LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp16 na. 2 tsa. 16
  • Kodi Baibulo Limakamba Ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibulo Limakamba Ciani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Tumitu
  • Kodi Mdyelekezi ndani?
  • Kodi Mdyelekezi angalamulile anthu?
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
wp16 na. 2 tsa. 16
Yesu akana mayeselo a Satana

Kodi Baibulo Limakamba Ciani?

Kodi Mdyelekezi ndani?

KODI MUMAONA KUTI Mdyelekezi ndi . . .

  • Munthu wauzimu?

  • Maganizo oipa a munthu?

  • Cinthu congoyelekezela?

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

Mdyelekezi anakamba ndi Yesu, ndi ‘kumuyesa.’ (Mateyu 4:1-4) Conco, Mdyelekezi si cinthu congoyelekezela kapena maganizo oipa a munthu. Iye ndi munthu woipa wauzimu.

ZINA ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

  • Poyamba, Satana anali mngelo wabwino, koma iye “sanakhazikike m’coonadi.” (Yohane 8:44) Iye anakhala wabodza ndipo anapandukila Mulungu.

  • Angelo enanso anapanduka ndi kugwilizana ndi Satana. —Chivumbulutso 12:9.

  • Mdyelekezi amacititsa anthu kuganiza kuti iye kulibe.​—2 Akorinto 4:4.

Kodi Mdyelekezi angalamulile anthu?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI zoti Mdyelekezi amalamulila anthu ndi nthano cabe, koma ena amaopa kugwidwa ndi ziŵanda. Nanga inu muganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mdyelekezi akusonkhezela anthu ambili kucita zoipa, koma sakulamulila anthu onse.

ZINA ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA

  • Mdyelekezi amagwilitsila nchito cinyengo kuti asokoneze anthu ambili.​—2 Akorinto 11:14.

  • Nthawi zina ziŵanda zimavutitsa anthu.​—Mateyu 12:22.

  • Mothandizidwa ndi Yehova, mungathe ‘kutsutsa Mdyelekezi.’​—Yakobo 4:7.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 10 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti ya www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani