Muziseŵenza na Yehova Tsiku Lililonse
“Ndife anchito anzake a Mulungu.”—1 AKOR. 3:9.
1. Kodi tingaseŵenze na Yehova m’njila zina ziti?
YEHOVA atalenga anthu oyamba, anafuna kuti iwo akhale anchito anzake pokwanilitsa cifunilo cake. Ngakhale kuti ndise opanda ungwilo, tikakhala okhulupilika, timakhala na mwayi woseŵenza na Yehova tsiku lililonse. Mwacitsanzo, timakhala “anchito anzake a Mulungu” mwa kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu na kupanga ophunzila. (1 Akor. 3:5-9) Kukamba zoona, ni mwayi waukulu ngako kuseŵenzela pamodzi na Mlengi wa cilengedwe conse komanso Wamphamvuzonse, pa nchito imeneyi, imene iye amaiona kuti ni yofunika kwambili! Komabe, kulalikila na kupanga ophunzila ni imodzi cabe mwa njila zambili zimene timaseŵenzela na Yehova. M’nkhani ino, tidzakambilana njila zina za mmene tingaseŵenzele na Mulungu. Mwacitsanzo, tidzakambilana za kuthandiza anthu a m’banja lathu na Akhristu anzathu, kukhala oceleza, kudzipeleka pa nchito za m’gulu la Yehova, komanso kuwonjezela zocita mu utumiki wathu.—Akol. 3:23.
2. N’cifukwa ciani si bwino kuyelekezela zimene timacita potumikila Yehova na zimene ena amacita?
2 Pamene tikambilana nkhaniyi, musayelekezele zimene mumacita potumikila Yehova na zimene ena amacita. Kumbukilani kuti zaka, thanzi, maluso, komanso mmene zinthu zilili mu umoyo wathu zimasiyana-siyana. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Aliyense payekha ayese nchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatelo adzakhala ndi cifukwa cosangalalila ndi nchito yake, osati modziyelekezela ndi munthu wina.”—Agal. 6:4.
MUZISAMALILA A M’BANJA LANU KOMANSO KUTHANDIZA AKHRISTU ANZANU
3. N’cifukwa ciani tingakambe kuti aliyense amene amasamalila a m’banja lake amacita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu?
3 Yehova amafuna kuti atumiki ake azisamalila mabanja awo. Mwacitsanzo, mungafunike kumaseŵenza kuti muzipeza ndalama zogwilitsila nchito posamalila banja lanu. Azimayi ambili amakhala pa nyumba kuti azisamalila ana awo. Ndipo ana ena aakulu amafunika kusamalila makolo awo odwala. Onsewa ni maudindo ofunika kwambili. Mau a Mulungu amati: “Ngati munthu sasamalila anthu amene ndi udindo wake kuwasamalila, maka-maka a m’banja lake, wakana cikhulupililo ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupilila.” (1 Tim. 5:8) Ngati muli na udindo wosamalila banja, ndiye kuti mwacidziŵikile simukhala na nthawi yoculuka yocita zinthu zauzimu ngati mmene mufunila. Koma musataye mtima! Yehova amakondwela mukamayesetsa kusamalila banja lanu.—1 Akor. 10:31.
4. Kodi makolo angaike bwanji zinthu za Ufumu patsogolo kuposa zofuna zawo? Nanga pangakhale zotulukapo zotani?
4 Makolo acikhristu amaseŵenza na Yehova pamene athandiza ana awo kukhala na zolinga zauzimu. Makolo ambili amene anacita zimenezi, pambuyo pake anaona ana awo akucoka pa nyumba kukacita utumiki wa nthawi zonse kutali na kwawo. Ena ni amishonale, ena akucita upainiya ku madela osoŵa, ndipo enanso akutumikila pa Beteli. N’zoona kuti makolowo saonana kawili-kawili ndi ana awo. Komabe, makolo amene ali na mtima wodzimana amalimbikitsa ana awo kupitiliza utumiki wawo. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti amapeza cimwemwe coculuka poona kuti ana awo akuika zinthu za Ufumu patsogolo. (3 Yoh. 4) Mwacionekele, ambili mwa makolo amenewa amamvela monga mmene Hana anamvelela. Iye anakamba kuti ‘anabweleketsa’ mwana wake Samueli kwa Yehova. Makolo amenewa amaona kuti kuseŵenza na Yehova mwa njila imeneyi ni mwayi waukulu. Iwo saona kuti analakwitsa kulimbikitsa ana awo kuyamba kutumikila Yehova.—1 Sam. 1:28 ftn.
5. Ni zinthu monga ziti zimene mungacite pothandiza abale na alongo mu mpingo mwanu? (Onani pikica kuciyambi.)
5 Ngati mulibe udindo waukulu wosamalila banja, kodi mungathandizeko Akhristu amene amasamalila makolo kapena acibululu odwala kapena okalamba? Kapena kodi mungathandizeko Akhrsitu ena amene ni odwala, okalamba, kapenanso amene ali na zosoŵa zina? Bwanji osafufuza mu mpingo mwanu kuti muone abale na alongo amene afunika thandizo? Mwina mungapatuleko nthawi yokhala na kholo lokalamba la mlongo winawake, kuti iye akhaleko na mpata wocita zinthu zina. Kapena mungathandizeko ena mwa kuwanyamula popita ku misonkhano, kukawagulilako zinthu, kuwanyamula popita kukaona odwala ku cipatala, kapenanso kuwatumikila m’njila zina. Mwa kucita izi, mungakhale mukuseŵenza pamodzi na Yehova poyankha pemphelo la Mkhristu winawake.—Ŵelengani 1 Akorinto 10:24.
MUZIKHALA OCELEZA
6. Kodi kukhala woceleza kumatanthauza ciani?
6 Anchito anzake a Mulungu amadziŵika na khalidwe la kuceleza. M’Malemba Acigiriki Acikhristu, liu lakuti “kuceleza” limatanthauza “kukomela mtima alendo.” (Aheb. 13:2) Mau a Mulungu amafotokoza zocitika zosiyana-siyana zimene zimatiphunzitsa kuonetsa cikondi mwa kukhala oceleza. (Gen. 18:1-5) Tiyenela kuseŵenzetsa mpata uliwonse umene tapeza kuti tithandize ena, kaya ni “abale ndi alongo athu m’cikhulupililo” kapena ayi.—Agal. 6:10.
7. Kodi muona kuti n’cifukwa ciani ni bwino kuceleza atumiki a nthawi zonse amene amabwela kudzacezela mpingo wanu?
7 Kodi mungaseŵenze na Mulungu mwa kuceleza atumiki a nthawi zonse amene abwela kudzacezela mpingo wanu? (Ŵelengani 3 Yohane 5, 8.) Kuceleza Akhristu amenewa kumatipatsa mwayi ‘wolimbikitsana mwa cikhulupililo.’ (Aroma 1:11, 12) Ganizilani citsanzo ca m’bale wina wacicepele, dzina lake Olaf. Iye akumbukila kuti zaka zambili m’mbuyomo, panalibe aliyense mu mpingo mwawo amene anali na nyumba yoti n’kulandililamo woyang’anila dela wawo, amene anali wosakwatila. Conco Olaf anapempha makolo ake, amene sanali Mboni, kuti woyang’anila delayo azikhala naye pa nyumba pawo. Iwo anavomela, koma anakamba kuti panthawiyo, Olaf adzafunika kumagona pa mpando wa sofa. Zimene iye anacita zinam’pindulitsa. Olaf anati: “Inali wiki yokondweletsa ngako! Ine na woyang’anila delayo tinali kuuka kuseni-seni, ndipo tinali kukambilana nkhani zambili zolimbikitsa pa nthawi ya cakudya ca m’maŵa. Zimene tinali kukambilanazo zinanilimbikitsa kuyamba utumiki wa nthawi zonse.” Kwa zaka 40 tsopano, Olaf wakhala akutumikila monga mmishonale m’maiko osiyana-siyana.
8. N’cifukwa ciani tiyenela kuonetsa kukoma mtima kwa anthu olo aoneka monga osayamikila? Fotokozani citsanzo.
8 Tingaonetse cikondi kwa alendo m’njila zambili olo poyamba aoneke ngati sanayamikile zimene tawacitila. Ganizilani citsanzo ici. Wofalitsa wina wa ku Spain anali kuphunzila Baibo na mzimayi wina wocokela ku Ecuador, dzina lake Yesica. Tsiku lina pamene anali kuphunzila naye, wofalitsayo anadabwa kuti Yesica anayamba kulila. Mlongoyo anamufunsa kuti n’cifukwa ciani anali kulila. Yesica anakamba kuti pamene anali ku Ecuador anali wosauka kwambili cakuti tsiku lina analibiletu cakudya. Ndipo cifukwa cosoŵa cakudya, mwana wake anali kungomumwetsa madzi. Yesica anayesa kum’tonthoza mwanayo kuti agone, kwinaku akupemphela kuti apeze thandizo. Patapita nthawi yocepa, a Mboni aŵili anafika pa nyumbapo. Koma Yesica sanawalandile bwino, ndipo anang’amba magazini amene anam’patsa. Iye anati: “Kodi ici ndiye cakudya cimene mufuna kuti nipatse mwana wanga?” Alongowo anayesa kum’tonthoza, koma sizinaphule kanthu. Patapita nthawi, iwo anakasiya basiketi ya zakudya pa khomo pake. Atayamba kuphunzila Baibo, Yesica anakhudzika pokumbukila cikondi cimene alongo aja anamuonetsa, moti anadziimba mlandu pokumbukila kuti sanayamikile zimene Mulungu anacita poyankha pemphelo lake. Koma panthawiyi, iye anali wotsimikiza mtima kuyamba kutumikila Yehova. Kodi si zotulukapo zabwino zimenezi za khalidwe la kuolowa manja?—Mlal. 11:1, 6.
MUZIDZIPELEKA PA NCHITO ZA M’GULU LA YEHOVA
9, 10. (a) Ni pa zocitika zina ziti za m’nthawi yakale, pamene atumiki odzipeleka anali kufunika pakati pa anthu a Mulungu? (b) Ni nchito zina ziti zimene zimasamalidwa na abale odzipeleka mu mpingo masiku ano?
9 Pa zocitika zosiyana-siyana m’mbili ya Aisiraeli, panali kufunika atumiki odzipeleka. (Eks. 36:2; 1 Mbiri 29:5; Neh. 11:2) Masiku ano, na ise tili na mipata yambili yoseŵenzetsa nthawi yathu, cuma, na maluso athu pothandiza Akhristu anzathu. Ndipo tikakhala odzipeleka, tidzapeza cimwemwe coculuka na madalitso ambili.
10 Mau a Mulungu amalimbikitsa amuna mu mpingo kuti ayenela kuseŵenza na Yehova mwa kukalamila maudindo na mautumiki ena m’gulu. (1 Tim. 3:1, 8, 9; 1 Pet. 5:2, 3) Abale amene amacita zimenezi ali na mtima wofuna kuthandiza ena mwauzimu, komanso pa mbali zina zofunikila. (Mac. 6:1-4) Kodi akulu anakupemphani kuti muzitumikila monga kalinde, kapena kuti muzisamalila mabuku, magawo, kuthandiza pokonza zowonongeka pa Nyumba ya Ufumu, kapena kucita nchito zina? Abale amene amacita zimenezi adzakuuzani kuti kuthandiza ena n’cinthu cokondweletsa ngako.
Kudzipeleka pa nchito za m’gulu la Mulungu kumatipatsa mwayi wopeza mabwenzi atsopano (Onani palagilafu 11)
11. Kodi mlongo wina anapindula bwanji na mabwenzi amene anapeza pa nchito zomanga m’gulu la Mulungu?
11 Akhristu amene amadzipeleka pa nchito zosiyana-siyana m’gulu la Mulungu amapeza mabwenzi. Mwacitsanzo, ganizilani za Margie, mlongo amene wakhala akugwila nchito yomanga Nyumba za Ufumu kwa zaka 18. Pa zaka zonsezi, wakhala akuthandiza alongo acicepele na kuwaphunzitsa nchito. Iye amaona kuti kugwila nchitoyi ni njila yabwino yolimbikitsilana mwauzimu wina na mnzake. (Aroma 1:12) Pa nthawi ya mavuto, Margie wakhala akulimbikitsidwa na mabwenzi amene anapeza pomanga Nyumba za Ufumu. Kodi imwe munagwilako nchito yomanga Nyumba ya Ufumu? Kaya muli na luso linalake lapadela kapena ayi, kodi mungadzipeleke pa nchitoyi?
12. Kodi tingathandize bwanji anthu amene akhudzidwa na masoka azacilengedwe?
12 Masoka azacilengedwe akacitika, ise anthu a Mulungu timakhala na mipata yoseŵenza na Mulungu mwa kuthandiza Akhristu anzathu m’njila zambili. Mwacitsanzo, timapeleka ndalama zothandizila anthu amene akhudzidwa na tsokalo. (Yoh. 13:34, 35; Mac. 11:27-30) Tikhozanso kuthandiza mwa kugwila nawo nchito yoyeletsa, kapena kukonzanso nyumba za okhudzidwawo. Mlongo wina wa ku Poland, dzina lake Gabriela, amene nyumba yake inaonongekelatu na madzi osefukila, anakondwela pamene abale a m’mipingo ya pafupi anabwela kudzam’thandiza. Iye anati: “Olo kuti n’nataya zinthu zambili, sinidandaula kwambili na zimenezo. Koma lekani nikuuzeni mapindu amene napeza. Zimene zinacitikazi zanithandiza kuona kuti kukhala mu mpingo wacikhristu ni mwayi waukulu, komanso kumabweletsa cimwemwe.” Ambili amene amalandila thandizo pakacitika masoka azacilengedwe amamvela cimodzi-modzi. Ndipo anthu amene amaseŵenza na Yehova mwa kupeleka thandizo pa zocitika ngati zimenezi, nawonso amapeza cimwemwe coculuka.—Ŵelengani Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 9:6, 7.
13. Kodi kudzipeleka pa nchito za m’gulu la Mulungu kungalimbitse bwanji ubwenzi wathu na Yehova? Fotokozani citsanzo.
13 Mlongo Stephanie na ofalitsa ena, anapeza cimwemwe cifukwa coseŵenza pamodzi na Mulungu, mwa kuthandiza abale othaŵa kwawo cifukwa ca nkhondo, amene anabwela ku United States. Iwo anathandiza abalewo na mabanja awo kupeza nyumba zokhalamo, mipando, matebulo, na zinthu zina za m’nyumba. Stephanie anati: “Tinacita cidwi ngako na mtima wawo woyamikila komanso cimwemwe cimene anali naco pamene anaona cikondi ca abale apadziko lonse.” Mlongoyo anawonjezela kuti: “Iwo anayamikila kuti tinawathandiza, koma m’ceni-ceni iwo ndiwo anatithandiza kwambili. Cikondi cawo, mgwilizano, cikhulupililo, komanso kudalila kwawo Yehova, zatithandiza kulimbitsa cikondi cathu pa iye. Zatithandizanso kukhala woyamikila kwambili pa zonse zimene timalandila m’gulu lake.”
ONJEZELANI ZOCITA MU UTUMIKI WANU
14, 15. (a) Kodi mneneli Yesaya anaonetsa mzimu wotani? (b) Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?
14 Kodi mungakonde kuwonjezela zocita poseŵenza na Yehova? Kodi mungakonde kukatumikila kumene kukufunika anchito ambili m’gulu la Mulungu? N’zoona kuti atumiki a Mulungu sacita kufunika kukatumikila kutali kuti aonetse kuti ni oolowa manja. Koma malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wawo, Akhristu ena amadzipeleka kukatumikila ku madela akutali. Iwo ali na mtima monga wa mneneli Yesaya. Yehova atamufunsa kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?” Yesaya anayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wanu, kodi ndimwe wokonzeka kucita utumiki uliwonse m’gulu la Mulungu? Nanga ni mautumiki ati amene alipo?
15 Pokamba za nchito yolalikila na kupanga ophunzila, Yesu anati: “Zokolola n’zoculuka, koma anchito ndi ocepa. Conco pemphani Mwini zokolola kuti atumize anchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Kodi mungadzipeleke kukatumikila kumalo osoŵa, mwina monga mpainiya? Kapena kodi mungathandizeko wina kucita zimenezo? Abale na alongo ambili amaona kuti njila yabwino kwambili yoonetsela kuti amakonda Mulungu na anansi awo, n’kukacita upainiya ku madela kapena ku magawo osoŵa. Kodi ni njila zina ziti zimene mungawonjezele nazo utumiki wanu? Dziŵani kuti tikawonjezela zocita mu utumiki wathu, timapeza cimwemwe coculuka.
16, 17. N’zinthu zina ziti zimene mungacite ngati mufuna kuwonjezela utumiki wanu kwa Yehova?
16 Kodi mungakonde kukatumikila pa Beteli, kapena kuthandizila pa nchito zomanga m’gulu la Mulungu, kaya monga mtumiki wodzipeleka wakanthawi, kapena monga wanchito woyendela kucoka kunyumba? Pakufunika abale na alongo ambili amene angadzipeleke kukatumikila Yehova kulikonse kumene angatumizidwe, komanso pa nchito iliyonse imene angapatsidwe, olo kuti alibe luso pa nchitoyo kapena sanaigwileko. Ndipo Yehova amayamikila mzimu wodzimana wa abale na alongo amene amadzipeleka kukatumikila kulikonse kumene kukufunika anchito ambili.—Sal. 110:3.
17 Kodi mumafuna kulandila maphunzilo owonjezeleka kuti mukwanitse kutumikila Mulungu mokwanila? Ngati n’conco, mungacite bwino kufunsila Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Sukulu imeneyi imaphunzitsa amuna na akazi auzimu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse, kuti akathandize kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu m’magawo osiyana-siyana. Akhristu amene amafunsila sukuluyi ayenela kukhala okonzeka kucita utumiki uliwonse umene angapatsidwe akatsiliza maphunzilo awo. Kodi mungakonde kuloŵako sukuluyi kuti mukhale na mwayi wowonjezela zocita mu utumiki wanu?—1 Akor. 9:23.
18. Timapeza mapindu anji ngati tiseŵenza na Yehova tsiku lililonse?
18 Pokhala anthu a Yehova, timayesetsa kukhala oolowa manja, okoma mtima, abwino, komanso acikondi kwa anansi athu. Timathandiza anzathu tsiku lililonse. Kucita zimenezi kumatibweletsela cimwemwe na mtendele. (Agal. 5:22, 23) Mulimonse mmene zinthu zilili mu umoyo wanu, mungathe kupeza cimwemwe mwa kutengela khalidwe la Yehova la kuolowa manja, komanso mwa kukhala mmodzi wa anchito anzake okondedwa.—Miy. 3:9, 10.