Zimene Tingaphunzilepo Pa Pemphelo Lokonzedwa Bwino
“Anthuwa atamande dzina lanu laulemelelo.”—NEH. 9:5.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Ndi zinthu zabwino ziti zimene Aisiraeli anacita pamene Alevi anawasonkhanitsa pamodzi?
Ndi citsanzo citi cimene cionetsa kuti Mulungu amakwanilitsa malonjezo ake?
Kodi pemphelo la Alevi limatiphunzitsa mfundo ziti?
1. Kodi tidzakambilana za msonkhano uti umene anthu a Mulungu anacita? Ndipo tiyenela kudzifunsa mafunso ati?
ALEVI anapempha anthu a Mulungu akale kuti asonkhane ndi kupemphela kwa Yehova. Iwo anati: “Dzukani, tamandani Yehova Mulungu wanu kuyambila kale-kale mpaka kale-kale.” Pemphelo limene anapeleka panthawiyo ndi limodzi mwa mapemphelo aatali olembedwa m’Baibo. (Neh. 9:4, 5) Iwo anasonkhana ku Yerusalemu pa tsiku la 24, m’mwezi wa Ayuda wa 7 wochedwa Tishiri, (September kapena October) m’caka ca 455 B.C.E. Pamene tikambilana zimene zinacitika tsiku lapadela limeneli lisanafike, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi makhalidwe abwino ati amene anapangitsa kuti cocitika ici cikhale cacipambano? Kodi ndi maphunzilo ena ati amene tingaphunzilepo pa pemphelo lokonzedwa bwino limeneli?’—Sal. 141:2.
MWEZI WAPADELA
2. Kodi Aisiraeli anatipatsa citsanzo cotani pa msonkhano umene anacita atamaliza kumanganso mpanda wa Yerusalemu?
2 Ayuda anacita msonkhano umenewu patapita mwezi umodzi kucokela pamene anamaliza kumanganso mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 6:15) Anthu a Mulungu anamaliza kugwila nchito imeneyi pambuyo pa masiku 52 cabe, ndipo atamaliza anayamba kusamalila zosoŵa zao za kuuzimu. Pa tsiku loyamba la mwezi wotsatila wa Tishiri, io anasonkhana m’bwalo lalikulu kuti amvetsele pamene Ezara ndi Alevi ena anali kuŵelenga ndi kufotokozela Cilamulo ca Mulungu. (Cithunzi-thunzi 1) Mabanja onse, kuphatikizapo onse “amene akanatha kumvetsela ndi kuzindikila,” anaimilila ndi kumvetsela “kuyambila m’mawa mpaka masana.” Cimeneci ndi citsanzo cabwino kwa ife masiku ano amene timasonkhana m’Nyumba za Ufumu zabwino. Kodi nthawi zina timayamba kuganizila zinthu zina zosafunika pamene tili pamisonkhano? Ngati ndi conco, kumbukilani citsanzo ca Aisiraeli akale amene anamvetsela ndi kusinkha-sinkha zimene anamva, ndipo anayamba kulila cifukwa cakuti mtundu wao unalephela kumvela Cilamulo ca Mulungu.—Neh. 8:1-9.
3. Kodi Aisiraeli anamvela langizo liti?
3 Komabe, iyi sinali nthawi youlula macimo ao. Pokhala tsiku la cikondwelelo, inali nthawi yakuti asangalale monga alambili a Yehova. (Cithunzi-thunzi 2) (Num. 29:1) Conco Nehemiya anauza anthuwo kuti: “Pitani mukadye zinthu zonona, kumwa zinthu zokoma ndi kugaŵa cakudya kwa anthu amene sanathe kudzikonzela cakudya, pakuti lelo ndi tsiku lopatulika kwa Ambuye wathu. Conco musadzimvele cisoni pakuti cimwemwe cimene Yehova amapeleka ndico malo anu acitetezo.” Anthuwo anamvela ndipo tsiku limenelo io ‘anakondwela kwambili.’—Neh. 8:10-12.
4. Kodi atsogoleli a mabanja a Aisiraeli anacita ciani? Nanga n’ciani cimene Alevi anali kucita tsiku lililonse pa Cikondwelelo ca Misasa?
4 Tsiku lotsatila, atsogoleli a mabanja onse anasonkhana kuti aphunzile Cilamulo ndi colinga cakuti azitsatila malamulo onse Mulungu. (Cithunzi-thunzi 3) Pamene anaphunzila Malemba, io anazindikila kuti anali kufunika kucita Cikondwelelo ca Misasa kuyambila pa tsiku la 15 mpaka pa tsiku la 22, m’mwezi wa 7 wa Tishiri. Ndipo tsiku lomaliza anali kufunika kucita msonkhano wapadela. Conco, io anayamba kukonzekela. (Cithunzi-thunzi 4) Cimeneci cinali Cikondwelelo ca Misasa cacipambano kwambili cimene sicinacitikepo kucokela m’nthawi ya Yoswa, ndipo panali “cisangalalo cacikulu.” Cinthu cacikulu cimene cinacitika pa cikondwelelo cimeneci n’cakuti Alevi anali kuŵelenga poyela Cilamulo ca Mulungu, “tsiku ndi tsiku, kucokela tsiku loyamba mpaka tsiku lomaliza.”—Neh. 8:13-18.
TSIKU LOULULA MACIMO
5. Kodi anthu a Mulungu anacita ciani Alevi asanapemphele kwa Yehova?
5 Patapita masiku aŵili nthawi inafika yakuti Aisiraeli aulule macimo. Imeneyi sinali nthawi ya madyelelo. Koma anthu a Mulungu anasala kudya ndi kuvala ziguduli kuti aonetsa cisoni cao. Alevi anaŵelengelanso anthu Cilamulo ca Mulungu kwa maola pafupi-fupi atatu m’mawa. Masana, anthuwo “anali kuulula macimo ao ndi kugwadila Yehova Mulungu wao.” (Cithunzi-thunzi 5) Ndiyeno, Alevi anapeleka pemphelo lokonzedwa bwino moimilako anthu onse. (Cithunzi-thunzi 6)—Neh. 9:1-4.
6. N’ciani cinathandiza Alevi kupeleka mapemphelo atanthauzo? Ndipo zimenezi zikutiphunzitsa ciani?
6 Mosakaikila, kuŵelenga Cilamulo ca Mulungu nthawi zonse kunathandiza Alevi kukonza mapemphelo ao kuti akhale atanthauzo. Mavesi 10 oyambilila maka-maka amakamba za nchito ndi makhalidwe a Yehova. Mbali yomaliza ya pemphelo limeneli imachula ‘cifundo cacikulu’ ca Mulungu mobweleza-bweleza, ndipo imaonetsa kuti Aisiraeli sanali oyenela kusonyezedwa cifundo cimeneco. (Neh. 9:19, 27, 28, 31) Mapemphelo athu kwa Yehova adzakhala atanthauzo ngati timasinkha-sinkha Mau a Mulungu masiku onse monga mmene Alevi anacitila. Mwakutelo, timalola Yehova kukamba nafe tisanapemphele.—Sal. 1:1, 2.
7. Kodi Alevi anapempha ciani kwa Mulungu? Ndipo tiphunzilapo ciani pamenepa?
7 M’pemphelo limeneli, Alevi anangopempha cinthu cimodzi. Cinthu cimeneci cimapezeka m’mbali yomaliza ya vesi 32. Vesi limeneli limati: “Tsopano Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi wocititsa mantha, wosunga pangano ndi kusonyeza kukoma mtima kosatha, musacepetse mavuto onse amene agwela ifeyo, mafumu athu, akalonga athu, ansembe athu, aneneli athu, makolo athu ndi anthu anu onse kucokela masiku a mafumu a Asuri mpaka lelo.” Conco, Alevi anatipatsa citsanzo cakuti tiyenela kutamanda ndi kuyamikila Yehova coyamba tisanapemphe zosoŵa zathu.
KUTAMANDA DZINA LA MULUNGU LA ULEMELELO
8, 9. (a) Kodi Alevi anakamba ciani modzicepetsa poyamba pemphelo lao? (b) Kodi Alevi anakamba za makamu aŵili ati a kumwamba?
8 Ngakhale kuti pemphelo la Alevi linali lokonzedwa bwino, io anali odzicepetsa ndipo anaona kuti mau ao sanali okwanila kupeleka citamando cimene Yehova ayenela kulandila. Conco, poyamba pemphelo lao, io modzicepetsa anapemphelela anthu a Mulungu kuti: “Anthuwa atamande dzina lanu laulemelelo, lokwezeka kuposa dalitso ndi citamando ciliconse.”—Neh. 9:5.
9 Iwo anapitiliza kupemphela kuti: “Inu ndinu Yehova, inu nokha. Ndinu amene munapanga kumwamba, ngakhale kumwamba-mwamba ndi makamu ake onse. Ndinu amene munapanga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo komanso nyanja ndi zonse zili momwemo. Ndinu amene mukusunga zinthu zonse kuti zikhale ndi moyo. Ndipo makamu akumwamba amakugwadilani.” (Neh. 9:6) Yehova Mulungu ndiye analenga cilengedwe conse, mmene muli milalang’amba ya nyenyezi zosaŵelengeka. Ndipo si apo pokha, analenganso zinthu zonse zimene zili padziko lathu lokongola limene lili ndi mphamvu zodabwitsa zokwanitsa kusunga zamoyo zosiyana-siyana zimene zimabelekana mwa mtundu wao. Angelo a Mulungu oyela amene amachedwanso kuti “makamu onse akumwamba,” anaona pamene iye anali kulenga zimenezi. (1 Maf. 22:19; Yobu 38:4, 7) Ndiponso io modzicepetsa amacita cifunilo ca Mulungu mwa kutumikila anthu ocimwa “amene adzalandile cipulumutso monga coloŵa cao.” (Aheb. 1:14.) Angelo amenewa amatipatsa citsanzo cabwino kwambili pamene titumikila Yehova mogwilizana monga gulu la asilikali lophunzitsidwa bwino.—1 Akor. 14:33, 40.
10. Kodi tikuphunzilapo ciani pa zimene Mulungu anacitila Abulahamu?
10 Ndiyeno, Alevi anachula zimene Mulungu anacitila Abulamu amene anafika zaka 99 alibe mwana cifukwa mkazi wake Sarai sanali kubeleka. Ndipo pa nthawi imeneyo, Yehova anasintha dzina lake kukhala Abulahamu, limene limatanthauza “tate wa mitundu yambili.” (Gen. 17:1-6, 15, 16) Mulungu analonjezanso Abulahamu kuti ana ake adzakhala m’dziko la Kanani. Nthawi zambili anthu amalephela kukwanilitsa malonjezo ao, koma Yehova samalephela. M’pemphelo lao, Alevi anati: “Inu ndinu Yehova Mulungu woona, amene munasankha Abulamu ndi kum’tulutsa ku Uri wa Akasidi ndipo munamucha dzina lakuti Abulahamu. Munamuona kuti anali ndi mtima wokhulupilika pamaso panu. Cotelo munacita naye pangano kuti mudzam’patsa dziko la Akanani, . . . Munacita naye pangano kuti mudzapeleka dziko limeneli kwa mbeu yake, ndipo munacitadi zimene munanena cifukwa ndinu wolungama.” (Neh. 9:7, 8) Tiyeni nafenso titsatile citsanzo ca Mulungu wathu wolungama mwa kuyesetsa kucita zimene talonjeza.—Mat. 5:37.
ANAFOTOKOZA ZOCITA ZA YEHOVA
11, 12. Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauzanji? Nanga zimene iye anacitila mbadwa za Abulahamu zimaonetsa bwanji kuti ndi woyenela dzina limeneli?
11 Dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti “Amacititsa Kukhala,” kuonetsa kuti Mulungu amakwanilitsa malonjezo ake. Zimenezi zimaoneka bwino ndi mmene Mulungu anasamalilila mbadwa za Abulahamu pamene zinali mu ukapolo ku Iguputo. Panthawi imeneyo, zinali kuoneka monga zosatheka kuti mtundu wa Asiraeli ungamasuke ndi kukhala m’Dziko Lolonjezedwa. Koma Mulungu anacita zonse zofunikila kuti akwanilitse lonjezo lake ndi kuonetsa kuti iye ndi woyenelela dzina lakuti Yehova, limene ndi lapadela ndiponso lokwezeka.
12 Pemphelo limene Nehemiya analemba limakamba za Yehova kuti: “Inu munaona nsautso ya makolo athu ku Iguputo ndipo munamvanso kulila kwao pa Nyanja Yofiila. Ndiyeno munaonetsa Farao zizindikilo ndi zozizwitsa zomukhaulitsa pamodzi ndi atumiki ake onse ndi anthu onse okhala m’dziko lake. Munatelo cifukwa munadziŵa kuti io anacita zinthu modzikuza kwa makolo athu. Pamenepo munadzipangila dzina kufikila lelo. Munagaŵa nyanja pamaso pao ndipo io anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja. Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama ngati mwala woponyedwa m’madzi amphamvu.” Pemphelo limeneli limakambanso zinthu zina zimene Yehova anacitila anthu ake kuti: “Munagonjetsa anthu okhala m’dzikolo, Akanani, . . . Iwo analanda mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambili. Analandanso nthaka yaconde, nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime, minda ya mpesa ndi ya maolivi ndi mitengo ya zipatso yoculuka. Atatelo, anayamba kudya, kukhuta, kunenepa ndi kukondwela ndi ubwino wanu waukulu.”—Neh. 9:9-11, 24, 25.
13. Kodi Yehova anawasamalila bwanji Aisiraeli mwa kuuzimu? Nanga io anacita ciani?
13 Pali zinthu zina zambili zimene Mulungu anacita kuti akwanilitse colinga cake. Mwacitsanzo, pamene Aisiraeli anatuluka mu Iguputo, Yehova anawapatsa zosoŵa zao za kuuzimu. Alevi anapitiliza kupemphela kwa Mulungu kuti: “Munatsikila paphili la Sinai ndi kulankhula nao muli kumwamba. Munawapatsa zigamulo zoongoka ndi malamulo a coonadi, mfundo zabwino ndi malangizo abwino.” (Neh. 9:13) Yehova anasankha Aisiraeli kukhala anthu ake ndipo analonjeza kuti adzawapatsa Dziko Lolonjezedwa. Conco, anawaphunzitsa kukhala ndi makhalidwe amene amalemekeza dzina lake loyela. Koma io analeka kutsatila zinthu zabwino zimene anaphunzila.—Ŵelengani Nehemiya 9:16-18.
ANAFUNIKILA KUPATSIDWA CILANGO
14, 15. (a) Kodi Yehova anasonyeza bwanji cifundo kwa anthu ake ocimwa? (b) Kodi zimene Mulungu anacitila mtundu wake zimatiphunzitsa ciani?
14 Pemphelo la Alevi limachula zinthu ziŵili zimene Aisiraeli analakwitsa atalonjeza kumene pa Phiri Sinai kuti adzasunga Malamulo a Mulungu. Cifukwa ca macimo amenewa, io anayenela kufa. Koma pemphelo limeneli limatamanda Yehova kuti: “Simunawasiye m’cipululu cifukwa ca cifundo canu cacikulu. . . . Kwa zaka 40 munawapatsa cakudya . . . Iwo sanasoŵe kanthu. Zovala zao sizinathe ndipo mapazi ao sanatupe.” (Neh. 9:19, 21) Masiku ano, Yehova amatipatsa ciliconse cimene timafunikila kuti tizim’tumikila mokhulupilika. Sitiyenela kukhala ngati Aisiraeli masauzande ambili amene anafa m’cipululu kaamba ka kusamvela ndi kusoŵa cikhulupililo. Ndipo zinthu zimenezi “zinalembedwa kuti ziticenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikila.”—1 Akor. 10:1-11.
15 N’zomvetsa cisoni kuti pamene Aisiraeli analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa, anayamba kulambila milungu ya Akanani ndipo anali kucita ciwelewele ndi kupeleka nsembe ana ao. Pa cifukwa cimeneco, Yehova analola anthu a mitundu ina kupondeleza anthu ake. Pamene io analapa, Yehova mwacifundo anawakhululukila ndi kuwapulumutsa kwa adani ao. Zimenezi zinacitika “mobweleza-bweleza.” (Ŵelengani Nehemiya 9:26-28, 31.) Alevi anati: “Munaleza nao mtima kwa zaka zambili ndipo munapitilizabe kuwacenjeza mwa mzimu wanu potumiza aneneli anu, koma io sanamvele. Pamapeto pake munawapeleka m’manja mwa mitundu ya anthu ya m’dzikolo.”—Neh. 9:30.
16, 17. (a) N’ciani cinacitika pamene Aisiraeli anayambanso kusamvela Yehova? (b) Kodi Aisiraeli anavomeleza ciani? Ndipo analonjeza kuti adzacita ciani?
16 Ngakhale pamene anabwela kucoka ku ukapolo, Aisiraeli anayambanso kusamvela. Kodi zotsatila zake zinali zotani? Alevi anapitiliza kupemphela kuti: “Onani, lelo ife ndife akapolo. Ndife akapolo m’dziko limene munapatsa makolo athu kuti adye zipatso zake ndi zinthu zake zabwino. Zokolola za m’dzikoli zaculukila mafumu amene mwatiikila cifukwa ca macimo athu . . . ndipo tili pamavuto aakulu.”—Neh. 9:36, 37.
17 Kodi Alevi anali kuonetsa kuti Mulungu analakwa kulola kuti Aisiraeli avutike? Ai si conco. Iwo anavomeleza kulakwa kwao ndi kunena kuti: “Inu ndinu wolungama pa zinthu zonse zimene zaticitikila, pakuti inu mwacita zinthu mokhulupilika koma ife tacita zinthu zoipa.” (Neh. 9:33) Ndiyeno, io anamaliza pemphelo lao lokonzedwa bwino mwa kulonjeza kuti mtundu wao udzamvela Malamulo a Mulungu. (Ŵelengani Nehemiya 9:38; 10:29) Motelo, atsogoleli 84 a Ayuda analemba cikalata ndi kusindikizapo zidindo zao.—Neh. 10:1-27.
18, 19. (a) Kodi tiyenela kucita ciani kuti tidzapulumuke ndi kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu? (b) Kodi tiyenela kupitiliza kupemphelela ciani? Nanga n’cifukwa ciani?
18 Timafunikila kulangizidwa ndi Yehova kuti tikapulumuke ndi kuloŵa m’dziko latsopano la cilungamo. Mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Ndi mwana wanji amene bambo ake samulanga?” (Aheb. 12:7) Timaonetsa kuti timalola Mulungu kutitsogolela pa umoyo wathu mwa kupitiliza kum’tumikila mokhulupilika ndiponso kulola kuti mzimu wake ugwile nchito pa ife. Ndipo ngati tacita chimo lalikulu, timakhala ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzatikhululukila ngati tilapa moona mtima ndi kulandila uphungu.
19 Posacedwapa, Yehova adzapangitsa dzina lake kutamandidwa kwambili kuposa mmene zinalili panthawi imene iye analanditsa Aisiraeli ku Iguputo. (Ezek. 38:23) Anthu akale a Mulungu analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Mofanana ndi zimenezi, ife tonse Akristu amene tikupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika tidzakhala ndi moyo m’dziko la Mulungu lolungama. (2 Pet. 3:13) Popeza kuti tikuyembekezela zinthu zosangalatsa zimenezi, tisaleke kupemphela kuti dzina la Mulungu laulemelelo liyeletsedwe. Nkhani yotsatila idzafotokoza pemphelo lina limene lingatithandize kucita zinthu zoyenela kuti tilandile madalitso a Mulungu panthawi ino ndi mtsogolo.
[Cithunzi papeji 20]
1
[Cithunzi papeji 20]
2
[Cithunzi papeji 20]
3
[Cithunzi papeji 21]
4
[Cithunzi papeji 21]
5
[Cithunzi papeji 21]
6