KALATA KWA AKOLOSE
1 Ine Paulo amene ndinakhala mtumwi wa Khristu Yesu malinga ndi cifunilo ca Mulungu, ndili limodzi ndi Timoteyo m’bale wathu. 2 Ndikulembela oyela ndi abale okhulupilika a ku Kolose amene ali mu mgwilizano ndi Khristu kuti:
Cisomo komanso mtendele wa Mulungu Atate wathu zikhale nanu.
3 Nthawi zonse timakuchulani m’mapemphelo athu, ndipo timayamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu. 4 Timatelo cifukwa tinamva za cikhulupililo canu mwa Khristu Yesu, komanso za cikondi cimene mumaonetsa kwa oyela onse. 5 Mukucita zimenezi cifukwa ca ciyembekezo ca zinthu zimene akusungilani kumwamba. Ciyembekezo cimeneci, munacimva m’mbuyomu pamene munamva uthenga wa coonadi 6 umene unafika kwa inu, ndipo ukubala zipatso komanso ukufalikila padziko lonse. Izi ndi zimenenso zakhala zikucitika kwa inu kuyambila tsiku limene munamva ndi kudziwa molondola za cisomo ca Mulungu cimene ndi ceniceni. 7 Izi n’zimene munaphunzila kwa Epafura, kapolo mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupilika wa Khristu m’malo mwa ife. 8 Iye ndi amenenso anatidziwitsa za cikondi canu cimene munationetsa mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu.*
9 N’cifukwa cake nafenso, kungoyambila tsiku limene tinamva zimenezo, sitinasiye kukupemphelelani. Ndipo takhala tikupemphanso kuti mudzadzidwe ndi cidziwitso colongosoka ca cifunilo ca Mulungu, kuti mukhale ndi nzelu zonse, komanso kuti muzimvetsetsa zinthu zauzimu. 10 Tacita izi kuti muziyenda mogwilizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti muzimukondweletsa pa ciliconse, pamene mukupitiliza kubala zipatso pa nchito iliyonse yabwino, komanso kuonjezela cidziwitso colongosoka ca Mulungu. 11 Ndipo tikupemphelelanso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu zake zonse zaulemelelo, ndi colinga coti muthe kupilila zinthu zonse moleza mtima, ndiponso mwacimwemwe, 12 kwinaku mukuyamika Atate, amene anakuyeneletsani kuti mulandile nao colowa ca oyela amene ali m’kuwala.
13 Iye anatipulumutsa ku ulamulilo wa mdima, n’kutisamutsila mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. 14 Kudzela mwa Mwana wakeyo, anatimasula ndi dipo,* ndipo macimo athu amakhululukidwa. 15 Iye ndi cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo, woyamba kubadwa wa cilengedwe conse. 16 Kupyolela mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse, za kumwamba ndi za padziko lapansi. Analenga zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka. Kaya ndi mipando yacifumu, ambuye, maboma, komanso maulamulilo. Inde, analenga zinthu zina zonse kudzela mwa iye ndiponso cifukwa ca iye. 17 Iye analipo kale zinthu zina zonse zisanakhaleko, ndipo zinthu zina zonse zinakhalapo kupitila mwa iye. 18 Iye ndi mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndi ciyambi, woyamba kubadwa kucokela kwa akufa, kuti adzakhale woyamba pa zinthu zonse. 19 Zili conco cifukwa cakuti Mulungu zinamusangalatsa kuti makhalidwe ake onse akhale mwa Yesu. 20 Komanso kuti kudzela mwa Mwana wakeyo ayanjanitsenso zinthu zina zonse ndi iyeyo, kaya zinthuzo ndi za padziko lapansi kapena za kumwamba. Anacita zimenezi pokhazikitsa mtendele kudzela m’magazi amene Yesu anakhetsa pamtengo wozunzikilapo.*
21 Kale inu munali otalikilana ndi Mulungu, ndiponso munali adani ake cifukwa maganizo anu anali pa nchito zoipa. 22 Koma tsopano wakuyanjaninso kudzela mu imfa ya mwana wake amene anapeleka thupi lake la nyama kuti inu mukhale oyela, opanda ulemali, ndiponso opanda cifukwa cokunenezelani pamaso pake, 23 malinga ngati mupitilizabe m’cikhulupililo, muli okhazikika pa maziko ndiponso olimba, komanso muli osasunthika pa ciyembekezo ca uthenga wabwino umene munamva, umenenso unalalikidwa padziko lonse. Ine Paulo ndinakhala mtumiki wa uthenga wabwino umenewu.
24 Tsopano ine ndikusangalala kuti ndikubvutika cifukwa ca inu. Ndipo ine ndikuona kuti ndikalibe kufikapo pa kusautsika kwenikweni monga ciwalo ca thupi la Khristu, limene ndi mpingo. 25 Ndinakhala mtumiki wa mpingo umenewu malinga ndi udindo umene Mulungu anandipatsa wakuti ndilalikile mau a Mulungu mokwanila, kuti inuyo mupindule. 26 Mau amenewa akuphatikizapo cinsinsi copatulika cimene dziko silinacidziwe, ndiponso cinali cobisika ku mibadwo ya m’mbuyomu. Koma tsopano cabvumbulidwa kwa oyela ake, 27 amene Mulungu zinamusangalatsa kuwadziwitsa oyelawo pakati pa mitundu ina za cinsinsi copatulika, inde cuma caulemelelo cimeneci. Cinsinsici n’cakuti Khristu ali mu mgwilizano ndi inu, ndipo muli ndi ciyembekezo codzagawana naye ulemelelo wake. 28 Tikulengeza, kulangiza, ndi kuphunzitsa munthu aliyense za iyeyu mu nzelu zonse, kuti tipeleke munthu aliyense ali wathunthu kwa Mulungu mu mgwilizano ndi Khristu. 29 Kuti zimenezi zitheke, ndikugwila nchito mwakhama komanso mokangalika podalila mphamvu zake zimene zikugwila nchito mwa ine.
2 Ndikufuna kuti mudziwe mabvuto aakulu amene ndikukumana nao cifukwa ca inu ndi anthu a ku Laodikaya, kuphatikizapo anthu onse amene sanandionepo maso ndi maso. 2 Ndikucita izi kuti mitima yao ilimbikitsidwe, ndiponso kuti onse akhale ogwilizana m’cikondi, komanso kuti alandile cuma conse cimene cimabwela cifukwa comvetsa bwino zinthu popanda kudodoma kulikonse, kuti apeze cidziwitso colongosoka ca cinsinsi copatulika ca Mulungu, comwe ndi Khristu. 3 Cuma conse cokhudzana ndi nzelu komanso kudziwa zinthu cinabisidwa mwa iye mosamala. 4 Ndikunena izi kuti munthu aliyense asakupusitseni ndi mfundo zokopa. 5 Ngakhale kuti sindili nanu kumeneko, mwa mzimu ndili nanu limodzi. Ndakondwela kumva kuti mumacita zinthu mwa dongosolo, komanso kuti muli ndi cikhulupililo colimba mwa Khristu.
6 Cotelo popeza mumakhulupilila Khristu Yesu Ambuye wathu, pitilizani kuyenda mogwilizana naye, 7 kukhala ozika mizu mwa iye ndi omangidwa pa iye, komanso okhazikika m’cikhulupililo, malinga ndi zimene munaphunzila. Ndipo mitima yanu izisefukila ndi mayamiko.
8 Cenjelani kuti wina asakugwileni ukapolo* ndi nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene anthu a dzikoli amayendela, osati malinga ndi Khristu, 9 pakuti mwa Khristu ndi mmene muli makhalidwe onse aumulungu. 10 Conco inu simukusowa kalikonse cifukwa ca iye, amene ndi mutu wa boma ndi ulamulilo wonse. 11 Popeza muli naye pa ubale munacita mdulidwe, ndipo mdulidwe wake sunacitike ndi manja a anthu, koma unacitika pamene munabvula thupi laucimo. Umenewo ndiwo mdulidwe wa Khristu. 12 Pakuti munaikidwa naye limodzi m’manda pobatizidwa ubatizo wofanana ndi wake. Ndipo popeza muli naye pa ubale, munaukitsidwa naye limodzi cifukwa ca cikhulupililo canu mu mphamvu ya Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa.
13 Kuonjezela apo, inu munali akufa cifukwa ca macimo anu, komanso cifukwa coti munali osadulidwa. Ngakhale n’telo, Mulungu anakupatsani moyo limodzi ndi Khristu. Mokoma mtima iye anatikhululukila macimo athu onse, 14 ndipo anafafaniza cikalata cimene cinali ndi malamulo ndipo cinali kutitsutsa. Iye anacicotsa pocikhomelela pamtengo wozunzikilapo.* 15 Pogwilitsila nchito mtengo wozunzikilapowo, iye anabvula maboma ndi olamulila n’kuwasiya osabvala, ndipo anawaonetsa poyela kwa anthu onse kuti aone kuti wawagonjetsa, n’kumayenda nao ngati akaidi pa cionetselo conyadila kupambana.
16 Conco musalole kuti munthu aliyense akuweluzeni pa nkhani ya cakudya ndi cakumwa, kapena cikondwelelo cinacake, kapenanso kusunga tsiku lokhala mwezi kapena kusunga sabata. 17 Zinthu zimenezi ndi mthunzi wa zimene zinali kubwela, koma zenizeni zake ndi Khristu. 18 Musalole munthu aliyense amene amasangalala ndi kudzicepetsa kwaciphamaso komanso kulambila angelo* kukulepheletsani kudzalandila mphoto. “Munthu woteloyo amaumilila” zinthu zimene waona, ndipo maganizo ake ocimwa amamusonkhezela kuti azidzitukumula popanda cifukwa comveka. 19 Iye salumikizana ndi mutu, yemwe kudzela mwa iye, thupi lonse limapeza zonse zimene limafunikila, ndipo ziwalo zake ndi zolumikizana bwino ndi mfundo za thupilo komanso minyewa yake, ndipo limakulabe mothandizidwa ndi Mulungu.
20 Popeza munafa limodzi ndi Khristu, ndipo simukutsatilanso mfundo zimene anthu a dzikoli amayendela, n’cifukwa ciani mukukhala ngati a dzikoli, popitiliza kugonjela malamulo akuti: 21 “Usagwile cakuti,” “usalawe cakuti,” kapena “usakhudze cakuti”? 22 Zinthu zimenezi zimatha anthu akamazigwilitsila nchito. Amenewa ndi malamulo ndi ziphunzitso za anthu. 23 Ngakhale kuti zinthu zimenezi zimaoneka ngati zanzelu, ndi kulambila kongodzipangila okha, kudzicepetsa kwaciphamaso, kuzunza thupi, ndipo sizithandiza munthu polimbana ndi zilakolako za thupi.
3 Komabe ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, pitilizani kufunafuna zinthu za kumwamba, kumene Khristu wakhala kudzanja lamanja la Mulungu. 2 Pitilizani kuganizila zinthu za kumwamba, osati za padziko lapansi. 3 Paja inu munafa, ndipo moyo wanu wakhala wobisidwa limodzi ndi Khristu amene ali mu mgwilizano ndi Mulungu. 4 Khristu amene ndi moyo wathu akadzaonetsedwa, inunso mudzaonetsedwa naye limodzi mu ulemelelo.
5 Conco iphani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi pa nkhani ya ciwelewele,* zinthu zodetsa, cilakolako cosalamulilika ca kugonana, cilakolako cofuna kucita zoipa, komanso dyela limene ndi kulambila mafano. 6 Cifukwa ca zinthu zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwela. 7 Kale, inunso munali kucita zimenezo, malinga ndi umoyo wanu wa panthawi imeneyo. 8 Koma tsopano muzitayile kutali ndi inu zinthu zonsezi. Mutaye mkwiyo, kupsya mtima, kuipa, komanso mau acipongwe, ndipo pakamwa panu pasatuluke mau otukwana. 9 Musamauzane mabodza. Bvulani umunthu* wakale pamodzi ndi nchito zake. 10 Ndipo mubvale umunthu watsopano umene cifukwa ca cidziwitso colondola, umakhala watsopano malinga ndi cifanizilo ca Mulungu amene anaulenga. 11 Mukatelo, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti,* kapolo kapena mfulu, cifukwa Khristu ndi zonse ndipo ali mwa onse.
12 Conco popeza Mulungu anakusankhani, inu oyela ndi okondedwa, bvalani cifundo cacikulu, kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa, komanso kuleza mtima. 13 Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana mocokela pansi pa mtima, ngakhale pamene wina ali ndi cifukwa comveka codandaulila za mnzake. Monga mmene Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso muzicita cimodzi-modzi. 14 Koma kuonjezela pa zonsezi, bvalani cikondi, cifukwa ndico comangila umodzi cangwilo.
15 Cinanso, lolani kuti mtendele wa Khristu uzilamulila m’mitima yanu, pakuti anakuitanani ku mtendele umenewu monga ziwalo za thupi limodzi. Ndipo muzionetsa kuti ndinu oyamikila. 16 Mau a Khristu akhazikike mofikapo mwa inu ndi nzelu zonse. Pitilizani kuphunzitsana ndi kulimbikitsana* wina ndi mnzake pogwilitsa nchito masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, komanso nyimbo zauzimu zoyamikila. Pitilizani kuimbila Yehova m’mitima yanu. 17 Ciliconse cimene mukucita, kaya mukulankhula kapena kugwila nchito, muzicita zonse m’dzina la Ambuye Yesu, ndipo muziyamika Mulungu Atate kudzela mwa iye.
18 Inu akazi, muzigonjela amuna anu, cifukwa ndi zimene Ambuye amafuna. 19 Inu amuna, muzikonda akazi anu ndipo musamawapsyele mtima.* 20 Inu ana, muzimvela makolo anu pa zinthu zonse, cifukwa zimenezi Ambuye amakondwela nazo. 21 Inu atate, musamakwiyitse* ana anu, kuti asakhale okhumudwa. 22 Inu akapolo, muzimvela ambuye anu pa zinthu zonse. Musamangocita zimenezi pamene muli pamaso pao, pofuna kukondweletsa anthu. Koma muzitelo moona mtima ndiponso moopa Yehova. 23 Ciliconse cimene mukucita, muzicicita ndi moyo wanu wonse, komanso mphamvu zanu zonse ngati kuti mukucitila Yehova, osati anthu, 24 cifukwa mukudziwa kuti Yehova ndiye adzakupatsani colowa monga mphoto. Tumikilani Ambuye wanu Khristu monga akapolo. 25 Ndithudi, amene akucita zolakwa sadzalephela kulandila cilango pa zolakwa zimene akucitazo, cifukwa Mulungu sakondela.
4 Inu ambuye, muzicitila akapolo anu zinthu zacilungamo ndi zoyenela, popeza mukudziwa kuti inunso muli ndi Ambuye kumwamba.
2 Muzilimbikila kupemphela. Ndipo pa nkhani imeneyi mukhale maso ndipo muziyamikila. 3 Komanso muzitipemphelela kuti Mulungu atitsegulile khomo kuti tithe kulalikila mau ndi kulankhula za cinsinsi copatulika conena za Khristu, cimene andimangila muno m’ndende, 4 ndi kuti ndidzalalikila za cinsinsico momveka bwino monga mmene ndiyenela kucitila.
5 Muziyenda mwanzelu pocita zinthu ndi anthu akunja, ndipo muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.* 6 Nthawi zonse mau anu azikhala okoma ngati kuti mwawathila mcele, kuti mudziwe mmene mungayankhile munthu aliyense.
7 Tukiko m’bale wanga wokondedwa, adzakuuzani zonse za ine. Iye ndi mtumiki wokhulupilika komanso kapolo mnzanga mwa Ambuye. 8 Ndikumutumiza kwa inu kuti mudziwe mmene tilili, komanso kuti adzalimbikitse mitima yanu. 9 Iye akubwela kwa inu limodzi ndi Onesimo m’bale wanga wokhulupilika ndi wokondedwa, amene anacokela pakati panu. Iwo adzakufotokozelani zonse zimene zikucitika kuno.
10 Arisitako mkaidi mnzanga akupeleka moni kwa nonsenu. Nayenso Maliko msuweni wa Baranaba, (amene ndinakulangizani kuti mumulandile nthawi iliyonse akadzafika kwa inu), 11 ndi Yesu wodziwikanso kuti Yusito, akuti moni. Iwo ali m’gulu la anthu odulidwa. Iwo okha ndi anchito anzanga pa za Ufumu wa Mulungu, ndipo amandilimbikitsa kwambili. 12 Epafura, amene anacokela pakati panu, amenenso ndi kapolo wa Khristu Yesu akuti moni. Iye amakupemphelelani mwakhama nthawi zonse kuti mupitilize kukhala olimba mwauzimu ndi osakaika ngakhale pang’ono za cifunilo conse ca Mulungu. 13 Ine ndikumucitila umboni kuti amadzipeleka kwambili cifukwa ca inu, komanso cifukwa ca abale a ku Laodikaya ndi ku Herapoli.
14 Luka, dokotala wokondedwa, komanso Dema akuti moni kwa nonsenu. 15 Mundipelekele moni kwa abale a ku Laodikaya komanso kwa Numfa ndi mpingo umene umasonkhana panyumba pake. 16 Mukaiwelenga kalatayi kwanuko, konzani zakuti ikawelengedwenso ku mpingo wa Alaodikaya. Inunso mukawelenge yocokela ku Laodikaya. 17 Komanso muuze Arikipo kuti: “Uonetsetse kuti utumiki umene unaulandila mwa Ambuye ukuukwanilitsa.”
18 Tsopano landilani moni umene ine Paulo ndalemba ndi dzanja langa. Pitilizani kukumbukila maunyolo anga kundende kuno. Cisomo ca Mulungu wathu cikhale nanu.
Kucokela ku Cigiriki, “munationetsa mwa mzimu.”
Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Kapena kuti, “asakugwileni ngati nyama.”
Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Kapena kuti, “kulambila monga mmene angelo amacitila.”
M’Cigiriki, por·neiʹa. Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Kucokela ku Cigiriki, “munthu.”
Mau akuti, “Msukuti,” amatanthauza munthu wosaphunzila, watulo, komanso mbuli.”
Kapena kuti, “kulangizana.”
Kapena kuti, “ndipo musamawacite nkhanza.”
Kapena kuti, “musamapsyetse mtima.”
Kucokela ku Cigiriki, “ndipo muzigula nthawi yoikidwilatu.”