LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 3 masa. 8-9
  • Onani Zimene Ena Amacita Bwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Onani Zimene Ena Amacita Bwino
  • Galamuka!—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta
  • Mfundo ya m’Baibo
  • Zimene Mungacite
  • Tsankho—Kodi Na Imwe Muli Nalo?
    Galamuka!—2020
  • Tikhale Amodzi, Monga Mmene Yehova na Yesu Alili Amodzi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • “Musamadziganizile Kuposa Mmene Muyenela Kudziganizila”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mmene Angakhalile Odzicepetsa
    Galamuka!—2019
Onaninso Zina
Galamuka!—2020
g20 na. 3 masa. 8-9
Zithunzi: 1. Mwamuna na mkazi wake amene akuthamangila kwinakwake akhumudwa poona kuti mayi wakhungu amene akudutsa kutsogolo kwawo akuwacedwetsa. 2. Pambuyo pake, banja limodzi-modzilo lacita cidwi kuona kuti mayi wakhungu uja akuimba gitala mocititsa cidwi.

Onani Zimene Ena Amacita Bwino

Cifukwa Cake Zingakhale Zovuta

Kudzikuza kumayambitsa tsankho. Munthu wodzikuza amadziona wofunika kwambili kuposa mmene alili. Amadziona kuti ni wapamwamba, ndipo anthu osiyana na iye amawaona kuti ni otsika. Aliyense angagwele mu msampha wa kudzikuza. Buku lakuti Encyclopædia Britannica limati: “M’zikhalidwe zambili, anthu amaona kuti mmene amacitila zinthu pa umoyo wawo, zakudya zawo, vovala, zizoloŵezi, zikhulupililo zawo, zokonda zawo, na zina zotelo ndiye zabwino kwambili kuposa za anthu ena.” Kodi tingapewe bwanji maganizo olakwika amenewa?

Mfundo ya m’Baibo

“Musacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzicepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”—AFILIPI 2:3.

Kodi mfundo imeneyi itanthauza ciani? Kuti tipewe kudzikuza, tifunika kukulitsa khalidwe la kudzicepetsa. Kudzicepetsa kumatithandiza kuzindikila kuti, pa zinthu zina, anthu ena amacita bwino kuposa ife. Palibe mtundu wa anthu umene uli na makhalidwe onse abwino na maluso.

Ganizilani citsanzo ca Stefan. Iye anakulila m’dziko la cikomyunizimu, koma anakwanitsa kuthetsa maganizo a tsankho oona kuti anthu a m’maiko amene si a cikomyunizimu ni otsika. Iye anati: “Niona kuti kuona ena kukhala otiposa n’kofunika kwambili polimbana na khalidwe la tsankho. Ine sinidziŵa zonse. Ndipo ningaphunzile cinacake kwa munthu aliyense.”

Zimene Mungacite

Muzidziona moyenela, ndipo musaiŵale kuti pali zina zimene simucita bwino. Vomelezani kuti ena amacita bwino pa mbali zimene imwe simucita bwino. Musakhale na maganizo akuti anthu onse a mtundu winawake ali na zofooka zofanana.

Mukakumana na munthu wocokela mu mtundu winawake, musathamangile kumuona kuti ali na vuto. Koma dzifunseni kuti:

Vomelezani kuti anthu ena amacita bwino pa mbali zina kuposa imwe

  • ‘Kodi makhalidwe amene sinikondwela nawo mwa munthu ameneyu ni oipadi, kapena ni osiyana cabe na makhalidwe anga?’

  • ‘Kodi munthu ameneyu anganipeze zifukwa ine?’

  • ‘Kodi ni mbali ziti zimene munthu ameneyu amacita bwino kuposa ine?’

Ngati mungayankhe mafunso amenewa moona mtima, mungathetse maganizo alionse olakwika amene muli nawo kwa munthuyo. Komanso mungazindikile kuti munthuyo ali na makhalidwe ena amene mungakonde.

Citsanzo ca Zocitika Zeni-Zeni: Nelson wa ku (United States)

“N’nakulila m’dela limene anthu ambili anali a mtundu umodzi komanso cikhalidwe cofanana. Koma nili na zaka 19, n’nakukila ku mzinda waukulu kukaseŵenza pa fakitale. Kumeneko, n’nayamba kuseŵenza ndi kukhala ndi anthu ocokela kosiyana-siyana, komanso a mitundu na zikhalidwe zosiyana-siyana.

“Pamene n’nawadziŵa bwino anzanga a kunchito na kupanga nawo ubwenzi, n’nazindikila kuti khungu la munthu, citundu cake, na dziko limene acokela sizinganithandize olo pang’ono kudziŵa kuti kaya munthuyo ni wolimbikila nchito, wodalilika, kapenanso kuti amaona zinthu motani.

“Patapita zaka n’nakwatila mkazi wocokela ku dziko lina, amenenso ni wa mtundu wosiyana na wanga. Ndipo ndine wokondwa ngako kudziŵa zakudya zosiyana-siyana na nyimbo zimene sin’nali kuzidziŵa. Naphunzila kuti tonse tili na zinthu zina zimene timacita bwino, ndiponso zina zimene siticita bwino. Kukamba zoona, nakhala munthu wabwino kwambili cifukwa cocita cidwi komanso kutengela makhalidwe abwino a anthu amene mtundu wawo na cikhalidwe cawo n’zosiyana ngako na zanga.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani