LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 218-nkhani 219 pala. 1
  • Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndani?
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Nkhani Zofanana
  • Zoona Zake Ponena za Angelo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Kodi Angelo Ndani Kwenikweni, Ndipo Amacita Ciyani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 218-nkhani 219 pala. 1

ZAKUMAPETO

Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndani?

MIKAYELI amene ndi colengedwa cauzimu samachulidwa kaŵili-kaŵili m’Baibo. Koma akachulidwa m’Baibo ndiye kuti akucita cinthu cinacake. Buku la Danieli limaonetsa Mikayeli akulimbana ndi angelo oipa; m’kalata ya Yuda iye atsutsana ndi Satana; ndipo m’buku la Chivumbulutso acita nkhondo ndi Mdyelekezi ndi ziŵanda zake. Mwa kucilikiza ulamulilo wa Yehova ndi kumenyana ndi adani a Mulungu, Mikayeli amacita zinthu mogwilizana ndi tanthauzo la dzina lake lakuti, Ndani Ali Ngati Mulungu?” Koma kodi Mikayeli ndani maka-maka?

Nthawi zina, anthu amadziŵika ndi maina angapo. Mwacitsanzo, Yakobo anali kuchedwanso Isiraeli, ndipo mtumwi Petulo nayenso anali Simoni. (Genesis 49:1, 2; Mateyu 10:2) Mofananamo, Baibo imaonetsa kuti Mikayeli ndi dzina lina la Yesu Kristu. Iye anali kuchedwa ndi dzina limeneli akalibe kubwela pa dziko lapansi, ngakhale pambuyo pa moyo wake wa pa dziko. Tiyeni tione zifukwa za m’Malemba pa mfundo imeneyi.

Mkulu wa angelo: Mau a Mulungu amachula Mikayeli kuti ndi “mkulu wa angelo.” (Yuda 9) Zimenezi zionetsa kuti pali mngelo mmodzi cabe wochedwa kuti mkulu wa angelo. Ndipo mau akuti “mkulu wa angelo” m’Baibo nthawi zonse amakamba za munthu mmodzi, osati anthu ambili. Ndiponso, Yesu amakambidwa kukhala ndi udindo wa mkulu wa angelo. Ponena za Ambuye Yesu Kristu amene anaukitsidwa, lemba la 1 Atesalonika 4:16 limati: “Ambuye mwini adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mau a mkulu wa angelo.” Conco, mau a Yesu akunenedwa kukhala a mkulu wa angelo. Mwa ici, lemba limeneli lionetsa kuti Yesu weni-weniyo ndiye Mikayeli mkulu wa angelo.

Mtsogoleli wa Gulu la Nkhondo. Baibo imati “Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi cinjoka . . . ndi angelo ake.” (Chivumbulutso 12:7) Apa tiona kuti Mikayeli amene ndi Yesu alinso Mtsogoleli wa gulu la nkhondo la angelo okhulupilika. (Chivumbulutso 19:14-16) Ndipo mtumwi Paulo anachula mwacindunji za “Ambuye Yesu” ndi “angelo ake amphamvu.” (2 Atesalonika 1:7) Inde, Baibo imakamba za Mikayeli ndi “angelo ake” ndi Yesu ndi “angelo ake.” (Mateyu 13:41; 16:27; 24:31; 1 Petulo 3:22) Popeza palibe pamene Mau a Mulungu amakamba kuti pali magulu ankhondo aŵili a angelo okhulupilika kumwamba, gulu lina lotsogoleledwa ndi Mikayeli ndipo linanso ndi Yesu, m’pomveka kunena kuti Mikayeli ndiye Yesu Kristu paudindo wake kumwamba.a

a Kuti mudziŵe zambili zakuti dzina la Mikayeli ndi dzina la Mwana wa Mulungu, onani Voliyamu 2, m’buku la Insight on the Scriptures, pamapeji 393 mpaka 394, lolembedwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani