NKHANI YA PACIKUTO | N’CIFUKWA CIANI YESU ANAVUTIKA NDI KUTIFELA?
Kodi Zinacitikadi?
Mu 33 C.E., Yesu wa ku Nazareti anaphedwa. Iye anapatsidwa mlandu wabodza woukila boma, anamenyedwa mwankhanza, ndipo anakhomeledwa pamtengo. Iye anafa imfa yoŵaŵa. Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, ndipo patapita masiku 40 Yesu anabwelela kumwamba.
Zocitika zapadela zimenezi zinalembedwa m’mabuku anai a Uthenga Wabwino a m’Malemba Acigiliki Acikristu, amene amadziŵika kuti Cipangano Catsopano. Kodi zimene zinalembedwa m’mauthenga amenewo zinacitikadi? Funso limeneli n’lofunika kwambili. Ngati zinthu zimenezo sizinacitike, ndiye kuti cikhulupililo ca Akristu n’copanda nchito, ndipo ciyembekezo cokhala ndi moyo m’Paladaiso ndi loto cabe. (1 Akorinto 15:14) Komabe, ngati zinthuzo zinacitikadi, ndiye kuti anthu ali ndi tsogolo labwino kwambili, limene inu mungauzeko ena. Koma kodi nkhani za m’Mauthenga Abwino zinacitika kapena sizinacitike?
ZIMENE MAUMBONI AKUONETSA
Mosiyana ndi nthano zabodza, nkhani za m’Mauthenga Abwino zinafufuzidwa mosamala ndi kulembedwa molondola. Mwacitsanzo, zimachula maina a malo enieni, ndipo ambili mwa malo amenewa anthu angapite kukawaona masiku ano. Cina, zimafotokoza anthu enieni, ndipo akatswili olemba mbili yakale amacitila umboni kuti anthuwo analikodi.—Luka 3:1, 2, 23.
Olemba ena a m’nthawi ya atumwi komanso a m’zaka za m’ma 100 C.E., anachulapo za Yesu.a Njila imene Yesu anaphedwela yofotokozedwa m’Mauthenga Abwino ndi yofanana ndi njila zimene Aroma anali kugwilitsila nchito pakupha munthu. Kuonjezela apo, zocitika zimene analemba ndi zofanana m’njila yakuti zinalembedwa molondola ndiponso mosapita m’mbali. Iwo analembanso ngakhale zolakwa za ophunzila ena a Yesu. (Mateyu 26:56; Luka 22:24-26; Yohane 18:10, 11) Maumboni onsewa akuonetsa kuti olemba Mauthenga Abwino anali oona mtima, ndipo analemba zinthu zokhudza Yesu molondola kwambili.
NANGA BWANJI ZA KUUKITSIDWA KWA YESU?
Ngakhale kuti ambili amakhulupilila kuti Yesu anabweladi padziko lapansi kenako anaphedwa, ena amakaikila zakuti iye anaukitsidwa. Atumwi ake naonso sanakhulupilile pamene anamva lipoti lakuti iye waukitsidwa. (Luka 24:11) Komabe, pamene io ndi ophunzila ena anamuona Yesu woukitsidwayo panthawi zosiyanasiyana, m’pamene anakhulupilila. Ndipo panthawi ina, Yesu anaonekela kwa anthu oposa 500.—1 Akorinto 15:6.
Molimba mtima, ophunzila a Yesu analengeza za kuukitsidwa kwake kwa anthu ambili kuphatikizapo amene anamupha, ngakhale kuti kucita zimenezo kunaika moyo wao pangozi. (Machitidwe 4:1-3, 10, 19, 20; 5:27-32) Kodi ophunzila ambili akanalimba mtima conco zikanakhala kuti sanali otsimikiza mtima kuti Yesu anaukitsidwadi? Kukamba zoona, mfundo yakuti Yesu anaukitsidwadi ndi imene inacititsa kuti Cikristu cifalikile kwambili m’nthawi zakale ngakhale masiku ano.
Nkhani zokhudza imfa ya Yesu ndi kuukitsidwa kwake zolembedwa m’Mauthenga Abwino, ndi umboni wakuti nkhani zonse zofotokoza mbili yakale n’zoona. Kuŵelenga nkhani zimenezi bwinobwino, kudzakuthandizani kukhulupilila kuti zinacitikadi. Ndipo cikhulupililo canu cidzalimbanso mukamvetsetsa cifukwa cake zinthuzo zinacitika. Nkhani yotsatila ifotokoza zimenezi.
a Ena mwa anthu amenewa ndi Tacitus, amene anabadwa mu 55 C.E. Iye analemba kuti Akristu anatengela dzinali kwa “Kristu” amene Pontiyo Pilato, mmodzi mwa olamulila athu, anamulamula kuti azunzidwe ndi kuphedwa mu ulamulilo wa mfumu Tiberiyo.” Enanso amene analemba za Yesu anali Suetonius, (wa m’nthawi ya atumwi), wolemba mbili yakale waciyuda Josephus (wa m’nthawi ya atumwi), ndi Pliny Wamng’ono amene anali bwanamkubwa wa ku Bituniya (wa kumayambililo kwa zaka za m’ma 100 C.E).