LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • nwt 1 Atesalonika 1:1-5:28
  • 1 Atesalonika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • 1 Atesalonika
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
1 Atesalonika

KALATA YOYAMBA KWA ATESALONIKA

1 Ine Paulo ndili limodzi ndi Silivano* komanso Timoteyo. Ndikulembela inu mpingo wa Atesalonika womwe uli mu mgwilizano ndi Mulungu Atate komanso ndi Ambuye Yesu Khristu kuti:

Cisomo komanso mtendele zikhale nanu.

2 Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamakuchulani nonsenu m’mapemphelo athu. 3 Timacita zimenezi cifukwa nthawi zonse timakumbukila nchito zanu za cikhulupililo, nchito zanu za cikondi, komanso kupilila kwanu cifukwa ca ciyembekezo cimene muli naco mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu amene ndi Atate wathu. 4 Abale athu, inu amene Mulungu amakukondani, tikudziwa kuti iye ndiye anakusankhani. 5 Tikunena zimenezi, cifukwa pamene tinali kulalikila uthenga wabwino kwa inu, sitinali kungolankhula basi, koma uthengawo unali wamphamvu, unabwela ndi mzimu woyela, komanso tinaulalikila motsimikiza mtima kwambili. Inunso mukudziwa zimene tinakucitilani pofuna kukuthandizani. 6 Ngakhale kuti munali pa mabvuto aakulu, munalandila mauwo ndi cimwemwe cimene mzimu umapeleka. Pocita zimenezo, munatengela citsanzo cathu komanso ca Ambuye, 7 moti munakhala citsanzo kwa okhulupilila onse ku Makedoniya ndi ku Akaya.

8 Sikuti mau a Yehova ocokela kwa inu angomveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha ai, koma kwina kulikonse cikhulupililo canu mwa Mulungu cafalikila, moti ife sitikufunika kunenapo kanthu. 9 Iwo akunenabe za mmene munatilandilila nthawi yoyamba imene tinakumana, komanso mmene munasiyila mafano anu ndi kutembenukila kwa Mulungu, kuti muzitumikila Mulungu wamoyo ndi woona, 10 komanso kuti muziyembekezela Mwana wake kucokela kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa. Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwelawo.

2 Abale, inu mukudziwa bwino kuti ulendo wathu wobwela kwa inu unali waphindu. 2 Monga mukudziwila, ngakhale kuti poyamba tinabvutika komanso anthu anaticita zacipongwe ku Filipi, Mulungu wathu anatithandiza kuti tilimbe mtima kuti tikuuzeni uthenga wabwino wa Mulungu panthawi imene anthu anali kutitsutsa kwambili.* 3 Zimene tikukulimbikitsani kuti mucite sizikucokela m’maganizo olakwika kapena odetsedwa, ndipo sitikuzikamba mwacinyengo. 4 Koma tikutelo cifukwa Mulungu wabvomeleza kutipatsa nchito yolalikila uthenga wabwino. Conco tikulankhula kuti tikondweletse Mulungu amene amasanthula mitima yathu, osati kuti tikondweletse anthu.

5 Inu mukudziwa kuti sitinalankhulepo mau oshashalika, kapena kucita zaciphamaso ndi zolinga zadyela. Ndipo pa nkhani imeneyi, Mulungu ndiye mboni yathu. 6 Komanso sitinali kungodzifunila ulemelelo wocokela kwa anthu ai, kaya kwa inu kapena kwa anthu ena. Sitinacite zimenezo ngakhale kuti monga atumwi a Khristu tikanakhala mtolo woonongetsa ndalama zambili. 7 M’malomwake, tinakhala odekha ngati mmene mai woyamwitsa amacitila posamalila ana ake. 8 Cifukwa timakukondani kwambili, tinacita khama* kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu, ngakhale kupeleka miyoyo yathu yeniyeniyo kuti tikuthandizeni, pakuti tinakukondani kwabasi.

9 Mukudziwa bwino abale, kuti pamene tinali pakati panu, tinayesetsa kugwila nchito mwakhama ndi mphamvu zathu zonse. Tinali kugwila nchito usana ndi usiku kuti tisasenzetse mtolo aliyense wa inu wotilipilila kalikonse pofuna kutithandiza, pamene tinali kulalikila uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu. 10 Pamene tinali ndi inu okhulupilila, tinacita zinthu mokhulupilika, mwacilungamo, ndipo tinalibe cifukwa cotinenezela. Inu komanso Mulungu ndinu mboni zathu pa nkhaniyi. 11 Mukudziwanso bwino kuti aliyense wa inu tinali kumulimbikitsa, kumutonthoza, komanso kumulangiza ngati mmene tate amacitila ndi ana ake. 12 Tinali kucita zimenezi kuti mupitilize kuyenda m’njila imene Mulungu amafuna. Iye ndi amene anakuitanani ku Ufumu wake ndi ulemelelo wake.

13 Ndithudi, mpake kuti ifenso timayamika Mulungu mosalekeza, cifukwa pamene munalandila mau a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandile monga mau a anthu ai, koma mmene alilidi, monga mau a Mulungu. Mau amenewa akugwilanso nchito mwa inu okhulupilila. 14 Pakuti inu abale munatengela citsanzo ca mipingo ya Mulungu imene ili mu mgwilizano ndi Khristu Yesu ku Yudeya. Tikutelo cifukwa anthu akwanu anakuzunzani, monga mmene Ayuda akuzunzila Akhristu a ku Yudeyawo. 15 Ayudawo anafika popha Ambuye Yesu komanso aneneli, ndipo ife anatizunza. Kuonjezela pamenepo, iwo sakondweletsa Mulungu, koma amatsekeleza zimene anthu onse afunikila. 16 Amacita zimenezi poyesa kutiletsa kuti tisauze anthu a mitundu ina uthenga umene ungawapulumutse. Pocita zimenezi, iwo nthawi zonse amaonjezela macimo ao. Koma tsopano mkwiyo wake wawafikila.

17 Pamene tinasiyana nanu abale kwa nthawi yocepa (pamaso-m’pamaso osati mumtima mwathu), tinayesetsa mwamphamvu kuti tikuoneni pamaso-m’pamaso* cifukwa ndi zimene tinali kulakalaka kwambili. 18 N’cifukwa cake tinali kufuna kubwela kwa inu, ndipo ine Paulo ndinayesetsa kuti ndibwele, osati kamodzi kokha koma kawili konse, kungoti Satana anachinga njila yathu. 19 Kodi ciyembekezo cathu kapena cimwemwe cathu n’ciani? Kodi mphoto imene tidzainyadile* pamaso pa Ambuye wathu Yesu, pa nthawi ya kukhalapo kwake n’ciani? Kodi si inuyo? 20 Ndithudi, inu ndinu ulemelelo wathu komanso cimwemwe cathu.

3 N’cifukwa cake pamene tinazindikila kuti sitingathenso kupilila, tinaona kuti ndi bwino kuti tikhalebe ku Atene. 2 Ndipo tinakutumizilani Timoteyo m’bale wathu yemwe ndi mtumiki wa Mulungu* amene akulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu. Tinamutumiza kuti adzakulimbikitseni ndi kukutonthozani kuti cikhulupililo canu cikhale colimba. 3 Tinatelo kuti aliyense wa inu asagwedezeke* ndi masautso amenewa. Pakuti inunso mukudziwa kuti sitingapewe kukumana ndi mabvuto ngati amenewa.* 4 Pamene tinali nanu limodzi, tinali kukuuzani kuti tidzakumana ndi mabvuto ndipo monga mmene mukudziwila, zimene tinakuuzanizo n’zimenedi zacitika. 5 N’cifukwa cake pamene sindikanathanso kupilila, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene cikhulupililo canu cilili. Ndinali kuopa kuti mwina Woyesayo anakuyesani ndipo n’kutheka kuti nchito imene tinagwila mwakhama inangopita pacabe.

6 Koma Timoteyo wangofika kumene kucokela kwanuko, ndipo watiuza nkhani yabwino ya kukhulupilika kwanu ndi cikondi canu. Watiuzanso kuti mukupitiliza kutikumbukila, mumatikonda, komanso kuti mukulakalaka kutiona ngati mmene ife tikulakalakila kukuonani. 7 N’cifukwa cake abale, m’mabvuto* ndi m’masautso athu onse tatonthozedwa cifukwa ca inu, komanso cifukwa ca kukhulupilika kumene mukuonetsa. 8 Pakuti inu mukakhala olimba mwa Ambuye, ife timapeza mphamvu.* 9 Kodi Mulungu tingamuyamikile bwanji kuti timubwezele pa cimwemwe cosefukila cimene tili naco pamaso pa Mulungu wathu cifukwa ca inu? 10 Timapemphela mocondelela kucokela pansi pa mtima usana ndi usiku kuti tidzakuoneni pamaso-m’pamaso,* n’kukupatsani zimene zikupelewela pa cikhulupililo canu.

11 Tsopano Mulungu Atate wathu komanso Ambuye wathu Yesu, atikonzele njila kuti zitheke kubwela kwa inu. 12 Komanso, Ambuye akuthandizeni kuti muzikondana kwambili, ndiponso kuti muzikonda anthu ena ngati mmene ife timakukondelani. 13 Acite zimenezi kuti alimbitse mitima yanu, kuti mukhale opanda colakwa ndi oyela pamaso pa Mulungu Atate wathu, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu, limodzi ndi oyela onse.

4 Pomaliza abale, tinakupatsani malangizo a mmene muyenela kuyendela kuti muzikondweletsa Mulungu, ndipo n’zimenedi mukucita. Ndiye tikukupemphani komanso kukucondelelani m’dzina la Ambuye Yesu, kuti mupitilize kuonjezela kucita zimenezi. 2 Pakuti mukudziwa malangizo* amene tinakupatsani m’dzina la Ambuye Yesu.

3 Cifunilo ca Mulungu n’cakuti mukhale oyela ndiponso kuti muzipewa ciwelewele.* 4 Aliyense wa inu azidziwa kulamulila thupi lake kuti likhale loyela komanso lolemekezeka pamaso pa Mulungu. 5 Musakhale ngati anthu a mitundu ina omwe sadziwa Mulungu, amenenso ali ndi cilakolako cosalamulilika ca kugonana komanso dyela. 6 Pa nkhaniyi, pasapezeke wina aliyense wopitilila malile ake n’kudyela masuku pamutu m’bale wake, pakuti Yehova adzalanga munthu aliyense amene akucita zinthu zimenezi, monga mmene tinakuuzilani kale komanso kukucenjezani mwamphamvu. 7 Popeza Mulungu sanatiitane kuti tikhale ndi makhalidwe odetsa, koma kuti tikhale oyela. 8 Conco munthu amene akunyalanyaza macenjezo amenewa sakunyalanyaza munthu, koma Mulungu amene amakupatsani mzimu wake woyela.

9 Koma pa nkhani yokonda abale, m’posafunika kuti ticite kukulembelani, cifukwa Mulungu amakuphunzitsani kuti muzikondana. 10 Ndipo kunena zoona, inu mukucita kale zimenezi kwa abale onse a ku Makedoniya. Koma tikukulimbikitsani abale kuti mupitilize kucita zimenezi moposelapo. 11 Muziyesetsa kukhala mwamtendele. Musamalowelele nkhani za ena, ndipo muzigwila nchito ndi manja anu. Muzicita zimenezi malinga ndi malangizo amene tinakupatsani. 12 Muzicita zimenezi kuti anthu akunja aziona kuti mukuyenda bwino ndiponso kuti mukhale osasowa kanthu.

13 Cina abale, tikufuna kuti mudziwe za amene akugona mu imfa, kuti cisoni canu cisakhale ngati ca anthu ena amene alibe ciyembekezo. 14 Pakuti ngati timakhulupilila kuti Yesu anafa n’kuukitsidwa, ndiye kuti Mulungu adzaukitsanso amene akugona mu imfa kupyolela mwa Yesuyo, kuti akakhale naye* limodzi. 15 Zimene tikukuuzani malinga ndi mau a Yehova n’zakuti, ife amene tidzakhalabe ndi moyo mpaka pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, sitidzatsogola pa amene akugona mu imfa. 16 Pakuti Ambuye adzatsika kucokela kumwamba ndi mfuu yaulamulilo atanyamula lipenga la Mulungu. Mau ao adzamveka kuti ndi a mkulu wa angelo. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzakhala oyambilila kuuka. 17 Kenako, ife amene tidzakhalebe amoyo limodzi ndi iwo, tidzatengedwa kupita m’mitambo kukakumana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuyewo nthawi zonse. 18 Conco pitilizani kutonthozana ndi mau amenewa.

5 Koma tsopano za nthawi ndi nyengo abale, m’posafunika kuti tikulembeleni ciliconse. 2 Pakuti inu nomwe mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati mbala usiku. 3 Akadzangonena kuti, “Bata ndi mtendele!” nthawi yomweyo cionongeko cidzawafikila modzidzimutsa ngati mmene ululu umene mkazi woyembekezela amamva akangotsala pang’ono kucila,* ndipo sadzapulumuka. 4 Koma inu abale simuli mumdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mmene mbala zimadzidzimukila kukazicela. 5 Pakuti nonsenu ndinu ana a kuwala komanso ana a masana. Si ndife anthu a usiku kapena a mdima.

6 Cotelo tisapitilize kugona ngati mmene ena onse akucitila. M’malomwake, tikhalebe maso komanso oganiza bwino. 7 Pakuti ogona amagona usiku, ndipo amene amaledzela, amaledzela usiku. 8 Koma popeza ndife a usana, tiyeni tikhalebe oganiza bwino, ndipo tibvalebe codzitetezela pacifuwa ca cikhulupililo ndi ca cikondi. Tibvalenso ciyembekezo ca cipulumutso ngati cisoti, 9 pakuti Mulungu sanatisankhe kuti adzatilange, koma anatisankha kuti tikapulumuke kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 10 Iye anatifela kuti kaya tikhale maso kapena tigone,* tikhale ndi moyo limodzi ndi iye. 11 Conco pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake ngati mmene mukucitila.

12 Tsopano tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwila nchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolelani mwa Ambuye komanso kukulangizani. 13 Muziwakonda komanso kuwacitila ulemu waukulu cifukwa ca nchito yao. Muzikhala mwamtendele pakati panu. 14 Komanso tikukulimbikitsani abale, kuti muzicenjeza* anthu ocita zosalongosoka. Muzikamba mau olimbikitsa kwa opsyinjika maganizo,* muzithandiza ofooka, ndiponso muzikhala oleza mtima kwa onse. 15 Onetsetsani kuti pasapezeke wina aliyense wobwezela coipa pa coipa kwa mnzake. Koma nthawi zonse muziyesetsa kucitilana zabwino wina ndi mnzake komanso kucitila zabwino anthu ena onse.

16 Muzikondwela nthawi zonse. 17 Muzipemphela nthawi zonse. 18 Muziyamika pa ciliconse. Cimeneci ndi cifunilo ca Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu. 19 Musazimitse moto wa mzimu. 20 Musamanyoze mau aulosi. 21 Muzitsimikizila zinthu zonse. Muzigwilitsitsa cabwino mwamphamvu. 22 Muzipewa zoipa za mtundu uliwonse.

23 Mulungu wamtendeleyo mwiniyo akuyeletseni kothelatu. Ndipo m’mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu, komanso thupi lanu, zikhale zopanda ulemali kapena colakwa ciliconse pa nthawi yakukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 24 Amene akukuitanani ndi wokhulupilika ndipo sadzalephela kucita zimenezi.

25 Abale, pitilizani kutipemphelela.

26 Mupeleke moni kwa abale onse, mwa kupsyompsyonana mwacikondi.*

27 Ndikukulamulani mwa Ambuye kuti mukawelenge kalatayi kwa abale onse.

28 Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Khristu cikhale nanu.

Amene anali kudziwikanso kuti Sila.

Ma Baibo ena amati, “imene tinali kubvutika kwambili.”

Kapena kuti, “tinali osangalala.”

Kucokela ku Cigiriki, “kuti tione nkhope zanu.”

Kucokela ku Cigiriki, “Kodi cisoti caulemelelo cimene tidzacinyadile.”

Ma Baibo ena amati, “ndi wanchito mnzake wa Mulungu.”

Kucokela ku Cigiriki, “asasocele.”

Kapena kuti, “kuti tiyenela kukumana ndi zimenezi.”

Kucokela ku Cigiriki, “pa zosowa zathu zonse.”

Kucokela ku Cigiriki, “ife timakhala ndi moyo.”

Kucokela ku Cigiriki, “kuti tidzaone nkhope zanu.”

Kapena kuti, “malamulo.”

M’Cigiriki, por·neiʹa. Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Kutanthauza Yesu.

Kapena kuti, “kubeleka.”

Kapena kuti, “kapena tigone mu imfa.”

Kapena kuti, “kuti muzilangiza.”

Kapena kuti, “kwa otaya mtima.”

Kucokela ku Cigiriki, “mwa kupsyompsyonana ndi mtima woyela.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani