LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lv nkhani 7 nkhani 74-85
  • Kodi Mumalemekeza Moyo Mmene Mulungu Amaulemekezela?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mumalemekeza Moyo Mmene Mulungu Amaulemekezela?
  • “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MOYO NDI MAGAZI N’ZOPATULIKA
  • KUGWILITSILA NCHITO MAGAZI MONGA MANKHWALA
  • MALAMULO A YEHOVA AMAONETSA KUTI NDI TATE WACIKONDI
  • PEWANI CIDANI
  • PEWANI MABUNGWE AMENE ALI NDI MLANDU WA MAGAZI
  • LEMEKEZANI MOYO MWA KULALIKILA UTHENGA WA UFUMU
  • Kodi Mumaona Moyo Mmene Mulungu Amauonela?
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Mmene Mulungu Amaonela Moyo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Muzilemekeza Mphatso Ya Moyo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Mmene Mulungu Amawaonela Magazi
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
“Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
lv nkhani 7 nkhani 74-85
Mlongo asaina cosankha cake pa khadi la DPA

NKHANI 7

Kodi Mumalemekeza Moyo Mmene Mulungu Amaulemekezela?

“Inu ndinu kasupe wa moyo.”—SALIMO 36:9.

1, 2. Kodi ndi mphatso iti yocokela kwa Mulungu imene ndi yofunika kwambili masiku ano? Ndipo n’cifukwa ciani zili conco?

ATATE wathu wakumwamba watipatsa colowa camtengo wapatali. Colowa cimeneco ndi mphatso ya moyo. Iye anatilenga ndi nzelu ndipo tingakwanitse kutengela makhalidwe ake. (Genesis 1:27) Cifukwa ca mphatso ya mtengo wapatali imeneyi, timadziŵa mmene mfundo za m’Baibulo zingatipindulitsile. Kugwilitsila nchito mfundo zimenezi kungatithandize kukhala anthu okhwima kuuzimu. Tidzakhala anthu amene amakonda Yehova ndiponso ‘amene mphamvu zao za kuzindikila zaphunzitsidwa kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.’—Aheberi 5:14.

2 Kuganizila mfundo za m’Baibulo ndi kofunika makamaka masiku ano, cifukwa m’dziko mumacitika zinthu zambili cakuti n’zosatheka kukhala ndi malamulo pambali iliyonse ya moyo. Umboni wa zimenezi ndi sayansi ya zacipatala, makamaka tikaganizila za cithandizo ca mankhwala ndi njila zothandizila odwala pogwilitsila nchito magazi. Mbali imeneyi ndi yofunika kwambili kwa onse ofuna kumvela Yehova. Koma ngati timvetsetsa mfundo za m’Baibulo, tingapange zosankha zanzelu zimene zidzatithandiza kukhala ndi cikumbumtima coyela kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu. (Miyambo 2:6-11) Taganizilani mfundo zina izi.

MOYO NDI MAGAZI N’ZOPATULIKA

3, 4. Kodi ndi liti pamene kupatulika kwa magazi kunachulidwa m’Malemba kwa nthawi yoyamba? Ndipo lamulo limeneli ndi lozikidwa pa mfundo ziti?

3 Pambuyo pakuti Kaini wapha m’bale wake Abele, Yehova kwa nthawi yoyamba anasonyeza kuti moyo ndi magazi n’zogwilizana ndi kuti n’zopatulika. Mulungu anati kwa Kaini: “Tamvela tsono. Magazi a m’bale wako akundililila munthaka.” (Genesis 4:10) Kwa Yehova, magazi a Abele anaimila moyo wake, umene unaphedwa mwankhanza. Conco, m’mau ena tingakambe kuti, magazi a Abele analilila Mulungu kuti abwezele.—Aheberi 12:24.

