LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • nwt 1 Akorinto 1:1-16:24
  • 1 Akorinto

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 1 Akorinto
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
1 Akorinto

KALATA YOYAMBA KWA AKORINTO

1 Ine Paulo, woitanidwa kukhala mtumwi wa Khristu Yesu mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu, pamodzi ndi Sositene m’bale wathu, 2 ndikulembela mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto. Inu amene mwayeletsedwa mwa Khristu Yesu, amene mwaitanidwa kuti mukhale oyela pamodzi ndi onse amene ali kulikonse omwe akuitanila pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wao komanso Ambuye wathu.

3 Cisomo ndi mtendele wocokela kwa Mulungu Atate wathu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu zikhale nanu.

4 Nthawi zonse ndimathokoza Mulungu wanga cifukwa ca inu, poona cisomo ca Mulungu cimene anakucitilani kudzela mwa Khristu Yesu. 5 Ndinu wolemela m’zinthu zonse cifukwa cogwilizana naye, ndipo wakuthandizani kukhala ndi luso la kulankhula komanso kudziwa zinthu zonse, 6 cifukwa umboni wonena za Khristu wakhazikika pakati panu. 7 Palibe mphatso imene mukupelewela pamene muyembekezela mwacidwi kubvumbulutsidwa kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 8 Komanso Mulungu adzakulimbitsani mpaka pamapeto, kuti musakhale ndi cifukwa cokunenezani naco m’tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu. 9 Mulungu amene anakuitanani kuti mukhale ogwilizana ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye wathu, ndi wokhulupilika.

10 Tsopano ndikukudandaulilani abale, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzikhala ogwilizana m’zokamba zanu, ndipo pakati panu pasakhale magawano, koma mukhale ogwilizana kwambili pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi. 11 Cifukwa ena a m’banja la Kuloe andiuza za inu, abale anga, kuti pakati panu pali magawano. 12 Ndikutanthauza kuti ena pakati panu amanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena amati, “Ine ndine wa Apolo,” enanso amati, “Ine ndine wa Kefa,”* pamene ena amati, “Ine ndine wa Khristu.” 13 Kodi Khristu ndi wogawikana? Kodi Paulo anapacikidwa pamtengo wozunzikilapo* kuti inu mupulumutsidwe? Kapena kodi munabatizidwa m’dzina la Paulo? 14 Ndikuthokoza Mulungu kuti sindinabatize aliyense wa inu kupatulapo Kirisipo ndi Gayo, 15 moti palibe wina anganene kuti anabatizidwa m’dzina langa. 16 N’zoona kuti ndinabatizanso anthu a m’banja la Sitefana. Koma za enawo, sindikumbukila ngati ndinabatizapo aliyense. 17 Pakuti Khristu sananditume kuti ndizibatiza anthu, koma kuti ndizilengeza uthenga wabwino, osati mwa luso la kulankhula,* kuopela kuti mtengo wozunzikilapo* wa Khristu ungakhale wopanda nchito.

18 Nkhani yokhudza mtengo wozunzikilapowo* ndi cinthu copusa kwa amene akupita ku cionongeko. Koma kwa ife amene tikupulumutsidwa, imeneyi ndi mphamvu ya Mulungu. 19 Pakuti Malemba amati: “Ndidzathetsa nzelu za anthu anzelu, ndipo ndidzakana* kucenjela kwa anthu anzelu.” 20 Kodi munthu wanzelu ali kuti? Mlembi* ali kuti? Katswili wa mtsutso wa nthawi* ino ali kuti? Kodi Mulungu sanapange nzelu za dzikoli kukhala zopusa? 21 Pakuti mwa nzelu zake, Mulungu sanalole kuti anthu a dzikoli agwilitse nchito nzelu zao pomudziwa. M’malomwake, Mulungu anaona kuti ndi bwino kupulumutsa anthu okhulupilila kupitila mu uthenga umene anthu ena amauona kuti ndi wopusa.

22 Ayuda amafuna kuona zizindikilo ndipo Agiriki amafuna-funa nzelu. 23 Koma ife timalalikila za Khristu amene anaphedwa pamtengo wozunzikilapo.* Kwa Ayuda izi n’zopunthwitsa ndipo kwa anthu amitundu ina n’zopusa. 24 Ngakhale n’conco, Ayuda ndi Agiriki amene anaitanidwa, amaona kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzelu ya Mulungu. 25 Cifukwa cinthu ca Mulungu cimene anthu amaciona kuti n’copusa, n’canzelu kuposa anthu. Ndipo cinthu ca Mulungu cimene anthu amaciona kuti n’cofooka, n’camphamvu kuposa anthu.

26 Mukuona abale mmene anakuitanilani, kuti si ambili amene anthu akuwaona kuti ndi anzelu amene anaitanidwa, si ambili amphamvu amene anaitanidwa, si ambili a m’mabanja olemekezeka amene anaitanidwa. 27 Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko kuti acititse manyazi anthu anzelu, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti acititse manyazi zinthu zamphamvu. 28 Mulungu anasankhanso zinthu zonyozeka za dzikoli, komanso zinthu zimene anthu amaziona ngati zopanda pake, zinthu zimene palibe, kuti acititse zinthu zimene zilipo kukhala zopanda mphamvu, 29 n’colinga coti pasapezeke munthu wodzitama pamaso pa Mulungu. 30 Koma inu ndinu wogwilizana ndi Khristu Yesu cifukwa ca Mulunguyo. Yesu ameneyo amationetsa nzelu za Mulungu komanso cilungamo ca Mulungu. Kudzela mwa iye, anthu akhoza kuyeletsedwa, ndipo kudzela mu dipo limenelo, akhoza kumasulidwa, 31 kuti pakhale kugwilizana ndi mmene Malemba amanenela kuti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”

2 Conco abale, pamene ndinabwela kwa inu kudzalengeza za cinsinsi copatulika ca Mulungu, sindinalankhule mokokomeza kapena moonetsa kuti ndili ndi nzelu zodabwitsa. 2 Pakuti pamene ndinali pakati panu, ndinasankha kuti ndisadziwe ciliconse kupatulapo Yesu Khristu amene anaphedwa pamtengo.* 3 Pobwela kwa inu, ndinali wofooka ndipo ndinali kunthunthumila ndi mantha. 4 Ndipo polankhula komanso polalikila, mau anga sanali okopa kapena oonetsa nzelu, koma oonetsa mzimu ndi mphamvu, 5 kuti musamakhulupilile nzelu za anthu koma mphamvu ya Mulungu.

6 Tsopano tikulankhula zokhudza nzelu kwa anthu okhwima kuuzimu, koma osati nzelu za nthawi* ino kapena za olamulila a nthawi ino amene adzawonongedwa. 7 Koma tikulankhula zokhudza nzelu ya Mulungu yomwe ndi nzelu yobisika, imene inaonekela mu cinsinsi copatulika, cimene Mulungu anakonzelatu kale-kale nthawi ino isanafike, kuti tikhale ndi ulemelelo. 8 Palibe wolamulila aliyense wa nthawi* ino amene anali kudziwa nzelu imeneyi, cifukwa akanaidziwa sakanapha Ambuye waulemelelo. 9 Koma malinga ndi mmene Malemba amanenela kuti: “Palibe munthu amene anaonapo, kapena kumva, kapenanso kuganizila zimene Mulungu wakonzela anthu amene amamukonda.” 10 Pakuti Mulungu anatiululila zinthu zimenezi kupitila mwa mzimu wake, cifukwa mzimuwo umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.

11 Kodi ndani amene angadziwe maganizo a munthu wina kupatulapo mwiniwakeyo? Mofananamo, palibe amene akudziwa maganizo a Mulungu, kupatulapo mzimu wa Mulungu. 12 Ife sitinalandile mzimu wa dziko, koma mzimu wocokela kwa Mulungu, kuti tidziwe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima. 13 Timalankhulanso zinthu zimenezi, osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzelu za anthu, koma ndi mau amene mzimu watiphunzitsa, pamene tikufotokoza zinthu zauzimu ndi mau auzimu.

14 Koma munthu wokonda zinthu za m’dziko* sabvomeleza* zinthu za mzimu wa Mulungu, cifukwa amaziona kuti ndi zopusa ndipo sangathe kuzidziwa, cifukwa zimafuna kuzifufuza mwauzimu. 15 Komabe munthu wauzimu amafufuza zinthu zonse, koma iye safufuzidwa ndi munthu aliyense. 16 Nanga “ndani akudziwa maganizo a Yehova kuti amulangize?” Koma ife tili ndi maganizo a Khristu.

3 Conco abale, sindinalankhule nanu ngati anthu auzimu, koma ngati anthu okonda zinthu za mʼdzikoli, ngati makanda mwa Khristu. 2 Ndinakupatsani mkaka, osati cakudya cotafuna, cifukwa munali musanalimbe mokwanila. Ndipo mpaka pano simunalimbebe, 3 pakuti mukuganizabe ngati anthu a m’dzikoli.* Popeza pakati panu pali nsanje ndiponso kukangana, kodi si ndiye kuti ndinu akuthupi, ndipo mukuyenda ngati anthu a m’dzikoli? 4 Ngati wina akunena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” koma wina n’kumati: “Ine ndine wa Apolo,” kodi si ndiye kuti mwangofanana ndi anthu a dziko?

5 Kodi Apolo ndani? Nanga Paulo ndani? Ife ndife cabe atumiki amene tinakuthandizani kukhala okhulupilila, mogwilizana ndi nchito imene Ambuye anapatsa aliyense wa ife. 6 Ine ndinabzala, Apolo anathilila, koma Mulungu ndiye anakulitsa. 7 Conco wofunika kwambili si wobzala kapena wothilila, koma Mulungu amene amakulitsa. 8 Wobzala ndi wothilila amakhala ndi colinga cimodzi,* koma aliyense adzalandila mphoto yake malinga ndi nchito yake. 9 Pakuti ndife anchito anzake a Mulungu. Inu ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa, nyumba ya Mulungu.

10 Mogwilizana ndi cisomo ca Mulungu cimene ndinacitilidwa, ndinayala maziko ngati munthu waluso* pa nchito zomangamanga. Koma amene akumanga pamaziko amenewo ndi munthu wina. Conco aliyense asamale mmene akumangilapo. 11 Cifukwa palibe munthu wina amene angayale maziko ena kupatulapo amene anayalidwa kale, amene ndi Yesu Khristu. 12 Tsopano ngati anthu akumanga pamazikowo ndi golide, siliva, miyala yamtengo wapatali, mitengo, udzu kapena mapesi, 13 nchito ya aliyense idzadziwika kuti ndi yotani.* Tsiku lina nchitoyo idzadziwika mmene ilili, cifukwa moto ndi umene udzaionetsa poyela. Ndipo motowo udzaonetsa kuti nchito ya munthu aliyense ndi yotani. 14 Ngati zimene munthu wamanga pamazikowo zidzakhalapobe, munthuyo adzalandila mphoto. 15 Ngati zimene wamangazo zidzapsya ndi moto, ndiye kuti zake zatayika, koma iyeyo adzapulumuka. Komabe zidzakhala monga wapulumuka pamoto.

16 Kodi inu simudziwa kuti ndinu kacisi wa Mulungu ndipo mzimu wa Mulungu ukukhala mwa inu? 17 Munthu aliyense ngati waononga kacisi wa Mulungu, Mulungu adzamuononga munthuyo, pakuti Mulungu ndi woyela, ndipo inu ndinu kacisiyo.

18 Munthu asamadzinamize. Ngati wina wa inu akuganiza kuti ndi wanzelu nthawi* ino, akhale wopusa kuti akhale wanzelu. 19 Kwa Mulungu, nzelu za m’dzikoli n’zopusa, cifukwa Malemba amati: “Iye amacititsa kuti anthu anzelu agwele m’misampha yao.” 20 Amanenanso kuti: “Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu anzelu ndi opanda pake.” 21 Conco pasakhale wina wodzitama cifukwa ca anthu, popeza zinthu zonse ndi zanu, 22 kaya Paulo, Apolo, Kefa,* dziko, moyo, imfa, zinthu zimene zilipo kapena zimene zikubwela, zonse ndi zanu. 23 Inu ndinu a Khristu ndipo Khristu ndi wa Mulungu.

4 Anthu aziona kuti ndife atumiki a Khristu komanso atumiki a zinsinsi zopatulika za Mulungu. 2 Pa nkhaniyi, cofunika kwa atumiki ndi kukhala okhulupilika. 3 Kwa ine, kuweluzidwa ndi inu kapena khoti iliyonse ya anthu ndi kosafunika kwenikweni. Ndipo ngakhale ine sindidziweluza ndekha. 4 Cikumbumtima canga sicikunditsutsa pa nkhani iliyonse. Koma izi sizitanthauza kuti ndine wolungama, cifukwa amene amandifufuza ndi Yehova. 5 Conco, musamaweluze kalikonse nthawi isanakwane mpaka Ambuye adzabwele. Iye adzacititsa kuti zinsinsi zamumdima zionekele, komanso adzaonetsa poyela zolinga zimene zili mumtima. Ndiyeno Mulungu adzayamikila aliyense payekha.

6 Tsopano abale, ndanena zimenezi zokhudza ineyo ndi Apolo kuti mumvetse mfundo yake n’colinga cakuti muphunzile kwa ife lamulo ili lakuti: “Musapitilile zinthu zolembedwa.” Sitikufuna kuti aliyense wa inu adzikuze n’kumacita zinthu mokondela. 7 Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana ndi ena n’ndani? Uli ndi ciani cimene sunacite kulandila? Ndiye ngati unacita kulandila zinthuzo, n’cifukwa ciani ukudzitama ngati kuti siunacite kulandila?

8 Kodi mwakhutila kale? Kodi mwalemela kale? Kodi mwayamba kale kulamulila monga mafumu popanda ife? Ndikanakonda kwambili mukanayamba kulamulila ngati mafumu kuti ifenso tizilamulila nanu limodzi ngati mafumu. 9 Ndikuona monga kuti Mulungu waika atumwife kumapeto pacionetselo monga anthu okaphedwa, cifukwa zili ngati tili m’bwalo lamasewela ndipo tikuonetsedwa ku dziko, kwa angelo, ndiponso kwa anthu. 10 Takhala opusa cifukwa ca Khristu, koma inu mwakhala ocenjela mwa Khristu. Ife ndife ofooka, inu ndinu olimba. Inu mukulemekezedwa, koma ife tikunyozedwa. 11 Mpaka pano tikali anjala, aludzu komanso ausiwa.* Tikumenyedwabe, tikusowabe pokhala, 12 ndipo tikugwilabe nchito molimbika ndi manja athu. Akamatinyoza, timawadalitsa, ndipo akamatizunza timapilila moleza mtima. 13 Akamatineneza zoipa, timayankha mofatsa. Takhala monga zinyalala za dziko, ndiponso zonyansa za zinthu zonse mpaka pano.

14 Ndikulemba zinthu izi, osati kuti ndikucititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni monga ana anga okondedwa. 15 Ngakhale mutakhala ndi anthu 10,000 okuyang’anilani mwa Khristu, mulibe atate ambili. Ine ndine tate wanu mwa Khristu Yesu cifukwa cokubweletselani uthenga wabwino. 16 Conco, ndikukulimbikitsani kuti muzitengela citsanzo canga. 17 Ndiye cifukwa cake ndikukutumizilani Timoteyo, pakuti iye ndi mwana wanga wokondedwa, komanso wokhulupilika mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimacitila* zinthu potumikila Khristu Yesu, monga mmene ndikuphunzitsila kulikonse mumpingo uliwonse.

18 Ena akudzikuza ngati kuti sindidzabwela kwanuko. 19 Yehova akalola, ndibwela posacedwa, ndipo sindidzafuna kumva mau ao odzikuza, koma ndidzafuna ndione mphamvu zao. 20 Pakuti Ufumu wa Mulungu si nkhani ya mau, koma mphamvu. 21 Kodi mungakonde ciani? Ndibwele kwa inu ndi mkwapu, kapena ndibwele ndi cikondi komanso mzimu wofatsa?

5 Mbili yamveka kuti pakati panu pakucitika ciwelewele,* ndipo mtundu wa ciweleweleco* ndi woti ngakhale anthu a mitundu ina sacita. Akuti mwamuna wina anatengana ndi mkazi wa atate ake. 2 Kodi inu mukusangalala nazo zimenezi m’malo momva cisoni, kuti munthu amene anacita zimenezi acotsedwe pakati panu? 3 Ngakhale kuti thupi langa silili kumeneko, mwauzimu ndili kumeneko, ndipo ndamuweluza kale munthu amene anacita zimenezi, ngati kuti ndili nanu limodzi. 4 Mukasonkhana m’dzina la Ambuye wathu Yesu, mudziwe kuti mwamzimu komanso m’mphamvu ya Ambuye wathu Yesu ndili nanu limodzi. 5 Conco, m’pelekeni kwa Satana munthu ameneyo kuti thupilo lionongedwe, n’colinga coti mzimuwo ukapulumutsidwe m’tsiku la Ambuye.

6 Kudzitama kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti yisiti wocepa amafufumitsa mtanda wonse? 7 Cotsani yisiti wa kaleyo kuti mukhale mtanda watsopano, popeza ndinu opanda zofufumitsa. Cifukwa Khristu wapelekedwa ngati nkhosa ya nsembe yathu ya Pasika. 8 Conco tiyeni ticite cikondwelelo ca Pasika cimeneci osati ndi yisiti wakale kapena yisiti woimila zoipa ndi ucimo, koma ndi mkate wopanda yisiti woimila kuona mtima ndi coonadi.

9 M’kalata yanga, ndinakulembelani kuti muleke kugwilizana ndi anthu aciwelewele.* 10 Sindikutanthauza kuti muzipewelatu anthu aciwelewele* a m’dzikoli kapenanso adyela, olanda ndi opembedza mafano. Zikanakhala conco ndiye kuti mukanafunika kutuluka m’dzikoli. 11 Koma tsopano ndikukulembelani kuti muleke kugwilizana ndi aliyense wochedwa m’bale amene ndi waciwelewele* kapena wadyela, wopembedza mafano, wolalata,* cidakwa kapenanso wolanda, ngakhale kudya naye munthu woteleyu n’kosayenela. 12 Nanga ndi udindo wanga ngati kuweluza anthu amene ali kunja? Kodi si paja inu mumaweluza anthu amene ali mkati, 13 pamene Mulungu amaweluza amene ali kunja? “M’cotseni munthu woipayo pakati panu.”

6 Wina wa inu akakangana ndi mnzake, kodi amalimba mtima kupita ku khoti kukaonekela pamaso pa anthu osalungama, m’malo mopita kwa oyelawo? 2 Kapena kodi simukudziwa kuti oyelawo adzaweluza dziko? Ngati inu mudzaweluza dziko, kodi simungakwanitse kuweluza milandu yaing’ono kwambili imeneyo? 3 Kodi inu simukudziwa kuti tidzaweluza angelo? Ndiye tingalephele bwanji kuweluza nkhani za mu umoyo uno? 4 Ndiye ngati muli ndi nkhani za mu umoyo uno zofunika kuweluza, kodi anthu amene mpingo sungawadalile ndiwo amene mwapatsa udindo woweluza? 5 Ndikulankhula izi kuti ndikucititseni manyazi. Kodi pakati panu palibe ngakhale mmodzi wanzelu amene angaweluze milandu ya abale ake? 6 Kodi zoona m’bale azipeleka m’bale wake kukhoti kwa anthu osakhulupilila?

7 Kukamba zoona, ngati mumatengelana kukhoti ndiye kuti mwalephela kale. Bwanji osangololela kulakwilidwa? Bwanji osangololela kubeledwa? 8 M’malomwake, inu mumacita zoipa komanso m’mabela ena ndipo m’mabelanso ngakhale abale anu.

