Malangizo Owonjezela Ku Mabanja
BAIBO IMAPELEKA CITSOGOZO CODALILIKA KWAMBILI kwa okwatilana, makolo, komanso kwa acicepele. Mfundo zake zingathandize munthu kuwonjezela luso lake la kuganiza na kupanga zosankha zabwino.—Miyambo 1:1-4.
BAIBO IMAYANKHANSO MAFUNSO OFUNIKA KWAMBILI MU UMOYO, MONGA AKUTI:
Kodi colinga ca moyo n’ciani?
Kodi tiyenela kuimba mlandu Mulungu cifukwa ca mavuto athu?
Kodi cimacitika n’ciani munthu akamwalila?
Tikupemphani kuti muziphunzila Baibo pamwekha kuti mupeze mayankho pa mafunso aya komanso ena. Tambani vidiyo yakuti, N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? Unikani kacidindo ka QR aka kapena yendani pa www. jw. org.