4 Pambuyo pa Cigumula ca Nowa, Mulungu analola anthu kudya nyama koma anawaletsa kudya magazi. Mulungu anati: “Musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake. Kuonjezela pamenepo, ndidzafunsa za magazi anu.” (Genesis 9:4, 5) Lamulo limeneli linapelekedwa kwa mbadwa zonse za Nowa ndipo likali kugwila nchito masiku ano. Zimenezi zimatsimikizila mau amene Mulungu ananena kwa Kaini osonyeza kuti magazi amaimila moyo wa zolengedwa zonse. Lamulo limeneli limaonetsanso kuti Yehova, amene ndi Kasupe wa moyo, adzaimba mlandu anthu onse amene salemekeza moyo ndi magazi.—Salimo 36:9.

5, 6. Kodi Cilamulo ca Mose cinaonetsa bwanji kuti magazi ndi oyela ndipo ndi amtengo wapatali? (Onaninso kabokosi kakuti “Muzilemekeza Moyo Wa Nyama.”)

5 Cilamulo ca Mose cinaonetsa mfundo zofunika ziŵili zakuti magazi amaimila moyo ndi kuti ndi opatulika. Lemba la Levitiko 17:10, 11 limati: “Munthu aliyense . . . akadya magazi alionse, ndidzam’kana ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake. Pakuti moyo wa nyama uli m’magazi ndipo ine ndakuikilani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbilani macimo. Zili conco popeza magazi ndiwo amaphimba macimo, cifukwa moyo uli m’magaziwo.”a—Onani kabokosi kakuti “Mphamvu ya Magazi Yophimba Macimo”.

MPHAMVU YA MAGAZI YOPHIMBA MACIMO

Mau a Mulungu amaonetsa kuti magazi ndi moyo. Conco, mu Isiraeli wakale, munthu wocimwa amene walapa anali kupeleka nyama monga nsembe pa guwa la nsembe la Mulungu, m’malo mwakuti aphedwe cifukwa cophwanya malamulo a Yehova. (Levitiko 4:27-31) Nsembe imeneyi inali kuphimba macimo kwa nthawi yocepa cabe.

M’Baibulo, liu lakuti ‘cophimba’ limapeleka lingalilo la “kusinthanitsa” kapena “kuphimba” monga mmene civindikilo ca poto cimavindikilila bwinobwino pa poto wake. N’zoona kuti palibe nyama imene ikanaphimba bwinobwino macimo a munthu. Komabe, nsembe za nyama zinali kuimila nsembe yangwilo yamtsogolo yodzaphimba macimo.—Aheberi 10:1, 4.

Nsembe imeneyi inapelekedwa “kudzela m’thupi la Yesu Kristu lopelekedwa nsembe kamodzi kokha.” (Aheberi 10:10) Moyo wangwilo wa Kristu umene unaimililidwa ndi “magazi amtengo wapatali, monga a nkhosa yopanda cilema ndi yopanda maŵanga,” unali wolingana ndendende ndi moyo umene Adamu anataya. (1 Petulo 1:19) Conco, Yehova anacita zinthu mwacilungamo ndipo “anatilanditsa kwamuyaya.”—Aheberi 9:11, 12; Yohane 3:16; Chivumbulutso 7:14.

6 Ngati magazi a nyama imene yakhetsedwa sanagwilitsilidwe nchito pa guwa la nsembe, anayenela kuthilidwa pansi. Conco mophiphilitsila, zinali ngati kuti abwezela moyo kwa Mwini Wake. (Deuteronomo 12:16; Ezekieli 18:4) Koma izi sizitanthauza kuti Aisiraeli anali kufunikila kucita kunyanya kuyesetsa kucotsa magazi onse mu mnofu wa nyama. Malinga ngati nyama aikhetsa bwino, Mwisiraeli aliyense akanadya nyama imeneyo ndi cikumbumtima coyela. Kukhetsa nyama mwa njila imeneyo kunali kusonyeza ulemu kwa Wopeleka Moyo.

7. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti anali kuona magazi kukhala opatulika?

7 Davide “munthu wapamtima” pa Mulungu, anamvetsetsa mfundo imeneyi yokhudza lamulo la Mulungu la magazi. (Machitidwe 13:22) Panthawi ina iye atamva ludzu kwambili, amuna atatu anakakamizika kupita ku msasa wa adani ao kukatapa madzi pa citsime kuti iye amwe. Kodi Davide atadziŵa zimenezi anacita ciani? Iye anafunsa kuti: “Kodi ndimwe magazi a amuna amene anaika miyoyo yao pangozi kuti akatunge madziwa?” Kwa Davide madziwo anali ngati magazi a amuna atatuwo, amene anaika miyoyo yao pangozi kuti akamutapile madzi. Ngakhale kuti iye anali ndi ludzu “anawapeleka kwa Yehova mwa kuwathila pansi.”—2 Samueli 23:15-17.

8, 9. Pamene mpingo wacikristu unakhazikitsidwa, kodi Mulungu anasintha mmene amaonela moyo ndi magazi? Fotokozani.

8 Patapita zaka 2,400 kucokela pamene Nowa anauzidwa za kupatulika kwa magazi, ndiponso patapita zaka 1,500 kucokela pamene pangano la Cilamulo linapelekedwa, Yehova anauzila bungwe lolamulila la mpingo woyambilila wacikristu kulemba kuti: “Mzimu woyela pamodzi ndi ife taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemela, kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi kupitiliza kupewa zinthu zopelekedwa nsembe kwa mafano, magazi, zopotola, ndi dama.”—Machitidwe 15:28, 29.

9 N’zoonekelatu kuti bungwe lolamulila linazindikila kuti magazi ndi opatulika, ndi kuti kuwagwilitsila nchito molakwika kunali cimodzimodzi ndi kulambila mafano kapena kucita dama. Akristu oona masiku ano amaonanso kuti magazi ndi opatulika. Ndiponso popeza kuti Akristu amatsatila mfundo za m’Baibulo, io amakondweletsa Yehova popanga zosankha zokhudza kugwilitsila nchito magazi.

KUGWILITSILA NCHITO MAGAZI MONGA MANKHWALA

Mlongo afotokoza cosankha cake pankhani ya kuseŵenzetsa magazi kwa dokotala wake

Kodi ndingafotokoze bwanji kwa dokotala cosankha canga pankhani yogwilitsila nchito zigawo zing’onozing’ono za magazi?

10, 11. (a) Kodi Mboni za Yehova zimaona bwanji kuikidwa magazi ndi zigawo zake zikuluzikulu? (b) Kodi Akristu angasiyane maganizo pambali ziti zokhudza magazi?

10 Mboni za Yehova zimazindikila kuti “kupewa . . . magazi” kumatanthauza kukana kuikidwa magazi ndiponso kupeleka magazi ao kapena kuwasunga ndi colinga cakuti akawaikenso m’thupi mwao. Cifukwa colemekeza lamulo la Mulungu limeneli, io salandila zigawo zikuluzikulu zinai za magazi izi: maselo ofiila, maselo oyela, maselo oundanitsa magazi, ndi madzi a m’magazi.

11 Masiku ano, mwa njila zina zamakono, zigawo zimenezi za magazi zimagaŵidwa m’zigawo zing’onozing’ono zimene zimagwilitsidwa nchito m’njila zosiyanasiyana. Kodi Mkristu ayenela kulandila zigawo zing’onozing’ono zimenezi? Kodi ayenela kuona zigawo zimenezi kukhala “magazi”? Aliyense ayenela kudzisankhila yekha zocita pankhani imeneyi. N’cimodzimodzinso ndi njila zina zothandizila wodwala zofuna kugwilitsila nchito magazi ake popanda kuwasunga pambali. Njila zimenezi ndi monga kusefa magazi, kuwasungunula ndi kupulumutsa maselo a magazi ake.—Onani Zakumapeto, mutu wakuti “Tuzigawo twa Magazi ndi Njila Zimene Amatsatila Pocita Opaleshoni.”

12. N’ciani cimene tiyenela kucita pankhani zokhudza cikumbumtima?

12 Kodi Yehova amakhudzidwa ndi zosankha zathu? Inde amakhudzidwa cifukwa amacita cidwi ndi zimene timaganiza ndi zolinga zathu. (Ŵelengani Miyambo 17:3; 24:12.) Conco, pambuyo popemphela ndi kufufuza mankhwala kapena cithandizo cina cake, tiyenela kutsatila cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibulo. (Aroma 14:2, 22, 23) Komabe, ena sayenela kutiuza zocita kapena ife kuwafunsa kuti, “Ngati munali ndi vuto monga langa, kodi mukanacita ciani?” Pankhani za conco, Mkristu aliyense ayenela “kunyamula katundu wake.”b—Agalatiya 6:5; Aroma 14:12; onani bokosi kakuti “Kodi Ndimaona Magazi Kukhala Opatulika?”

MALAMULO A YEHOVA AMAONETSA KUTI NDI TATE WACIKONDI

13. Kodi malamulo ndiponso mfundo za Yehova zimavumbula ciani za iye? Pelekani citsanzo.

13 Malamulo ndiponso mfundo za m’Baibulo zimaonetsa kuti Yehova ndiye Wotipatsa Malamulo wanzelu ndipo ndi Tate wacikondi amene amasamalila ana ake. (Salimo 19:7-11) Lamulo la ‘kupewa . . . magazi’ silinapelekedwe monga lamulo la za umoyo. Komabe, limatiteteza ku mavuto amene amabwela cifukwa coikidwa magazi. (Machitidwe 15:20) Madokotala ambili amaona kuti kupanga maopaleshoni popanda kugwilitsila nchito magazi ndi “njila yabwino koposa” yopelekela cithandizo masiku ano. Kwa Akristu oona, zinthu ngati zimenezi zimatsimikizila kuti Yehova ali ndi nzelu zakuya ndipo ndi Tate wacikondi.—Ŵelengani Yesaya 55:9; Yohane 14:21, 23.

14, 15. (a) Kodi cikondi ca Mulungu kwa anthu ake cinaonekela m’malamulo ati? (b) Kodi mungagwilitsile nchito bwanji mfundo zotiteteza ku ngozi?

14 Malamulo ambili amene Mulungu anapeleka kwa Aisiraeli akale, anaonetsa kuti iye amasamalila anthu ake. Mwacitsanzo, iye analamula kuti nyumba iliyonse ya Mwisiraeli inayenela kukhala ndi kam’panda kuzungulila mtenje [tsindwi] kuti pasacitike ngozi, popeza kuti pamtenje ndi pamene io anali kucezela ndi kucitila zinthu zambili. (Deuteronomo 22:8; 1 Samueli 9:25, 26; Nehemiya 8:16; Machitidwe 10:9) Mulungu analamulanso kuti ng’ombe zoopsa anayenela kuziyang’anila. (Ekisodo 21:28, 29) Kunyalanyaza malangizo amenewa kunali kuonetsa kusalemekeza ena, ndipo munthu wocita zimenezi anali kukhala ndi mlandu wa magazi.

15 Kodi mfundo zimene zili m’malamulo amenewa mungazigwilitsile nchito motani? Ganizilani za galimoto yanu, mmene mumayendetsela galimoto, ziŵeto zanu, nyumba yanu, kumene mumagwilila nchito ndi zosangulutsa zimene mumasankha. M’maiko ena, ngozi ndi zimene zimapha acinyamata ambili, cifukwa cakuti nthawi zambili io sasamala m’zocita zao. Komabe, acinyamata amene amafuna kukhalabe m’cikondi ca Mulungu, amalemekeza moyo ndipo amapewa zosangulutsa zovulaza. Iwo saganiza mopanda nzelu kuti acinyamata sangavulale. M’malo mwake, amasangalala ndi unyamata wao mwa kupewa zinthu zimene zingaike moyo wao pangozi.—Mlaliki 11:9, 10.

16. Kodi ndi mfundo ya m’Baibulo iti imene imaletsa kucotsa mimba? (Onaninso mau a munsi.)

16 Ngakhale moyo wa mwana amene sanabadwe ndi wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu. Mu Isiraeli wakale, ngati munthu wavulaza mzimai amene ali ndi pakati, ndipo mzimaiyo kapena mwana amene ali mimba wafa, Mulungu anali kuona kuti munthu wovulaza mzimaiyo ali ndi mlandu wopha munthu, ndipo anayenela kupeleka “moyo kulipila moyo.”c (Ŵelengani Ekisodo 21:22, 23) Conco, ganizilani mmene Yehova amamvelela akaona ana ambilimbili amene amafa caka ciliconse cifukwa cocotsa mimba, ndipo ana ambili amenewa amaphedwa cifukwa ca dyela ndi uhule wa amai ao.

17. Kodi mungam’tonthoze bwanji munthu amene anacotsapo mimba asanaphunzile miyezo ya Mulungu?

17 Nanga bwanji ngati mzimai anacotsapo mimba asanaphunzile coonadi ca m’Baibulo? Kodi Mulungu angamukhululukile? Inde. Munthu akalapa angayembekezele Yehova kum’khululukila pamaziko a nsembe ya Yesu. (Salimo 103:8-14; Aefeso 1:7) Ndithudi, ndiye cifukwa cake Kristu anati: “Ine sindinabwele kudzaitana anthu olungama, koma ocimwa kuti alape.”—Luka 5:32.

PEWANI CIDANI

18. N’ciani cimene Baibulo limanena kuti n’cimene cimacititsa anthu kukhetsa magazi?

18 Kuonjezela pa kusavulaza ena, Yehova amafuna kuti ticotse udani m’mitima yathu cifukwa ndiwo umacititsa anthu kukhetsa magazi. Mtumwi Yohane analemba kuti; “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu.” (1 Yohane 3:15) Munthu waconco sazonda cabe m’bale wake, koma amafunanso kuti afe ndithu. Udani umenewu umaonekela pamene amaneneza m’bale wake nkhani zabodza, zimene ngati zitakhala zoona, m’bale wakeyo angafunikile kulangidwa ndi Yehova. (Levitiko 19:16; Deuteronomo 19:18-21; Mateyu 5:22) Conco, n’kofunika kuti tiyesetse kucotsa udani ulionse umene ungakhale m’mitima yathu.—Yakobo 1:14, 15; 4:1-3.

19. Kodi munthu amene amatsatila mfundo za m’Baibulo amaona bwanji mau a pa Salimo 11:5 ndi Afilipi 4:8, 9?

19 Anthu amene amalemekeza moyo monga mmene Yehova amacitila, ndiponso amene amafuna kukhalabe m’cikondi cake, amapewa ciwawa ca mtundu uliwonse. Lemba la Salimo 11:5 limati: “Mulungu amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa.” Lembali silikamba cabe za khalidwe la Mulungu koma palinso mfundo imene tiyenela kutsatila. Limalimbikitsa anthu amene amakonda Mulungu kupewa zosangulutsa zilizonse zimene zimalimbikitsa ciwawa. Mofananamo, mau akuti Yehova ndi “Mulungu wamtendele” amalimbikitsa atumiki ake kudzaza maganizo ndi mitima yao ndi zinthu zacikondi, zabwino ndi zotamandika, zimene zimabweletsa mtendele.—Ŵelengani Afilipi 4:8, 9.

PEWANI MABUNGWE AMENE ALI NDI MLANDU WA MAGAZI

20-22. Kodi Akristu amaliona bwanji dziko? Ndipo n’cifukwa ciani?

20 Mulungu amaona kuti dziko lonse la Satana lili ndi mlandu wa magazi. Malemba amaonetsa kuti maboma ndi zilombo zolusa, ndipo apha anthu mamiliyoni ambili, kuphatikizapo atumiki a Yehova ambilimbili. (Danieli 8:3, 4, 20-22; Chivumbulutso 13:1, 2, 7, 8) Anthu amalonda ndi asayansi, agwilizana ndi maboma amene ali ngati zilombo kupanga zida zoopsa kwambili, ndipo apeza phindu la ndalama zambili. N’zoonadi kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

21 Popeza kuti otsatila a Yesu ‘sali mbali ya dzikoli’ ndipo satenga mbali pa ndale ndi pa nkhondo, amapewa mlandu wa magazi.d (Yohane 15:19; 17:16) Ndipo motsatila citsanzo ca Kristu, io sabwezela anthu amene amawazunza. M’malo mwake, amakonda adani ao, ndipo amawapemphelela.—Mateyu 5:44; Aroma 12:17-21.