9 Kodi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu? Musasoceletsedwe.* Anthu aciwelewele,* olambila mafano, acigololo, amuna amene amalola kugonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo,* 10 akuba, anthu adyela, zidakwa, olalata,* kapena olanda, sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu. 11 Ndipo ena a inu munali otelo, koma mwasambikidwa n’kukhala oyela. Mwayeletsedwa, ndipo mwaonedwa monga olungama m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.

12 Zinthu zonse ndi zololeka kwa ine, koma si zonse zopindulitsa. Zinthu zonse ndi zololeka kwa ine, koma sindidzalola cinthu ciliconse kuti cizindilamulila. 13 Cakudya ndi ca mimba, ndipo mimba ndi ya cakudya, koma Mulungu adzaziononga zonsezi. Thupi ndi la Ambuye, si locitila ciwelewele,* ndipo Ambuye ndiwo amapeleka zofunikila za thupilo. 14 Koma Mulungu anaukitsa Ambuye ndipo adzaukitsanso ife mwa kugwilitsa nchito mphamvu zake.

15 Kodi inu simukudziwa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu? Ndiye kodi nditenge ziwalo za Khristu n’kuzilumikiza kwa hule? Sindingayese! 16 Kodi simukudziwa kuti aliyense wogonana ndi hule amakhala thupi limodzi ndi hulelo? Pakuti Mulungu anati, “Awiliwo adzakhala thupi limodzi.” 17 Koma aliyense wogwilizana ndi Ambuye amakhala naye thupi limodzi mu mzimu. 18 Thawani ciwelewele.* Chimo lililonse limene munthu angacite ndi la kunja kwa thupi lake, koma munthu amene amacita ciwelewele amacimwila thupi lake. 19 Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi kacisi wa mzimu woyela umene uli mwa inu, womwe Mulungu anakupatsani? Ndipo inu ndinu wa Mulungu, 20 popeza munagulidwa pa mtengo wokwela. Yesetsani kulemekeza Mulungu ndi matupi anu mmene mungathele.

7 Tsopano pa nkhani ija imene munandilembela, zingakhale bwino kuti mwamuna asakhudze* mkazi. 2 Koma cifukwa ca kuculuka kwa ciwelewele,* mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wake-wake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wake-wake. 3 Mwamuna azipeleka mangawa kwa mkazi wake,* mkazinso azipeleka mangawa kwa mwamuna wake. 4 Mkazi alibe ulamulilo pathupi lake. Koma amene ali ndi ulamulilo ndi mwamuna wake. Mwamuna nayenso alibe ulamulilo pathupi lake, koma mkazi wake ndi amene ali ndi ulamulilo. 5 Musamakanizane, kupatulapo ngati mwacita kugwilizana kuti muimitse kwa kanthawi kuti mugwilitse nchito nthawiyo kupemphela. Pambuyo pake n’kuyambanso mwa nthawi zonse. Muzitelo kuti Satana asapitilize kukuyesani mukalephela kudziletsa. 6 Ndalankhula izi osati monga lamulo, koma kuti mudziwe zimene zili zololeka. 7 Ndikanakonda amuna onse akanakhala ngati ine. Ngakhale n’telo, munthu wina aliyense ali ndi mphatso imene Mulungu anamupatsa, wina m’njila iyi winanso m’njila ina.

8 Tsopano ndikuuza anthu osakwatila komanso akazi amasiye kuti zingakhale bwino kwa iwo kupitiliza kukhala mmene ine ndilili. 9 Koma ngati sangakwanitse kudziletsa akwatile, cifukwa kukwatila kuli bwino kusiyana n’kumabvutika ndi cilakolako.

10 Kwa anthu okwatila ndikupeleka malangizo awa, osati ine koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna wake. 11 Koma ngati angamusiye, mkaziyo akhalebe wosakwatiwa. Apo ai, abwelelane ndi mwamuna wake. Nayenso mwamuna asasiye mkazi wake.

12 Koma kwa enawo, ineyo osati Ambuye, ndikuwauza kuti: Ngati m’bale ali ndi mkazi wosakhulupilila, ndipo akulola kukhala naye, asamusiye mkaziyo. 13 Komanso ngati mkazi ali ndi mwamuna wosakhulupilila, ndipo akulola kukhala naye, asamusiye mwamunayo. 14 Pakuti mwamuna wosakhulupilila amayeletsedwa cifukwa ca mkazi wake. Ndipo mkazi wosakhulupilila amayeletsedwa cifukwa ca m’baleyo. Apo ai, ana anu akanakhala odetsedwa, koma tsopano ndi oyela. 15 Koma ngati wosakhulupililayo wasankha kucoka,* mulekeni acoke. Zikakhala telo, m’bale kapena mlongo sakhala womangika, koma Mulungu wakuitanani kuti mukhale mwamtendele. 16 Mkaziwe, udziwa bwanji kuti mwina ungapulumutse mwamuna wako? Kapenanso mwamunawe, udziwa bwanji kuti mwina ungapulumutse mkazi wako?

17 Ngakhale n’telo, munthu aliyense akhalebe mmene analili pamene Yehova Mulungu anamuitana. Conco ndikupeleka malangizo awa ku mipingo yonse. 18 Kodi pali mwamuna amene anaitanidwa ali wodulidwa? Akhalebe conco wodulidwa. Kodi pali mwamuna amene anaitanidwa ali wosadulidwa? Ameneyo asadulidwe. 19 Mdulidwe, kapena kukhala wosadulidwa zilibe tanthauzo lililonse. Koma cofunika ndi kusunga malamulo a Mulungu. 20 Munthu aliyense akhalebe mmene analili pomwe anaitanidwa. 21 Kodi unaitanidwa uli kapolo? Zimenezo zisakudetse nkhawa. Koma ngati ungakhale ndi mwai womasuka, ugwilitse nchito mwai umenewo. 22 Munthu aliyense amene anaitanidwa mwa Ambuye ali kapolo ndi mtumiki womasulidwa wa Ambuye. Mofananamo, aliyense amene anaitanidwa ali mfulu ndi kapolo wa Khristu. 23 Munagulidwa pa mtengo wodula, lekani kukhala akapolo a anthu. 24 Abale, munthu aliyense akhalebe mmene analili pomwe anaitanidwa ndi Mulungu.

25 Ponena za amene sanakwatiwepo* kapena kukwatilapo, ndilibe lamulo lililonse la Ambuye. Koma ndikupeleka malingalilo anga ngati munthu amene anacitilidwa cifundo ndi Ambuye kuti ndikhale wokhulupilika. 26 Conco, ndiganiza kuti zingakhale bwino kuti mwamuna akhalebe mmene alili cifukwa ca kubvuta kwa zinthu palipano. 27 Kodi ndiwe womangika kwa mkazi? Leka kufuna-funa njila yomasukila. Kodi ndiwe womasuka kwa mkazi? Leka kufuna-funa mkazi. 28 Koma ngati ungakwatile, sikuti wacimwa ai. Ndipo ngati munthu amene sali pabanja walowa m’banja, munthuyo sanacimwe ai. Komabe amene alowa m’banjawo adzakhala ndi nsautso m’matupi ao. Koma ndikungoyesa kukutetezani.

29 Komanso, ndikukuuzani izi abale: Nthawi yotsalayi yafupika. Kuyambila tsopano, amene ali ndi akazi azikhala ngati amene alibe, 30 ndipo amene akulila azikhala ngati aja amene sakulila, amene akusangalala azikhala ngati amene sakusangalala, ndipo amene amagula zinthu azikhala ngati amene alibe kanthu. 31 Amene akuligwilitsa nchito dzikoli azikhala ngati amene sakuligwilitsa nchito mokwanila cifukwa zocitika pa dzikoli zikusintha. 32 Kukamba zoona, ndikufuna kuti mukhale opanda nkhawa. Mwamuna wosakwatila amadela nkhawa za Ambuye, mmene angakhalile woyanjidwa ndi Ambuye. 33 Koma mwamuna wokwatila amadela nkhawa zinthu za dziko mmene angakondweletsele mkazi wake, 34 ndipo amakhala wogawikana. Nayenso mkazi wosakwatiwa komanso namwali, amadela nkhawa zinthu za Ambuye kuti thupi ndi maganizo ake zikhale zoyela. Koma mkazi wokwatiwa amadela nkhawa zinthu za dziko mmene angakondweletsele mwamuna wake. 35 Ndikukamba izi kaamba ka ubwino wanu, osati kuti ndikupanikizeni* ai, koma kuti ndikulimbikitseni kucita zoyenela, komanso kuti nthawi zonse mukhale odzipeleka kwa Ambuye popanda cosokoneza.

36 Koma ngati wina amene sali pa banja akulephela kuugwila mtima cifukwa ca cilakolako, ndipo munthuyo wapitilila cimake ca unyamata, zimene ziyenela kucitika ndi izi, mulekeni akwatile ngati n’zimene akufuna, iye sakucimwa. 37 Koma ngati wina watsimikiza mumtima mwake, ndipo sakuona cifukwa colowela m’banja, komanso akutha kulamulila cilakolako cake, komanso mumtima mwake wasankha kukhalabe wosakwatila,* wacita bwino. 38 Nayenso amene wakwatila wacita bwino. Koma amene wacita bwino kwambili ndi amene sanakwatile.

39 Mkazi amakhala womangika pa nthawi yonse imene mwamuna wake ali moyo. Koma ngati mwamuna wake wamwalila, amakhala womasuka kukwatiwanso kwa aliyense amene wafuna, koma kokha mwa Ambuye. 40 Koma ndikuona kuti mkaziyo angakhale wacimwemwe kwambili ngati angakhalebe mmene alili. Ndipo sindikukaikila kuti pamenepa ndilinso ndi mzimu wa Mulungu.

8 Tsopano pa nkhani ya zakudya zopelekedwa kwa mafano, tikudziwa kuti tonse tili ndi cidziwitso. Cidziwitso cimapangitsa munthu kudzitukumula, koma cikondi cimamangilila. 2 Ngati wina akuganiza kuti akudziwa zinazake, ndiye kuti zinthuzo sanazidziwebe bwino. 3 Koma ngati munthu amakonda Mulungu, ndiye kuti munthuyo amadziwika kwa Mulungu.

4 Tsopano pa nkhani ya zakudya zopelekedwa kwa mafano, tikudziwa kuti fano ndi lopanda nchito m’dzikoli, ndipo kulibe Mulungu wina kupatulapo mmodzi yekhayo. 5 Pakuti ilipo yochedwa milungu kaya kumwamba kapena padziko lapansi. Ndipo ndi zoona, kuli “milungu” yambili ndi “ambuye” ambili. 6 Koma ife tili ndi Mulungu mmodzi yekha amene ndi Atate. Ndipo palinso Ambuye mmodzi, Yesu Khristu, amene zinthu zonse zinakhalapo kudzela mwa iye.

7 Komabe si onse amene amadziwa zimenezi. Koma cifukwa cakuti ena kale anali kulambila mafano, akamadya cakudyaco amaona ngati akudya cakudya copelekedwa kwa mafano. Ndipo cifukwa cakuti ndi ofooka, cikumbumtima cao cimawabvutitsa. 8 Cakudya sicingatithandize kuyandikila Mulungu. Ngati sitinadye, sikuti timakhala oipa ai, ndipo ngati tadya sikutinso timakhala abwino kwambili ai. 9 Koma samalani kuti ufulu wanu wosankha usakhale copunthwitsa mwa njila ina yake kwa amene ndi ofooka. 10 Ngati wina angakuone iwe wodziwa zinthu ukudya cakudya m’kacisi wa mafano, kodi cikumbumtima ca munthu wofooka sicidzamutuntha kuti adye zakudya zopelekedwa kwa mafano? 11 Conco cifukwa ca cidziwitso cako, cikhulupililo ca munthu wofookayo cidzaonongeka, m’bale wako amene Khristu anamufela. 12 Ngati mukucimwila abale anu mwa njila imeneyi ndi kubvulaza cikumbumtima cao cofooka, mukucimwila Khristu. 13 Ndiye cifukwa cake, ngati kudya nyama kukukhumudwitsa m’bale wanga, sindidzadyanso nyama ngakhale pang’ono, kuti ndisamukhumudwitse m’bale wanga.

9 Kodi si ndine womasuka? Kodi si ndine mtumwi? Kodi ine sindinamuonepo Yesu Ambuye wathu? Kodi inu si ndinu nchito yanga mwa Ambuye? 2 Ngakhale kuti kwa ena si ndine mtumwi, koma kwa inu ndithu ndine mtumwi. Pakuti inu ndinu cidindo cotsimikizila utumwi wanga mwa Ambuye.

3 Kwa amene akunditsutsa, kudziteteza kwanga ndi uku: 4 Ndili ndi ufulu* wa kudya ndi kumwa, si conco? 5 Tili ndi ufulu woyenda ndi akazi* athu okhulupilila monga atumwi ena onse, komanso monga abale athu mwa Ambuye amacitila kuphatikizapo Kefa,* si conco? 6 Kodi Baranaba ndi ine ndife tokha amene tilibe ufulu woleka kugwila nchito kuti tizipeza zofunikila pa umoyo? 7 Ndani amene amagwila nchito ya usilikali koma n’kumadzilipila yekha? Ndani amene amalima munda wampesa koma osadyako zipatso zake? Ndi m’busa wanji amene amaweta ziweto koma osamwako mkaka wake?

8 Kodi ndikunena izi potengela maganizo a anthu? Kodi sizimenenso Cilamulo cimanena? 9 Pakuti Cilamulo ca Mose cimanena kuti: “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbeu.” Kodi Mulungu amadela nkhawa ng’ombe zokha? 10 Kapena kwenikweni anakamba mau amenewa poganizila ife? Mau amenewa anawalembadi kaamba ka ife, cifukwa munthu amene akulima komanso amene akupuntha mbeu amagwila nchito ali ndi ciyembekezo kuti alandila kenakake.

11 Ngati tinabzala zinthu zauzimu mwa inu, kodi n’kulakwa kulandila* zinthu zofunikila pa umoyo kucokela kwa inu? 12 Ngati anthu ena amakuyembekezelani kuti muzicita zimenezi, kodi ife si ndiye oyenelela kwambili kuticitila zimenezi? Ngakhale n’telo, ife sitinagwilitse nchito ufulu umenewo, koma tikupilila zonse kuti mwa njila inayake tisatsekeleze uthenga wabwino wokamba za Khristu. 13 Kodi inu simukudziwa kuti anthu amene amagwila nchito zopatulika amadya za m’kacisi? Ndiponso kodi simukudziwa kuti anthu amene amatumikila paguwa lansembe nthawi zonse, amalandilako zinthu zina zopelekedwa paguwa lansembelo? 14 Mwa njila imeneyi, Ambuye analamula kuti amene amalengeza uthenga wabwino azipeza zofunikila pa umoyo wawo kudzela mu uthenga wabwino.

15 Koma ine sindinagwilitseko nchito makonzedwe amenewo. Kukamba zoona, sikuti ndakulembelani zimenezi kuti muyambe kugwilitsa nchito makonzedwe amanewa pa ine, cifukwa ndi bwino kuti ndife kusiyana n’kuti ndicite zimenezi. Palibe munthu amene angandicotsele zifukwa zimene ndili nazo zodzitamila! 16 Tsopano ngati ndikulengeza uthenga wabwino, cimeneco cisakhale cifukwa codzitamila, cifukwa ndinalamulidwa kuti ndizicita zimenezo. Ndipo tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino! 17 Ndikamacita zimenezi modzifunila, ndidzalandila mphoto. Koma ngati ndimacita mokakamizika, ndinebe mtumiki woyang’anila malinga ndi udindo umene unaikidwa mwa ine. 18 Kodi ndiye mphoto yanga ndi yotani? Ndi yakuti ndikalengeza uthenga wabwino, ndiziulengeza kwaulele, kuti ndisagwilitse nchito ulamulilo* wanga molakwika pa zinthu zokhudza uthenga wabwino.

19 Ngakhale kuti ndine womasuka kwa anthu onse, ndadzipanga kukhala kapolo kwa anthu onse, kuti ndikope anthu ambili mmene ndingathele. 20 Kwa Ayuda ndinakhala ngati Myuda kuti ndikope Ayuda. Kwa amene amatsatila Cilamulo ndinakhala ngati munthu amene amatsatila Cilamulo kuti ndikope amene amatsatila Cilamulo, ngakhale kuti ine sinditsatila Cilamulo. 21 Kwa anthu amene satsatila Cilamulo, ndinakhala ngati wopanda Cilamulo, ngakhale kuti ine ndimatsatila malamulo a Mulungu komanso lamulo la Khristu. Ndinacita izi kuti ndikope anthu amene satsatila Cilamulo. 22 Kwa ofooka ndinakhala wofooka, kuti ndikope ofooka. Ndakhala zinthu zonse kwa anthu a mtundu uliwonse, kuti ngati n’kotheka ndipulumutseko ena. 23 Koma ndimacita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino, kuti ndiugawile kwa ena.

24 Kodi simukudziwa kuti pa mpikisano onse amathamanga, koma ndi mmodzi cabe amene amalandila mphoto? Muzithamanga m’njila yoti mukalandile mphotoyo. 25 Koma munthu amene amacita nao mpikisano amakhala wodziletsa m’zinthu zonse. Amatelo kuti alandile mphoto ya nkhata yamaluwa imene imaonongeka. Koma ife timafuna kukapeza nkhata yamaluwa imene singaonongeke. 26 Conco, mmene ndikuthamangila sikuti ndikungothamangilamo, osadziwa kumene ndikupita. Mmene ndikuponyela makofi anga, sikuti ndikungomenya m’mphepo ai. 27 Koma ndimapumphuntha* thupi langa ndi kulipangitsa kukhala ngati kapolo, ndi colinga coti pambuyo polalikila ena, ndisapezeke wosayenela* mwa njila ina.

10 Tsopano ndikufuna kuti mudziwe abale, kuti makolo athu akale onse anali pansi pa mtambo, ndipo anaoloka nyanja. 2 Komanso onse anabatizidwa mwa Mose kupitila mu mtambo komanso nyanja. 3 Ndipo onse anali kudya cakudya cauzimu cofanana. 4 Onse anali kumwa madzi auzimu ofanana. Cifukwa anali kumwa kucokela pathanthwe lauzimu limene linali kuwatsatila, ndipo thanthwelo litanthauza* Khristu. 5 Ngakhale n’telo, Mulungu sanakondwele ndi ambili a iwo, moti anaphedwa m’cipululu.

6 Tsopano izi zinacitika kuti zikhale citsanzo kwa ife, kuti tisamalakelake zinthu zoipa mmene iwo anacitila. 7 Komanso kuti tisamalambile mafano mmene ena a iwo anacitila, monga mmene Malemba amakambila kuti: “Anthuwo anakhala pansi kuti adye ndi kumwa, kenako anaimilila kuti asangalale.” 8 Musamacite ciwelewele* monga mmene ena a iwo anacitila, zimene zinacititsa kuti anthu 23,000 aphedwe pa tsiku limodzi. 9 Tisamamuyese Yehova mmene ena a iwo anamuyesela, iwo analumidwa ndi njoka ndipo anafa. 10 Tisakhale ong’ung’udza ngati mmene ena a iwo anang’ung’udzila, n’kuphedwa ndi mngelo wa Mulungu.* 11 Zinthuzi zinawacitikila kuti zikhale citsanzo kwa ife, ndipo zinalembedwa monga cenjezo kwa ife amene mapeto a nthawi ino atifikila.

12 Conco amene akuona kuti ali cilili asamale kuti asagwe. 13 Palibe mayeselo amene mumakumana nao osiyana ndi amene anthu ena amakumana nao. Koma Mulungu ndi wokhulupilika, ndipo sadzalola kuti muyesedwe kuposa mlingo umene simungathe kupilila. Koma pamene mukukumana ndi mayeselowo, iye adzakonza njila yopulumukila kuti mukwanitse kupilila.

14 Conco okondedwa anga, thawani kupembedza mafano. 15 Ndikukamba ndi inu ngati anthu ozindikila. Weluzani nokha ngati zimene ndikukamba ndi zoona kapena ai. 16 Kodi kapu ya madalitso imene timadalitsa, siitanthauza kugawana magazi a Khristu? Kodi mkate umene timaubenthula-benthula, sutanthauza kugawana thupi la Khristu? 17 Cifukwa cakuti pali mtanda umodzi wa mkate, ngakhale kuti ife tilipo ambili, ndife thupi limodzi. Pakuti tonse timadya mtanda umodzi wa mkatewo.

18 Ganizilani za Aisiraeli: Kodi sikuti aja amene amadya zopelekedwa nsembe amagawana ndi guwa la nsembe? 19 Ndiye ndi kukamba ciani? Kodi zopelekedwa nsembe kwa mafano ndi zaphindu, kapena fano ndi laphindu? 20 Ayi, koma ndikunena kuti, nsembe zimene anthu a mitundu ina amapeleka, amazipeleka kwa ziwanda, osati kwa Mulungu. Ndipo sindikufuna kuti inu muzigwilizana ndi ziwanda. 21 N’zosatheka kuti muzimwa za m’kapu ya Yehova ndi za m’kapu ya ziwanda. N’zosatheka kumadya “pathebulo la Yehova” komanso pathebulo la ziwanda. 22 Kodi ‘tikufuna kuti Yehova acite nsanje’?

23 Ife si ndife amphamvu kuposa iye, si conco? Zinthu zonse n’zololeka, koma si zonse zopindulitsa. Zinthu zonse n’zololeka, koma si zonse zolimbikitsa. 24 Munthu aliyense asamangofuna zopindulila iye yekha koma zopindulilanso anthu ena.

25 Muzidya ciliconse cogulitsidwa pamsika wa nyama, musamafunse mafunso pocitila cikumbumtima canu. 26 Pakuti “dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zokhala mmenemo.” 27 Ngati munthu wosakhulupilila wakuitanani, ndipo mukufuna kupita, muzidya zilizonse zimene akupatsani popanda kufunsa mafunso pocitila cikumbumtima canu. 28 Koma ngati wina wakuuzani kuti, “Izi zinapelekedwa nsembe,” musadye kucitila amene wakuuzani komanso cikumbumtima. 29 Sindikutanthauza cikumbumtima cako, koma ca munthu winayo. N’cifukwa ciani ufulu wanga uziimbidwa mlandu ndi cikumbutima ca munthu wina? 30 Ngakhale nditadya ndi kuyamika Mulungu kaamba ka cakudyaco, kodi ndicitebe zimenezo ngati sindingapangitse ena kunditsutsa?

31 Cotelo, kaya mukudya kapena kumwa, kapena kucita cina ciliconse, citani zonse kuti mupeleke ulemelelo kwa Mulungu. 32 Conco, muzipewa kukhala copunthwitsa kwa Ayuda, kwa Agiriki, komanso ku mpingo wa Mulungu. 33 Cifukwa inenso ndikuyesetsa kukondweletsa anthu onse m’zinthu zonse. Sindikucita zopindulila ine ndekha, koma zopindulilanso anthu ambili kuti apulumutsidwe.

11 Tengelani citsanzo canga, mmenenso ine ndikutengela citsanzo ca Khristu.

2 Ndikukuyamikilani cifukwa cakuti mumandikumbukila mu zinthu zonse, ndipo mukusunga mosamala miyambo monga mmene ndinaipelekela kwa inu. 3 Koma ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu. 4 Mwamuna aliyense amene akupemphela kapena kulosela atabvala cinacake kumutu amacititsa manyazi mutu wake. 5 Koma mkazi aliyense amene akupemphela kapena kulosela popanda kubvala cakumutu amacititsa manyazi mutu wake, cifukwa kutelo zikhala ngati kuti wameta mpala. 6 Pakuti ngati mkazi sabvala cophimba kumutu, azimeta tsitsi lake. Koma ngati izi n’zocititsa manyazi kwa mkazi kuti amete tsitsi lake kapena kumeta mpala, azibvala cophimba kumutu.

7 Mwamuna sayenela kubvala cophimba kumutu, cifukwa ndiye cifanizilo komanso ulemelelo wa Mulungu, koma mkazi ndi ulemelelo wa mwamuna. 8 Pakuti mwamuna sanacokele kwa mkazi, koma mkazi ndiye anacokela kwa mwamuna. 9 Kuonjezela apo, mwamuna sanalengedwele mkazi, koma mkazi ndiye analengedwela mwamuna. 10 N’cifukwa cake mkazi ayenela kukhala ndi cizindikilo kumutu kwake coonetsa kuti ali pansi pa ulamulilo wa mwamuna monga cizindikilo coonekela kwa angelo.

11 Mwa Ambuye, mkazi amadalila mwamuna, ndiponso mwamuna amadalila mkazi. 12 Mkazi amacokela kwa mwamuna, cimodzi-modzinso mwamuna amacokela kwa mkazi. Koma zinthu zonse zimacokela kwa Mulungu. 13 Weluzani nokha: Kodi m’poyenela kuti mkazi azipemphela kwa Mulungu popanda kubvala cophimba kumutu? 14 Kodi cibadwa sicikukuuzani* kuti zimakhala zocititsa manyazi mwamuna kukhala ndi tsitsi lalitali? 15 Ngati mkazi ali ndi tsitsi lalitali, umenewo umakhala ulemelelo wake. Pakuti iye anapatsidwa tsitsi m’malo mwa cophimba kumutu. 16 Ngati wina akufuna kutsutsa zimenezi pofuna cikhalidwe cina, ife komanso mpingo wa Mulungu tilibe cikhalidwe cina.

17 Koma sikuti pokupatsani malangizo amenewa ndikukuyamikilani ai, cifukwa mumasonkhana pamodzi osati pa zifukwa zabwino koma zoipa. 18 Coyamba, ndamva kuti mukasonkhana pamodzi mumpingo, pakati panu pamakhala magawano. Kumbali ina ndikhulupilila kuti zimenezi n’zoona. 19 Pakati panu payeneladi kukhala magulu ampatuko, kuti amene ndi obvomelezeka pakati panu adziwike.

20 Mukasonkhana pamalo amodzi kuti mudye Mgonelo wa Ambuye,* simucita zimenezo m’njila yoyenela. 21 Cifukwa nthawi ya cakudyaco isanafike, aliyense wa inu amakhala atadyelatu cakudya cake camadzulo. Wina amakhala ndi njala koma wina amakhala woledzela. 22 Kodi inu mulibe nyumba zimene mungadyeleko ndi kumwa? Kapena mukunyozela mpingo wa Mulungu, ndipo mukucititsa manyazi amene alibe kanthu? Ndikuuzeni ciani pamenepa? Ndikuyamikileni? Pa izi zokha ai, sindingakuyamikileni.

23 Pakuti zimene ndinalandila kwa Ambuye, n’zimenenso ndinakuphunzitsani kuti usiku umene Ambuye Yesu anapelekedwa anatenga mkate, 24 ndipo atayamika anaunyema-nyema n’kukamba kuti: “Mkate uwu ukuimila thupi langa limene likupelekedwa kaamba ka inu. Muzicita zimenezi pondikumbukila.” 25 Anacitanso cimodzi-modzi ndi kapu pambuyo pa cakudya camadzulo. Iye anati: “Kapu iyi ikuimila cipangano catsopano pamaziko a magazi anga. Muzicita zimenezi mukamamwa za m’kapuyi pondikumbukila.” 26 Pakuti nthawi zonse mukamadya mkatewu ndi kumwa za m’kapuyi, mumalengeza za imfa ya Ambuye mpaka pamene adzabwele.

27 Conco, aliyense amene akudya mkate, kapena kumwa za m’kapu ya Ambuye mosayenelela, adzakhala ndi mlandu wokhudza thupi komanso magazi a Ambuye. 28 Cotelo munthu ayenela kudzifufuza coyamba, pambuyo pake m’pomwe angadye mkate ndi kumwa za m’kapuyi. 29 Pakuti munthu amene amadya ndi kumwa popanda kuzindikila kuti zinthuzo zikuimila thupilo, amadzibweletsela cilango. 30 N’cifukwa cake ambili a inu ndinu ofooka komanso odwala, ndipo ambilinso afa.* 31 Koma ngati tingathe kuzindikila mmene tilili, sitingaweluzidwe. 32 Komabe, tikaweluzidwa ndiye kuti tikulangizidwa ndi Yehova, kuti tisaweluzidwile pamodzi ndi dzikoli. 33 Conco abale, mukasonkhana pamodzi kuti mudye Mgonelo wa Ambuye,* muziyembekezana. 34 Ngati wina ali ndi njala, azidya kunyumba, kuti mukasonkhana pamodzi musaweluzidwe. Koma nkhani zimene zatsala ndidzazisamalila ndikadzafika kumeneko.

12 Tsopano kunena za mphatso zauzimu abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa zinthu. 2 Inu mudziwa kuti pamene munali osakhulupilila,* munali kutsogoleledwa komanso kusoceletsedwa ndi mafano osalankhula. 3 Tsopano ndikufuna kuti mudziwe kuti palibe munthu wotsogoleledwa ndi mzimu wa Mulungu amene angakambe kuti: “Yesu ndi wotembeleledwa!” Palibenso amene angakambe kuti: “Yesu ndi Ambuye!” popanda kutsogoleledwa ndi mzimu woyela.

4 Pali mphatso zosiyana-siyana koma mzimu ulipo umodzi. 5 Ndipo pali mautumiki osiyana-siyana koma Ambuye alipo mmodzi. 6 Palinso nchito zosiyana-siyana, koma Mulungu amene amapeleka mphamvu zogwilila nchitozo kwa aliyense alipo mmodzi. 7 Koma thandizo la mzimu woyela limaonekela mwa aliyense, ndipo Mulungu amaupeleka kuti upindulile ena. 8 Pakuti mzimu umathandiza wina kulankhula mau anzelu, ndipo mzimu womwewo umathandiza wina kulankhula mau ozindikila. 9 Mzimu umodzi-modziwo umathandiza wina kukhala ndi cikhulupililo, pamene wina umamuthandiza kukhala ndi mphatso za kucilitsa. 10 Koma wina umam’patsa mphatso yocita nchito zamphamvu, wina kulosela, wina kuzindikila mau ouzilidwa, wina kulankhula malilime,* komanso wina kumasulila malilime. 11 Koma nchito zonsezi zimatheka ndi mzimu umodzi-modziwo, ndipo umapatsa munthu aliyense mphatsozi malinga ndi mmene ukufunila.

12 Thupi lili ndi ziwalo zambili, ngakhale ntelo, ziwalozo zimapanga thupi limodzi. N’cimodzi-modzinso ndi Khristu. 13 Pakuti tonsefe, tinabatizidwa ndi mzimu umodzi kuti tikhale thupi limodzi. Kaya Ayuda kapena Agiriki, akapolo kapena mfulu, tonsefe tinalandila* mzimu umodzi.

14 Pakuti thupi silikhala ndi ciwalo cimodzi, koma zambili. 15 Ngati phazi lingakambe kuti: “Popeza ine si ndine dzanja, sindili mbali ya thupi,” zimenezo sizitanthauza kuti si lilidi mbali ya thupi. 16 Ndipo ngati khutu lingakambe kuti: “Popeza kuti ine si ndine diso, si ndili mbali ya thupi,” zimenezo sizitanthauza kuti si lilidi mbali ya thupi. 17 Thupi lonse likanakhala diso, tikanamva ndi ciani? Thupi lonse likanakhala khutu, tikananunkhiza ndi ciani? 18 Koma Mulungu anaika ciwalo ciliconse pamalo ake, malinga ndi kufuna kwake.

19 Kodi thupi likanakhalapo ngati ziwalo zonse zinakakhala ciwalo cimodzi? 20 Conco pali ziwalo zoculuka, koma thupi ndi limodzi. 21 Diso silingauze dzanja kuti: “Ndilibe nawe nchito,” kapena mutu sungauze mapazi kuti: “Ndilibe nanu nchito.” 22 Koma ziwalo za thupi zooneka ngati zofooka, ndi zofunika. 23 Ndipo ziwalo za thupi zimene timaziyesa kuti n’zocepelapo ulemu, timazipatsa ulemu woonjezeleka. Conco, ziwalo zathu zotsikilapo timazilemekeza mokulilapo, 24 pamene ziwalo zathu zooneka bwino kale sizifunikila cisamalilo cimeneco. Ngakhale n’conco, Mulungu analumikiza bwino thupi lonse, anaika ulemu woculuka pa ziwalo zimene panalibe ulemuwo. 25 Anatelo kuti thupi lake likhale losagawika, koma kuti ziwalo zake zizisamalilana. 26 Cotelo, ciwalo cimodzi cikabvutika ziwalo zina zonse zimabvutikila naco limodzi. Komanso ciwalo cimodzi cikalemekezedwa, ziwalo zina zonse zimasangalalila naco limodzi.

27 Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi ciwalo ca thupilo. 28 Ndipo Mulungu wapatsa munthu aliyense zocita zosiyana-siyana mumpingo. Coyamba atumwi, caciwili aneneli, cacitatu aphunzitsi, ndiyeno nchito zamphamvu, mphatso zakucilitsa, utumiki wothandiza anthu, luso loyendetsa zinthu, komanso mphatso yolankhula malilime osiyana-siyana. 29 Sizingatheke kuti onse akhale atumwi. Sizingatheke kuti onse akhale aneneli, zingatelo ngati? Kodi onse angakhale aphunzitsi? Si onse amene amacita nchito zamphamvu, ndi onse ngati? 30 Ndipo si onse amene ali ndi mphatso zocilitsa, ndi onse ngati? Si onse amene amalankhula malilime, ndi onse ngati? Si onse amene ndi omasulila,* ndi onse ngati? 31 Conco, yesetsani* kuti mulandile mphatso zazikulu. Komabe, ndidzakuonetsani njila yopambana.

13 Ngati ndimalankhula malilime a anthu komanso a angelo koma ndilibe cikondi, ndiye kuti ndakhala belu yolila kapena cimbale ca citsulo coliza. 2 Ndipo ngati ndili ndi mphatso ya kulosela komanso ndikumvetsa zinsinsi zonse zopatulika ndiponso kudziwa zinthu zonse, ndipo ngati ndili ndi cikhulupililo conse moti ndikutha kusuntha naco mapili, koma ndilibe cikondi, zimene ndimacitazo zilibe nchito. 3 Ngati ndapeleka zinthu zanga zonse kuti ndidyetse ena, komanso ngati ndapeleka thupi langa pofuna kudzitama, koma ndilibe cikondi, sindingapindule m’pang’ono pomwe.

4 Cikondi n’coleza mtima komanso n’cokoma mtima. Cikondi sicicita nsanje, sicidzitama, sicidzitukumula. 5 Cikondi sicicita zosayenela, sicicita zofuna zake zokha, sicikwiya, komanso sicisunga zifukwa.* 6 Sicisangalala ndi zosalungama, koma cimasangalala ndi coonadi. 7 Cimakwilila zinthu zonse, cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse.

8 Cikondi sicitha. Koma ngati pali mphatso za kulosela zidzatha, kaya kulankhula malilime* kudzatha, ndipo kaya pali mphatso ya kudziwa zinthu, nayonso idzatha. 9 Pakuti sitidziwa zonse ndipo timalosela mopelewela. 10 Koma tikadzadziwa zonse zopelewelazi zidzatha. 11 Ndili mwana, ndinali kulankhula ngati mwana, kuganiza ngati mwana, ndiponso kuona zinthu ngati mwana. Koma popeza tsopano ndakula, ndinaleka kucita zacibwana. 12 Koma palipano sitikutha kuona bwino-bwino cifukwa tikugwilitsa nchito galasi* losaonetsa bwino-bwino. Koma m’tsogolo tidzaona bwino-bwino. Palipano cidziwitso canga n’copelewela, koma cidzakhala colondola ngati mmene Mulungu amandidziwila bwino. 13 Tsopano, patsala zinthu zitatu izi: Cikhulupililo, ciyembekezo, komanso cikondi. Koma cacikulu koposa pa zonsezi ndi cikondi.

14 Khalani ndi cikondi, koma yesetsani kuti mulandile mphatso zauzimu, maka-maka mphatso ya kulosela. 2 Pakuti wolankhula malilime salankhula ndi anthu, koma amalankhula ndi Mulungu. Cifukwa palibe amene amamva zimene akulankhula, koma amalankhula zinsinsi zopatulika mothandizidwa ndi mzimu. 3 Komabe wolosela amathandiza, kulimbikitsa, komanso kutonthoza anthu ndi mau ake. 4 Wolankhula malilime amadzilimbikitsa yekha, koma wolosela amalimbikitsa mpingo. 5 Ndikanakonda kuti nonsenu muzilankhula malilime, koma comwe ndingakonde kwambili ndi coti muzilosela. Ndithudi wolosela amaposa wolankhula malilime, pokhapo wolankhula malilimeyo atamasulila kuti mpingo ulimbikitsidwe. 6 Abale, ngati panthawi ino ndingabwele kwa inu ndikulankhula malilime, kodi mungapindulepo ciani ngati simukuwadziwa? Zingakhale zothandiza ngati ndingabwele kwa inu ndi bvumbulutso locokela kwa Mulungu, kapena mphatso yodziwa zinthu, kapena kulosela, kapenanso kuphunzitsa.

7 N’cimodzi-modzinso ndi zipangizo zoimbila monga citolilo kapena zeze. Ngati malilidwe a citolilo kapena zeze sasintha-sintha, kodi zingatheke bwanji kudziwa nyimbo imene ikuimbidwa? 8 Ngati lipenga silikulila momveka bwino, ndani angakonzekele nkhondo? 9 Mofananamo, ngati mukulankhula zinthu zobvuta kumvetsa, kodi munthu angadziwe bwanji zimene mukunena? Mudzakhala mukulankhula ku mphepo. 10 Padziko lapansi pali zinenelo zambili, koma palibe ngakhale cimodzi cimene cilibe tanthauzo. 11 Ngati sindikumva tanthauzo la zimene munthu akulankhula, ndimakhala mlendo kwa munthu wolankhulayo, ndipo amene akulankhulayo amakhala mlendo kwa ine. 12 N’cimodzi-modzinso ndi inu, pakuti mukufunitsitsa mphatso za mzimu, muziyesetsa kukhala ndi mphatso zimene zingalimbikitse mpingo.

13 Conco amene amalankhula malilime, apemphele kuti azitha kumasulila. 14 Pakuti ngati ndikupemphela m’malilime, mphatso yanga ya mzimu ndi imene ikupemphela, koma maganizo anga sakucita ciliconse. 15 Ndiye ndicite ciani? Ndidzapemphela ndi mphatso ya mzimu, ndipo ndidzapemphelanso ndi maganizo anga. Ndidzaimba nyimbo zotamanda ndi mphatso ya mzimu, koma ndidzaimbanso nyimbo zotamanda ndi maganizo anga. 16 Ngati mukutamanda Mulungu ndi mphatso ya mzimu, kodi munthu wamba amene ali pakati panu adzanena bwanji kuti “ameni” pa pemphelo lanu loyamikila, pakuti munthuyo sakudziwa zimene mukukamba? 17 N’zoona kuti mukupeleka pemphelo loyamikila Mulungu m’njila yabwino, koma munthu winayo sakulimbikitsidwa. 18 Ndimayamika Mulungu kuti ndimalankhula zinenelo* zambili kuposa nonsenu. 19 Ngakhale n’telo, ndi bwino kuti mumpingo ndizilankhula mau asanu omveka bwino* kuti ndiphunzitsenso ena, m’malo molankhula mau 10,000 m’cinenelo* cacilendo.

20 Abale, musakhale ana aang’ono pa kumvetsa zinthu. Koma khalani ana aang’ono ku zinthu zoipa. Ndipo khalani aakulu pa nkhani yomvetsa zinthu. 21 M’Cilamulo muli mau akuti: “‘Ndi malilime a anthu acilendo komanso milomo ya anthu acilendo, ndidzalankhula ndi anthu awa. Ngakhale n’telo, iwo adzakana kundimvela,’ watelo Yehova.” 22 Conco malilime si cizindikilo ca anthu okhulupilila, koma anthu osakhulupilila. Pamene kulosela ndi cizindikilo ca anthu okhulupilila, osati osakhulupilila. 23 Conco ngati mpingo wonse wasonkhana pamodzi, ndipo onse akulankhula malilime, ndiyeno anthu wamba kapena osakhulupilila alowa, kodi iwo sadzanena kuti mwacita misala? 24 Koma ngati nonse mukulosela, ndipo munthu wosakhulupilila kapena munthu wamba walowa, iye adzadzudzulidwa komanso kufufuzidwa mosamala ndi nonsenu. 25 Ndiyeno zinsinsi za mumtima mwake zimaonekela, moti amawelama n’kulambila Mulungu, ndipo amalengeza kuti: “Mulungu alidi pakati panu.”

26 Ndiye zinthu zizicitika motani abale? Mukasonkhana pamodzi, wina angakhale ndi salimo, wina kuphunzitsa, wina bvumbulutso, wina kulankhula cinenelo* cacilendo, wina n’kumamasulila. Muzicita zonsezi kuti mulimbikitsane. 27 Ngati pali anthu olankhula zinenelo* zacilendo, azingokhala awili kapena atatu basi, ndipo azilankhula mopatsana mpata, komanso wina azimasulila. 28 Koma ngati palibe womasulila, wolankhula malilimeyo azikhala cete mumpingo, ndipo azikamba ndi Mulungu camumtima. 29 Aneneli awili kapena atatu azilankhula, ndipo ena onse azimvetsa tanthauzo lake. 30 Koma ngati wina walandila bvumbulutso locokela kwa Mulungu ali khale pansi, woyamba uja azikhala cete. 31 Pakuti nonse mungalosele, koma mopatsana mpata kuti onse aphunzile komanso kulimbikitsidwa. 32 Ndipo aneneli ayenela kukhala odziletsa akamagwilitsa nchito mphatso za mzimu woyela. 33 Pakuti Mulungu si Mulungu wacisokonezo, koma wamtendele.

Monga mmene zilili m’mipingo yonse ya oyelawo, 34 akazi azikhala cete m’mipingo, pakuti n’kosaloleka kuti azilankhula. M’malomwake, iwo azigonjela monga mmene Cilamulo cimakambila. 35 Ngati iwo akufuna kumvetsa zinazake, azifunsa amuna ao kunyumba, pakuti n’zocititsa manyazi mkazi kulankhula ndi mpingo.*

36 Kodi mau a Mulungu anacokela kwa inu, kapena anangofika kwa inu nokha basi?

37 Ngati wina akuganiza kuti ndi mneneli, kapena ali ndi mphatso ya mzimu, abvomeleze kuti zinthu izi zimene ndakulembelani ndi lamulo la Ambuye. 38 Koma ngati wina akunyalanyaza zimenezi, nayenso adzanyalanyazidwa.* 39 Conco abale anga, yesetsani kuti muzilosela, komabe musaletse kulankhula malilime.* 40 Koma zinthu zonse zizicitika moyenela ndi mwadongosolo.

15 Tsopano abale, ndikukumbutsani za uthenga wabwino umene ndinaulengeza kwa inu, umenenso inu munaulandila komanso kuukhulupilila mwamphamvu. 2 Mukupulumutsidwa ngati mwagwila mwamphamvu uthenga wabwino umene ndinaulalikila kwa inu. Popanda kutelo ndiye kuti munakhala okhulupilila pacabe.

3 Pa zinthu zoyamba zimene ndinakuphunzitsani zimenenso ine ndinalandila, panali zakuti Khristu anafa kaamba ka macimo athu, mogwilizana ndi Malemba. 4 Komanso zakuti anaikidwa m’manda, ndiyeno anaukitsidwa pa tsiku lacitatu mogwilizana ndi Malemba. 5 Ndipo anaonekela kwa Kefa,* kenako kwa atumwi 12. 6 Pambuyo pake, anaonekela kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambili a iwo tikali nao, koma ena anafa.* 7 Ndiyeno anakaonekela kwa Yakobo, kenako kwa atumwi onse. 8 Ndipo pothela pake anaonekela kwa ineyo, amene ndinali ngati khanda lobadwa masiku osakwana.

9 Ine ndine wamng’ono kwambili pa atumwi onse, ndipo sindine woyenela kuchedwa mtumwi, cifukwa ndinali kuzunza mpingo wa Mulungu. 10 Koma cifukwa ca cisomo ca Mulungu, ndili mmene ndililimu. Ndipo cisomo cimene anandicitila sicinapite pacabe, cifukwa ndinagwila nchito mwakhama kuposa atumwi onse. Komabe sindinacite zimenezi ndi mphamvu zanga zokha ai, koma cifukwa ca cisomo cimene Mulungu anandicitila. 11 Conco, kaya munaphunzitsidwa ndi ine, kapena iwo, uthenga umene tikulalikila ndi womwewo umene munaukhulupilila.

12 Tsopano ngati timalalikila kuti Khristu anaukitsidwa, n’cifukwa ciani ena a inu mumakamba kuti akufa sadzaukitsidwa? 13 Cifukwa ngati kuuka kwa akufa kulibe, ndiye kuti Khristu nayenso sanaukitsidwe. 14 Koma ngati Khristu sanaukitsidwe, kulalikila kwathu kulibe phindu, ndipo cikhulupililo canu cilibenso phindu. 15 Kuonjezela apo, ndiye kuti ndife mboni zabodza za Mulungu. Cifukwa ngati akufa sadzauka, ndiye kuti tapeleka umboni wonamizila Mulungu kuti anaukitsa Khristu pamene sanamuukitse. 16 Pakuti ngati akufa sadzaukitsidwa, ndiye kuti Khristu nayenso sanaukitsidwe. 17 Cina, ngati Khristu sanaukitsidwe, cikhulupililo canu cilibe nchito. Ndipo macimo anu sadzakhululukidwa. 18 Ndiye kuti naonso amene anafa mogwilizana ndi Khristu, zao zonse zinathela pomwepo. 19 Ngati tinali ndi ciyembekezo mwa Khristu pa moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa cisoni kuposa munthu wina aliyense.

20 Koma tsopano Khristu anaukitsidwa kwa akufa monga cipatso coyambilila ca amene anagona mu imfa. 21 Pakuti imfa inabwela kudzela mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa nakonso kudzabwela kupitila mwa munthu mmodzi. 22 Monga mmene zilili kuti onse amafa cifukwa ca Adamu, onse adzakhalanso ndi moyo kudzela mwa Khristu. 23 Koma aliyense pa nthawi yake: Coyamba Khristu amene ndi cipatso coyambilila, ndiyeno onse amene ndi a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake. 24 Ndiyeno pamapeto pake, adzapeleka Ufumu m’manja mwa Mulungu wake ndi Atate wake, pamene adzathetsa maboma onse, maulamulilo onse, ndi mphamvu zonse. 25 Cifukwa ayenela kulamulila monga mfumu mpaka pamene Mulungu adzaike adani ake onse pansi pa mapazi ake. 26 Ndiponso imfa, mdani womaliza idzaonongedwa. 27 Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Koma pamene anati ‘waika zinthu zonse pansi pa mapazi ake,’ n’zoonekelatu kuti sakuphatikizapo Mulunguyo, amene anaika zinthu zonse pansi pa iye. 28 Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwana nayenso adzaonetsa kuti ali pansi pa ulamulilo wa Mulungu, amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulunguyo akhale zinthu zonse kwa aliyense.

29 Tsopano, kodi amene akubatizidwa kuti akhale akufa adzacita ciani? Ngati akufa sadzaukitsidwa konse, n’cifukwa ciani anthuwo akubatizidwa kuti akhale akufa?* 30 N’cifukwa ciani ifenso timaika moyo wathu pa ciopsyezo nthawi zonse? 31 Tsiku lililonse ndimakhala pa ciopsyezo cakuti ndikhoza kufa. Izi n’zoona monga mmene zilili zoona kuti ndimakunyadilani cifukwa ca ubwenzi wanu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu. 32 Ngati ndinamenyana ndi zilombo za kuchile ku Efeso, monga mmene ena anacitila,* kodi ndidzapindulapo ciani? Ngati akufa sadzaukitsidwa, “tiyeni tidye ndi kumwa, cifukwa mawa tidzafa.” 33 Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumaononga makhalidwe abwino. 34 Yambani kuganiza bwino ndipo muzicita zoyenela komanso musamacite chimo. Pakuti ena a inu simudziwa Mulungu. Ndikulankhula izi kuti ndikucititseni manyazi.

35 Koma wina angakambe kuti: “Kodi akufa adzaukitsidwa bwanji? Nanga adzaukitsidwa ndi thupi lotani?” 36 Iwe munthu wopanda nzelu! Cinthu cimene wabzala sicingakhale ndi moyo pokha-pokha citafa coyamba. 37 Ndipo pa zimene umabzala, umangobzala mbeu cabe, osati mmela umene udzakule, kaya mbeuyo ikhale ya tiligu kapena mbeu ina iliyonse. 38 Koma Mulungu amaipatsa thupi mwa kufuna kwake, ndipo thupi la mbeu ina iliyonse ikamakula imakhala yosiyana ndi inzake. 39 Sikuti matupi onse ndi ofanana. Pali matupi a anthu, matupi a ng’ombe, matupi a mbalame, komanso matupi a nsomba. 40 Ndipo palinso matupi akumwamba ndi matupi apadziko lapansi, koma ulemelelo wa matupi akumwamba ndi wina, komanso ulemelelo wa matupi apadziko lapansi ndi winanso. 41 Ulemelelo wa dzuwa ndi wina, ndipo ulemelelo wa mwezi ndi winanso. Naonso ulemelelo wa nyenyezi ndi wina, ndipo ulemelelo wa nyenyezi iliyonse umakhala wosiyana ndi ulemelelo wa nyenyezi ina.

