Dokowe
Phunzilani ku Mbalame za M’mlenga-lenga
“Funsa, . . . zouluka zam’mlengalenga, ndipo zikuuza. Ndani pa zonsezi sadziŵa bwino kuti dzanja la Yehova ndi limene lacita zimenezi?”—Yobu 12:7, 9.
ZAKA zoposa 3,000 zapita, Yobu wa m’nthawi yakale anazindikila kuti mbalame za m’mlenga-lenga zingatiphunzitse zambili ponena za nchito za Mulungu. Komanso zimene mbalamezo zimacita zingakhale mafanizo abwino amene tingaseŵenzetse. Nthawi zambili, zimene Baibo imakamba ponena za mbalame za m’mlenga-lenga, zimatiphunzitsa mfundo zofunika pa umoyo ndi pa ubwenzi wathu na Mulungu. Tiyeni tioneko zitsanzo zina zocepa.
KUMENE NAMZEZE AMAMANGILA CISA CAKE
Namzeze
Anthu okhala ku Yerusalemu anali kuzidziŵa bwino mbalame zochedwa namzeze (ena amati nyamkalema), zimene nthawi zambili zimamanga zisa munsi mwa mtenje wa nyumba. Zina mwa mbalame zimenezi zinali kumanga zisa m’kacisi amene Solomo anamanga. N’zosakayikitsa kuti mbalame zimene zinali kumanga zisa zawo pa kacisi caka ciliconse, zinali kukhala zotetezeka ndipo zinali kulela ana awo popanda cosokoneza.
Wolemba Salimo 84, amene ndi mmodzi wa ana a Kora, anali kutumikila pa kacisi wiki imodzi pa miyezi 6 iliyonse. Iye anali kuona zisa za anamzeze pa kacisi. Iye analaka-laka kukhala monga namzeze amene anali na malo okhalitsa pa nyumba ya Yehova. Anakamba kuti: “Inu Yehova wa makamu, ine ndimakondadi cihema canu cacikulu! Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookelatu cifukwa colakalaka mabwalowo . . . Ngakhale mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu. Namzeze wadzimangila cisa cake pamenepo, ndi kuikamo ana ake!” (Salimo 84:1-3) Kodi ife pamodzi ndi ana athu timalaka-laka kuti nthawi zonse tizisonkhana pamodzi na anthu a Mulungu monga anacitila wamasalimo?—Salimo 26:8, 12.
DOKOWE AMADZIŴA BWINO NTHAWI YAKE
Mneneli Yeremiya analemba kuti: “Dokowe, mbalame youluka m’mlengalenga, imadziŵa bwino nthawi yake yoikidwilatu.” Mosakayikila, iye anali kudziŵa bwino za adokowe amene anali kudutsa m’Dziko Lolonjezedwa. M’malanga, adokowe ena oposa 300,000 amacoka ku Africa kupita kumpoto kwa Europe kudzela m’cigwa ca Yorodani. Iwo amadziŵa kuti nthawi yakwana yakuti abwelele kumalo kumene amaikila. Mofanana na mbalame zina zokuka-kuka, adokowe ‘amadziŵa nyengo yobwelela kumene anacokela.’—Yeremiya 8:7.
Buku lina lokamba za mbalame limati: “Codabwitsa kwambili na mbalame zokuka-kuka n’cakuti zimacita conco mwa nzelu zawo zacibadwa.” (Collins Atlas of Bird Migration) Yehova anapatsa mbalame zokuka-kuka nzelu zacibadwa kuti zizidziŵa nthawi yokuka. Koma anthu anawapatsa luso lozindikila tanthauzo la nthawi na nyengo. (Luka 12:54-56) Mosiyana na nzelu zacibadwa za dokowe, kudziŵa Mulungu ndi kumene kumathandiza anthu kuzindikila tanthauzo la zinthu zimene zicitika masiku ano. Aisraeli a m’nthawi ya Yeremiya sanali kudziŵa tanthauzo la zimene zinali kucitika m’nthawi yawo. Mulungu anafotokoza cimene cinapangitsa. Iye anati: “Iwo akana mawu a Yehova. Kodi ali ndi nzelu yotani tsopano?”—Yeremiya 8:9.
Masiku ano tili na umboni woculuka woonetsa kuti tili m’nthawi imene Baibo imacha kuti “masiku otsiliza.” (2 Timoteyo 3:1-5) Kodi mudzayesetsa kudziŵa tanthauzo la ‘nthawi’ ino mofanana ndi dokowe amene amadziŵa nthawi yake yokuka?
CIWOMBANKHANGA CIMAONA KUTALI KWAMBILI
Ciwombankhanga
Ciwombankhanga cimachulidwa kaŵili-kaŵili m’Baibo ndipo zithunzi zake zinali zojailika m’Dziko Lolonjezedwa. Baibo imakamba kuti ciwombankhanga “cimafunafuna cakudya” kucokela pa cisa cake cimene cimakhala pamwamba pa thanthwe. “Maso ake amaona kutali kwambili.” (Yobu 39:27-29) Maso a ciwombankhanga ndi amphamvu kwambili cakuti cingathe kuona kalulu ali pa mtunda wokwana kilomita imodzi.
Mofanana ndi ciwombankhanga cimene ‘cimaona kutali kwambili,’ Yehova nayenso amatha kuona zimene zidzacitika m’tsogolo kwambili. N’cifukwa cake iye anati: “Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambila pa ciyambi. Kuyambila kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinacitike.” (Yesaya 46:10) Tikamatsatila malangizo a Yehova, timapindula na nzelu zake zosayelekezeka ndi luso lake lodziŵa za mtsogolo.—Yesaya 48:17, 18.
Baibo imayelekezelanso anthu amene amakhulupilila Yehova na ziwombankhanga. Imati: “Anthu odalila Yehova adzapezanso mphamvu. Iwo adzaulukila m’mwamba ngati ali ndi mapiko a ciwombankhanga.” (Yesaya 40:31) Ciwombankhanga cimaseŵenzetsa mphepo yothuma kuti ciuluke m’mwamba kwambili. Cikapeza malo amene pali mphepo yothuma, ciwombankhanga cimatambasula mapiko ake n’kumauluka mozungulila pamalopo mpaka kupita m’mwamba kwambili. Kuti ciwombankhanga ciuluke m’mwamba kwambili ndi kuyenda mtunda wautali, sicidalila mphamvu zake zokha. Mofananamo, anthu okhulupilila Yehova angadalile “mphamvu yoposa ya cibadwa” imene iye amawalonjeza.—2 Akorinto 4:7, 8.
MMENE NKHUKU IMASONKHANITSILA ANA AKE
Nkhuku ndi anapiye
Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, iye anaima na kuyang’ana Yerusalemu, mzinda waukulu wa Ayuda. Ndiyeno anaudandaulila kuti: “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneli iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe. Mobwelezabweleza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsila anapiye ake m’mapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo.”—Mateyu 23:37.
Mwacibadwa, mbalame zimafunitsitsa kuteteza ana awo. Maka-maka zimene zimaikila pansi monga nkhuku, zimakhala chelu kwambili kuyang’ana adani. Nkhuku ikaona kamtande akuuluka m’mwamba imalila mokweza kucenjeza ana ake, ndipo anawo amabwela mwamsanga kukabisala m’mapiko ake. M’mapikomo, ndi mmenenso anapiye ake amabisalila mvula yamphamvu ndi dzuwa. Mofananamo, Yesu anafuna kuteteza anthu a mu Yerusalemu mwauzimu. Masiku anonso Yesu amatipempha kubwela kwa iye kuti titsitsimulidwe na kutetezedwa ku zolemetsa na nkhawa za pa umoyo wathu.—Mateyu 11:28, 29.
Kukamba zoona, pali zambili zimene tingaphunzile ku mbalame. Mukamaona zocita za mbalame, muziyesanso kukumbukila zimene Malemba amakamba zokhudza mbalamezo. Mwacitsanzo, mukaona namzeze, muzikumbukila kuyamikila nyumba yolambililamo Yehova. Ndipo monga ciwombankhanga cimene cimauluka m’mwamba kwambili, muzidalila Mulungu amene amapeleka ciyembekezo cimene cingakupatseni mphamvu. Komanso, bwelani kwa Yesu kuti akuphunzitseni coonadi cimene cingakutetezeni mofanana ndi mmene nkhuku imatetezela ana ake. Ndipo mukaona dokowe, muzikumbukila kuti mufunika kukhalabe chelu kuti mudziŵe tanthauzo la zocitika za padziko masiku ano.