KALATA KWA AGALATIYA
1 Ndine mtumwi Paulo. Sindine mtumwi wocokela kwa anthu kapena wotumidwa ndi munthu. Koma ndine mtumwi wosankhidwa ndi Yesu Khristu kudzela mwa Mulungu Atate amene anamuukitsa kwa akufa. 2 Ine pamodzi ndi abale onse amene ndili nao, tikupeleka moni ku mipingo ya ku Galatiya:
3 Cisomo komanso mtendele zocokela kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu zikhale nanu. 4 Iye anadzipeleka kaamba ka macimo athu kuti atipulumutse ku nthawi ino yoipa, malinga ndi cifunilo ca Mulungu Atate wathu. 5 Ndipo ulemelelo upite kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ameni.
6 Ndikudabwa kuti mwapatuka mwamsanga kucoka kwa Mulungu amene anakuitanani mwa cisomo ca Khristu, ndipo mwakopeka ndi uthenga wabwino wa mtundu wina. 7 Sikuti palinso uthenga wina wabwino ai. Koma pali ena pakati panu amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza uthenga wabwino wonena za Khristu. 8 Ngakhale n’telo, ngati ife kapena mngelo wocokela kumwamba angalengeze uthenga wabwino wosiyana ndi uthenga wabwino umene tinaulengeza kwa inu, ameneyo akhale wotembeleledwa. 9 Ndipo monga ndakambila kale, ndibwelezanso kuti, ngati kuli aliyense amene akulengeza uthenga wabwino wosiyana ndi umene munaulandila kale, munthu ameneyo akhale wotembeleledwa.
10 Kodi ndikufuna kuti anthu azindikonda kapena kuti Mulungu azindikonda? Kapena kodi ndikuyesa kukondweletsa anthu? Ndikanafuna kupitiliza kukondweletsa anthu, sindikanakhala kapolo wa Khristu. 11 Ndikufuna kuti mudziwe abale, kuti uthenga wabwino umene ndinaulengeza kwa inu sunacokele kwa anthu. 12 Sindinaulandile kucokela kwa munthu aliyense, ndipo sindinacite kuphunzitsidwa. Koma Yesu Khristu ndiye anandiululila uthengawu.
13 Munamva zimene ndinali kucita pamene ndinali m’Ciyuda. Ndinali kuzunza mpingo wa Mulungu koopsa,* ndipo ndinali kuusakaza. 14 Ndinali kucita bwino kwambili m’Ciyuda kuposa Ayuda anzanga ambili a msinkhu wanga, cifukwa ndinali wokangalika kwambili pa miyambo ya makolo anga. 15 Koma Mulungu amene anacititsa kuti ndibadwe, komanso amene anandiitana mwa cisomo cake, anaona kuti m’poyenela kuti 16 aulule za Mwana wake kudzela mwa ine. Anatelo kuti ndilengeze uthenga wabwino wokhudza iye kwa anthu a mitundu ina. Ataulula zimenezi ine sindinapite kukafunsila kwa munthu aliyense* nthawi yomweyo. 17 Sindinapitenso ku Yerusalemu kwa amene anakhala atumwi ine ndisanakhale, koma ndinapita ku Arabiya, kenako ndinabwelelanso ku Damasiko.
18 Ndiyeno patapita zaka zitatu, ndinapita ku Yerusalemu kukaonana ndi Kefa,* ndipo ndinakhala naye masiku 15. 19 Koma sindinaonane ndi atumwi ena onse kupatulapo Yakobo, m’bale wa Ambuye. 20 Ndikukutsimikizilani pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulembelanizi sindikunama.
21 Kenako ndinapita m’zigawo za Siriya ndi Kilikiya. 22 Koma mipingo ya ku Yudeya yomwe inali yogwilizana ndi Khristu, siinali kundidziwa bwino-bwino. 23 Iwo anali kungomva mbili yakuti: “Munthu uja amene anali kutizunza kale, tsopano akulengeza uthenga wabwino wonena za cikhulupililo cimene kale anali kucisakaza.” 24 Conco iwo anayamba kupeleka ulemelelo kwa Mulungu cifukwa ca ine.
