Mau Oyamba
Mulungu ali monga tate wacikondi. 1 Petulo 5:6, 7
Mulungu ni Mlengi wathu, ndipo amatisamalila. Tate wacikondi amaphunzitsa ana ake. Naye Mulungu amaphunzitsa anthu kulikonse mmene io angakhalile bwino.
Mulungu amatidziŵitsa coonadi camtengo wapatali cimene cimatipatsa cimwemwe ndi ciyembekezo.
Ngati mumamvetsela kwa Mulungu, iye adzakutsogolelani ndi kukuchinjilizani ndipo adzakuthandizani pa mavuto.
Koma palinso zina, mudzakhala ndi moyo wamuyaya!