22 Koposa zonse, Akristu oona amapewa kugwilizana ndi “Babulo Wamkulu,” ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama. Babulo Wamkulu ali ndi mlandu wa magazi koposa onse. Mau a Mulungu amati: “Mwa iye munapezeka magazi a aneneli, a oyela, ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” Conco, akuticenjeza kuti: “Tulukani mwa iye anthu anga.”—Chivumbulutso 17:6; 18:2, 4, 24.

23. Kodi kutuluka m’Babulo Wamkulu kumatanthauzanji?

23 Kutuluka m’Babulo Wamkulu kumaphatikizapo zambili osati cabe kufafanizitsa dzina m’buku la kuchalichi. Kumaphatikizaponso kudana ndi zinthu zoipa zimene cipembedzo conama cimalekelela kapena kulimbikitsa, monga ciwelewele, kutenga mbali m’ndale, ndi kufunafuna cuma mwadyela. (Ŵelengani Salimo 97:10; Chivumbulutso 18:7, 9, 11-17) Zinthu zimenezi nthawi zambili zimacititsa anthu kuphana.

24, 25. (a) Kodi Mulungu angacitile cifundo munthu wolapa amene ali ndi mlandu wa magazi pa maziko ati? (b) Nanga zimenezi zitikumbutsa makonzedwe ati a m’nthawi za m’Baibulo?

24 Tisanaphunzile coonadi, aliyense wa ife m’njila inayake anacilikiza dongosolo la Satana, ndipo tinali ndi mlandu wa magazi. Komabe, cifukwa cakuti tinasintha khalidwe lathu, tinakhulupilila nsembe ya dipo la Kristu ndi kudzipeleka kwa Mulungu, iye anaticitila cifundo ndipo amatiteteza mwakuuzimu. (Machitidwe 3:19) M’nthawi za m’Baibulo, citetezo cimeneco cimatikumbutsa mizinda yothaŵilako kapena kuti yopulumukilako.—Numeri 35:11-15; Deuteronomo 21:1-9.

25 Kodi makonzedwe amenewa anali kugwila nchito motani? Ngati Mwisiraeli wapha munthu mwangozi, anayenela kuthaŵila ku umodzi wa mizinda imeneyi. Pambuyo pakuti oweluza oyenelela aweluza mlandu wake, wopha munthu mwangozi anayenela kukhala mumzinda wopulumukilako mpaka mkulu wa ansembe atafa. Ndiyeno, iye anali womasuka kukhala kulikonse. Zimenezi zinaonetsa kuti Mulungu ali ndi cifundo cacikulu, ndipo amalemekeza moyo kwambili. Mofanana ndi mizinda yopulumukilako yakale imeneyo, masiku ano makonzedwe a Mulungu kudzela mu nsembe ya dipo la Kristu, amatiteteza ngati taphwanya lamulo la Mulungu mwangozi lokhudza kupatulika kwa moyo ndi magazi. Kodi mumayamikila makonzedwe amenewa? Kodi mungaonetse bwanji kuti mumayamikila? Njila imodzi ndi kuthandiza anthu ena kuti adziŵe za citetezo ca dipo cimeneco cimene Mulungu wapeleka, cifukwa “cisautso cacikulu” cayandikila kwambili.—Mateyu 24:21; 2 Akorinto 6:1, 2.

LEMEKEZANI MOYO MWA KULALIKILA UTHENGA WA UFUMU

26-28. Mmene zinthu zilili kwa ife masiku ano, zimafanana bwanji ndi mmene zinalili kwa mneneli Ezekieli? Nanga tiyenela kucita ciani kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu?

26 Masiku ano, anthu a Mulungu amafanana ndi mneneli Ezekieli, amene anapatsidwa nchito ndi Yehova yokhala mlonda wa kuuzimu wa nyumba ya Isiraeli. Mulungu anati: “Umve mau ocokela pakamwa panga ndi kundicenjezela anthuwo.” Ezekieli akananyalanyaza lamulo limene anapatsidwa, akanakhala ndi mlandu wa magazi a anthu amene anaphedwa pamene Yerusalemu anaonongedwa. (Ezekieli 33:7-9) Koma Ezekieli anamvela ndipo sanakhale ndi mlandu wa magazi.

27 Tsopano, mapeto a dziko lonse la Satana ali pafupi kwambili. Conco, Mboni za Yehova zimaona kuti zili ndi udindo ndi mwai wolengeza “tsiku lobwezela” la Mulungu polalikila uthenga wa Ufumu. (Yesaya 61:2; Mateyu 24:14.) Kodi inuyo mumagwila mokwanila nchito yofunika imeneyi? Mtumwi Paulo anali wacangu kwambili pa nchito yolalikila. Ndiye cifukwa cake ananena kuti: “Ine ndine woyela pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisileni kanthu, koma ndinakuuzani cifunilo conse ca Mulungu.” (Machitidwe 20:26, 27) Cimeneci n’citsanzo cabwino cimene tiyenela kutsatila.

28 Komabe, kuti tikhalebe m’cikondi ca Atate wathu Yehova, tiyenela kucita zambili osati cabe kuona moyo ndi magazi mmene Yehova amazionela. Tifunikanso kupitiliza kukhala oyela pamaso pake, monga mmene tidzaphunzilila m’nkhani yotsatila.

a Ponena za mau amene Mulungu anakamba akuti “moyo wa nyama uli m’magazi,” buku lakuti Scientific American linati: “Mau amenewa si ophiphilitsa cabe, koma amakamba zenizeni cifukwa selo lililonse la magazi limacilikiza moyo.”

b Onani Galamukani! ya August 2006, patsamba 3 mpaka 12, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

c Anthu olemba mabuku ofotokoza Baibulo amati mau aciheberi pa lembali, “amaonetsa kuti mau amenewa sakamba za kuvulala kwa mai yekha.” Ndipo Baibulo silinena kuti Yehova anali kupeleka ciweluzo modalila miyezi ya mwana amene ali m’mimba.

d Onani Nkhani 5 yakuti, “Mmene Tingakhalile Olekana ndi Dziko.”

KODI NDIMAONA MAGAZI KUKHALA OPATULIKA?

Mfundo yofunika: ‘Pewani . . . magazi.’ —Machitidwe 15:20.

Mafunso ena amene mungadzifunse

  • Kodi ndingafotokoze bwanji kusiyana pakati pa zigawo zikuluzikulu za magazi ndi tuzigawo tung’onotung’ono?e

  • N’cifukwa ciani ndiyenela kudzisankhila ndekha kulandila kapena kukana tuzigawo tung’onotung’ono twa magazi, kapenanso kukana njila zina zofuna kugwilitsila nchito magazi anga?—Aroma 12:2; Agalatiya 6:5.

  • Kodi ndingafotokoze bwanji kwa adokotala cifukwa cake ndingalandile kapena kukana tuzigawo tung’onotung’ono twa magazi?—Miyambo 13:16.

e Kuti mudziŵe zambili, onani Zakumapeto, mutu wakuti “Tuzigawo twa Magazi Ndiponso Njila Zimene Amatsatila Pocita Opaleshoni”

MUZILEMEKEZA MOYO WA NYAMA

Ngakhale kuti Yehova amatilola kupha nyama kuti tipeze cakudya ndi zovala kapena kuti tipewe kuvulazidwa, tiyenela kucita zimenezo mwa njila yoyenela ndi mokoma mtima. (Genesis 3:21; 9:3) Sitiyenela kukhala ngati Nimurodi, wosaka nyama wankhanza amene anali kupha nyama pofuna kudzisangalatsa yekha. (Genesis 10:9) M’malo mwake, tiyenela kutsatila citsanzo ca Yehova, amene amasamalila nyama zonse, ngakhale tumpheta.—Yona 4:11; Mateyu 10:29.

Cilamulo ca Mose cinaonetsa kuti Mulungu amasamalila moyo wa nyama. (Ekisodo 23:4, 5, 12; Deuteronomo 22:10; 25:4) Mogwilizana ndi Cilamulo cimeneco, lemba la Miyambo 12:10 limati: “Wolungama amasamalila moyo wa ciŵeto cake, koma cisamalilo ca anthu oipa n’cankhanza.” Posacedwapa, anthu ankhanza adzaonongedwa limodzi ndi zocita zao zankhanza.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani