LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp16 na. 4 tsa. 8
  • Cifukwa Cake Baibulo Yapulumuka

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cifukwa Cake Baibulo Yapulumuka
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Nkhani Zofanana
  • Baibo ni Uthenga wa Mulungu kwa Ife
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Nkhani Yofunika Kwambili
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • 12 Zolinga
    Galamuka!—2018
  • Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
    Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
wp16 na. 4 tsa. 8
Munthu aŵelenga Baibulo

NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA

Cifukwa Cake Baibulo Yapulumuka

Baibulo yapulumuka zambili. Pa cifukwa cimeneci, masiku ano tili na mwai wokhala nayo ndi kuiŵelenga. Ngati mwasankha kuŵelenga Baibulo lomasulidwa bwino, mungatsimikizile kuti muŵelenga Malemba ogwilizana kwambili ndi zolemba zoyambilila.a Baibulo siinawole ngakhale kuti inalembedwa pa zinthu zosalimba, ndipo inatetezeka kwa anthu otsutsa ndi kwa omasulila amene anafuna kusintha uthenga wake. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Kodi buku limeneli lili ndi uthenga wabwanji kwenikweni?

“Tsopano nikhulupilila kuti Baibulo imene nili nayo ni mphatso yocokela kwa Mulungu”

Anthu ambili amene amaphunzila Baibulo afika pokamba mau amene mtumwi Paulo analemba akuti: “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Iwo akhulupilila kuti Baibulo lapulumuka cifukwa ni Mau a Mulungu, ndi kuti Iye ndiye waiteteza kufikila masiku ano. Faizal amene takamba m’nkhani yoyambilila, anaganiza zophunzila Baibulo n’colinga cakuti adzionele yekha ngati n’locokeladi kwa Mulungu. Zimene anapeza ataiphunzila, zinam’cititsa cidwi. Posapita nthawi, iye anazindikila kuti ziphunzitso zambili zimene zili m’machechi osiyanasiyana si zipezeka m’Baibulo. Kuwonjezela apo, iye anakhudzidwa kwambili atadziŵa colinga ca Mulungu ca dziko lapansi cimene Mau Ake amakamba.

Iye anakambanso kuti: “Tsopano nikhulupilila kuti Baibulo imene nili nayo ni mphatso yocokela kwa Mulungu. Ngati Mulungu anapanga cilengedwe conse, iye sangalephele kutipatsa Baibulo ndi kuiteteza. Ndipo ngati ningaganize kuti Mulungu sangateteze Baibulo, zingakhale monga nikamba kuti Mulungu alibe mphamvu. Kumeneku kungakhale kukaikila Mulungu Wamphamvuyonse. Koma ndine ndani kuti nicite zimenezo?”—Yesaya 40:8.

a Onani nkhani imene ili mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008, ya mutu wakuti: “Kodi Mungadziŵe Bwanji Baibulo Lomasulilidwa Bwino?

Tingatsimikize bwanji kuti Baibulo imakamba zoona?

Nkhani zotsatizana za m’magazini ino, zafotokoza mmene Baibulo inapulumukila. Kodi mungatsimikize bwanji kuti Baibulo ni “mawu a Mulungu” osati maganizo a anthu kapena nthano zabodza? (1 Atesalonika 2:13) Tambani kavidiyo kakafupi kakuti Kodi Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona? Kamene kapezeka pa www.jw.org. (Pitani pa malo ofufuzila zinthu a pa intaneti ndi kulemba mutu wa kavidiyo kameneka)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani