Mau kwa Makolo
Kodi ndi mphatso yamtengo wapatali iti imene mungapatse ana anu? Pali zambili zimene ana amafunikila, io amafunikila cikondi, citsogozo, ndi citetezo. Koma cinthu camtengo wapatali kwambili cimene mungapatse ana anu ndi kudziŵa Yehova ndi coonadi copezeka m’Mau ake Baibo. (Yohane 17:3) Cidziŵitso cimeneci cingathandize ana anu kuti akulitse cikondi cao pa Yehova ndi kuti am’tumikile ndi mtima wonse akali ana kwambili.—Mateyu 21:16.
Makolo ambili aona kuti ana aang’ono amamva msanga ngati aphunzila zinthu zocepa komanso ngati sacita zinthu zambili. Ndife okondwa kukudziŵitsani kuti takonza kabuku kakuti, Zimene Ndimaphunzila m’Baibo. Phunzilo lililonse lakonzedwa kuti lithandize kuphunzitsa m’njila yosavuta. Zithunzi-thunzi ndi mau ake zakonzedwela maka-maka ana a zaka zitatu kapena zocepelapo. Kalinso ndi mbali ya zimene makolo ayenela kucita. Kabuku aka sikoseŵeletsa iyai, koma ndi kophunzitsila ana. Kapangidwa m’njila yakuti muziŵelengela ana anu, zimene zidzathandiza kuti muzikambitsilana nao momasuka.
Ndife otsimikiza kuti kabuku aka kadzakhala kothandiza kwambili kuti muphunzitse ana anu coonadi ca m’Baibo kuyambila pa ‘ukhanda wao.’—2 Timoteyo 3:14, 15.
Ife abale anu,
Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova
[Cithunzi papeji 3]