse mnyamatayu kwa inu cifukwa ali nanu mawu.” 19 Mkulu wa asilikali uja anamugwila dzanja mnyamatayo nʼkupita naye pambali ndi kumufunsa kuti: “Kodi ukufuna kundiuza ciyani?” 20 Iye anati: “Ayuda agwilizana zokupemphani kuti mawa mukapeleke Paulo ku Bungwe Lalikulu la Ayuda ngati kuti akufuna kumvetsa bwino mlandu wake. 21 Koma musalole kuti akunyengeleleni, cifukwa amuna opitilila 40 afuna kumubisalila panjila. Iwo alumbila mocita kudzitembelela kuti sadzadya kapena kumwa kalikonse mpaka atamupha. Panopa ndi okonzeka, ndipo akungoyembekezela cilolezo canu.” 22 Mkulu wa asilikaliyo anauza mnyamatayo kuti azipita atamulamula kuti: “Usauze aliyense kuti wandidziwitsa zimenezi.”

23 Ndiyeno anaitanitsa atsogoleli awili a asilikali nʼkuwauza kuti: “Uzani asilikali 200 kuti akonzekele kupita ku Kaisareya. Muuzenso amuna 70 okwela pa mahachi* ndi asilikali 200 onyamula mikondo kuti apite ca m’ma 9 koloko* usiku uno. 24 Mupelekenso mahosi oti Paulo akwelepo kuti akafike ali wotetezeka kwa bwanamkubwa Felike.” 25 Ndipo analembanso kalata yokhala ndi mawu akuti:

26 “Ine Kalaudiyo Lusiya, ndikulembela inu Wolemekezeka Bwanamkubwa Felike: Landilani moni! 27 Munthu uyu Ayuda anamugwila ndipo anatsala pangʼono kumupha. Koma ine ndinabwela mwamsanga ndi asilikali anga n’kumupulumutsa, cifukwa ndinamva kuti iye ndi nzika ya Roma. 28 Ndipo pofuna kudziwa cimene analakwa, ndinapita naye ku Bungwe Lalikulu la Ayuda. 29 Ndinapeza kuti iwo akumuimba mlandu pa nkhani zokhudza Cilamulo cawo. Koma analibe mlandu ulionse woti n’kuphedwa nawo kapena kumutsekela m’ndende. 30 Koma cifukwa cakuti ciwembu cimene anakonzela munthuyu ine ndacidziwa, ndikumutumiza kwa inu, ndipo ndalamula omuimba mlanduwo kuti adzanene mlandu wake pamaso panu.”

31 Conco asilikaliwo anatenga Paulo mogwilizana ndi zimene analamulidwa n’kupita naye ku Antipatiri usiku. 32 Tsiku lotsatila analola amuna okwela pa mahachi kuti apitebe naye, koma iwo anabwelela kumalo okhala asilikali. 33 Amuna okwela pa mahachi aja anafika ku Kaisareya n’kupeleka kalata ija kwa bwanamkubwa ndipo anapelekanso Paulo kwa iye. 34 Conco iye anaiwelenga kalatayo, ndipo anafunsa Paulo cigawo cimene anali kucokela. Iye anamuuza kuti anali kucokela ku Kilikiya. 35 Kenako iye anati: “Ndimvetsela mlandu wako wonse anthu okuimba mlanduwo akafika.” Ndipo analamula kuti amusunge m’nyumba ya Mfumu Herode n’kumamulonda.

24 Patapita masiku asanu, mkulu wa ansembe Hananiya anabwela pamodzi ndi akulu ena, komanso munthu wina wodziwa kulankhula,* dzina lake Teritulo. Iwo anafotokoza mlandu wa Paulo kwa bwanamkubwayo. 2 Teritulo atapatsidwa mwayi wolankhula, anayamba kuimba mlandu Paulo kuti:

“Ife tikusangalala ndi mtendele waukulu cifukwa ca inu. Komanso cifukwa ca nzelu zanu zoona patali. Zinthu zikusintha mu mtundu wathuwu. 3 Conco nthawi zonse komanso kulikonse timaona zimenezi, inu Wolemekezeka a Felike, ndipo timayamikila kwambili. 4 Koma kuti ndisakutayitseni nthawi, ndikukupemphani mwa kukoma mtima kwanu kuti mutimvetseleko pang’ono. 5 Ife tapeza kuti munthu uyu ndi kadoyo kowononga,* iye akuyambitsa zoukila boma pakati pa Ayuda ndi dziko lonse. Ndipo akutsogolela gulu lampatuko la anthu a ku Nazareti. 6 Iye anali kufunanso kudetsa kacisi, conco tinamugwila. 7* —— 8 Mukamufunsa, mupeza kuti zonse zimene tikunenazi, n’zoona.”

9 Atakamba zimenezi, Ayuda nawonso analowelelapo n’kuyamba kutsimikizila kuti zinthuzo zinali zoona. 10 Bwanamkubwayo atagumulila mutu Paulo kuti alankhule, Paulo anayankha kuti:

“Podziwa bwino kuti inu mwakhala woweluza wa mtundu uwu kwa zaka zambili, ndine wokonzeka kulankhula kuti ndidziteteze. 11 Inu mukhoza kupeza umboni wotsimikizila kuti sipanapite masiku 12 kucokela pamene ndinapita ku Yerusalemu kukalambila. 12 Ndipo anthu awa sanandipeze kuti ndikukangana ndi wina aliyense m’kacisi, kapena kuyambitsa cipolowe m’masunagoge, kapenanso pena paliponse mumzinda wonsewo. 13 Ndipo pano anthu awa sangapeleke umboni wotsimikizila zinthu zimene akundinenezazi. 14 Koma cinthu cimene ndikuvomeleza kwa inu n’cakuti: Njila imene iwowa akuichula kuti gulu lampatuko, ndi imene ine ndikuitsatila pocita utumiki wopatulika kwa Mulungu wa makolo anga akale. Cifukwa ndimakhulupilila zinthu zonse za m’Cilamulo, komanso zolemba za aneneli. 15 Ndipo ine ndili ndi ciyembekezo ngati cimenenso anthu awa ali naco, kuti Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe. 16 Cifukwa ca izi, ndimayesetsa kukhala ndi cikumbumtima cabwino kwa Mulungu komanso kwa anthu. 17 Ndiyeno pambuyo pa zaka zambili, ndinabwela kudzapeleka mphatso za cifundo kwa anthu a mtundu wanga, komanso kudzapeleka nsembe. 18 Pamene ndinali kucita zimenezi, anthu awa anandipeza m’kacisi nditadziyeletsa motsatila mwambo. Panalibe khamu la anthu kapena cipolowe, koma panali Ayuda ena ocokela m’cigawo ca Asia. 19 Iwo akanakhala nane n’cifukwa, ndi amene akanayenela kubwela kwa inu kudzandiimba mlandu. 20 Kapena muwalole anthu ali panowa kuti akambe okha ngati anandipeza ndi mlandu nditaimilila pamaso pa Bungwe Lalikulu la Ayuda.* 21 Mawu amodzi okha amene ndinakamba pamene ndinaimilila pakati pawo ndi akuti: ‘Lelo ndikuweluzidwa pamaso panu cifukwa ca ciyembekezo cakuti akufa adzauka’”

22 Koma popeza Felike anali kudziwa bwino nkhani yonse yokhudza Njila imeneyi, anaimitsa mlanduwo ndipo anati: “Mkulu wa asilikali Lusiya akadzabwela, ndidzapeleka cigamulo pa nkhani yanu imeneyi.” 23 Iye analamula mtsogoleli wa asilikali kuti amusungebe m’ndende. Koma anam’patsako ufulu woti azilola anzake kudzamuthandiza pa zofunikila zake.

24 Patapita masiku angapo Felike anafika pamodzi ndi mkazi wake Durusila, amene anali Myuda. Kenako Felike anaitanitsa Paulo ndipo anamumvetsela pamene anali kufotokoza za kukhulupilila Khristu Yesu. 25 Koma pamene Paulo anali kukamba za cilungamo, kudziletsa, komanso ciweluzo cimene cikubwela, Felike anacita mantha moti anati: “Pita coyamba, ndikadzapeza nthawi, ndidzakuitananso.” 26 Pa nthawi imodzimodzi, iye anali kuyembekezela kuti Paulo amupatsa ndalama. Conco anali kumuitanitsa pafupipafupi n’kumakambilana naye. 27 Koma patapita zaka ziwili, Felike analowedwa m’malo ndi Porikiyo Fesito. Ndipo popeza Felike anali kufuna kuti Ayuda azimukonda, anangomusiya m’ndende Paulo.

25 Fesito anafika m’cigawoco n’kuyamba kulamulila. Patapita masiku atatu ananyamuka ku Kaisareya n’kupita ku Yerusalemu. 2 Kumeneko, ansembe aakulu ndi amuna olemekezeka pakati pa Ayuda anamuuza zinthu zoipa zokhudza Paulo. Conco iwo anayamba kucondelela Fesito 3 kuti awakomele mtima n’kuitanitsa Paulo kuti abwele ku Yerusalemu. Koma anakonza zakuti abisalile Paulo panjila kuti amuphe. 4 Koma Fesito anawayankha kuti Paulo ayenela kusungidwila ku Kaisareya, komanso kuti iye watsala pang’ono kubwelela kumeneko. 5 Iye anati, “Amene ali ndi ulamulilo pakati panu, apite nane limodzi kuti akamuimbe mlandu munthu uyu ngati pali cimene analakwa.”

6 Conco iye atakhala nawo masiku osapitilila 8 kapena 10, anabwelela ku Kaisareya. Tsiku lotsatila anakhala pa mpando woweluzila milandu n’kulamula anthu kuti abweletse Paulo kwa iye. 7 Paulo atafika, Ayuda amene anabwela kucokela ku Yerusalemu anaimilila momuzungulila, ndipo anayamba kumuneneza milandu yambili ikuluikulu imene sanathe kupeleka umboni wake.

8 Koma Paulo podziteteza anati: “Ine sindinacimwile Cilamulo ca Ayuda, kapena kacisi, kapenanso Kaisara.” 9 Pofuna kukondweletsa Ayuda, Fesito anafunsa Paulo kuti: “Kodi ungakonde kupita ku Yerusalemu kuti nkhani yako ikaweluzidwile kumeneko pamaso panga?” 10 Koma Paulo anayankha kuti: “Ine ndaimilila patsogolo pa mpando woweluzila milandu wa Kaisara pamene ndiyenela kuweluzidwa. Ayuda sindinawalakwile ciliconse, ndipo inunso mukuona zimenezi. 11 Ngati ndinalakwadi, ndipo ndinacita ciliconse coyenela imfa, sindikukana kufa. Koma ngati anthu awa alibe umboni pa zimene akundinenezazi, palibe munthu amene ali ndi ufulu wondipeleka kwa iwo pofuna kuwasangalatsa. Conco ndikucita apilo kuti ndikaonekele kwa Kaisara!” 12 Ndiyeno Fesito atakambilana ndi bungwe la akulu, anayankha kuti, “Popeza wacita apilo kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.”

13 Patapita masiku angapo, Mfumu Agiripa ndi Berenike anafika ku Kaisareya kudzaona Fesito. 14 Popeza iwo anakhala kumeneko kwa masiku ndithu, Fesito anafotokozela mfumuyo nkhani ya Paulo. Anati:

“Pali munthu wina amene Felike anamusiya m’ndende. 15 Ndipo pamene ndinali ku Yerusalemu, ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda anandiuza zoipa zokhudza munthuyu. Ndipo iwo anapempha kuti iye alandile ciweluzo cakuti aphedwe. 16 Koma ine ndinawayankha kuti Aroma sapeleka munthu kwa omuneneza pofuna kuwakondweletsa munthuyo asanakumane ndi omunenezawo pamasom’pamaso kuti adziteteze pa mlanduwo. 17 Conco atafika kuno sindinacedwe. Tsiku lotsatila ndinakhala pa mpando woweluzila milandu n’kulamula kuti munthuyo amubweletse kwa ine. 18 Omunenezawo ataimilila n’kuyamba kufotokoza, sananene zoipa zilizonse zimene ndinali kuganiza kuti munthuyu anacita. 19 Iwo anangotsutsana naye pa nkhani yokhudza mmene amalambilila Mulungu,* komanso za munthu wina dzina lake Yesu amene anafa. Koma Paulo amanenabe motsimikiza kuti ali moyo. 20 Nditalephela kupeza njila ya mmene ndingathetsele mkangano wa nkhani zimenezi, ndinamufunsa ngati angakonde kuti apite ku Yerusalemu kuti akaweluzidwile kumeneko. 21 Koma Paulo atapempha kuti timusungebe m’ndende kuti cigamulo cikapelekedwe ndi Mfumu yaikulu, ndinalamula kuti asungidwebe kufikila nditamutumiza kwa Kaisara.”

22 Ndiyeno Agiripa anauza Fesito kuti: “Ndingakonde kuti ndimve ndekha pamene munthuyu akulankhula.” Iye anati: “Mudzamumvetsela mawa.” 23 Conco tsiku lotsatila, Agiripa ndi Berenike anabwela ndi ulemelelo waukulu n’kulowa m’bwalo limene munali anthu pamodzi ndi akuluakulu a asilikali komanso anthu ochuka a mu mzindamo. Ndipo Fesito atalamula kuti Paulo abwele kwa iye, anamubweletsa. 24 Kenako Fesito anakamba kuti: “Mfumu Agiripa ndi nonsenu amene muli nafe pano, munthu uyu amene mukumuona ndi amene Ayuda onse ku Yerusalemu ndi kuno komwe, anandipempha kuti sakuyenelelanso kukhalabe ndi moyo, ndipo iwo anali kunena izi mofuula. 25 Koma ndinaona kuti sanalakwe ciliconse kuti ayenelele kuphedwa. Conco munthuyu atapempha kuti akaonekele kwa Mfumu yaikulu, ndinaganiza zomutumiza. 26 Koma ndilibe mfundo iliyonse yomveka imene ndingalembele Mbuye wanga yokhudza munthuyu. Conco ndamubweletsa kwa nonsenu, makamaka kwa inu Mfumu Agiripa, kuti akafunsidwa mafunso ndipeze colemba. 27 Cifukwa ndikuona kuti si canzelu kutumiza mkaidi, koma osachula milandu yake.”

26 Agiripa anauza Paulo kuti: “Ungalankhule mbali yako kuti udziteteze.” Ndiyeno Paulo anatambasula dzanja lake n’kuyamba kulankhula modziteteza kuti:

2 “Inu Mfumu Agiripa, ine ndine wokondwa kuti lelo ndidziteteza pa maso panu, pa zinthu zonse zimene Ayuda akundineneza. 3 Makamaka cifukwa cakuti ndinu katswili pa miyambo yonse komanso pa zimene Ayuda amakangana. Cotelo, ndikukupemphani kuti mundimvetsele moleza mtima.

4 “Ndithudi, umoyo umene ndakhala kuyambila ndili mnyamata, pakati pa anthu a mtundu wanga ndiponso mu Yerusalemu, ndi wodziwika bwino kwa Ayuda onse 5 amene akhala akundidziwa kwa nthawi yaitali. Ngati afuna angandicitile umboni, kuti ndinalidi Mfarisi wa m’gulu lokhwimitsa zinthu kwambili pa kulambila kwathu. 6 Koma cifukwa ca ciyembekezo ca zimene Mulungu analonjeza makolo athu akale ndikuimbidwa mlandu. 7 Mafuko athu 12 nawonso akuyembekezela kuona kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli mwa kucita utumiki wopatulika modzipeleka usana ndi usiku. Inu Mfumu, Ayuda akundiimba mlandu cifukwa ca ciyembekezo cimeneci.

8 “N’cifukwa ciyani mukuona* kuti n’zosatheka Mulungu kuukitsa akufa? 9 Ine ndinali wotsimikiza mtima kuti ndiyenela kucita zambili zotsutsana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti. 10 Izi n’zimene ndinacitadi ku Yerusalemu. Ndipo ndinatsekela m’ndende oyela ambili cifukwa ndinapatsidwa mphamvu ndi ansembe aakulu. Akaweluzidwa kuti aphedwe, ine ndinalikuponya voti yovomeleza. 11 Nthawi zambili ndinali kuwapatsa cilango m’masunagoge onse pofuna kuwakakamiza kuti ataye cikhulupililo cawo. Popeza ndinali nditawakwiyila kwambili, ndinafika ngakhale powazunza m’mizinda yakutali.

12 “Ndili mkati mocita zimenezi, ndinanyamuka ulendo wopita ku Damasiko, nditapatsidwa mphamvu komanso cilolezo ndi ansembe aakulu. 13 Dzuwa lili paliwombo, kuwala kwakukulu koposa kuwala kwa dzuwa kunandiunika kucokela kumwamba, kunandizungulila ndipo kunazungulilanso anthu amene ndinali nawo pa ulendowo. 14 Ndiyeno tonse titagwa pansi, ndinamva mawu m’Ciheberi ondiuza kuti: ‘Saulo! Saulo! n’cifukwa ciyani ukundizunza? Ukudzivulaza wekha ngati nyama imene ikumenya zisonga zotokosela.’* 15 Koma ine ndinati: ‘Ndinu ndani Ambuye?’ Ndipo Ambuyewo anayankha kuti: ‘Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza. 16 Komabe, uka uimilile. Ndiye cifukwa cake ndaonekela kwa iwe kuti ndikusankhe kukhala mtumiki wanga, ndiponso ukhale mboni ya zinthu zimene waona komanso zinthu zimene ndidzakuonetsa zokhudza ine. 17 Ndipo ndidzakupulumutsa kwa anthu awa komanso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutumizako, 18 kuti ukawatsegule maso kuwacotsa mu mdima n’kuwapititsa kowala, ndiponso kuwacotsa m’manja mwa Satana n’kuwapititsa kwa Mulungu. Ukacite zimenezi kuti macimo awo akhululukidwe, komanso kuti akalandile colowa pamodzi ndi oyeletsedwa cifukwa condikhulupilila.’

19 “Conco inu Mfumu Agiripa, ine ndinamvela masomphenya akumwambawo. 20 Kuyambila kwa anthu a ku Damasiko, ku Yerusalemu, ndiponso m’dziko lonse la Yudeya kuphatikizapo anthu a mitundu ina, ndinali kuwauza uthenga wakuti ayenela kulapa ndi kubwelela kwa Mulungu mwa kucita nchito zoonetsa kulapa. 21 Ici ndico cifukwa cimene Ayuda anandigwilila m’kacisi n’kumafuna kundipha. 22 Koma cifukwa ndaona Mulungu akundithandiza, ine ndapitiliza kucitila umboni mpaka lelo kwa anthu otsika ndiponso ochuka. Sindikunena ciliconse kupatulapo zimene aneneli komanso Mose ananena kuti zidzacitika. 23 Zakuti Khristu adzavutika, ndipo monga woyamba kuukitsidwa kwa akufa, adzalalikila kwa anthu awa komanso kwa a mitundu ina za kuwala.”

24 Pamene Paulo anali kulankhula zinthu zimenezi podziteteza, Fesito analankhula mokweza mawu kuti: “Iwe Paulo, wacita misala eti! Kuphunzila kwambili kwakufunthitsa!” 25 Koma Paulo anayankha kuti: “Inu Wolemekezeka a Fesito, ine sindinacite misala, koma ndikulankhula mawu a coonadi ndipo ndili bwinobwino. 26 Pakuti mfumu imene ndikulankhula nayo momasuka ikudziwa bwino zinthu zimenezi. Ine ndine wotsimikiza kuti palibe ngakhale cimodzi mwa zinthu zimenezi cimene sakucidziwa, cifukwa palibe ciliconse cimene cinacitika mobisa. 27 Kodi inu, Mfumu Agiripa, mumakhulupilila zimene aneneli analemba? Ine ndikudziwa kuti mumakhulupilila.” 28 Koma Agiripa anauza Paulo kuti: “M’kanthawi kocepa ukhoza kundikopa kuti ndikhale Mkhristu.” 29 Paulo atamva izi anati: “Pemphelo langa kwa Mulungu ndi lakuti, kaya m’kanthawi kocepa kapena kwa nthawi yaitali, onse amene akundimvetsela lelo osati inu nokha, akhale ngati ine kupatulapo maunyolo okhawa.”

30 Ndiyeno mfumuyo, bwanamkubwa, komanso Berenike ndi anthu omwe anakhala nawo pamodzi anaimilila. 31 Koma pamene anali kucoka, iwo anayamba kukambilana kuti: “Munthu uyu sanacite ciliconse coyenela kumuphela kapena com’mangila.” 32 Ndiyeno Agiripa anauza Fesito kuti: “Munthu uyu akanapanda kucita apilo kwa Kaisara, akanamasulidwa.”

27 Tsopano ulendo wathu wa pamadzi wopita ku Italy utatsimikizika, Paulo ndi akaidi ena anapelekedwa m’manja mwa mtsogoleli wa asilikali dzina lake Yuliyo, wa m’gulu la asilikali a Augusito. 2 Tinakwela ngalawa ya ku Adiramutiyo imene inali itatsala pang’ono kunyamuka ulendo wopita ku madoko a m’mbali mwa nyanja m’cigawo ca Asia. Ndiyeno tinanyamuka pamodzi ndi Arisitako Mmakedoniya wa ku Tesalonika. 3 Tsiku lotsatila tinakafika ku Sidoni, ndipo Yuliyo anacita zinthu mokoma mtima kwa Paulo moti anamulola kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalile.

4 Titapitiliza ulendo wa panyanja kucokela kumeneko, tinayenda m’mbali mwa cisumbu ca Kupuro cimene cinali kutichingila ku mphepo imene inali kuwomba kucokela kumene tinali kupita. 5 Tinayenda panyanja molambalala kupitila ca ku Kilikiya ndi Pamfuliya, ndipo tinakafika pa doko la Mura ku Lukiya. 6 Kumeneko, mtsogoleli wa asilikali anapeza ngalawa ya ku Alekizandiriya yomwe inali kupita ku Italy, ndipo anatiuza kuti tikwele mmenemo. 7 Titayenda pang’onopang’ono kwa masiku angapo tinafika ku Kinido, koma movutikila. Cifukwa ca mphepo imene inali kuwomba kucokela kutsogolo, tinapitila ku Salimone kuti cisumbu ca Kerete cititeteze ku mphepoyo. 8 Titayenda movutikila m’mbali mwa cisumbu cimeneci, tinafika pamalo ena ochedwa Madoko Okoma, amene anali pafupi ndi mzinda wa Laseya.

9 Tsopano panali patapita kale nthawi yaitali, ndipo kuyenda panyanja kunali koopsa cifukwa ngakhale nthawi ya kusala kudya kwa Tsiku la Mwambo Wophimba Macimo* linali litadutsa kale. Conco Paulo anapeleka malangizo. 10 Iye anawauza kuti: “Anthu inu, ndikuona kuti ulendowu tikauyamba palipano utiwonongetsa zambili. Utiwonongetsa katundu, ngalawa, ngakhalenso miyoyo yathu.” 11 Koma mtsogoleli wa asilikali anamvela woyendetsa ngalawa ndi mwini ngalawayo m’malo momvela zimene Paulo anakamba. 12 Popeza kuti dokolo silinali bwino kukhalapo m’nyengo yozizila, ambili anakamba kuti zingakhale bwino atacokako. Iwo anali kufuna kuona ngati zingatheke kukakhala ku Finikesi m’nyengo yozizila. Finikesi linali doko la ku Kerete lopenya kumpoto cakum’mawa, komanso kum’mwela cakum’mawa.

13 Mphepo yakum’mwela itayamba kuwomba pang’onopang’ono, iwo anaganiza kuti colinga cawo cidzatheka. Conco anakweza nangula nʼkuyamba kuyenda mʼmbali mwa cisumbu ca Kerete. 14 Koma posapita nthawi, namondwe wochedwa Yulakilo* anayamba kuwomba ngalawayo. 15 Pomwe ngalawayo inali kuwombedwa ndi mphepo yamphamvu, sitinathe kuiwongolela kuti iziyenda mopenyana ndi mphepoyo. Conco tinagonja ndipo tinatengedwa nayo. 16 Ndiyeno tinayenda mʼmbali mwa cisumbu cina cacingʼono cochedwa Kauda cimene cinali kutiteteza ku mphepoyo. Koma tinavutika kwambili kuti titeteze bwato* laling’ono limene ngalawayo inali kukoka. 17 Koma atakokela bwatolo mʼngalawa, anayamba kumanga ngalawayo ndi zomangila kuti ilimbe. Poopa kuti ngalawayo ingatitimile mu mcenga ku Suriti, iwo anatsitsa nthambo zomangila cinsalu ca ngalawa moti inali kukankhidwa ndi mphepo. 18 Cifukwa cakuti tinali kukankhidwa ndi cimphepo camphamvu, tsiku lotsatila anthu anayamba kutaya katundu kuti ngalawa ipepuke. 19 Tsiku lacitatu, anataya nthambo zokwezela cinsalu ca ngalawayo.

20 Titaona kuti dzuwa komanso nyenyezi sizinaonekele kwa masiku ambili, ndipo namondwe uja anali kutikankha mwamphamvu, tinayamba kukayikila ngati tipulumuka. 21 Anthu aja atakhala nthawi yaitali osadya kalikonse, Paulo anaimilila pakati pawo n’kukamba kuti: “Anthu inu mukanamvela malangizo anga akuti tisanyamuke ulendo kucoka ku Kerete, sitikanavutika conci komanso sitikanawonongetsa katundu. 22 Ngakhale n’telo, ndikukulimbikitsani kuti musataye mtima cifukwa palibe amene adzafa, koma ngalawa yokhayi ndi imene iwonongeke. 23 Lelo usiku, mngelo wa Mulungu wanga amene ndikumucitila utumiki wopatulika, anaimilila pafupi ndi ine. 24 Iye wandiuza kuti: ‘Usaope Paulo. Uyenela kukaima pamaso pa Kaisara. Ndipo dziwa kuti Mulungu adzapulumutsa anthu onse amene uli nawo pa ulendowu cifukwa ca iwe.’ 25 Conco limbani mtima anthu inu, cifukwa ine ndikhulupilila kuti zonse zicitika mmene Mulungu wandiuzila. 26 Komabe, ngalawa yathuyi idzapasuka pafupi ndi cisumbu cinacake.”

27 Pa usiku wa nambala 14, mphepo inali kutikankhila uku ndi uku panyanja ya Adiriya. Kenako pakati pa usiku, oyendetsa ngalawa anayamba kuganiza kuti akuyandikila kumtunda. 28 Iwo anapima kuzama kwa nyanja nʼkupeza kuti ndi mamita 36. Atayendako pangʼono anapimanso kuzama kwake nʼkupeza kuti ndi mamita 27. 29 Poopa kuti tidzagunda miyala, anatsitsa anangula anayi kumbuyo kwa ngalawayo, ndipo anali kungolakalaka kuti kuce. 30 Koma oyendetsa ngalawayo anali kufuna kuthawamo. Conco iwo anayamba kutsitsila bwato laling’ono lija panyanja ponamizila kuti akufuna kutsitsa anangula amene anali kutsogolo kwa ngalawayo. 31 Conco Paulo anauza mtsogoleli wa asilikali ndi asilikaliwo kuti: “Ngati anthu awa acoke mʼngalawa ino, simupulumuka.” 32 Kenako asilikali aja anadula nthambo za bwatolo nʼkulileka kuti lipite.

33 Kutatsala pangʼono kuca, Paulo analimbikitsa anthu onsewo kuti adye cakudya. Anati: “Lelo ndi tsiku la 14 kucokela pamene munayamba kuyembekezela muli ndi nkhawa, ndipo simunadye kalikonse. 34 Conco, ndikukulimbikitsani kuti mudye kuti mukhalebe ndi moyo. Pakuti ngakhale tsitsi limodzi la m’mutu mwanu siliwonongeka.” 35 Atakamba izi, anatenga mkate n’kuyamika Mulungu pamaso pa onse. Kenako anaunyemanyema n’kuyamba kudya. 36 Conco onse analimba mtima n’kuyamba kudya. 37 Tonse pamodzi tinalimo anthu 276 m’ngalawamo. 38 Atadya n’kukhuta, anataila tiligu panyanja kuti ngalawayo ipepuke.

39 Kutaca, sanadziwe kuti ali kuti, koma anaona gombe linalake lamchenga ndipo anali ofunitsitsa kuti ngati angathe akaimitse ngalawayo kumeneko. 40 Conco anadula nthambo za anangula n’kuwaleka kuti agwele m’nyanja. Anamasulanso nthambo zomangila nkhafi zopalasila. Atakweza m’mwamba nsalu yakutsogolo kwa ngalawa, anayamba kuyenda molowela ku gombelo. 41 Kenako anagunda cimulu ca mcenga comwe mafunde anali kuciwomba mbali zonse. Mbali ya kutsogolo ya ngalawayo inajomba* mu mcengawo osasunthika, ndipo mafunde amphamvu anayamba kuwomba kumbuyo kwa ngalawayo n’kuyamba kuipasula zidutswazidutswa. 42 Zitatelo, asilikali anaganiza zopha akaidi kuti pasapezeke wina aliyense wonyaya* n’kuthawa. 43 Koma mtsogoleli wa asilikali anali kufunitsitsa kuti Paulo akafike naye bwinobwino, conco anawaletsa kucita zimene anali kufunazo. Ndiyeno analamula kuti amene angathe kunyaya alumphile m’nyanja kuti akhale woyamba kukafika kumtunda. 44 Ndipo ena onse awatsatila m’mbuyo. Ena anakwela pa matabwa, ndipo ena pa zidutswa za ngalawayo. Conco onse anafika bwinobwino ku mtunda.

28 Titapulumuka, tinamva kuti cisumbuco cimachedwa Melita. 2 Ndipo anthu olankhula cinenelo cacilendo* anationetsa kukoma mtima kwapadela. Iwo anatisonkhela moto ndi kutilandila tonse mokoma mtima cifukwa kunali kugwa mvula, ndiponso kunali kozizila. 3 Koma Paulo atatenga nkhuni n’kuziponya pamoto, panatuluka njoka yamphili cifukwa ca kutentha kwa motowo, ndipo inamuluma n’kukangamila kudzanja lake. 4 Anthu olankhula cinenelo cacilendowo, ataona kuti njoka yapoizoni ikulendewela ku dzanja lake anayamba kuuzana kuti: “Ndithu munthu uyu ndi wopha anthu, ndipo ngakhale kuti anayenda panyanja kudzafika kuno ali bwinobwino, Cilungamo* sicinalole kuti akhalebe ndi moyo.” 5 Koma iye anangokutumulila njokayo pa moto ndipo sanavulazidwe. 6 Koma iwo anali kuyembekezela kuti atupa kapena kugwa mwadzidzidzi n’kufa. Atayembekezela kwa nthawi yaitali n’kuona kuti palibe coipa ciliconse cimene cikumucitikila, anasintha maganizo awo n’kuyamba kunena kuti iye ndi mulungu.

7 Tsopano pafupi ndi malowa panali minda ya woyangʼanila cisumbuco, dzina lake Papuliyo. Iye anatilandila bwino kwambili ndipo anaticeleza kwa masiku atatu. 8 Koma atate ake Papuliyo, anali gone cifukwa codwala malungo* komanso m’mimba mwakamwazi. Conco Paulo anapita kukalowa mmene munali bambowo n’kuwapemphelela, ndipo anaika manja ake pa iwo n’kuwacilitsa. 9 Izi zitacitika, anthu ena onse odwala okhala pa cisumbuco, nawonso anayamba kubwela kwa iye ndipo anawacilitsa. 10 Komanso iwo anatilemekeza potipatsa mphatso zambili, ndipo pamene tinali kunyamuka anatipatsa zonse zimene tinali kufunikila.

11 Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pa ngalawa yokhala ndi cifanizilo ca “Ana a Zeu.” Ngalawayo inali ya ku Alekizandiriya, ndipo inaima pa cisumbupo poyembekezela kuti nyengo yozizila ithe. 12 Kenako tinafika padoko lina ku Surakusa, ndipo tinakhalapo masiku atatu. 13 Titacoka kumeneko, tinayenda mpaka kukafika ku Regio. Pambuyo pa tsiku limodzi, kunayamba kuwomba mphepo ya kum’mwela ndipo tinafika ku Potiyolo pa tsiku laciwili. 14 Kumeneko tinapeza abale, ndipo anaticondelela kuti tikhale nawo masiku 7. Pambuyo pake tinapitiliza ulendo wathu wa ku Roma. 15 Abale a kumeneko atamva za ife, anayenda mpaka kudzafika ku Msika wa Apiyo ndi ku Nyumba Zitatu za Alendo kudzaticingamila. Paulo atawaona, anathokoza Mulungu ndipo analimba mtima. 16 Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kumakhala yekha ndi msilikali womulonda.

17 Pambuyo pa masiku atatu, Paulo anaitanitsa akuluakulu a Ayuda. Atasonkhana pamodzi, iye anawauza kuti: “Amuna inu, abale, ngakhale kuti sindinacite ciliconse cotsutsana ndi anthu, kapena miyambo ya makolo athu akale, ndinapelekedwa m’manja mwa Aroma monga mkaidi kucokela ku Yerusalemu. 18 Ndipo atafufuza, anafuna kundimasula cifukwa sanandipeze ndi mlandu ulionse woyenela cilango ca imfa. 19 Koma Ayuda atakana ndinakakamizika kucita apilo kwa Kaisara. Koma osati cifukwa cakuti ndinali kufuna kudzaneneza mtundu wanga ayi. 20 N’cifukwa cake ndinapempha kudzaonana nanu n’kulankhula nanu, pakuti ndamangidwa unyolowu cifukwa ca ciyembekezo cimene Aisiraeli ali naco.” 21 Iwo anamuyankha kuti: “Ife sitinalandilepo makalata alionse okamba za iwe kucokela ku Yudeya. Palibenso m’bale aliyense wocokela kumeneko amene watiuza kapena kunena ciliconse coipa cokhudza iwe. 22 Koma tikuona kuti ndibwino titamva maganizo ako, cifukwa kukamba zoona, ife tidziwa kuti gulu lampatuko limeneli amalinenela zoipa kulikonse.”

23 Conco iwo anakonza tsiku loti akakumane naye, ndipo anabwela ambili kumene iye anali kukhala. Conco kuyambila m’mawa mpaka madzulo, iye anawafotokozela nkhaniyo, ndipo anacitila umboni mokwanila za Ufumu wa Mulungu. Anawalimbikitsa kukhulupilila Yesu mwa kugwilitsa mfundo zocokela m’Cilamulo ca Mose ndi zimene aneneli analemba. 24 Ena anayamba kukhulupilila zimene iye ananena, koma ena sanazikhulupilile. 25 Conco, popeza anali kutsutsana, anayamba kucoka. Koma Paulo ananena mawu awa othela:

“Mzimu woyela unakamba zoona kwa makolo anu kudzela mwa mneneli Yesaya 26 kuti, ‘Pita kwa anthu awa ndipo ukawauze kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma simudzamvetsa tanthauzo lake. Kuona mudzaona ndithu, koma simudzazindikila zimene mukuona. 27 Pakuti anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi matu awo, koma osacitapo kanthu, komanso atseka maso awo. Acita zimenezi kuti asaone ndi maso awo, komanso kuti asamve ndi matu awo. Ndiponso kuti mitima yawo isamvetse zinthu n’kutembenuka kuti ine ndiwacilitse.”’ 28 Conco dziwani kuti cipulumutso cimeneci cocokela kwa Mulungu catumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo mosakayikila, iwo adzamvetsela.” 29* ——

30 Conco Paulo anakhalabe kumeneko kwa zaka ziwili zathunthu m’nyumba imene anali kucita lendi, ndipo anthu onse amene anali kubwela kudzamuona anali kuwalandila mokoma mtima. 31 Iye anali kuwalalikila za Ufumu wa Mulungu ndi kuwaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu, ali ndi ufulu wonse wa kulankhula* popanda coletsa.

Kapena kuti, “mpaka kumadela a kutali kwambili.”

M’cinenelo coyambilila, “Mtunda wa pa tsiku la Sabata.” Uyu ndi mtunda umene Myuda anali kuloledwa kuyenda pa Sabata.

Kapena kuti, “Khamu lonse linali pafupifupi anthu 120.”

Kapena kuti, “anaphulika pakati.”

Kapena kuti, “malilime osiyanasiyana.”

Kapena kuti, “m’cinenelo cobadwa naco?”

M’cinenelo coyambilila, “ola lacitatu.”

Kapena kuti, “zizindikilo.”

Ma Baibo ena amati, “nthambo.”

Kapena kuti, “pamaso panga.”

Kapena kuti, “Hade,” kutanthauza manda a anthu onse.

Kapena kuti, “nikakhala pamaso panu.”

Kapena kuti, “Hade,” kutanthauza manda a anthu onse.

Kapena kuti, “watipungulila.”

M’cinenelo coyambilila, “anawalasa mtima.”

Kapena kuti, “kugawana zinthu.”

M’cinenelo coyambilila, “ola la 9.”

Kutanthauza tumafupa tolumikiza mapazi ndi miyendo.

M’cinenelo coyambilila, “kucokela pa nkhope ya Yehova.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

Kapena kuti, “anawamanga.”

M’cinenelo coyambilila, “mutu wakona.”

Kutanthauza kuti, “sanaphunzile ku masukulu a Arabi.” Satanthauza kusadziŵa kulemba na kuŵelenga.

M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”

Kapena kuti, “cizindikilo.”

Kapena kuti, “Khristu wake.”

Kapena kuti, “atapemphela mocokela pansi pamtima.”

M’cinenelo coyambilila, “anali ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.”

Kapena kuti, “n’kumanga.”

M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”

Kapena kuti, “analasidwa mtima.”

Kapena kuti, “n’kuwamenya.”

M’cinenelo coyambilila, “zosakondweletsa.”

M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “kuwakhaulitsa.”

Ma Baibo ena amati, “Isaki anacitanso cimodzimodzi ndi.”

Kapena kuti, “kukayendela.”

M’cinenelo coyambilila, “gulu la nkhondo la kumwamba.”

Kapena kuti, “analasidwa mtima.”

Kapena kuti, “anagona tulo ta imfa.”

Ma Baibo ena amati, “mzinda wina wake wa ku.”

Kapena kuti, “zozizwitsa.”

M’cinenelo coyambilila, “ndulu yowawa.”

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yodalilika ya makedzana ya Cigiriki.

Mawu akuti Njilayo akutanthauza, “umoyo wa Cikhristu komanso zimene Akhristu amaphunzila.”

M’cinenelo coyambilila, “kuti apite nawo ali omanga.”

Dzina lakuti “Dorika” ndi la Cigiriki, ndipo lakuti “Tabita” ndi la Ciaramu. Maina onsewa amatanthauza, “Mbawala.”

Kapena kuti, “zovala za kunja.”

Anali kuyang’anila asilikali 100.

Gulu la asilikali a Ciroma amene anali kukhala 600.

M’cinenelo coyambilila, “ola la 9.”

M’cinenelo coyambilila, “ola la 6.”

M’cinenelo coyambilila, “ola la 9.”

Kapena kuti, “Mulungu anaipungulilanso.”

M’cinenelo coyambilila, “malilime.”

Kapena kuti, “kulimbana naye.”

Kapena kuti, “nditsekeleze njila ya Mulungu.”

M’cinenelo coyambilila, “anakhala cete.”

Kapena kuti, “kucita utumiki wothandiza anthu.”

Kapena kuti, “anamudwalitsa.”

Kapena kuti, “kutumikila Yehova poyela.”

Kapena kuti, “kuwaika manja.”

Kapena kuti, “amene anali kuwathandiza.”

“Bwanamkubwa woyang’anila cigawo.”

Kapena kuti, “manda acikumbutso.”

Kapena kuti, “zakutsutsanako.”

Kapena kuti, “msasa; nyumba.”

Kapena kuti, “maganizo anga.”

Kapena kuti, “zopelekedwa ku mafano.”

M’Cigiriki, “pornei’a.” Onani matanthauzo a mawu ena.

Kapena kuti, “nyama imene yaphedwa popanda kukhetsa magazi ake.”

Kapena kuti, “nyama imene yaphedwa popanda kukhetsa magazi ake.”

M’Cigiriki, “pornei’a.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mukhale ndi thanzi labwino.”

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yodalilika ya makedzana ya Cigiriki.

Kapena kuti, “popanda kutizenga mlandu.”

Kapena kuti, “ayambitsa mavuto.”

Kapena kuti, “ndalama za belo.”

Kapena kuti, “alendo opita kumeneko.”

Kapena kuti, “ndinu opembedza kwambili.”

Kutanthauza ku sunagoge.

Kutanthauza bwanamkubwa wa cigawo ca Roma.

Zioneka kuti anapita ku Yerusalemu.

Kapena kuti, “anaphunzitsidwa ndi mawu apakamwa.”

Kapena kuti, “anaumitsa mitima yawo, ndipo sanakhulupilile.”

Kapena kuti, “maepuloni.”

Bwanamkubwa wa cigawo ca Roma.

M’cinenelo coyambilila, “ananyemanyema mkate n’kuyamba kudya.”

Kapena kuti, “molimbikitsidwa.”

Kapena kuti, “zolinga zonse za Mulungu.”

Kapena kuti, “kumupsompsona.”

Kapena kuti, “kumbali imene kunali doko.”

M’cinenelo coyambilila, “anamwali.”

M’cinenelo coyambilila, “tinakhala cete.”

Kapena kuti, “nyama imene yaphedwa popanda kukhetsa magazi ake.”

M’Cigiriki, “pornei’a.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

M’cinenelo coyambilila, “Pamene magazi a mboni yanu Stefano anali kukhetsedwa.”

M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”

M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”

Kapena kuti, “amalengeza poyela.”

Kapena kuti, “mahosi.”

M’cinenelo coyambilila, “pafupifupi ola lacitatu.”

Kapena kuti, “Loya.”

Kapena kuti, “ndi wovutitsa kwambili.” M’cinenelo coyambilila, “mlili.”

Mawu a pa vesi iyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yodalilika ya makedzana ya Cigiriki

M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”

Kapena kuti, “yokhudza cipembedzo cawo.”

M’cinenelo coyambilila, “mukuweluza.”

Cisonga cotokosela, ndi ndodo yosongoka imene anali kutokosela nyama za pa joko kuti ziziyenda mofulumila.

Nthawiyi inali mwezi wa Tishiri, pomwe mvula imayamba komanso nyanja imawinduka

Imeneyi ndi mphepo yocokela kumpoto cakum’mawa.

Bwatoli linali lopulumukilamo.

Kapena kuti, “inatitimila.”

Ena amati, “kusambila.”

Kapena kuti, “anthu okhala kumeneko.”

M’Cigiriki Di’ke, mawuwa mwina akukamba za mulungu wamkazi wobwezela kuti pacitike cilungamo. Kapenanso anangowagwilitsa nchito potanthauza cilungamo.

M’cinenelo coyambilila, “kutentha thupi.”

Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

Kapena kuti, “molimba mtima kwambili.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani