Phunzilo 4
Mailesi adandaula kuti, lelo kuli mvula.
“Siningatuluke panja.
N’cifukwa ciani siileka?”
Tsopano Mailesi wakondwela!
Cifukwa dzuŵa layamba kuwala.
Ndipo mvula yatha.
Ndiyeno athamangila panja, ndipo asangalala, cifukwa paoneka bwino.
Mailesi akamba kuti, “sindinadziŵe kuti ndi Mulungu amene amagwetsa mvula kuti maluŵa amele.”
ZOCITA
Muŵelengeleni mwana wanu:
Uzani mwana wanu kuti aloze:
Windo Mbalame Mailesi
Mtengo Maluŵa
Pezani zinthu zobisika.
Kanunda (Cikumbu) Ndege
M’funseni mwana wanu:
N’cifukwa ciani Yehova analenga mvula?
[Cithunzi 10]
[Cithunzi 10]
[Cithunzi 11]