2 Ndiyeno patapita zaka 14, ndinapitanso ku Yerusalemu limodzi ndi Baranaba, ndipo ndinatenganso Tito. 2 Ndinapita kumeneko cifukwa ca bvumbulutso limene ndinalandila, ndipo ndinafotokozela abalewo uthenga wabwino umene ndikuulalikila kwa anthu a mitundu ina. Ndinacita zimenezi mseli pamaso pa amuna odalilika, pofuna kutsimikizila kuti utumiki umene ndinali kucita kapena umene ndinali nditacita, usapite pacabe. 3 Ndipotu ngakhale kuti Tito amene ndinali naye anali Mgiriki, sanakakamizidwe kuti adulidwe. 4 Koma nkhani ya mdulidweyi inabuka cifukwa ca abale acinyengo amene analowa mwakacete-cete pakati pathu. Iwo analowa mozemba ngati akazitape kuti asokoneze ufulu umene tikusangalala nao mogwilizana ndi Khristu Yesu, n’colinga coti atigwile ukapolo. 5 Koma sitinawagonjele anthu amenewa ngakhale pang’ono kuti inu musataye coonadi ca uthenga wabwino.
6 Koma za aja amene anali kuoneka ngati ofunika kwambili, kaya anali otani, kwa ine zilibe kanthu, cifukwa Mulungu sayendela maonekedwe a munthu. Amuna odalilikawo sanaonjezele cidziwitso ciliconse catsopano mwa ine. 7 Komabe, iwo anaona kuti ndinapatsidwa nchito yolalikila uthenga wabwino kwa anthu osadulidwa, monga mmene Petulo anapatsidwila nchito yolalikila uthenga wabwino kwa anthu odulidwa. 8 Popeza amene anapatsa mphamvu Petulo kuti akhale mtumwi kwa anthu odulidwa, ndi amenenso anandipatsa mphamvu kuti ndikalalikile kwa anthu a mitundu ina. 9 Ndipo iwo atazindikila cisomo cimene ndinapatsidwa, Yakobo, Kefa,* ndi Yohane amene anali ngati mizati, anagwila canza ineyo ndi Baranaba poonetsa kuti agwilizana nazo zoti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndi kuti iwo apite kwa anthu odulidwa. 10 Koma iwo anangotipempha kuti tipitilize kukumbukila osauka, ndipo ndayesetsa kucita zimenezo moona mtima.
11 Koma Kefa* atabwela ku Antiokeya, ndinamutsutsa* pamasom’pamaso, cifukwa zinali zoonekelatu kuti anali wolakwa. 12 Zinali conco cifukwa anthu ena ocokela kwa Yakobo asanafike, iye anali kudya limodzi ndi anthu a mitundu ina. Koma iwo atafika, iye analeka kudya nao komanso kuceza nao poopa anthu odulidwa. 13 Ayuda enawo anayamba kucita naye zinthu zaciphamaso* zimenezi, moti nayenso Baranaba anayamba kucita nao zaciphamasozi.* 14 Koma nditaona kuti sakuyenda mogwilizana ndi coonadi ca uthenga wabwino, ndinauza Kefa* pamaso pa onse kuti: “Ngati iwe pokhala Myuda ukucita zinthu ngati anthu a mitundu ina, osati monga Myuda, n’cifukwa ciani ukulimbikitsa anthu a mitundu ina kuti azicita zinthu ngati Ayuda?”
15 Ife amene tinabadwa Ayuda, osati ocimwa ocokela m’mitundu ina, 16 timadziwa kuti munthu amayesedwa wolungama osati mwa kucita nchito za cilamulo, koma kokha mwa kukhulupilila Yesu Khristu. Conco, takhulupilila Khristu Yesu kuti tiyesedwe olungama cifukwa cokhulupilila iye, osati cifukwa ca nchito za cilamulo, cifukwa palibe munthu amene amayesedwa wolungama mwa kucita nchito za cilamulo. 17 Tsopano ngati ife tapezekanso kuti ndife ocimwa pamene tikuyesedwa olungama mwa Khristu, kodi ndiye kuti Khristu wakhala mtumiki wa ucimo? Kutalitali! 18 Ngati zinthu zomwezo zimene ndinagwetsa ndikuzimanganso, ndiye kuti ndikusonyeza kuti ndine wophwanya malamulo. 19 Koma cifukwa cakuti ndinali kutsatila cilamulo, ndinafa ku cilamulo kuti ndikhale ndi moyo n’kumatumikila Mulungu. 20 Ndinakhomeleledwa pamtengo limodzi ndi Khristu. Sindinenso amene ndikukhala ndi moyo, koma ndi Khristu amene akukhala ndi moyo mogwilizana ndi ine. Zoonadi, moyo umene ndikukhala tsopano, ndikukhala mokhulupilila Mwana wa Mulungu amene anandikonda n’kudzipeleka kaamba ka ine. 21 Sindikukana* kulandila cisomo ca Mulungu, cifukwa ngati munthu amayesedwa wolungama ndi nchito za cilamulo, ndiye kuti Khristu anafa pacabe.
3 Agalatiya opusa inu! Ndani anakupotozani maganizo, inu amene munakhala ngati mwaona Yesu Khristu atam’khomelela pamtengo? 2 Ndifuna ndikufunseni* funso limodzi ili: Kodi munalandila mzimu cifukwa cocita nchito za cilamulo, kapena cifukwa cokhulupilila zimene munamva? 3 Kani ndinu opusa conci? Inu munayamba ndi nchito za mzimu, kodi mukufuna kutsiliza ndi nchito za thupi? 4 Kodi kubvutika konse kuja kunangopita pacabe? Ndikukhulupilila kuti sikunapite pacabe. 5 Cotelo, amene amakupatsani mzimu ndi kucita nchito zamphamvu* pakati panu, kodi amatelo cifukwa cakuti mumacita nchito za cilamulo kapena cifukwa cakuti munakhulupilila zimene munamva? 6 N’cimodzi-modzinso Abulahamu, iye “anakhulupilila mwa Yehova ndipo anamuyesa wolungama.”
7 Inu mukudziwa bwino kuti anthu okhawo amene ali ndi cikhulupililo ndiwo ana a Abulahamu. 8 Malemba anakambilatu kuti Mulungu adzaona anthu a mitundu ina kukhala olungama cifukwa ca cikhulupililo. Ndipo Mulungu analengezelatu uthenga wabwino kwa Abulahamu wakuti: “Kudzela mwa iwe, anthu a mitundu yonse adzadalitsidwa.” 9 Conco amene ali ndi cikhulupililo akudalitsidwa limodzi ndi Abulahamu, munthu amene anali ndi cikhulupililo.
10 Onse amene amadalila nchito za cilamulo ndi otembeleledwa, cifukwa Malemba amati: “Wotembeleledwa ndi aliyense amene satsatila zonse zolembedwa mu mpukutu wa Cilamulo.” 11 Ndiponso, n’zodziwikilatu kuti kulibe munthu amene Mulungu amamuyesa wolungama cifukwa ca cilamulo, pakuti “wolungama adzakhala ndi moyo cifukwa ca cikhulupililo cake.” 12 Tsopano maziko a Cilamulo si cikhulupililo. Koma “aliyense amene akucita nchito za m’Cilamulo adzakhala ndi moyo cifukwa ca cilamuloco.” 13 Khristu anatigula n’kutimasula ku tembelelo la Cilamulo. Anatelo mwa kukhala tembelelo m’malo mwa ife, pakuti Malemba amati: “Wotembeleledwa ndi aliyense amene wapacikidwa pamtengo.” 14 Iye anatelo n’colinga cakuti madalitso amene analonjezedwa kwa Abulahamu abwele kwa anthu a mitundu ina kudzela mwa Khristu Yesu. Zinatelo kuti ndi cikhulupililo, tilandile mzimu wolonjezedwawo.
15 Abale anga, ndiloleni ndifotokoze fanizo la zimene zimacitikila anthu: Cipangano cikakhazikitsidwa, ngakhale kuti n’capakati pa anthu, palibe amene angacithetse kapena kuonjezelamo mfundo zina. 16 Tsopano malonjezowo ananenedwa kwa Abulahamu ndi kwa mbadwa* yake. Malemba sanena kuti, “ndi kwa mbadwa* zako,” monga kuti mbadwazo n’zambili ai. M’malomwake, Malemba amati, “ndi kwa mbadwa* yako,” kutanthauza munthu mmodziyo, Khristu. 17 Zimene ndikutanthauza ine ndi izi: Mulungu anacita cipangano ndi Abulahamu, ndipo patapita zaka 430, anapeleka cilamulo kwa anthu ake. Koma zimenezi sizinaphwanye cipangano cimene Mulungu anacita ndi Abulahamu, moti n’kulepheletsa lonjezolo kugwila nchito. 18 Pakuti ngati colowa cidalila cilamulo, ndiye kuti colowaco sicidalila lonjezo. Koma Mulungu mwa cisomo cake, anapatsa Abulahamu colowa kudzela m’lonjezo.
19 Tsopano, n’cifukwa ciani Cilamulo cinapelekedwa? Cinapelekedwa kuti macimo aonekele, mpaka mbadwa* imene inapatsidwa lonjezolo itafika. Ndipo Cilamuloco cinapelekedwa ndi angelo kudzela mwa mkhalapakati. 20 Mkhalapakati amafunika ngati cipangano cili pakati pa anthu awili osati mmodzi. Ndi mmenenso zinalili ndi Mulungu, anali yekha, moti sipanafunikile mkhalapakati. 21 Kodi Cilamulo cikutsutsana ndi malonjezo a Mulungu? M’pang’ono pomwe! Ngati lamulo limene lingapeleke moyo n’limene linapelekedwa, ndiye kuti kukhalanso wolungama kukanatheka kudzela m’cilamulo. 22 Koma Malemba amaonetsa kuti anthu akulamulidwa ndi ucimo kuti lonjezolo limene limakhalapo mwa kukhulupilila Yesu Khristu lipatsidwe kwa amene akumukhulupilila.
23 Komabe, cikhulupililoco cisanafike, cilamulo cinali kutiyang’anila, ndipo tinapelekedwa m’manja mwake kuti citisunge. Pa nthawi imeneyo, tinali kuyembekezela cikhulupililo cimene cinali citatsala pang’ono kubvumbulidwa. 24 Conco Cilamulo cinakhala ngati mtsogoleli* wathu wotifikitsa kwa Khristu, kuti tiyesedwe olungama mwa cikhulupililo. 25 Ndiye popeza cikhulupililoco cafika, sitilinso pansi pa wotitsogolela.*
26 Inu nonse ndinu ana a Mulungu cifukwa mumakhulupilila Khristu Yesu. 27 Popeza inu nonse munabatizidwa mwa Khristu, mwabvala Khristu. 28 Motelo, palibe Myuda kapena Mgiriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, cifukwa nonsenu ndinu amodzi mogwilizana ndi Khristu Yesu. 29 Ndipo, ngati ndinu ake a Khristu, ndiye kuti ndinudi mbadwa* za Abulahamu, olandila colowa malinga ndi lonjezolo.
4 Tsopano zimene ndikufuna kunena ndi izi, malinga ngati wolandila colowa akali mwana, sipakhala kusiyana pakati pa iye ndi kapolo, ngakhale kuti mwanayo ndiye mwini zonse. 2 Koma amakhalabe pansi pa omulela komanso akapitawo oyang’anila cuma cake mpaka tsiku limene atate ake anaikilatu. 3 Mofananamo, nafenso pamene tinali ana, tinali akapolo cifukwa tinali kuyendela mfundo zimene anthu a m’dzikoli amayendela. 4 Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake amene anadzabadwa kwa mkazi, ndipo anakhala pansi pa cilamulo. 5 Anatelo kuti aombole amene anali pansi pa cilamulo n’colinga cakuti Mulungu atitenge n’kukhala ana ake.
6 Tsopano pakuti ndinu ana ake, Mulungu watumiza mzimu wa Mwana wake m’mitima yathu, ndipo umafuula kuti: “Abba,* Atate!” 7 Conco, sindiwenso kapolo koma mwana. Ndipo ngati ndiwe mwana, ndiye kuti ndiwenso wolandila colowa cimene Mulungu adzakupatse.
8 Ngakhale n’telo, pamene simunali kudziwa Mulungu, munali akapolo a zinthu zimene kwenikweni si milungu. 9 Koma tsopano popeza mwadziwa Mulungu, kapena ndinene kuti mwadziwidwa ndi Mulungu, mukubwelelanso bwanji ku mfundo za m’dzikoli zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake, n’kumafunanso kukhala akapolo ake? 10 Mukusunga masiku, miyezi, nyengo, ndi zaka mosamala kwambili. 11 Ndikuda nkhawa kuti mwina, khama langa pa inu langopita pacabe.
12 Abale, ndikukucondelelani kuti mukhale mmene ndilili, cifukwa inenso ndinali monga inu. Koma dziwani kuti simunandilakwile ciliconse. 13 Inu mukudziwa bwino kuti kudwala kwanga n’kumene kunandipatsa mwai woti ndilengeze uthenga wabwino nthawi yoyamba kwa inu. 14 Ngakhale kuti matenda anga anali mayeso kwa inu, simunandinyoze kapena kunyansidwa nane.* Koma munandilandila ngati mngelo wa Mulungu komanso ngati Khristu Yesu. 15 Kodi cimwemwe canu capoyamba paja cinapita kuti? Pakuti ndikucitila umboni kuti zikanakhala zotheka, mukanakolowola maso anu n’kundipatsa. 16 Kodi tsopano ndakhala mdani wanu, cabe cifukwa ndakuuzani zoona? 17 Iwo akuyesetsa mwakhama kuti akukopeni, kuti muziwatsatila, koma osati ndi colinga cabwino. Iwo akufuna kukucotsani kwa ine, kuti mukhale ofunitsitsa kuwatsatila. 18 Komabe ndi bwino kuti munthu nthawi zonse azicita khama pokuonetsani cidwi ali ndi colinga cabwino, osati pokhapo ndikakhala nanu. 19 Inu ana anga, tsopano ndikumvanso zowawa ngati za pobeleka mpaka pamene Khristu adzapangike mwa inu. 20 Ndikanakonda ndikanakhala nanu limodzi tsopano kuti ndilankhule nanu mwa njila ina, cifukwa ndathedwa nanu nzelu.
21 Ndiuzeni, inu amene mukufuna kukhala pansi pa cilamulo, kodi simukumva zimene Cilamuloco cikunena? 22 Mwacitsanzo, Malemba amati Abulahamu anali ndi ana aamuna awili, wina kwa wanchito wake wamkazi, ndipo wina kwa mkazi amene anali mfulu. 23 Koma amene anabadwa kwa wanchito wamkaziyo anabadwa mmene ana onse amabadwila, pomwe mwana winayo wobadwa kwa mkazi amene anali mfulu, anabadwa mwa lonjezo. 24 Nkhani imeneyi ili ndi tanthauzo lophiphilitsa. Azimai awiliwa akuimila zipangano ziwili. Cipangano coyamba ndi ca pa Phili la Sinai cimene cimabeleka ana oti akhale akapolo. Ndipo cipanganoco cikuimila Hagara. 25 Tsopano Hagara akuimila Sinai, phili la ku Arabiya, ndipo akufanana ndi Yerusalemu wa lelolino, pakuti ali mu ukapolo limodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wokwezeka ndi mfulu, ndipo iye ndi mai wathu.
27 Paja Malemba amati: “Sangalala iwe mkazi wosabeleka, amene sunabelekepo mwana. Pfuula mwacisangalalo mkazi iwe, amene sunamvepo zowawa za pobeleka. Pakuti ana a mkazi wosiyidwa ndi ambili kuposa ana a mkazi amene ali ndi mwamuna.” 28 Tsopano inu abale, ndinu ana a lonjezo monga analili Isaki. 29 Koma monga mmene zinalili kuti mwana wobadwa monga ana onse anayamba kuzunza mwana wobadwa mwa mzimu, ndi mmenenso zilili palipano. 30 Ngakhale n’telo, kodi Malemba amati ciani? “Thamangitsa wanchito wamkazi ndi mwana wake, pakuti mwana wa wanchito wamkaziyo sadzalandila colowa pamodzi ndi mwana wa mkazi amene ndi mfulu.” 31 Conco abale, ife ndife ana a mkazi yemwe ndi mfulu, osati a wanchito wamkazi.
5 Khristu anatimasula kuti tikhale ndi ufulu umenewu. Cotelo cilimikani, ndipo musalole kuti mumangidwenso mu joko ya ukapolo.
2 Tamvelani! Ine Paulo, ndikukuuzani kuti ngati mungacite mdulidwe, Khristu sadzakhala waphindu kwa inu. 3 Ndikubwelezanso kuuza munthu aliyense amene akucita mdulidwe kuti afunikanso kutsatila zonse za m’Cilamulo. 4 Inu amene mukufuna kuyesedwa olungama mwa cilamulo, mwadzilekanitsa ndi Khristu. Komanso mwatayana ndi cisomo cake. 5 Kunena za ife, kudzela mwa mzimu, tikuyembekezela mwacidwi cilungamo colonjezedwa cimene cimabwela mwa cikhulupililo. 6 Pakuti mwa Khristu Yesu, kudulidwa kapena kusadulidwa kulibe phindu. Koma cofunika ndi cikhulupililo cimene cimaonekela kudzela m’cikondi.
7 Inu munali kuthamanga bwino-bwino. Ndani anakuletsani kuti musiye kumvela coonadi? 8 Kukopeka kwanuku sikukucokela kwa amene anakuitanani. 9 Yisiti* wocepa amafufumitsa mtanda wonse. 10 Ndili ndi cidalilo kuti inu amene muli mu mgwilizano ndi Ambuye, simudzasintha maganizo. Koma amene akukubvutitsaniyo, kaya akhale ndani, adzalandila ciweluzo comuyenelela. 11 Koma kunena za ine abale, ngati ndikulalikilabe kuti anthu azidulidwa, n’cifukwa ciani ndikuzunzidwabe? Zikanakhala conco, ndiye kuti mtengo wozunzikilapo sukanakhalanso copunthwitsa kwa anthu. 12 Ndikanakonda kuti amuna amene akukubvutaniwo, akanangodzifula okha.
13 Abale, munaitanidwa kuti mukhale aufulu. Koma musagwilitse nchito ufulu umenewu ngati mpata wotsatila zilakolako za thupi. Koma tumikilanani mwacikondi monga akapolo. 14 Pakuti Cilamulo conse cagona* pa lamulo limodzi lakuti:* “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” 15 Koma ngati mupitiliza kulumana ndi kukhadzulana nokha-nokha, samalani kuti mungaonongane.
16 M’malomwake, ndikuti pitilizani kuyenda ndi mzimu, ndipo simudzacita zolakalaka za thupi ngakhale pang’ono. 17 Pakuti zimene thupi limalakalaka zimalimbana ndi mzimu, ndipo naonso mzimu umalimbana ndi thupi. Ziwilizi zimatsutsana kuti musacite zinthu zimene mufuna kucita. 18 Ndiponso ngati mukutsogoleledwa ndi mzimu, simuli pansi pa cilamulo.
19 Tsopano nchito za thupi zimaonekela, ndizo ciwelewele,* zinthu zodetsa, khalidwe lotayilila,* 20 kupembedza mafano, za mizimu, cidani, ndeu, nsanje, kupsya mtima, mikangano, magawano, magulu ampatuko, 21 kaduka, kumwa mwaucidakwa, maphwando oipa,* ndi zina zotelo. Ponena za zinthu zimenezi, ndikukucenjezelanitu monga ndinacitila poyamba paja, kuti amene amacita zimenezi sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.
22 Koma makhalidwe amene mzimu* woyela umabala mwa anthu ndi cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, cikhulupililo, 23 kufatsa, ndi kudziletsa. Palibe lamulo loletsa makhalidwe amenewa. 24 Komanso anthu amene ndi ake a Khristu Yesu, anakhomelela pamtengo thupi lao pamodzi ndi zikhumbo zake komanso zilakolako zake.
25 Ngati mzimu ukutitsogolela, tiyeni tipitilize kuyenda molongosoka mwa mzimuwo. 26 Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu komanso ocitilana kaduka.
6 Abale, ngati munthu wapatuka n’kuyamba kutenga njila yolakwika mosadziwa, inu oyenelela mwauzimu yesani kumuthandiza munthu woteloyo ndi mzimu wofatsa. Koma pamene mukutelo, inunso khalani maso kuopela kuti mungayesedwe. 2 Pitilizani kunyamuzana mitolo yolemela, ndipo mwa njila imeneyi mudzakhala mukukwanilitsa cilamulo ca Khristu. 3 Pakuti ngati wina akudziona kuti ndi wofunika koma sali kanthu, akudzinamiza yekha. 4 Koma aliyense asanthule nchito zake kuti aone kuti ndi zotani. Akatelo adzakhala ndi cifukwa cosangalalila, osati modziyelekezela ndi munthu wina. 5 Pakuti aliyense ayenela kunyamula katundu wake.*
6 Ndiponso aliyense amene akuphunzitsidwa zinthu zabwino, agawane zinthu zonse zabwino ndi amene akumuphunzitsayo.
7 Musanamizidwe: Mulungu sapusitsika. Zilizonse zimene munthu wabzala, adzakololanso zomwezo. 8 Pakuti amene amabzala n’colinga copindulitsa thupi lake, adzakolola cionongeko kucokela m’thupi lakelo, koma amene akubzala n’colinga copindulitsa mzimu, adzakolola moyo wosatha kucokela ku mzimuwo. 9 Conco tisaleke kucita zabwino, cifukwa panyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa. 10 Cotelo ngati tingathe,* tiyeni ticitile anthu onse zabwino, koma maka-maka abale ndi alongo athu m’cikhulupililo.
11 Taonani zilembo zikulu-zikulu zimene ndakulembelani ndi dzanja langali.
12 Onse amene akufuna kuti azioneka ngati abwino pamaso pa anthu, ndi amene akukuumilizani kuti muzicita mdulidwe. Amatelo kuti asazunzidwe cifukwa ca mtengo wozunzikilapo* wa Khristu. 13 Pakuti ngakhale amene akudulidwawo sasunga Cilamulo, koma akufuna kuti inu muzidulidwa kuti iwo azidzitama cifukwa ca zimene zacitika pathupi lanu. 14 Koma ine sindidzadzitama pa cifukwa cina ciliconse, kupatulapo cifukwa ca mtengo wozunzikilapo wa Ambuye wathu Yesu Khristu. Kwa ine, dziko linaweluzidwa kuti liphedwe kudzela mwa iye, koma malinga ndi kuona kwa dziko, ine ndinaweluzidwa kuti ndiphedwe kudzela mwa iye. 15 Pakuti kudulidwa kapena kusadulidwa si kanthu, koma cofunika ndi kukhala wolengedwa mwatsopano. 16 Koma kwa onse amene akuyenda molongosoka motsatila lamulo limeneli, mtendele ndi cifundo zikhale nao, inde zikhale ndi Isiraeli wa Mulungu.
17 Kuyambila tsopano pasapezeke munthu wondibvutitsa, pakuti pa thupi langa ndili ndi zipsyela zoonetsa kuti ndine kapolo* wa Yesu.
18 Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Khristu cikhale nanu abale, cifukwa ca makhalidwe abwino amene mumaonetsa. Ameni.
Kucokela ku Cigiriki, “Ndinafika pozunza mopambanitsa mpingo wa Mulungu.”
Kucokela ku Cigiriki, “kwa anthu athupi la nyama ndi magazi.”
Wochedwanso Petulo.
Wochedwanso Petulo.
Wochedwanso Petulo.
Kapena kuti, “ndinamudzudzula.”
Kapena kuti, “zacinyengo.”
Kapena kuti, “zacinyengo.”
Wochedwanso Petulo.
Kapena kuti, “Sindikukankhila pambali.”
Kucokela ku Cigiriki, “Ndikufuna mundidziwitse.”
Kapena kuti, “kucita zozizwitsa.”
Kucokela ku Cigiriki, “kwa mbeu.”
Kucokela ku Cigiriki, “ kwa mbeu.”
Kucokela ku Cigiriki, “kwa mbeu.”
Kucokela ku Cigiriki, “mpaka mbeu.”
Kapena kuti, “ngati wotiyang’anila.”
Kapena kuti, “pa wotiyang’anila.”
Kucokela ku Cigiriki, “ndinudi mbeu.”
Liu la Ciheberi kapena Ciaramu lotanthauza, “Atate kapena Ababa.”
Kapena kuti, “kapena kundilabvulila malobvu.”
Kapena kuti, “Cofufumitsa.”
Kapena kuti, “cimakwanilitsidwa.”
Ma Baibo ena amati, “conse cimamangidwa pa mkota umodzi wakuti.”
M’Cigiriki por-nei’a. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Kapena kuti, “khalidwe locititsa manyazi.” M’Cigiriki a-sel’gei-a, Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Kapena kuti, “maphwando aphokoso.”
Kucokela ku Cigiriki, “Koma cipatso cimene mzimu.”
Kapena kuti, “ayenela kusamalila udindo wake.”
Kapena kuti, “ngati tili ndi mpata.”
Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Kapena kuti, “ndi cidindo coonetsa kuti ndine kapolo.”