LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 November masa. 18-19
  • “Munthu Wopatsa Mowolowa Manja Adzalandila Mphoto”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Munthu Wopatsa Mowolowa Manja Adzalandila Mphoto”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Nkhani Zofanana
  • “Nchitoyi Ndi Yaikulu”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Muziyamikila Kuolowa Manja kwa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • “Okonzeka Kupeleka Mphatso kwa Yehova”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 November masa. 18-19
Hana akupeleka Samueli ku cihema ali wacicepele

“Munthu Wopatsa Mowolowa Manja Adzalandila Mphoto”

KUYAMBILA kale, anthu a Mulungu akhala akupeleka nsembe monga mbali ya kulambila koona. Mwacitsanzo, Aisiraeli anali kupeleka nsembe za nyama, ndipo Akhristu nthawi zonse akhala akupeleka nsembe zotamanda Mulungu. Komabe, pali nsembe zinanso zimene Mulungu amakondwela nazo. (Aheb. 13:15, 16) Nsembe zimenezi zimabweletsa cimwemwe na madalitso, monga mmene tidzaonela m’zitsanzo zotsatila.

Hana, mtumiki wokhulupilika wakale wa Mulungu, anali kufunitsitsa kukhala na mwana. Koma sanali kubeleka. Nthawi ina, iye popemphela anacita lumbilo pamaso pa Yehova kuti ngati adzakhala na mwana wamwamuna, ‘adzam’peleka kwa Yehova masiku onse a moyo wake.’ (1 Sam. 1:10, 11) M’kupita kwa nthawi, Hana anakhala na pakati, ndipo anabala mwana wamwamuna dzina lake Samueli. Samueli ataleka kuyamwa, Hana anapita kukam’peleka ku cihema, mogwilizana na lumbilo lake. Yehova anam’dalitsa Hana cifukwa ca kudzimana kwake. Iye anabalanso ana ena asanu, ndipo Samueli anakhala mneneli ndi wolemba Baibo.—1 Sam. 2:21.

Molingana na Hana na Samueli, ise Akhristu masiku ano tili na mwayi woseŵenzetsa moyo wathu potumikila Mlengi wathu. Yesu anakamba kuti ngati tidzimana zinthu zina cifukwa colambila Yehova, tidzadalitsidwa maningi.—Maliko 10:28-30.

M’nthawi ya atumwi, mkazi wina wacikhristu dzina lake Dorika anali kudziŵika ngako cifukwa ‘cocita nchito zabwino, na kupeleka mphatso zacifundo.’ Inde, anali wodzipeleka pothandiza ena. Koma n’zomvetsa cisoni kuti iye “anadwala n’kumwalila.” Zimenezi zinacititsa kuti mpingo wonse ukhale na cisoni. Ophunzila a Yesu atamvela kuti Petulo ali pafupi, anapita kukamupempha kuti abwele mwamsanga. Ganizilani cabe cisangalalo cimene ophunzilawo anakhala naco pamene Petulo anabwela na kuukitsa Dorika. Iye ni munthu woyamba wochulidwa m’Baibo amene anaukitsidwa na atumwi. (Mac. 9:36-41) Mulungu sanaiŵale zinthu zabwino zimene Dorika anacita. (Aheb. 6:10) Mbili ya kuwoloŵa manja kwake inalembewa m’Mau a Mulungu monga citsanzo cabwino cimene ise tonse tiyenela kutengela.

Nayenso mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino kwambili mwa kudzipeleka na kugwilitsila nchito nthawi yake pothandiza ena. Polembela Akhristu a ku Korinto, iye anati: “Koma ineyo ndidzagwilitsa nchito zinthu zanga zonse ndipo ndidzadzipeleka ndi moyo wanga wonse cifukwa ca miyoyo yanu.” (2 Akor. 12:15) Pa utumiki wake, Paulo anaphunzila kuti kudzipeleka pothandiza anthu ena kumabweletsa cimwemwe. Komanso kuposa pamenepo, kumapangitsa kuti Yehova atiyanje na kutidalitsa.—Mac. 20:24, 35.

N’zoonekelatu kuti Yehova amakondwela ngati tiseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu popititsa patsogolo zinthu za Ufumu na pothandiza okhulupilila anzathu. Nanga n’ciani cina cimene tingacite pocilikiza nchito yolalikila Ufumu? Kuwonjezela pa nchito zathu za cikondi, tingalemekeze Mulungu mwa kucita zopeleka zaufulu. Zopeleka zimenezi amaziseŵenzetsa popititsa patsogolo nchito yolalikila padziko lonse. Izi ziphatikizapo kucilikiza amishonale na atumiki a nthawi zonse apadela. Komanso, zopeleka zathu zaufulu zimathandiza pa nchito yokonza na kumasulila mabuku na mavidiyo, nchito yothandiza okhudzidwa na masoka, ndi yomanga Nyumba za Ufumu zatsopano. Sitiyenela kukayikila kuti “munthu wopatsa mowoloŵa manja adzalandila mphoto.” Kuwonjezela apo, Yehova amalemekezeka ngati tim’patsa zinthu zathu zamtengo wapatali.—Miy. 3:9; 11:25.

Zimene Ena Amapeleka Pocilikiza Nchito Ya Padziko Lonse

Monga mmene zinalili m’nthawi ya mtumwi Paulo, ambili masiku ano amapanga bajeti kapena kuika kandalama “kenakake pambali” kuti akaponye m’bokosi ya zopeleka za “Nchito Yapadziko Lonse.” (1 Akor. 16:2) Mwezi uliwonse, mipingo imatumiza zopeleka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anila dela lawo. N’zothekanso kutumiza mwekha zopeleka zanu ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko limene mukhala. Mungafunsile ku ofesi ya nthambi m’dziko limene mukhala kuti mudziŵe mmene mungacitile zimenezi. Adresi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.jw.org. Malinga ndi mmene zinthu zilili kwanuko, mungapeleke zopeleka zanu m’njila izi:

ZOPELEKA MWACINDUNJI

  • Mungapeleke zopeleka zanu kupitila ku banki, kapena mungaseŵenzetse makhadi a ku banki. M’madela ena, n’zothekanso kucita copeleka canu kupitila pa jw.org kapena webusaiti ina.

  • Mungapeleke ndalama, masikiyo, mphete, zibangili, na zinthu zina zamtengo wapatali. Tumizani zinthuzo pamodzi na kalata yokamba kuti ni copeleka.

ZOBWELEKETSA

  • Mungapeleke ndalama n’kufotokoza kuti mudzaziitanitsa mukadzazifuna.

  • Tumizani ndalamazo pamodzi na kalata yokamba kuti n’zobweleketsa.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezela pa kupeleka mphatso za ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali, pali njila zinanso zopelekela zinthu zothandiza pa nchito ya Ufumu padziko lonse. Njila zimenezi zili munsimu. Mukalibe kusankha njila iliyonse, muyenela kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziŵe njila zimene n’zotheka m’dziko limene mukhala. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenela kufunsanso anthu odziŵa bwino za malamulo na misonkho.

Inshuwalansi na Penshoni: Mungakonze zakuti gulu la Mboni za Yehova lidzalandile ndalama zanu za inshuwalansi kapena za penshoni.

Maakaunti a Kubanki: Mungakonze zakuti mukadzamwalila, maakaunti anu a kubanki adzapelekedwe ku gulu la Mboni za Yehova mogwilizana na malamulo a mabanki m’dziko limene mukhala.

Masheya: Mungapeleke ku gulu la Mboni za Yehova masheya amene muli nawo m’kampani kapena mungakonze zakuti lidzalandile masheyawo mukadzamwalila.

Malo na Nyumba: Mungapeleke ku gulu la Mboni za Yehova malo na nyumba zimene angagulitse. Ngati nyumbayo ni imene mukukhalamo, mukhoza kuipeleka koma n’kupitiliza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli na moyo.

Cuma Camasiye: Mukhoza kulemba mu wilu yovomelezeka na boma kuti gulu la Mboni za Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, inuyo mukadzamwalila.

Ngati mufuna kudziŵa zambili, tinikani pa mau akuti “Citani Copeleka ku Nchito Yathu ya Padziko Lonse” pansi pa peji yoyamba pa jw.org, kapena mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko limene mukhala.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani