LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 202-nkhani 204 pala. 2
  • Coonadi Ponena za Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyela

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Coonadi Ponena za Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyela
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Tumitu
  • “MAU NDIYE MULUNGU”
  • DZIŴANI MFUNDO ZOONJEZELEKA
  • TSIMIKIZILANI MFUNDO ZIMENEZI
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 202-nkhani 204 pala. 2

ZAKUMAPETO

Coonadi Ponena za Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyela

ANTHU amene amakhulupilila ciphunzitso ca Utatu amakamba kuti mwa Mulungu mmodzi muli milungu itatu—mulungu Atate, mulungu Mwana, ndi mulungu Mzimu Woyela. Amati atatu amenewa amapanga Mulungu mmodzi. Amakhulupilila kuti onse atatu amenewa amalingana mphamvu ndipo onse alibe ciyambi. Conco, malinga ndi ciphunzitso ca Utatu, Atate ndi Mulungu, Mwana ndi Mulungu, Mzimu Woyela ndi Mulungu. Komabe amati kuli Mulungu mmodzi cabe.

Ambili amene amakhulupilila Utatu amavomeleza kuti samakwanitsa kufotokoza ciphunzitso cimeneci. Ngakhale ndi conco, io amaonabe kuti ndi ciphunzitso ca m’Baibo. Koma cofunika kudziŵa n’cakuti ngakhale liu cabe lakuti “Utatu” m’Baibo mulibe. Nanga ciphunzitso ca Utatu kodi cilimo m’Baibo? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione lemba limene nthawi zambili anthu amene amacilikiza ciphunzitso ca Utatu amagwilitsila nchito.

“MAU NDIYE MULUNGU”

Lemba la Yohane 1:1 limati: “Paciyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.” (Buku Lopatulika) Pa vesi lina m’caputala cimeneci, mtumwi Yohane amaonetsa bwino kwambili kuti “Mau” ni Yesu. (Yohane 1:14) Koma popeza kuti Mau amachedwa Mulungu, ena amaganiza kuti onse aŵili, Mwana ndi Atate, ali mbali ya Mulungu mmodzi.

Kumbukilani kuti mbali ya Baibo imeneyi inalembedwa m’Cigiriki. Pambuyo pake, otembenuza anatembenuzila mau a Cigiriki amenewa m’zinenelo zina. Koma otembenuza Baibo ena sanagwilitsile nchito mau akuti “Mau ndiye Mulungu.” N’cifukwa ciani? Malinga ndi zimene anali kudziŵa zokhudza Cigiriki ca m’Baibo, otembenuza amenewa anaona kuti mau akuti “Mau ndiye Mulungu” anayenela kutembenuzidwa mosiyana. Kodi anawatembenuza bwanji? Tiyeni tione zitsanzo zocepa: “Logosi [Mau] anali waumulungu.” (A New Translation of the Bible) “Mau anali kwa Mulungu “ ndipo anali waumulungu.” (The Translator’s New Testament) Malinga ndi Mabaibo amenewa, Mau si Mulungu Wamphamvuyonse.a Koma cifukwa ca malo ake apamwamba pakati pa zolengedwa za Yehova, Mau amachulidwa kuti ni “mulungu.” Conco, pano mau akuti “mulungu” amatanthauza “wamphamvu.”

DZIŴANI MFUNDO ZOONJEZELEKA

Anthu ambili samadziŵa Cigiriki ca m’Baibo. Conco, kodi mungadziŵe bwanji zimene mtumwi Yohane anali kutanthauza m’ceni-ceni? Tiyeni tione citsanzo ici: Tinene kuti mphunzitsi akufotokozela ana asukulu nkhani ina. Ndiyeno, ana asukulu aja asiyana kamvedwe ka nkhani imeneyo. Kodi ana asukulu aja angathetse bwanji vuto limenelo? Ayenela kufunsa mphunzitsi wao kuti awafotokozele zambili za nkhaniyo. Mosakaikila, kuphunzila mfundo zoonjezeleka kungawathandize kuti amvetse bwino kwambili nkhani imeneyo. Mofananamo, kuti mumvetse tanthauzo la Yohane 1:1, muyenela kuŵelenga Uthenga Wabwino wa Yohane kuti mudziŵe zambili za udindo wa Yesu. Kudziŵa mfundo zoonjezeleka pankhani imeneyi kudzakuthandizani kuti mudziŵe zeni-zeni.

Mwacitsanzo, onani zina zimene Yohane analemba m’caputala 1, vesi 18. Iye anati: “Palibe munthu anaonapo Mulungu [Wamphamvuyonse] ndi kale lonse.” Koma anthu anamuonapo Yesu, Mwanayo, cifukwa Yohane anati: “Mau [Yesu] anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemelelo wake.” (Yohane 1:14, Buku Lopatulika) Nanga Mwana angakhale bwanji mbali ya Mulungu Wamphamvuyonse? Yohane amakambanso kuti “Mau anali kwa Mulungu.” Koma zingatheke bwanji kuti munthu wina akhale kwa wina wake koma panthawi imodzi-imodzi n’kukhala munthuyo? Ndiponso, mogwilizana ndi Yohane 17:3, Yesu anaonetsa bwino kwambili kusiyana kumene kuli pakati pa iye mwini ndi Atate ake akumwamba. Iye amacha Atate ake kuti “Mulungu yekhayo amene ali woona.” Ndipo kumapeto kwa Uthenga wake Wabwino, Yohane anatsiliza nkhaniyi ndi mau akuti: “Izi zalembedwa kuti mukhulupilile kuti Yesu alidi Kristu Mwana wa Mulungu.” (Yohane 20:31) Onani kuti Yesu amachedwa Mwana wa Mulungu, osati Mulungu. Mfundo yoonjezeleka imeneyi yopezeka mu Uthenga Wabwino wa Yohane imaonetsa mmene tiyenela kumvelela lemba la Yohane 1:1. Yesu, kapena kuti Mau, ndi “mulungu” m’lingalilo lakuti iye ali ndi malo apamwamba, koma si wolingana ndi Mulungu Wamphamvuyonse.

TSIMIKIZILANI MFUNDO ZIMENEZI

Ganizilaninso za citsanzo ca mphunzitsi ndi ana asukulu. Tinene kuti ena akali kukaikilabe, ngakhale pambuyo pomvetsela mfundo zina zoonjezeleka zimene mphunzitsi wafotokoza. Kodi io angacite ciani? Angapite kwa mphunzitsi wina kuti awafotokozele mfundo zina pankhani imeneyi. Ngati mphunzitsi winayo avomeleza mfundo za mphunzitsi woyamba uja, ana asukulu ambili angasiye kukaikila. Mofananamo, ngati simuli wotsimikiza za zimene wolemba Baibo Yohane anali kutanthauza ponena za ubwenzi umene ulipo pakati pa Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse, mungaone zimene wolemba Baibo wina anakamba. Mwacitsanzo, onani zimene Mateyu analemba. Ponena za mapeto a nthawi ya pansi pano, anagwila mau a Yesu akuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziŵa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36) Kodi mau awa atsimikizila bwanji kuti Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse?

Yesu anati Atate amadziŵa zambili kuposa zimene Mwana amadziŵa. Komabe, ngati Yesu anali mbali ya Mulungu Wamphamvuyonse, iye akanadziŵa zinthu zofanana ndi zimene Atate ake amadziŵa. Conco, Mwana ndi Atate sangakhale olingana. Koma ena angakambe kuti: ‘Nthawi zina Yesu anali kukhala Mulungu ndipo nthawi zina anali kukhala munthu. Ndipo palemba limeneli anali kulankhula monga munthu.’ Koma ngakhale zikanakhala conco, nanga bwanji za mzimu woyela? Ngati uli mbali ina ya Mulungu mofanana ndi Atate, n’cifukwa ciani Yesu sanakambe kuti mzimuwo umadziŵa zimene Atate amadziŵa.

Pamene mupitiliza kuphunzila Baibo, mudzadziŵa nkhani zambili za m’Baibo zokhudza mfundo imeneyi. Nkhani zimenezi zimatsimikizila coonadi cokamba za Atate, Mwana, ndi mzimu woyela.—Salimo 90:2; Machitidwe 7:55; Akolose 1:15.

a Kuti mudziŵe zambili za Yohane 1:1, onani mapeji 24 ndi 25 a Nsanja ya Olonda ya November 1, 2008, yolembedwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani