KODI MUDZIŴA?
N’cifukwa ciani zigaŵenga anali kuzithyola miyendo pozipha?
Ponena za kuphedwa kwa Yesu ndi zigaŵenga ziŵili, Uthenga wabwino umati: “Ayudawo . . . anapempha Pilato kuti opacikidwawo awathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo.”—Yohane 19:31.
Ayuda anali ndi lamulo lakuti ngati cigaŵenga cafa pamtengo umene capacikidwapo, mtembo wake “usakhale pamtengopo usiku wonse.” (Deuteronomo 21:22, 23) Zikuoneka kuti Ayuda anali kutsatila lamulo limeneli ngati anthu apacikidwa pamtengo ndi Aroma. Kuthyola munthu miyendo kunali kucititsa kuti afe mwamsanga, ndiyeno anali kuikidwa m’manda Sabata lisanayambe m’madzulo.
Pakupha munthu, anthu anali kukhokhomela miyendo ndi manja ake pamtengo ndi misomali. Akaimilitsa mtengo, munthuyo anali kumva ululu kwambili cifukwa thupi lake lonse linali kulelemba pa misomali. Kuti apume, munthu wopacikidwa anali kupuluputa. Koma mafupa a miyendo yake akathyoka, sanali kukwanitsa kupuma ndipo anali kufa mwamsanga.
Mmene anthu anali kugwilitsila nchito gulaye pomenya nkhondo m’nthawi zakale
Davide anagwilitsila nchito gulaye kuti aphe cimphona cochedwa Goliyati. Mwacionekele, Davide anaphunzila kugwilitsila nchito cida cimeneci pamene anali m’busa wacicepele.—1 Samueli 17:40-50.
Gulaye imapezeka m’zolemba za Aiguputo ndi Asuri za m’nthawi za m’Baibulo. Cida cimeneci cinali kupangidwa ndi cikopa cimene cinali kumangidwa ku zingwe ziŵili. Munthu anali kuika m’gulaye mwala wosalala wolemela mwina magalamu 250. Ndiyeno anali kuzungulitsa gulaye ndi kuponya mwalawo mwamphamvu kwambili.
Pa zinthu zam’mabwinja zimene zinafukulidwa ku Middle East, panali miyala imene inali kugwilitsidwa nchito pomenya nkhondo ndi gulaye m’nthawi zakale. Asilikali aluso ayenela kuti anali kuponya miyalayi pa liwilo la makilomita 160 mpaka 240 pa ola. Akatswili ofufuza zinthu amakaikila ngati gulaye inali m’gulu la uta. Komabe, gulaye inali cida coononga.—Oweruza 20:16.