Ndandanda ya Mlungu wa October 22
MLUNGU WA OCTOBER 22
Nyimbo 71 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 14 ndime 1-5, ndi bokosi pa tsamba 112 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Hoseya 1–7 (Mph. 10)
Na. 1: Hoseya 6:1–7:7 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Gulu la Yehova la Padziko Lapansi Lingadziŵike Bwanji?—rs tsa. 143 ndime 1-7 (Mph. 5)
Na. 3: Tengelani Citsanzo ca Yesu Amene Sanaope Kucititsidwa Manyazi—Aheb. 12:2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 130
Mph. 10: Danga la Mafunso. Kukambilana ndi omvela. Kumbutsani makolo za udindo wao woyang’anila ana ao nthawi zonse popita ndi pobwelako ku Nyumba ya Ufumu, ndi pamene ali pamalo a Nyumba ya Ufumu. Thandizani omvela kudziŵa zinthu zimene zingacititse ngozi pakhomo la Nyumba ya Ufumu, kumalo oikako magalimoto ndi malo ozungulila.
Mph. 10: Samalilani Thanzi Lanu M’njila Yogwilizana ndi Malemba. Kukambilana kozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya November 15, 2008, tsamba 25-26, ndime 11-16. Gogomezani kufunika kopewa anthu ocilitsa amene amagwilitsila nchito njila kapena zinthu zokhudzana ndi zamizimu.—gf phunzilo 13 tsa. 21.
Mph. 10: Kodi ‘Mudzamuyesa Yehova’? Nkhani yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya July 15, 2012, masamba 3-6. Gwilitsilani nchito mfundo za mu Nsanjayo pa nkhani yokatumikila kumalo osoŵa m’dela lanu. Ngati alipo, kambilanani ndi wofalitsa mmodzi kapena aŵili amene anakwanitsa kutumikila kumalo osoŵa.
Nyimbo 89 ndi Pemphelo