LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • nwt 2 Akorinto 1:1-13:14
  • 2 Akorinto

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 2 Akorinto
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
2 Akorinto

KALATA YACIWILI KWA AKORINTO

1 Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa cifunilo ca Mulungu, ndili limodzi ndi Timoteyo m’bale wathu, ndipo ndikulembela mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, kuphatikizapo oyela onse okhala m’cigawo conse ca Akaya.

2 Cisomo ndi mtendele zocokela kwa Mulungu Atate wathu komanso kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, zikhale nanu.

3 Atamandike Mulungu komanso Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Tate wacifundo cacikulu, Mulungu amene amatitonthoza pa bvuto lililonse. 4 Iye amatitonthoza* pa mayeso* athu onse, kotelo kuti ifenso tizitonthoza ena pa mayeso* alionse ndi citonthozo cocokela kwa Mulungu. 5 Pamene tikukumana ndi zowawa zoculuka cifukwa ca Khristu, timalandilanso citonthozo coculuka kudzela mwa Khristuyo. 6 Tikamakumana ndi mayeso,* timakumana ndi mayesowo kuti inuyo mutonthozedwe komanso kuti mupeze cipulumutso. Ndipo tikatonthozedwa, inunso mutonthozedwe cifukwa mumathandizika kupilila zowawa zimene ifenso tikukumana nazo. 7 Ciyembekezo cathu pa inu sicikugwedezeka, pakuti tikudziwa kuti mukukumana ndi zowawa ngati zathu, inunso mudzatonthozedwa.

8 Abale, tikufuna kuti mudziwe, za masautso amene tinakumana nao m’cigawo ca Asia. Mabvuto oposa msinkhu wathu anatipsyinja kwambili, moti tinali kukaikila ngati tipulumuke. 9 Ndipotu tinamva ngati atiweluza kuti tiphedwe. Zinatelo kuti tisadzidalile, koma tizidalila Mulungu amene amaukitsa akufa. 10 Iye anatipulumutsa ku zinthu zimene zikanatipha, ndipo adzatipulumutsanso. Sitikukaikila kuti adzapitiliza kutipulumutsa. 11 Inunso mungathandizepo mwa kutipelekela mapemphelo ocondelela, kuti pakhale anthu ambili otipelekela mapemphelo oyamikila thandizo limene Mulungu amapeleka, poyankha mapemphelo a anthu ambili.

12 Cifukwa cimene timadzitamandila ndi ici, cikumbumtima cathu cikuticitila umboni kuti m’dzikoli, tacita zinthu zoyela maka-maka kwa inuyo, mogwilizana ndi kuona mtima kocokela kwa Mulungu. Tacita izi, osati ndi nzelu za m’dzikoli, koma cifukwa ca cisomo ca Mulungu. 13 Pakuti sitikukulembelani zinthu zimene simungathe kuzimvetsa, koma zokhazo zimene mungathe kuziwelenga* ndi kuzimvetsa. Ndipo ndikhulupilila kuti zinthu zimenezi mupitiliza kuzimvetsa mokwanila.* 14 Monga mmene ena a inu mukudziwila kale, mukudzitamandila cifukwa ca ife ngati mmene ifenso tidzadzitamandile cifukwa ca inu pa tsiku la Ambuye wathu Yesu.

15 Conco ndi cidalilo cimeneci, ndinali kufuna kuti ndibwele kwa inu coyamba, kuti mudzakhalenso ndi mwai wina wosangalala.* 16 Cifukwa ndinali kufuna kuti paulendo wanga wopita ku Makedoniya ndidzadutsile kwanuko kudzakucezelani. Ndipo pocoka ku Makedoniya ndinali kufuna kuti ndidzadutsilenso kumekeko, kenako mudzandipelekeze popita ku Yudeya. 17 Pamene ndinali ndi colinga cimeneci, sindinaone nkhaniyi mopepuka. Zimene ndinali kufuna kucita sindinali kufuna kuzicita ndi colinga cadyela, kuti ndikati “Inde” nthawi yomweyo n’kusintha n’kukamba kuti “Ai.” 18 Koma khulupililani Mulungu kuti zimene tinakamba n’zoona. Sitingakuuzeni kuti “inde” kenako n’kusintha n’kunena kuti “ai.” 19 Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene ine, Silivano,* ndi Timoteyo tinalalikila za iye, sakamba kuti “inde” kenako “ai,” koma iye akati “inde” amakhalabe “inde.” 20 Pakuti kaya malonjezo a Mulungu akhale oculuka cotani, amakhala “inde” kupitila mwa iye. Cotelo kudzela mwa iye timanena “Ameni” kwa Mulungu kuti Mulungu alandile ulemelelo kudzela mwa ife. 21 Koma Mulungu ndi amene amatitsimikizila kuti inu ndi ife tili a Khristu. Iye ndi amene anatidzoza. 22 Iye watidinda cidindo cake. Cidindo cimeneci ndi mzimu woyela umene uli m’mitima yathu, ndipo cidindico cili ngati cikole ca madalitso a m’tsogolo.

23 Mulungu ndiye mboni yanga kuti cifukwa cimene sindinabwelele ku Korinto mpaka pano, n’cakuti sindinafune kuonjezela cisoni canu. 24 Sikuti ndife olamulila cikhulupililo canu ai, koma ndife anchito anzanu kuti muzisangalala, pakuti ndinu okhazikika cifukwa ca cikhulupililo canu.

2 Pakuti ndatsimikiza mtima kuti ndisadzabwelenso kwa inu ndili wacisoni. 2 Ngati ndingakumvetseni cisoni nonsenu, palibe amene adzandisangalatsa kupatulapo inuyo amene ndakumvetsani cisoni. 3 Ndinalemba zonse zija kuti ndikadzafika kumeneko ndisadzakhale wacisoni cifukwa ca anthu amene ndiyenela kusangalala nao. Ndili ndi cikhulupililo kuti zimene zimandisangalatsa, zimasangalatsanso inu nonse. 4 Ndinakulembelani kalata ija ndili wosautsika, komanso ndikubvutika kwambili mumtima, kwinaku ndikugwetsanso misozi, osati kuti mucite cisoni, koma kuti mudziwe kuzama kwa cikondi cimene ndili naco pa inu.

5 Ngati wina wacita zinthu zomvetsa cisoni, sanamvetse ine cisoni, koma kwenikweni wamvetsa cisoni inu nonse. Komabe sindikufuna kukamba mwamphamvu za nkhani imeneyi. 6 Cidzudzulo copelekedwa ndi anthu ambili n’cokwanila kwa munthu wotelo. 7 Tsopano mukhululukileni mocokela pansi pa mtima ndipo mumutonthoze, kuti iye asakhale ndi cisoni copitilila malile n’kutaya* naco mtima. 8 Conco ndikukulimbikitsani kuti mum’tsimikizile kuti mumam’konda. 9 Ici ndiye cifukwa cakenso ndinakulembelani kuti ndidziwe ngati mumamvela pa zinthu zonse. 10 Ngati mwakhululukila munthu wina ciliconse, inenso ndimukhululukila. Ndipo ciliconse cimene ndakhululukila munthu (ngati cilipo cinthu cimeneco) ndatelo cifukwa ca inu pamaso pa Khristu, 11 kuti Satana asaticenjelele, pakuti ife sindife mbuli ku ziwembu zake.*

12 Tsopano nditafika ku Torowa kuti ndilengeze uthenga wabwino wonena za Khristu, komanso mwai wogwila nchito ya Ambuye utanditsegukila, 13 mtima wanga sunakhazikike cifukwa coti sindinamupeze m’bale wanga Tito. Conco ndinatsanzikana ndi abale kumeneko n’kupita ku Makedoniya.

14 Alemekezeke Mulungu amene nthawi zonse amatitsogolela pamodzi ndi Khristu, ngati kuti tikuguba pa cionetselo conyadila kupambana. Ndipo kupitila mwa ife, kapfungo konunkhila bwino kodziwa Mulungu kakufalikila konse-konse. 15 Pakuti kwa Mulungu ndife kapfungo kabwino konunkhila ka uthenga wabwino wa Khristu, kwa amene akupita ku cipulumutso komanso amene akupita kucionongeko. 16 Tsopano kwa amene akupita kukaonongedwa, ndife pfungo la imfa lotsogolela ku imfa. Koma kwa amene akupulumutsidwa, ndife kapfungo kabwino kotsogolela ku moyo. Ndipo ndani ali woyenela kugwila nchito imeneyi? 17 Ndife oyenelela. Pakuti siticita nao malonda mau a Mulungu monga mmene anthu ambili amacitila, koma timalalikila moona mtima monga otumidwa ndi Mulungu pamodzi ndi Khristu pamaso pa Mulungu.

3 Kodi tayambanso kudzicitila tokha umboni? Kapena tikufunikila makalata oticitila umboni obwela kwa inu kapena ocokela kwa inu mofanana ndi anthu ena? 2 Inuyo ndinu kalata yathu, yolembedwa pamitima yathu, yodziwika komanso yowelengedwa ndi anthu onse. 3 Pakuti n’zoonekelatu kuti inu ndinu kalata yocokela kwa Khristu yolembedwa ndi ife atumiki a Mulungu. Kalatayo si yolembedwa ndi inki, koma ndi mzimu wa Mulungu wamoyo. Si yolembedwa pa miyala koma m’mitima.*

4 Tingakambe zimenezi molimba mtima pamaso pa Mulungu kudzela mwa Khristu. 5 Sitingakambe kuti ndife oyenelela kwambili kugwila nchitoyi cifukwa ca mphamvu zathu ai, koma ndife oyenelela kwambili cifukwa ca Mulungu, 6 ndipo iye anationa kuti ndife oyenela kukhala atumiki a cipangano catsopano osati mwa malamulo olembedwa koma mwa mzimu. Pakuti malamulo olembedwa amapha, koma mzimu umapatsa munthu moyo.

7 Malamulo amene amabweletsa imfa, amenenso analembedwa pa miyala, anabwela ndi ulemelelo waukulu moti Aisiraeli sanakwanitse kuyang’anitsitsa nkhope ya Mose cifukwa inali kuwala ndi ulemelelo umene unatha patapita nthawi. 8 Kodi si ndiye kuti mzimu uyenela kupelekedwa ndi ulemelelo waukulu kuposa pamenepa? 9 Ngati malamulo oweluza anthu kuti alangidwe anapelekedwa ndi ulemelelo, ndiye kuti cilungamo ciyenela kupelekedwa ndi ulemelelo woposa pamenepo. 10 Ndipo ngakhale kuti malamulo olembedwa anapatsidwa ulemelelo, ulemelelo wake wacotsedwa cifukwa ulemelelo umene wabwela pambuyo pake ndi waukulu kuposa woyambawo. 11 Ngati malamulo olembedwa amene anatha patapita nthawi anapelekedwa ndi ulemelelo, ndiye kuti malamulo amene sadzatha adzakhala ndi ulemelelo waukulu kuposa pamenepo.

12 Popeza tili ndi ciyembekezo cimeneci, tili ndi ufulu waukulu wakulankhula. 13 Siticita zimene Mose anacita amene anaphimba nkhope yake ndi nsalu, kuti ana a Isiraeli asaone kutha kwa ulemelelo wosakhalitsawo. 14 Ndipo maganizo ao anacita khungu. Pakuti mpaka lelo, nsaluyo imakhalabe yophimba pamene akuwelenga cipangano cakale cija, cifukwa nsaluyo imacotsedwa kokha kudzela mwa Khristu. 15 Ndipo mpaka pano, akamawelenga zimene Mose analemba, mitima yao imakhalabe yophimba. 16 Koma munthu akasintha n’kutembenukila kwa Yehova, cophimbaco cimacotsedwa. 17 Yehova ndi Mzimu, ndipo pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu. 18 Tonsefe tili ndi nkhope zosaphimba, ndipo tili monga magalasi oonela amene amaonetsa ulemelelo wa Yehova. Tikamaonetsa ulemelelo umenewo, timasintha kukhala ngati cifanizilo cake, ndipo timaonetsa ulemelelo woonjezeleka-onjezeleka* mofanana ndendende ndi mmene Yehova, amene ndi Mzimu,* watisinthila.

4 Conco, popeza tili ndi utumiki umenewu mwa cifundo cimene anaticitila, sititaya mtima. 2 Koma taleka zinthu zocititsa manyazi zocitikila mseli, ndipo sitiyenda mwacinyengo kapena kuipitsa mau a Mulungu. Koma podziwikitsa coonadi, takhala citsanzo cabwino kwa munthu aliyense pamaso pa Mulungu. 3 Ndipo ngati uthenga wabwino umene tikulalikila ndi wophimbika, ndi wophimbika kwa anthu amene akupita kucionongeko. 4 Pakati pa anthu amenewa, mulungu wa nthawi ino wacititsa khungu maganizo a anthu osakhulupilila kuti asaone kuwala kwa uthenga wabwino waulemelelo wokamba za Khristu yemwe ndi cifanizilo ca Mulungu. 5 Pakuti sitikulalikila za ife koma za Yesu Khristu, kuti ndi Ambuye ndipo ife ndife akapolo anu cifukwa ca Yesu. 6 Popeza Mulungu ndiye anakamba kuti: “Kuwala kuunike kucokela mu mdima.” Iye waunika mitima yathu kuti ikhale yowala. Wacita zimenezi mwa kugwilitsa nchito cidziwitso caulemelelo ca Mulungu kudzela pa nkhope ya Khristu.

7 Koma tili ndi cuma cimeneci m’ziwiya zadothi,* kuti mphamvu yoposa yacibadwa icokele kwa Mulungu, osati kwa ife. 8 Timapanikizika m’njila zosiyana-siyana, koma osati mpaka kufika popsyinjika moti n’kulephela kusuntha. Timathedwa nzelu, koma osati mpaka kusowelatu kothawila.* 9 Timazunzidwa, koma sitisiyidwa tokha. Timagwetsedwa, koma sitiphwanyika.* 10 Nthawi zonse timapilila mazunzo amene tingafe nao ngati aja amene Yesu anapilila, ndipo timacita zimenezi kuti moyo umene Yesu anali nao uonekelenso mwa ife.* 11 Pakuti ife amene tili moyo, nthawi zonse timayang’anizana ndi imfa cifukwa ca Yesu, n’colinga cakuti moyo wa Yesu uonekelenso m’matupi athu amene angafe. 12 Conco ife tili pa ciopsezo cakuti tikhoza kufa, koma inu moyo ndi wanu.

13 Tsopano ife tili ndi cikhulupililo* mofanana ndi zimene zinalembedwa kuti: “Ndinali ndi cikhulupililo, n’cifukwa cake ndinalankhula.” Nafenso tili ndi cikhulupililo, n’cifukwa cake timalankhula, 14 podziwa kuti amene anaukitsa Yesu ifenso adzatiukitsa mmene anacitila ndi Yesu, ndipo iye adzatipeleka kwa Yesu pamodzi ndi inu. 15 Zonsezi zacitika kaamba ka ubwino wanu, kuti cisomo ca Mulungu cimene cikuonjezeka, cionjezekebe cifukwa anthu ambili akupeleka mapemphelo oyamikila, ndipo izi zikupeleka ulemelelo kwa Mulungu.

16 Conco sititaya mtima, ngakhale kuti munthu wathu wakunja akutha, mosakaika munthu wathu wamkati akukhala watsopano tsiku ndi tsiku. 17 Ndipo ngakhale kuti masautso* amene tikukumana nao ndi akanthawi komanso opepuka, amacititsa kuti tilandile ulemelelo umene ukuonjezeka-onjezekela, umenenso ndi wamuyaya. 18 Pamene tikuika maso athu pa zinthu zosaoneka, osati pa zinthu zooneka, cifukwa zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.

5 Tikudziwa kuti nyumba yathu ya padziko lapansi kapena kuti tenti ino ikadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba yocokela kwa Mulungu. Nyumba imeneyo siidzakhala yomangidwa ndi manja, koma yamuyaya ndipo idzakhala kumwamba. 2 M’nyumba imene tikukhalamoyi timabuula, ndipo tikufunitsitsa kubvala nyumba yathu ya kumwamba, 3 kuti tikadzaibvala nyumbayo, tisakapezeke amalisece. 4 Ndipo ife amene tili mu tenti iyi timabuula komanso kulemedwa, cifukwa sitikufuna kuibvula ai, koma tikufuna kubvala nyumba inayo, kuti thupi limene lingafeli, lilowedwe m’malo ndi moyo. 5 Amene anatikonzekeletsa zinthu zimenezi ndi Mulungu, ndipo ndi amenenso anatipatsa mzimu monga cikole ca zinthu zakutsogolo.*

6 Conco timalimba mtima nthawi zonse, ndipo tikudziwa kuti malinga ngati nyumba yathu ili m’thupi, timakhala kutali ndi Ambuye. 7 Cifukwa tikuyenda mwa cikhulupililo, osati mwa zooneka ndi maso. 8 Tikulimba mtima ndipo tingakonde kukhala ndi Ambuye m’malo mokhala m’thupili. 9 Conco kaya tikhale pafupi ndi iye kapena tikhale kutali ndi iye, colinga cathu n’cakuti tikhale obvomelezeka kwa iye. 10 Pakuti tonse tiyenela kudzaonekela ku mpando wa Khristu woweluzila milandu, n’colinga cakuti aliyense alandile mphoto yake malinga ndi zimene anacita ali m’thupi, kaya zabwino kapena zoipa.

11 Cotelo, popeza tikudziwa kuti Ambuye ayenela kuopedwa, tikupitiliza kukopa anthu, ndipo Mulungu akudziwa bwino zolinga zathu. Komabe ndikhulupilila kuti inunso cikumbumtima canu cikudziwa bwino zolinga zathu. 12 Sikuti tayambanso kudzicitila tokha umboni kwa inu. Koma tikukupatsani cifukwa codzitamandila pa ife, kuti muthe kuyankha amene amadzitama cifukwa ca maonekedwe akunja, osati zimene zili mumtima. 13 Ngati tinacita ngati ofuntha, tinacita zimenezo kuti tikondweletse Mulungu. Koma ngati maganizo athu ali bwino-bwino, ndi zothandiza kwa inu. 14 Pakuti cikondi cimene Khristu ali naco cimatikakamiza, cifukwa ife tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafela anthu onse, cifukwa onse anali atafa kale. 15 Iye anafela anthu onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma wosangalatsa amene anawafela n’kuukitsidwa.

16 Kuyambila tsopano, sitiona munthu aliyense mwakuthupi. Ngakhale kuti Khristu tinamuonapo mwakuthupi, tsopano sitikumuonanso motelo. 17 Conco, ngati aliyense ndi wogwilizana ndi Khristu, ndiye kuti ndi colengedwa catsopano. Zinthu zakale zinacoka, ndipo pabwela zinthu zatsopano. 18 Koma zinthu zonse zicokela kwa Mulungu, amene anatithandiza kuti tiyanjanenso naye kudzela mwa Khristu, ndipo anatipatsa utumiki wothandiza anthu kuti ayanjanenso ndi Mulungu. 19 Utumiki wake ndi wakuti tilalikile zakuti Mulungu akuyanjanitsa dziko kwa iye kudzela mwa Khristu, moti Mulungu sanawelengele anthuwo zolakwa zao, ndipo watipatsa nchito yolengeza uthenga wothandiza anthu kuyanjananso ndi iye.

20 Cotelo, ndife akazembe moimilako Khristu, monga kuti Mulungu akucondelela anthu kupitila mwa ife. Monga akazembe a Khristu, tikucondelela anthu powauza kuti: “Yanjananinso ndi Mulungu.” 21 Munthu amene anali wopanda ucimoyo, Mulungu anamusandutsa kukhala ucimo* cifukwa ca ife, kuti kudzela mwa iye, Mulungu ayambe kutiona kuti ndife olungama.

6 Pamene tikugwila nchito naye limodzi, tikukulimbikitsani kuti musalandile cisomo ca Mulungu n’kuphonya colinga ca cisomoco. 2 Cifukwa iye anati: “Pa nthawi yobvomelezeka ndinakumvela, ndipo pa tsiku la cipulumutso ndinakuthandiza.” Ndithudi, ino ndiyo nthawi yeniyeni yobvomelezeka. Lelo ndilo tsiku la cipulumutso.

3 Sitikucita ciliconse cokhumudwitsa, kuti anthu asaupeze cifukwa utumiki wathu . 4 Koma m’njila iliyonse, tikuonetsa kuti ndife atumiki a Mulungu. Tikucita zimenezi popilila mabvuto ambili, pokumana ndi masautso, pokhala opanda zinthu zofunikila, pokumana ndi zobvuta, 5 pomenyedwa, poikidwa m’ndende, pokumana ndi zipolowe, pogwila nchito mwakhama, posagona tulo, komanso posowa cakudya. 6 Tikucitanso zimenezi mwa kukhala oyela, acidziwitso , oleza mtima, okoma mtima, potsogoleledwa ndi mzimu woyela, poonetsa cikondi copanda cinyengo, 7 polankhula zoona, komanso pokhala ndi mphamvu ya Mulungu. Ndiponso tikucita zimenezi ponyamula zida zacilungamo kudzanja lamanja komanso lamanzele, 8 popatsidwa ulemelelo komanso ponyozedwa, poneneledwa zoipa komanso zabwino. Timaonedwa ngati anthu acinyengo koma ndife acilungamo, 9 ngati osadziwika koma ndife odziwika bwino, ngati kuti tikufa koma tikukhalabe ndi moyo, ngati olandila cilango koma osapita kukaphedwa, 10 ngati acisoni koma acimwemwe nthawi zonse, ngati osauka koma olemeletsa anthu oculuka, ngati anthu opanda kalikonse koma okhala ndi zinthu zonse.

11 Tatsegula pakamwa pathu kuti tilankhule ndi inu* Akorinto, ndipo tafutukula mtima wathu. 12 Ife sitimaumila pokuonetsani cikondi, koma inu mumaumila potionetsa cikondi. 13 N’cifukwa cake ndikulankhula nanu ngati ana anga, kuti inunso muzifutukula mitima yanu.*

14 Musamangidwe mu joko ndi anthu osakhulupilila, cifukwa ndinu osiyana. Kodi pali mgwilizano wanji pakati pa cilungamo ndi kuphwanya malamulo? Kapena pali kugwilizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima? 15 Komanso pali mgwilizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?* Kapena munthu wokhulupilila* angagawane ciani ndi munthu wosakhulupilila? 16 Ndipo pali kugwilizana kotani pakati pa kacisi wa Mulungu ndi mafano? Pakuti ife ndife kacisi wa Mulungu wamoyo, monga mmene Mulungu anakambila kuti: “Ndidzakhala pakati pao komanso kuyenda pakati pao. Ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwo adzakhala anthu anga.” 17 “‘Conco cokani pakati pao ndipo mulekane nao,’ watelo Yehova. ‘Musakhudze cinthu codetsedwa,’” “‘ndipo ine ndidzakulandilani.’” 18 “‘Ndidzakhala atate wanu ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’ watelo Yehova Wamphamvuzonse.”

7 Conco okondedwa, popeza anatilonjeza zinthu zimenezi, tiyeni tidziyeletse mwa kucotsa ciliconse codetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyela poopa Mulungu.

2 Tipezeleni malo m’mitima yanu.* Ife sitinalakwile munthu aliyense, sitinaipitse aliyense, komanso sitinadyele masuku pamutu munthu aliyense.* 3 Sindikukamba izi kuti ndikuimbeni mlandu ai. Pakuti ndanena kale kuti inuyo muli m’mitima yathu, kuti tifele limodzi kapena tikhale moyo limodzi. 4 Ndili ndi ufulu waukulu wolankhula kwa inu. Ndipo ndimakunyadilani kwabasi. Ndalimbikitsidwa koposa, ndipo ndikusefukila ndi cimwemwe pa mabvuto onse amene tikukumana nao.

5 Titafika ku Makedoniya sitinapumule koma tinapitiliza kukumana ndi masautso osiyana-siyana, monga anthu kutiukila komanso kudela nkhawa abale. 6 Koma Mulungu amene amalimbikitsa anthu opsyinjika mtima, anatilimbikitsa ndi kufika kwa Tito. 7 Komabe cimene cinatilimbikitsa si kufika kwake kokha ai, koma mmenenso inu munamulimbikitsila. Iye anatibweletselanso uthenga wakuti mukufunitsitsa kundiona, muli ndi cisoni kwambili, ndiponso kuti mukundidela nkhawa. Zimenezi zinandisangalatsanso koposa.

8 Ngakhale kuti ndinakumvetsani cisoni ndi kalata yanga, sindikudziimba mlandu kuti ndinailembelanji. Ngakhale kuti poyamba ndinadziimba mlandu, (ndikuona kuti kalatayo inakumvetsani cisoni, koma kwa kanthawi kocepa). 9 Pano ndikusangalala, osati cifukwa ndinakumvetsani cisoni, koma cifukwa cakuti cisoni canuco cinakuthandizani kulapa. Popeza munamva cisoni ca umulungu, zimene tinalembazo sizinakubvulazeni. 10 Cisoni ca umulungu cimathandiza munthu kulapa kuti apeze cipulumutso, popanda munthuyo kudziimba mlandu. Koma cisoni ca dzikoli cimabweletsa imfa. 11 Taonani cangu cacikulu cimene cisoni canu ca umulungu cabala mwa inu. Cabala mtima wofuna kudziyeletsa, kuipidwa nazo zolakwa, kuopa Mulungu, kufunitsitsa kulapa, kukangalika, komanso kukonza zolakwazo. Mwaonetsadi m’njila iliyonse kuti ndinu oyela* pa nkhani imeneyi. 12 Conco pokulembelani, sindinalembe cifukwa ca amene analakwayo, kapena amene analakwilidwayo ai. Ndinatelo kuti khama lanu lofuna kutimvetsela lionekele pakati panu, pamaso pa Mulungu. 13 Zimenezi zatilimbikitsa kwambili.

Kuonjezela pa kulimbikitsidwa kwathuko, tinakondwela kwambili poona cimwemwe ca Tito, cifukwa nonsenu munamusangulutsa. 14 Ndinamuuzadi kuti ndimakunyadilani, ndipo inu simunandicititse manyazi. Conco zonse zimene tinakuuzani zinali zoona. Nazonso zimene tinauza Tito zakuti timakunyadilani, n’zoona. 15 Ndipo cikondi cake pa inu cimakula kwambili akakumbukila kuti nonsenu munali omvela ndipo munamulandila ndi ulemu waukulu. 16 Ndine wokondwa kuti ndingathe kukukhulupililani pa zonse.*

8 Tsopano abale, tikufuna kuti mudziwe za cisomo cimene Mulungu wacitila mipingo ya ku Makedoniya. 2 Panthawi ya kusautsika kwao, ndi mayeso aakulu, iwo anakhala owolowa manja mwacimwemwe cosefukila, ngakhale kuti anali pa umphawi wadzaoneni. 3 Ndikucitila umboni kuti anapeleka malinga n’kupeza kwao kopelewelako, moti anacita zoposa pamenepo. 4 Iwo okha anacita kuticondelela kuti apatsidwe mwai wopeleka thandizo, kuti naonso aciteko utumiki wothandiza oyelawo. 5 Ndipo anathandizadi kuposa mmene tinali kuyembekezela. Coyamba anadzipeleka kwa Ambuye, kenako anadzipelekanso kwa ife mwa cifunilo ca Mulungu. 6 Conco tinalimbikitsa Tito kuti, popeza iye ndiye anayambitsa nchito yosonkhanitsa zopeleka zanu, iye ayenela kumalizitsanso nchito yotolela mphatso zanu zacifundo. 7 Inu mukucita bwino koposa pa ciliconse, monga pa cikhulupililo, luso la kulankhula, cidziwitso, pa khama, komanso mumakonda ena mmene ife timakukondelani. Conco, pa nkhani ya kupeleka, mucitenso cimodzi-modzi.

8 Sindikukamba izi mokulamulani ai, koma ndifuna kuti mudziwe za khama limene ena aonetsa, komanso kuti ndione ngati cikondi canu ndi ceniceni. 9 Pakuti mukudziwa cisomo ca Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemela, iye anakhala wosauka cifukwa ca inu, kuti kudzela mu umphawi wake, mukhale olemela.

10 Malangizo anga pamenepa ndi awa: Mungacite bwino kumalizitsa nchito ya zopelekayi imene munaiyamba caka catha cifukwa munaonetsa kale mtima wofunitsitsa kucita zimenezi. 11 Conco malizitsani nchito imene munaiyamba. Pakuti munali ofunitsitsa kucita zimenezi, mumalizitsenso kuzicita malinga ndi zimene muli nazo. 12 Mulungu amakondwela nayo mphatso yocokela pansi pa mtima, cifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apeleke zimene angakwanitse, osati zimene sangakwanitse. 13 Sindikufuna kuti zinthu zikhale zopepuka kwa ena, koma zobvuta kwa inu. 14 Koma ndikufuna kuti zinthu zambili zimene muli nazo palipano, zithandizile pa zimene iwo alibe, komanso zinthu zambili zimene iwo ali nazo, zithandizile pa zimene inu mulibe kuti pakhale kufanana. 15 Monga mmene Malemba amakambila kuti: “Munthu amene anali ndi zambili sanakhale ndi zoculuka kupitilila muyeso, ndipo amene anali ndi zocepa, sanakhale ndi zocepa kwambili.”

16 Tikuyamika Mulungu pothandiza Tito kuti azikudelani nkhawa moona mtima monga mmene ifeyo timacitila. 17 Popeza iye walandila cilimbikitso cimene tinamupatsa, ndipo akufunitsitsa kuthandiza, akubwela kwa inu mwa kufuna kwake. 18 Koma tikumutumiza limodzi ndi m’bale wina amene mipingo yonse ikumutamanda cifukwa ca nchito zimene akucita zokhudzana ndi uthenga wabwino. 19 Cinanso, mipingo inasankha m’bale ameneyu kuti aziyenda nafe limodzi pamene tikupeleka mphatso zacifundozi kuti Ambuye alandile ulemelelo, komanso kuti tionetse kuti ndife okonzeka kuthandiza ena. 20 Conco, sitikufuna aliyense kutikaikila pa kayendetsedwe ka zopeleka zacifundo zoculukazi zimene tikubweletsa. 21 Tikucita zimenezi cifukwa ‘tikufuna kusamalila zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha, koma ngakhale pamaso pa anthu.’

22 Abalewa tikuwatumizanso limodzi ndi m’bale wathu amene tamuyesa mobweleza-bweleza, ndipo waonetsa kuti ndi wakhama pa zinthu zambili. Panopa iye waonetsanso kuti ndi wakhama cifukwa amakudalilani kwambili. 23 Koma ngati mukumukaikila Tito pa ciliconse, ndikufuna ndikutsimikizileni kuti iye ndi mnzanga komanso wanchito mnzathu pokuthandizani. Ngatinso mukuwakaikila abale athu enawo, iwo ndi otumidwa ndi mipingo ndipo Khristu amalandila ulemelelo cifukwa ca iwo. 24 Conco aonetseni kuti mumawakonda, komanso onetsani mipingo cifukwa cake timakunyadilani.

9 Ponena za utumiki wothandiza oyelawo, m’posafunikila kuti ndicite kukulembelani. 2 Cifukwa ndikudziwa kuti muli ndi mtima wofunitsitsa, ndipo ndikunena zimenezi kwa anthu a ku Makedoniya mocita kunyadila. Ndakhala ndikuwauza kuti abale a ku Akaya akhala okonzeka kwa caka cimodzi tsopano, ndipo kudzipeleka kwanu kwalimbikitsa abale oculuka kumeneko. 3 Koma ndikutumiza abale kuti kukunyadilani kwathu kusapite pacabe pa nkhani imeneyi, koma kuti mukhalebe okonzeka monga momwe ndinanenela. 4 Pakuti ngati ndabwela kumeneko ndi anthu a ku Makedoniya n’kupeza kuti sindinu okonzeka, ifeyo ndi inuyo, tingadzacite manyazi cifukwa tikukudalilani kuti ndinu okonzeka. 5 Conco ndaona kuti ndi bwino kuti ndipemphe abale kuti atsogole kubwela kwa inu ife tisanafike, kuti akuthandizeni kukonzelatu mphatso ija imene munalonjeza kuti mudzaipeleka mowolowa manja. Cotelo mphatsoyo idzakhala yokonzelatu, ndipo mudzaipeleka mowolowa manja, osati mokakamizika.

6 Pa nkhani imeneyi, aliyense amene akubzala moumila adzakololanso zocepa. Ndipo aliyense amene akubzala mowolowa manja adzakololanso zoculuka. 7 Aliyense acite malinga ndi zimene watsimikiza mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu amene amapeleka mocokela pansi pa mtima.

8 Komanso Mulungu angathe kukuonetsani cisomo cake kuti musasowe zinthu zofunikila pa umoyo wanu, ndiponso kuti mukhale ndi zinthu zambili zokuthandizani kugwila nchito iliyonse yabwino. 9 (Monga mmene Malemba amakambila kuti: “Iye wapeleka mphatso zake mowolowa manja kwa osauka, cilungamo cake cidzakhalapo mpaka muyaya.” 10 Tsopano Mulungu amene amapeleka mbeu mosaumila kwa obzala, komanso cakudya kuti anthu adye, adzakupatsani ndi kuculukitsa mbeu zoti mubzale. Ndipo adzaculukitsanso zokolola zanu za cilungamo.) 11 Pa ciliconse, Mulungu adzakudalitsani kuti mukhale owolowa manja pa zonse, ndipo kudzela m’kuwolowa manja kwanu anthu adzatamanda Mulungu. 12 Cifukwa utumiki wothandiza anthu umenewu, sikuti ukungothandiza oyelawa kuti apeze zimene akufunikila ai, koma ukuthandizanso kuti anthu oculuka aziyamika Mulungu m’mapemphelo ao. 13 Cifukwa ca umboni umene utumiki umenewu ukupeleka, anthuwo akulemekeza Mulungu. Zili conco cifukwa inu mwagonjela uthenga wabwino wokamba za Khristu umene mukuulengeza poyela. Komanso mwawagawila mowolowa manja iwowo ndi anthu onse. 14 Iwo amakupemphelelani mocondelela kwa Mulungu, ndipo amaonetsa kuti amakukondani cifukwa ca cisomo cimene Mulungu wakucitilani.

15 Tikuyamika Mulungu cifukwa ca mphatso yake yaulele yosatheka kuifotokoza.

10 Tsopano ine Paulo, ndikukudandaulilani mwa kufatsa ndi kukoma mtima kwa Khristu. Ine amene anthu ena amati ndine wofooka ndikamalankhula nanu pamaso m’pamaso, koma wolimba mtima ndikamalankhula nanu ndikakhala kwina. 2 Ndikhulupilila kuti ndikadzafika kumeneko, anthu ena amene akuona kuti ife tinacita zinthu ngati anthu a m’dzikoli adzakhala atasintha kuti ndisadzawadzudzule mwamphamvu. 3 Ngakhale kuti moyo wathu ndi wofanana ndi wa anthu ena onse, sitikumenya nkhondo motsatila maganizo a m’dzikoli. 4 Pakuti zida zathu za nkhondo si zida za m’dzikoli, koma ndi zida zamphamvu zimene Mulungu watipatsa kuti tizigwetsela zinthu zozikika molimba. 5 Pakuti tikugubuduza maganizo komanso cochinga ciliconse cotsutsana ndi kudziwa Mulungu, ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvela Khristu. 6 Komanso ndife okonzeka kupeleka cilango kwa munthu aliyense wosamvela, inu mukaonetsa kuti ndinu omvela pa ciliconse.

7 Mumaona zinthu potengela maonekedwe akunja. Ngati aliyense mumtima mwake amakhulupilila kuti ndi wa Khristu, ndi bwino aziganizilanso mfundo iyi yakuti: Ifenso ndife a Khristu ngati mmene munthuyo alili. 8 Ambuye anatipatsa ulamulilo kuti tikulimbikitseni, osati kukufooketsani. Ndipo ngati ndingadzitamandile mopitililako malile za ulamulilo umenewu, sindingacite manyazi. 9 Pakuti sindikufuna kuoneka ngati ndikukuopsezani ndi makalata anga. 10 Popeza ena amati: “Makalata ake amakhala ndi uthenga wamphamvu, koma mwiniwake akakhala pakati pathu amaoneka wofooka, ndipo zokamba zake n’zogwetsa ulesi.” 11 Anthu a maganizo amenewo adziwe kuti zimene tikunena m’makalata athu tili kutali, tidzacitanso zomwezo tikadzabwela. 12 Pakuti sitidziona ngati ndife ofanana ndi anthu amene amadzikweza, ndiponso sitidziyelekezela ndi anthu amenewo. Koma iwo akamayezana okha-okha posewenzetsa mfundo zao n’kumadziyelekezela okha-okha, samvetsa ciliconse.

13 Komabe ife sitidzadzitamandila pa zinthu zimene zili kunja kwa malile amene anatiikila. Koma tidzadzitamandila pa zinthu zimene zili mkati mwa malile a gawo limene Mulungu watipatsa lomwe linafika mpaka kwanuko. 14 Conco sitikudutsa malile a gawo lathu ngati kuti gawolo silifika kwanuko. Pakuti tinali oyamba ndife kufika kwanuko ndi uthenga wabwino wokamba za Khristu. 15 Sikutinso tikudzitamandila pa nchito ya munthu wina imene ili kunja kwa gawo limene anatipatsa. Koma tili ndi cidalilo kuti cikhulupililo canu cikadzaonjezeka, nayonso nchito yathu idzakula m’gawo lathu. Zikatelo tidzakhala ndi zocita zambili, 16 kuti tikalalikile uthenga wabwino ku maiko akutali kupitilila kwanuko, n’colinga cakuti tisadzitamandile pa nchito imene yagwilidwa kale m’gawo la munthu wina. 17 “Koma amene akudzitama, adzitamandile mwa Yehova.” 18 Pakuti munthu amene amabvomelezedwa, si amene amadziyeneleza yekha, koma amene Yehova wamuyeneleza.

11 Ndikanakonda mukanandilola kuti ndidzikweze pang’ono. Ndipo zoona zake n’zakuti, mwandilola kale. 2 Nsanje imene ndimakucitilani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi, Khristu, kuti ndidzakupelekani kwa iye monga namwali woyela. 3 Koma nkhawa yanga ndi yakuti, monga mmene njoka inapusitsila Hava mocenjela, naonso maganizo anu angapotozedwe ndipo mungasiye kukhala oona mtima komanso oyela, makhalidwe amene munthu wa Khristu ayenela kukhala nao. 4 Pakuti ngati wina wabwela kwa inu ndi uthenga wosiyana ndi umene tinaulalikila, kapena wabweletsa mzimu wosiyana ndi umene munaulandila, kapenanso uthenga wabwino wosiyana ndi umene munaubvomeleza, inu mumangomulandila munthu woteloyo. 5 Koma ndikuona kuti sindine wotsika mwa njila iliyonse poyelekezela ndi atumwi anu apamwambawo. 6 Ngati ndilibe luso la kulankhula, sikuti ndine wosadziwanso zinthu ndipo tinakuonetsani zimenezi m’njila iliyonse komanso pa zinthu zonse.

7 Kodi ndinacimwa pamene ndinadzicepetsa kuti inuyo mukwezedwe, cabe cifukwa cakuti ndinalalikila uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu kwaulele? 8 Ndinalandila thandizo kucokela kumipingo ina, ndipo kucita zimenezo kunali ngati kuwabela kuti ndikutumikileni inuyo. 9 Pamene ndinali nanu ndipo ndinafunikila thandizo, sindinakhale mtolo kwa aliyense wa inu, popeza abale a ku Makedoniya anandipatsa zimene ndinali kufunikila. Ndithu, ndinayesetsa kuti ndisakhale mtolo mwa njila iliyonse, ndipo ndikupitilizabe kutelo. 10 Popeza ndimalankhula coonadi ca Khristu, sindidzasiya kudzitamandila m’madela a ku Akaya. 11 Kodi ndikucita zimenezi pa cifukwa citi? Cifukwa cakuti sindikukondani? Ayi ndithu. Ngakhale Mulungu adziwa kuti ndimakukondani.

12 Ndipitiliza kucita zimene ndikucita, kuti ndisapatse mpata anthu amene akuyesetsa kupeza cifukwa conenela kuti ndi ofanana ndi ife pa zinthu zimene amadzitamandila. 13 Anthu amenewa ndi atumwi onama, anchito acinyengo, ndipo amadzicititsa kuoneka* ngati atumwi a Khristu. 14 Izi n’zosadabwitsa, cifukwa ngakhale Satana amadzicititsa kuoneka* ngati mngelo wakuwala. 15 Conco, n’zosadabwitsa ngati naonso atumiki ake amadzipangitsa kukhala* ngati atumiki acilungamo. Koma mapeto ao adzakhala monga mwa nchito zao.

16 Ndikubwelezanso kunena kuti, wina aliyense asandione ngati wopanda nzelu. Koma ngati mukundionabe kuti ndine wopanda nzelu, mungobvomeleza kuti ndi mmene ndilili, kuti nanenso ndidzitame pang’ono. 17 Zimene ndikunenazi, sindikuzinena ngati munthu wotsatila citsanzo ca Ambuye. Koma ngati munthu wopusa, wodzitama, komanso wodzidalila kwambili. 18 Popeza anthu ambili akudzitama cifukwa ca zinthu za m’dzikoli, inenso ndikudzitama. 19 Popeza mumadziona “anzelu” kwambili, sizimakubvutani kucita nao zinthu anthu opanda nzelu. 20 Ndipo mumalolela aliyense, kaya akupangeni akapolo ake, akutengeleni zinthu zanu, akulandeni zimene muli nazo, adzione kuti ndi wapamwamba kuposa inuyo, ndiponso aliyense amene wakuwazani mbama.

21 Ndikunena izi modzinyoza tokha, popeza ena angaone ngati tacita zinthu mofooka.

Koma ngati anthu ena akucita zinthu molimba mtima, ndikulankhula ngati wopanda nzelu, inenso ndikucita zinthu molimba mtima. 22 Kodi iwo ndi Aheberi? Inenso cimodzi-modzi. Kodi ndi Aisiraeli? Nanenso ndine Mwisiraeli. Kapena iwo ndi mbadwa* za Abulahamu? Inenso cimodzi-modzi. 23 Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankha ngati wamisala, ine ndiye mtumiki wa Khristu woposa iwo. Ndacita nchito zambili kuposa iwo, ndinaponyedwapo m’ndende mobweleza-bweleza, ndinamenyedwa kosawelengeka, ndipo ndinatsala pafupi kufa kambili-mbili. 24 Maulendo asanu Ayuda anandikwapula zikoti 39.* 25 Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandiponya miyala, katatu konse ngalawa inandiswekelapo, kamodzi ndinakhala panyanja usiku ndi masana onse. 26 Ndinayenda maulendo ambili-mbili, ndinakumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za acifwamba, zoopsa kucokela kwa anthu a mtundu wanga, zoopsa zocokela kwa anthu a mitundu ina, ndinakumana ndi zoopsa m’mizinda, m’cipululu, panyanja, ndi pakati pa abale onyenga. 27 Ndinali kugwila nchito zolemetsa komanso zotulutsa thukuta. Nthawi zambili sindinali kugona usiku, ndinali kukhala ndi njala komanso ludzu. Nthawi zambilinso ndinali kukhala wosadya, ndinali kukongwa, komanso ndinalibe zobvala zokwanila.*

28 Kuonjezela pa izi, palinso cinthu cina cimene cimandibvutitsa maganizo tsiku ndi tsiku.* Ndimadela nkhawa mipingo yonse. 29 Ndani angafooke ine osafooka? Ndani angakhumudwitsidwe ine osakwiya nazo?

30 Ngati ndiyenela kudzitama, ndidzadzitamandila pa zinthu zimene zimaonetsa kufooka kwanga. 31 Mulungu komanso Atate wa Ambuye Yesu, amene ndi woyenela kumutamanda mpaka muyaya akudziwa kuti sindikunama. 32 Ku Damasiko, bwanamkubwa wa Areta mfumu anaika alonda pamageti a mzinda wa Damasiko kuti andigwile. 33 Koma anthu anandiika m’dengu n’kunditsitsila pawindo ya mpanda wa mzindawo, ndipo ndinapulumuka m’manja mwake.

12 Ndiyenela kudzitama ndithu. N’zoona kuti kudzitama kulibe phindu, koma lekani ndilankhule nkhani yokhudza masomphenya ndi mabvumbulutso ocokela kwa Ambuye. 2 Ndikudziwa munthu wina wogwilizana ndi Khristu. Zaka 14 zapitazo, munthuyu anatengedwa ndi kupita naye kumwamba kwacitatu. Kaya anatengedwa ali ndi thupi lake lenileni kapena ai, sindikudziwa. Akudziwa ndi Mulungu. 3 Ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati anatengedwa ali ndi thupi lake lenileni kapena ai, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. 4 Munthuyo anatengedwa n’kupita naye m’paradaiso, ndipo anamva mau amene munthu sangawachule komanso n’kosaloleka kuwakamba. 5 Ndidzadzitamandila ponena za munthu ameneyo, koma ponena za ine mwini, sindidzadzitama kupatulapo pa zofooka zanga zokha. 6 Pakuti ngakhale nditafuna kudzitama, sindidzakhala wopanda nzelu cifukwa ndidzanena coonadi. Koma ndimapewa kutelo cifukwa sindikufuna kuti wina anditamande kwambili kuposa pa zimene akuona mwa ine, kapena kumva kwa ine, 7 cabe cifukwa ca mabvumbulutso apadela amene ndinalandila.

Koma kuti ndisamadzikweze mopitilila muyeso, ndinaikidwa munga m’thupi mwanga umene umandilasa. Mungawo ndi mngelo wa Satana amene amandimenya nthawi zonse kuti ndisamadzikweze mopitilila muyeso. 8 Katatu konse ndinapempha Ambuye mocondelela kuti mungawu undicokele. 9 Koma anandiuza kuti: “Cisomo canga cimene ndakuonetsa n’cokukwanila, cifukwa mphamvu zanga zimaonekela bwino kwambili iweyo ukakhala wofooka.” Conco ndidzadzitamandila mokondwela pa zofooka zanga, kuti mphamvu za Khristu zikhalebe pamutu panga ngati tenti. 10 Ndipo cifukwa ca Khristu ndimakondwela ndikakhala wofooka, ndikamanyozedwa, ndikamasowa zofunikila pa umoyo, ndikamazunzidwa, komanso pa zobvuta zina cifukwa ca Khristu. Pakuti ndikakhala wofooka, m’pamene ndimakhala ndi mphamvu.

11 Apa tsopano ndakhala munthu wopanda nzelu. Inu ndi amene mwandikakamiza kutelo. Paja ndinu munafunikila kundiyamikila pa zabwino zimene ndacita. Pakuti si ndine wotsika mwa njila iliyonse poyelekeza ndi atumwi anu apamwambawo, ngakhale kuti mumandiona kuti si ndine kanthu. 12 Kunena zoona, inu munaona umboni wakuti ndine mtumwi. Munaonanso kuti ndinapilila kwambili, ndinacita zizindikilo, zinthu zodabwitsa, komanso nchito zamphamvu. 13 Kodi n’ciani cimene ndinacitila mipingo ina inu osakucitilani, kupatulapo cokhaco cakuti sindinakhale mtolo kwa inu? Conde mundikhululukile pa colakwaci.

14 Aka ndi kacitatu ine kukhala wokonzeka kubwela kwa inu. Ndipo sindidzakhala katundu wolemetsa cifukwa sindikufuna zinthu zanu, koma inuyo. Pakuti si udindo wa ana kusungila makolo ao cuma, koma ndi udindo wa makolo kusungila ana ao cuma. 15 Koma ine ndidzagwilitsa nchito zinthu zanga zonse, ndidzadzipeleka ndi moyo wanga wonse cifukwa ca inu, ndipo ndidzacita zimenezi mosangalala. Conco ngati ine ndimakukondani kwambili conci, kodi inu muyenela kundikonda pang’ono? 16 Koma mulimonsemo, sindinakulemetseni. Komabe inu mumakamba kuti “ndinakupusitsani” komanso “ndinakucenjelelani.” 17 Ndipo inunso mukudziwa kuti sindinakudyeleni masuku pamutu kudzela mwa wina aliyense amene tinamutumiza kwa inu. Ndinatelo ngati? 18 Ndinalimbikitsa Tito kuti abwele kwanuko, ndipo ndinamutumiza limodzi ndi m’bale wina. Tito sanakudyeleni masuku pamutu, anatelo ngati? Iye ndi ine tinaonetsa mzimu umodzi-modzi, ndipo tinacita zinthu mofanana, si conco?

19 Kodi nthawi yonseyi mwakhala mukuganiza kuti tikudzichinjiliza pamaso panu? Dziwani kuti zimene tikunenazi, tikuzinena pamaso pa Mulungu mogwilizana ndi Khristu. Koma okondedwa, ciliconse cimene timacita, timatelo kuti tikulimbikitseni. 20 Ndikuopa kuti mwina ndikadzafika sindidzakupezani mmene ndikufunila. Komanso kuti mwina inenso, sindidzakhala mmene mukufunila. M’malomwake, ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupsyelana mtima, magawano, misece, manong’onong’o, kudzitukumula cifukwa ca kunyada, komanso cipwilikiti. 21 Mwina ndikadzabwelanso, Mulungu wanga angadzandicititse manyazi pamaso panu. Ndipo mwina ndidzalila cifukwa ca anthu ambili amene anacimwa koma sanalape pa khalidwe lao lonyansa la ciwelewele,* ndiponso khalidwe lao lopanda manyanzi limene akhala akucita.

13 Ulendo uno wobwela kwa inu umene ndakonza ndi wacitatu. “Nkhani iliyonse izitsimikizika ndi umboni wa anthu awili kapena atatu.” 2 Ngakhale kuti sindili kumeneko palipano, zili ngati ndili nanu limodzi kaciwili. Ndipo ndikupelekelatu cenjezo ndisanafike kumeneko kwa amene anacimwa komanso kwa ena onse, kuti ndikadzafikanso kumeneko sindidzawacitila cifundo. 3 Ndikutelo cifukwa mukufuna umboni wakuti Khristu yemwe si wofooka kwa inu, koma ndi wamphamvu, akulankhuladi kudzela mwa ine. 4 Ndithudi iye anaphedwa pamtengo cifukwa ca kufooka, koma ali moyo cifukwa ca mphamvu ya Mulungu. Zoonadi ifenso ndife ofooka limodzi naye, koma tidzakhala naye limodzi cifukwa ca mphamvu ya Mulungu yomwe ikugwila nchito mwa inu.

5 Pitilizani kudziyesa kuti mutsimikize ngati mukali ndi cikhulupililo. Pitilizani kudzisanthula kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani. Kodi simukuzindikila kuti ndinu ogwilizana ndi Yesu Khristu? Muyenela kudziwa zimenezi, pokhapo ngati ndinu osabvomelezeka. 6 Ndikukhulupilila kuti mudzazindikila kuti ndife obvomelezeka.

7 Tsopano tikupemphela kwa Mulungu kuti musacite colakwa ciliconse, osati kuti tioneke ngati obvomelezeka, koma kuti mucite zoyenela ngakhale titaoneka ngati osabvomelezeka. 8 Cifukwa sitingacite ciliconse cotsutsana ndi coonadi, koma zokhazo zogwilizana ndi coonadi. 9 Timasangalala tikakhala ofooka, inu n’kukhala amphamvu. Ndipo pemphelo lathu ndi lakuti mupitilize kupanga masinthidwe oyenelela. 10 N’cifukwa cake ndikulemba zinthu zimenezi ndisanafike kwa inu, kuti ndikadzabwela kumeneko ndisadzagwilitse nchito ulamulilo wanga mwamphamvu, cifukwa Ambuye anandipatsa ulamulilowu kuti ndizikulimbikitsani osati kukufooketsani.

11 Potsiliza abale, pitilizani kukondwela, kusintha maganizo, kulimbikitsidwa, kukhala ogwilizana, ndiponso kukhala mwamtendele. Mwakutelo, Mulungu wacikondi komanso wamtendele, adzakhala nanu. 12 Patsanani moni mwa kupsompsonana kwaubale. 13 Oyela onse akupeleka moni wao.

14 Cisomo ca Ambuye Yesu Khristu, cikondi ca Mulungu, komanso madalitso a mzimu woyela, zikhale ndi inu nonse.

Kapena kuti, “amatilimbikitsa.”

Kapena kuti, “m’masautso.”

Kapena kuti, “m’masautso.”

Kapena kuti, “masautso.”

Ma Baibo ena amati, “zimene mukuzidziwa kale bwino.”

Kucokela ku Cigiriki, “kuzimvetsa mpaka mapeto.”

Ma Baibo ena amati, “kuti mudzapindule kaciwili.”

Wochedwanso Sila.

Kapena kuti, “kuti asamezedwe ndi cisoni.”

Kapena kuti, “ku zolinga zake; mapulani ake.”

Kucokela ku Cigiriki, “pa zolembapo za mnofu, m’mitima.”

Kucokela ku Cigiriki, “kucoka pa ulemelelo, kupita pa ulemelelo wina.”

Ma Baibo ena amati, “mwa mzimu wa Yehova.”

Kapena kuti, “m’mitsuko yadothi.”

Ma Baibo ena amati, “kusowelatu mtengo wogwila.”

Kapena kuti, “sitifa.”

Kucokela ku Cigiriki, “m’matupi athu.”

Kucokela ku Cigiriki, “mzimu wa cikhulupililo.”

Kapena kuti, “mayeso.”

Kapena kuti, “citsimikizo ca (lonjezo la mphamvu la) zinthu zakutsogolo.”

Kapena kuti, “nsembe ya ucimo.”

Kapena kuti, “Talankhula nanu moona mtima.”

Kapena kuti, “tsegulani kwambili mitima yanu.”

Kucokera ku liu la Ciheberi lotanthauza, “Wopanda Pake,” ndipo amalisewenzetsa pokamba za Satana.

Kapena kuti, “munthu wokhulupilika.”

Kapena kuti, “muzitikonda.”

Kapena kuti, “komanso sitinacenjelele munthu aliyense.”

Kapena kuti, “opanda cifukwa; opanda mlandu.”

Ma Baibo ena amati, “ndimalimba mtima cifukwa ca inu.”

Kapena kuti, “ndipo amadzizimbaitsa kuti aoneke.”

Kapena kuti, “Satana amadzizimbaitsa kuti aoneke.”

Kapena kuti, “amadzizimbaitsa kuti akhale.”

Kucokela ku Cigiriki, “mbeu.”

Kucokela ku Cigiriki, “40 kucotsela cimodzi.”

Kucokela ku Cigiriki, “ndinali kukhala wosabvala.”

Kapena kuti, “cimandipsyinja tsiku ndi tsiku.”

M’Cigiriki, por·neiʹa. Onani Matanthauzo a Mau Ena.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani