“Ufumu Wanu Ubwele”—Kodi Udzabwela Liti?
“Mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziŵe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo peni-peni.”—MAT. 24:33.
1, 2. (a) Kodi n’ciani cimacititsa anthu kuiwala zinthu zina zake? (b) Nanga n’ciani cimene timadziŵa ponena za Ufumu wa Mulungu?
MWINA munaonapo kuti anthu amene anaona cocitika cinacake, nthaŵi zambili amakumbukila cocitikaco mosiyana-siyana. Mwacitsanzo, zimakhala zovuta kwa anthu ena kukumbukila zonse zimene a dokotala angawauze pambuyo powapima. Anthu ena angavutike kufuna-funa makiyi ao kapena magalasi ao a m’maso pamene mwina ali nao pafupi. Akatswili ena amanena kuti zimenezi zimacitika cifukwa ca khungu la mtundu winawake limene limacititsa munthu kusaona kapena kuiŵala cinacake cifukwa cokhala wotangwanika. Anthu ena amati zimenezi zimangosonyeza mmene ubongo wathu umagwilila nchito.
2 Mofanana ndi zimenezi anthu ambili masiku ano ali ndi “khungu” ponena za zinthu zimene zikucitika m’dzikoli. Iwo angavomeleze kuti dziko lasintha kwambili kuyambila 1914, koma amalephela kuona tanthauzo la zimene zikucitikazi. Monga ophunzila Baibo, tinganene kuti Ufumu wa Mulungu unabwela m’caka ca 1914 pamene Yesu anaikidwa monga Mfumu kumwamba. Koma timadziŵanso kuti pemphelo lakuti: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano,” silinayankhidwe kothelatu. (Mat. 6:10) Pemphelo limeneli lidzayankhidwa kothelatu pamene dziko loipali lidzacotsedwa. Zimenezi zikadzacitika m’pamene cifunilo ca Mulungu cidzacitika padziko lapansi monga mmene zilili kumwamba.
3. Kodi kuphunzila Mau a Mulungu kumatithandiza kudziŵa ciani?
3 Cifukwa cakuti timaphunzila Mau a Mulungu, timadziŵa kuti maulosi ambili akukwanilitsidwa masiku ano. Zimenezi zimatisiyanitsa ndi anthu ambili m’dzikoli. Iwo ndi otangwanika kwambili ndi moyo wao ndi zocita zao cakuti amalephela kuona umboni wooneka bwino wosonyeza kuti Kristu wakhala akulamulila kuyambila 1914, ndi kuti posacedwapa adzaononga dziko loipali. Koma muyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakhulupililadi kuti mapeto a dzikoli ali pafupi kwambili ndi kuti zimene zikucitika padziko zimatsimikizila mfundo imeneyi?’ Ngakhale kuti mwina munakhala Mboni caposacedwapa, kodi mumaika maganizo anu pa ciani? Kaya yankho lanu ndi lotani, tiyeni tikambilane zifukwa zitatu zamphamvu zimene zimatipangitsa kukhulupilila kuti cifunilo ca Mulungu cidzacitika posacedwapa padziko lapansi.
APAKAVALO AONEKELA
4, 5. (a) Kodi Yesu wakhala akucita ciani kuyambila 1914? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Kodi anthu atatu okwela pa akavalo amene akutsatila Yesu amaimila ciani? Kodi ulosi umenewu ukukwanilitsidwa bwanji?
4 M’caka ca 1914, Yesu Kristu anapatsidwa kolona wakumwamba kutanthauza kuti iye anakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ulosi wolembedwa pa Chivumbulutso caputala 6 umafotokoza Yesu atakwela pa kavalo woyela. Atangokhala Mfumu, iye anayamba nkhondo yolimbana ndi dziko loipali. (Ŵelengani Chivumbulutso 6:1, 2) Ulosi umenewu unanenelatu kuti pambuyo pakuti Ufumu wa Mulungu wayamba kulamulila, zinthu padziko lapansi zidzaipilatu. Nkhondo, njala, matenda, ndi zinthu zina zimene zimaphetsa anthu zidzaculuka. Mu ulosi umenewu, zinthu zoipa zimene zikucitika zikuimilidwa ndi okwela pa akavalo atatu amene akuyendetsa akavalo ao mofulumila kwambili ndipo akutsatila Yesu Kristu m’mbuyo.—Chiv. 6:3-8.
5 Monga mmene ulosi unanenela, mtendele ‘unacotsedwa padziko lapansi’ ngakhale kuti mayiko akhala akucita mapangano a mtendele. Kupatulapo nkhondo yoyamba ya padziko lonse, pacitika nkhondo zina zoopsa zimene zacotsa mtendele padzikoli. Cakudya cikusoŵabe ngakhale kuti kuyambila m’caka ca 1914 anthu apita patsogolo pa zacuma ndi zasayansi. Ndiponso palibe amene angatsutse kuti anthu ambili amafa caka ciliconse cifukwa ca matenda osiyana-siyana, masoka acilengedwe ndi milili yakupha. Masiku ano, zinthu zoopsa zimenezi zimacitika kaŵili-kaŵili ndipo zimapha anthu ambili kuposa kale lonse. Kodi mukudziŵa tanthauzo la zocitika zimenezi?
6. Kodi ndani amene anadziŵa kuti ulosi wa m’Baibo wakwanilitsidwa? Nanga zimenezi zinawapangitsa kucita ciani?
6 Anthu ambili anasokonezeka maganizo cifukwa ca nkhondo yoyamba ya padziko lonse ndi fuluwenza ya ku Spain. Komabe, Akristu odzozedwa anali kuyembekezela mwacidwi kutha kwa “Nthawi za Akunja,” kapena kuti “nthawi zoikika za amitundu,” m’caka ca 1914. (Luka 21:24) Odzozedwa sanali kudziŵa kuti ulosi wa m’Baibo udzakwanilitsidwa bwanji kweni-kweni. Koma anali kudziwa kuti cinthu cinacake capadela cokhudza Ufumu wa Mulungu cidzacitika m’caka ca 1914. Atangozindikila kukwanilitsidwa kwa ulosi wa m’Baibo, io analengeza molimba mtima kwa anthu ena kuti Ufumu wa Mulungu wayamba kulamulila. Iwo anazunzidwa mwankhanza cifukwa colalikila uthenga wa Ufumu. Ndipo zimenezo zinalinso kukwanilitsa ulosi wa m’Baibo. Kwa zaka zambili, adani a Ufumu “anayambitsa mavuto mwa kupanga malamulo,” kumenya abale athu, kuwaika m’ndende, ngakhalenso kuwapha mocita kuwamangilila, kuwaombela ndi mfuti, kapena kuwadula mitu ndi colinga cakuti asiye kulalikila.—Sal. 94:20; Chiv. 12:15.
7. N’cifukwa ciani anthu ambili sadziŵa tanthauzo la zimene zikucitika m’dzikoli?
7 Ngakhale kuti pali maumboni ambili osonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kale kumwamba, n’cifukwa ciani anthu ambili amakana kuvomeleza mfundo imeneyi? N’cifukwa ciani amalephela kuona kuti zinthu zimene zikucitika m’dzikoli zikukwanilitsa ulosi wa m’Baibo monga mmene atumiki a Mulungu akhala akulalikilila kwa zaka zambili? Kapena kodi anthu ambili amakhulupilila cabe zimene amaona? (2 Akor. 5:7) Kodi io ndi otangwanika kwambili ndi moyo cakuti amalephela kuona zimene Mulungu akucita? (Mat. 24:37-39) Kodi anthu ena asokonezeka maganizo cifukwa ca zocita ndi mabodza a Satana? (2 Akor. 4:4) Tifunika kukhala ndi cikhulupililo ndiponso kuona zinthu ndi maso akuuzimu kuti tidziŵe zimene Ufumu wa Mulungu ukucita. Ndife osangalala cifukwa cakuti tikudziŵa bwino zimene zikucitika.
ANTHU OCITA ZOIPA AFIKA POIPA KWAMBILI
8-10. (a) Kodi lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 likukwanilitsidwa motani? (b) N’cifukwa ciani tinganene kuti anthu ocita zoipa afika poipa kwambili?
8 Pali cifukwa cina cimene cimatipangitsa kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila dziko posacedwapa. Anthu ocita zoipa m’dzikoli aipa kwambili. Kwa zaka pafupi-fupi 100 tsopano, takhala tikuona kukwanilitsidwa kwa ulosi wopezeka pa 2 Timoteyo 3:1-5. Makhalidwe amene anafotokozedwa pa lembali ali ponse-ponse m’dzikoli. Kodi inu simumaziona zimenezi? Tiyeni tipende zitsanzo zina za makhalidwe amenewo.—Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1, 13.
9 Yelekezelani zinthu zimene anthu anali kuona kuti ndi zoipa kwambili m’ma 1940 ndi 1950, ndi zimene zikucitika masiku ano m’malo anchito, pa nkhani ya zosangulutsa, zamasewela ndiponso kavalidwe. Ciwawa ndi ciwelewele zili paliponse. Anthu amacita kupanga mpikisano kuti adziŵike kuti io ndi aukali kwambili, ankhanza ndiponso aciwelewele. Zinthu zimene anthu anali kuona kuti n’zosayenela kupenyelela pa TV m’ma 1950, masiku ano anthu ena amacita kuzionelela pamodzi monga banja pofuna kuonetsa kuti zilibe vuto. Masiku ano anthu amene amagona ndi amuna kapena akazi anzao amagwilitsidwa nchito mu zosangulutsa pa nkhani ya kavalidwe n’colinga cofuna kuonetsa kuti khalidwe lao ndi lovomelezeka. Koma ndife osangalala cifukwa cakuti tikudziŵa mmene Mulungu amaonela khalidwe limeneli.—Ŵelengani Yuda 14, 15.
10 Mwina Mkristu angakumbukilenso zimene acicepele anali kuona kuti ndi khalidwe loipa m’ma 1950 ndi zimene zikucitika masiku ano. Zaka zambuyomu makolo anali kudela nkhawa kuti mwina mwana wao amasuta fodya, amamwa moŵa kapena kuvina monyanyula. Koma masiku ano timamva malipoti oipa kwambili. Mwacitsanzo, mwana wa sukulu wa zaka 15 anaombela ana a sukulu anzake a m’kalasi mwao, ndipo anapha anthu aŵili n’kuvulaza anthu 13. Gulu la acinyamata oledzela linapha mwankhanza mtsikana wa zaka 9 ndi kumenyanso bambo ake ndi msuweni wake. Dziko lina ku Asia linacitila lipoti kuti m’zaka 10 zapitazi, acinyamata ambili kumeneko ndi amene anapalamula milandu ikuluikulu. Kodi ndani angatsutse kuti zinthu masiku ano zaipilatu?
11. N’cifukwa ciani anthu ambili sazindikila kuti zinthu zikuipila-ipila?
11 Mtumwi Petulo ananenelatu kuti: “M’masiku otsiliza kudzakhala onyodola amene azidzatsatila zilako-lako zao, amene azidzati: ‘Kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kucokela tsiku limene makolo athu anamwalila, zinthu zonse zikupitililabe cimodzi-modzi ngati mmene zakhalila kuyambila pa ciyambi ca cilengedwe.’” (2 Pet. 3:3, 4) Kodi n’ciani cimene cimapangitsa anthu ena kuganiza conco? Tikamaona cinthu cina cake mobweleza-bweleza, timayamba kucizolowela kwambili. Pamene bwenzi lathu lasintha khalidwe lake mwadzidzidzi, tikhoza kudabwa. Koma ngati khalidwe la anthu ambili layamba kusintha pang’ono-pang’ono, zimakhala zovuta kuzindikila. Koma zimenezi zimabweletsa mavuto aakulu.
12, 13. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kutaya mtima ndi zimene zikucitika m’dzikoli? (b) N’ciani cimene cingatithandize kulimbana ndi zinthu ‘zovuta’?
12 Mtumwi Paulo anaticenjezelatu kuti ‘m’masiku otsiliza’ zinthu zidzakhala ‘zovuta.’ (2 Tim. 3:1) Izi sizikutanthauza kuti sitingakwanitse kulimbana nazo. Tikhoza kulimbana ndi mavuto ndi zinthu zina zoopsa mothandizidwa ndi Yehova, mzimu wake ndiponso mpingo wacikristu. N’zotheka kukhalabe okhulupilika. “Mphamvu yoposa yacibadwa” imacokela kwa Mulungu, osati kwa ife.—2 Akor. 4:7-10.
13 N’zocititsa cidwi kuti Paulo anayamba kufotokoza ulosi wa masiku otsiliza ndi mau akuti “dziŵa kuti.” Mau amenewa amasonyeza kuti ulosi umenewu udzakwanilitsidwadi. Dzikoli lidzaipila-ipilabe kufikila pamene Yehova adzaliononga. Mbili imasonyeza kuti mfundo za makhalidwe abwino zikalowa pansi, mabungwe ndi maboma amagwa. M’mbili yonse ya dziko lapansi, makhalidwe sanalowepo pansi monga mmene zilili masiku ano. Anthu ambili anganyalanyaze mfundo imeneyi, koma zinthu zapadela zimene zakhala zikucitika kuyambila 1914 ziyenela kutipangitsa kukhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu udzacitapo kanthu posacedwapa.
M’BADWO UWU SUDZATHA WONSE
14-16. Kodi n’cifukwa cacitatu citi cimene cimatipangitsa kukhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu ‘udzabwela’ posacedwapa?
14 Pali cifukwa cacitatu cimene cimatipangitsa kukhulupilila kuti mapeto ali pafupi. Zimene zakhala zikucitika pakati pa anthu a Mulungu zimasonyeza kuti mapeto ayandikila. Mwacitsanzo, ufumu wa Mulungu utatsala pang’ono kukhazikitsidwa kumwamba, gulu la Akristu odzozedwa linali lotangwanika kutumikila Mulungu. Kodi io anacita ciani pamene zinthu zina zimene anali kuyembekezela sizinacitike m’caka ca 1914? Ambili a io anapitilizabe kutumikila Yehova mokhulupilika ndipo anapilila zizunzo ndi ziyeso. M’kupita kwa zaka, ambili a Akristu odzozedwa amenewa amaliza moyo wao wa padziko lapansi mokhulupilika.
15 Pofotokoza ulosi wake wonena za mapeto a dongosolo lino la zinthu, Yesu anati: “M’badwo uwu sudzatha wonse kucoka kufikila zinthu zonsezi zitacitika.” (Ŵelengani Mateyu 24:33-35) Pamene Yesu anakamba kuti “m’badwo uwu,” iye anali kunena za magulu aŵili a odzozedwa. Gulu loyamba ndi Akristu odzozedwa amene anali ndi moyo mu 1914, ndipo anazindikila kuti Yesu anayamba kulamulila m’cakaco. Amene amapanga gululi anali kale odzozedwa monga ana a Mulungu m’caka cimeneco kapena cakaco cisanafike.—Aroma 8:14-17.
16 Odzozedwa a m’gulu laciŵili la “m’badwo uwu” anadzozedwa ndi mzimu woyela panthawi imene odzozedwa a m’gulu loyamba anali ndi moyo padziko lapansi. Conco, si odzozedwa onse masiku ano amene ali mbali ya “m’badwo uwu” umene Yesu anachula. Masiku ano, odzozedwa amene ali m’gulu laciŵili la “m’badwo uwu” ndi okalamba. Koma mau a Yesu a pa Mateyu 24:34 amatitsimikizila kuti odzozedwa a ‘m’badwo uwu sadzatha onse kucoka’ cisautso cacikulu cisanayambe. Izi ziyenela kuonjezela cikhulupililo cathu kuti kwangotsala kanthawi kocepa cabe kuti Mfumu ya Ufumu wa Mulungu iononge anthu oipa ndi kubweletsa dziko latsopano lolungama.—2 Pet. 3:13.
KRISTU ADZAPAMBANA PA NKHONDO YAKE POSACEDWAPA
17. Kodi taphunzila ciani pa maumboni atatu amene takambilana oonetsa kuti tikukhala m’masiku otsiliza?
17 Kodi taphunzila ciani pambuyo popenda maumboni atatu osonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiliza? Monga mmene Yesu anakambila, sitikudziŵa tsiku leni-leni kapena ola pamene mapeto adzafika. (Mat. 24:36; 25:13) Koma tingathe kudziŵa “nyengo ino,” ndipo tikuidziŵa monga mmene Paulo anakambila. (Ŵelengani Aroma 13:11) Tikukhala m’nyengo imeneyo, imene ndi masiku otsiliza. Ngati timakhala chelu ndi kukwanilitsidwa kwa maulosi a m’Baibo ndiponso zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu akucita, sitidzalephela kuona umboni wakuti tikukhala kumapeto kweni-kweni kwa dongosolo lino la zinthu.
18. Kodi n’ciani cidzacitikila anthu amene amakana Yesu Kristu kukhala Mfumu yao?
18 Posacedwapa, anthu amene amakana kuvomeleza ulamulilo wa Yesu Kristu, yemwe ndi Wokwela pahatchi yoyela, adzakakamizika kuvomeleza kuti analakwitsa zinthu kwambili. Iwo adzasoŵa kothawila. Panthawiyo, anthu ambili adzafuula mwamantha kuti: “Ndani angaimilile pamaso pao?” (Chiv. 6:15-17) Yankho timalipeza m’caputala 7 ca buku la Chivumbulutso. Odzozedwa pamodzi ndi anthu amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi ‘adzaima’ patsikulo cifukwa cakuti Mulungu adzawavomeleza. Ndiyeno “khamu lalikulu” la nkhosa zina lidzapulumuka cisautso cacikulu.—Chiv. 7:9, 13-15.
19. Popeza kuti mumakhulupilila kuti mapeto adzafika posacedwapa, kodi mukuyembekezela zotani?
19 Pamene tiganizila za kukwanilitsidwa kwa ulosi wa m’Baibo wokhudza nthawi yathu ino, sitidzasokonezedwa ndi dziko la Satana. Ndiponso tidzamvetsetsa tanthauzo leni-leni la zimene zikucitika m’dzikoli. Posacedwapa, Kristu adzapambana nkhondo yolimbana ndi dziko loipali pa Aramagedo. (Chiv. 19:11, 19-21) Tangoganizilani mmene tidzasangalalila pambuyo pa zimenezi.—Chiv. 20:1-3, 6; 21:3, 4.