42 Ndi mmenenso zilili ndi kuuka kwa akufa. Thupi limene lingathe kuola limafoceledwa. Koma thupi limene silingathe kuola limaukitsidwa. 43 Thupi pofoceledwa limakhala lonyozeka, koma limaukitsidwa lili lamphamvu. 44 Limafoceledwa lili la mnofu, koma limaukitsidwa lili lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu. 45 Malemba amati: “Munthu woyambilila, Adamu, anakhala munthu wamoyo.” Koma Adamu wothela anakhala mzimu wopatsa moyo. 46 Komabe, thupi loyamba si lauzimu, koma la mnofu. Pambuyo pake panabwela thupi lauzimu. 47 Munthu woyamba anacokela padziko lapansi, ndipo anapangidwa ndi dothi. Munthu waciwili anacokela kumwamba. 48 Anthu a m’dzikoli ali ngati munthu amene Mulungu anapanga kucokela ku dothi. Koma akumwamba ali ngati uja amene anacokela kumwamba. 49 Monga mmene zilili kuti palipano tikufanana ndi amene anapangidwa ndi dothi uja, tidzafanananso ndi uja wakumwamba.

50 Koma ndikukuuzani izi abale, kuti mnofu ndi magazi sizingalowe mu Ufumu wa Mulungu. Ndipo cinthu cimene cingaole sicingalandile kusaola. 51 Taonani! Ndikukuuzani cinsinsi copatulika: Si tonse amene tidzagona mu imfa, koma tonse tidzasintha, 52 m’kanthawi kocepa, m’kuphetila kwa diso pa kulila kwa lipenga lothela. Pakuti lipenga lidzalila, ndiyeno akufa adzaukitsidwa ndi matupi amene sangaole ndipo tidzasintha. 53 Cifukwa matupi amene angaole adzasintha n’kukhala amene sangaole, ndipo ao amene angafe adzasintha n’kukhala amene sangafe. 54 Koma matupi ao amene angaole akadzasintha n’kukhala amene sangaole, komanso matupi ao amene angafe akadzasintha n’kukhala amene sangafe, pamenepo zimene Malemba amakamba zidzakwanilitsidwa zakuti: “Imfa idzamezedwa kwamuyaya.” 55 “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, kodi kuluma* kwako kuli kuti?”* 56 Kuluma kumene kumabweletsa imfa,* ndi ucimo, koma Cilamulo n’cimene cimaonetsa mphamvu ya ucimo. 57 Koma tiyamika Mulungu cifukwa amatithandiza kupambana kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

58 Conco okondedwa abale anga, khalani olimba, musasunthike. Ndipo nthawi zonse muzikhala ndi zocita zambili mu nchito ya Ambuye, podziwa kuti zimene mukucita mu nchito ya Ambuye sizidzapita pacabe.

16 Ponena za nkhani ya zopeleka zopita kwa oyelawo, mungatsatile malangizo amene ndinapeleka ku mipingo ya ku Galatiya. 2 Pa tsiku loyamba la mlungu uliwonse, aliyense wa inu aziika kenakake pambali malinga ndi mapezedwe ake, kuti pasadzakhale zosonkha-sonkha zopeleka ine ndikadzafika. 3 Koma ndikadzafika kumeneko, ndidzatumiza amuna amene inu munawabvomeleza m’makalata anu kuti adzapeleke mphatso zanu za cifundo ku Yerusalemu. 4 Koma ngati m’pofunika kuti inenso ndipite kumeneko, tidzapitila limodzi.

5 Koma ndidzafika kwa inu pocoka ku Makedoniya, cifukwa ndidzadzela ku Makedoniya. 6 Ndikhoza kudzakhala nanu kumeneko, mwinanso nthawi yonse yozizila, kuti mudzandipelekeze kumene ndidzapite. 7 Cifukwa ulendo uno sindifuna ndidzakuoneni mothamanga ai. Yehova akalola, ndikufuna kuti ndidzakhale nanu kwa kanthawi ndithu. 8 Koma ndidzakhalabe kuno ku Efeso kufikila nthawi ya Cikondwelelo ca Pentekosite, 9 cifukwa khomo lalikulu la zocita landitsegukila, koma pali otsutsa ambili.

10 Tsopano Timoteyo akadzafika, mudzaonetsetse kuti asadzacite mantha pakati panu, cifukwa iye akugwila nchito ya Yehova mmene ine ndikucitila. 11 Conco pasapezeke munthu womudelela. Mukamupelekeze mwamtendele kuti abwele kuno, cifukwa ine ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale.

12 Tsopano ponena za Apolo m’bale wathu, ndinamucondelela kwambili kuti abwele kwa inu pamodzi ndi abale. Sicinali colinga cake kuti abwele kwa inu palipano, koma adzabwela akapeza mpata.

13 Khalani maso, imani zolimba m’cikhulupililo, citani zinthu molimba mtima,* ndipo khalani amphamvu. 14 Zinthu zonse zimene mukucita, muzizicita ndi cikondi.

15 Mukudziwa abale, kuti anthu a m’banja la Sitefana ndiwo anali oyamba kukhala okhulupilila* ku Akaya, ndipo iwo anadzipeleka kutumikila oyelawo. Cotelo ndikukulimbikitsani kuti, 16 inunso pitilizani kugonjela anthu ngati amenewo, komanso onse amene akugwila nchito molimbika. 17 Koma ndine wosangalala kuti Sitefana, Fotunato, ndi Akayiko ali nane kuno. 18 Popeza inu simuli kuno, iwo alowa m’malo mwanu. Anthu amenewa anditsitsimula komanso atsitsimula inu. Conco amuna ngati amenewa muziwalemekeza.

19 Mipingo ya ku Asia ikukutumizilani moni. Akula pamodzi ndi Purisika komanso mpingo umene umasonkhana m’nyumba yao, akukupatsani moni wacikondi mwa Ambuye. 20 Abale onse akuti moni. Muzipatsana moni wacikondi.*

21 Tsopano landilani moni wanga ine Paulo, wolembedwa ndi dzanja langa.

22 Ngati wina sakonda Ambuye, ameneyo atembeleledwe. Inu Ambuye wathu, bwelani! 23 Cisomo ca Ambuye Yesu cikhale nanu. 24 Ndikukutsimikizilani kuti ndimakukondani inu nonse ophunzila a Khristu Yesu.

Wochedwanso Petulo.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Kapena kuti, “kulankhula mocenjela.”

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Kapena kuti, “Ndidzakankhila kumbali.”

Kutanthauza katswili wa Cilamulo.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

M’cinenelo coyambilila, “munthu wakuthupi.”

Kapena kuti, “kulandila.”

M’cinenelo coyambilila, “anthu akuthupi.”

M’cinenelo coyambilila, “ndi amodzi.”

Kapena kuti, “woyang’anila nchito wanzelu.”

M’cinenelo coyambilila, “idzaonekela.”

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Wochedwanso Petulo.

M’cinenelo coyambilila, “komanso amalisece.”

M’cinenelo coyambilila, “njila zanga.”

M’Cigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.

M’Cigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena, ciwelewele.

Onani Matanthauzo a Mau Ena, ciwelewele.

Onani Matanthauzo a Mau Ena, ciwelewele.

Kapena kuti, “munthu wolankhula monyoza.”

Kapena kuti, “musanyengedwe.”

Onani Matanthauzo a Mau Ena, “ciwelewele.”

Kapena kuti, “amathanyula.”

Kapena kuti, “olankhula monyoza.”

M’Cigiriki, por.nei’a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.

M’Cigiriki, por.nei’a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Kutanthauza kugonana.

M’Cigiriki ndi por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Kutanthauza nkhani za kugonana.

Kapena kuti, “kupatukana ndi mnzake; kusalana ndi mnzake.”

M’cinenelo coyambilila, “anamwali.”

M’cinenelo coyambilila, “kukumangani mu khwekhwe kapena kuti gango.”

M’cinenelo coyambilila, “kusungabe unamwali wake.”

M’cinenero coyambilila, “ulamulilo”

Kapena kuti, “alongo amene ndi akazi athu.”

Wochedwanso Petulo.

Kapena kuti, “kukolola”

Kapena kuti, “ufulu.”

Kapena kuti, “kulanga; kukhaulitsa.”

Kapena kuti, “wopelewela.”

Kapena kuti, “linali.”

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

M’cinenelo coyambilila, “mngelo woononga.”

Kapena kuti, “sicikukuphunzitsani.”

Kapena kuti, “Cakudya Camadzulo ca Ambuye.”

Ayenela kuti akutanthauza kufa kuuzimu.

Kapena kuti, “Cakudya Camadzulo ca Ambuye.”

M’cinenelo coyambilila, “pamene munali anthu a mitundu ina.”

Kapena kuti, “zinenelo.”

Kapena kuti, “tinamwetsedwa.”

Kapena kuti, “omasulila zinenelo.”

Kapena kuti, “pitilizani kufuna-funa mwakhama.”

Kapena kuti, “cakukhosi.”

Kapena kuti, “kulankhula zinenelo zina mozizwitsa.”

Galasi yake inali ya citsulo.

M’cinenelo coyambilila, “malilime.”

Kapena kuti, “ndi maganizo anga.”

M’cinenelo coyambilila, “lilime.”

M’cinenelo coyambilila, “lilime.”

M’cinenelo coyambilila, “malilime.”

M’cinenelo coyambilila, “kulankhula mumpingo.”

Mabaibo ena amati, “ngati wina sakudziwa zinthu, adzakhalabe wosadziwa zinthu.”

Kapena kuti, “m’zinenelo zacilendo.”

Wochedwanso Petulo.

Kapena kuti, “anagona mu imfa.”

Kutanthauza kukhala ndi moyo ndi colinga coti adzafe ali okhulupilika kwa Mulungu.

Ma Baibo ena amati, “monga mmene anthu ena amaonela.”

Kapena kuti, “mbola yako ili kuti?”

Kuluma monga kwa cinkhanila.

Kapena kuti, “Mbola imene imabweletsa imfa,”

M’cinenelo coyambilila, “mwacamuna.”

M’cinenelo coyambilila, “zipatso zoyambilila.”

M’cinenelo coyambilila, “kisi yoyela.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani