Ndandanda ya Mlungu wa March 4
MLUNGU WA MARCH 4
Nyimbo 62 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 19 ndime 12-20 pa tsa. 152 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Maliko 9–12 (Mph. 10)
Na. 1: Maliko 11:19–12:11 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Munthu Akafa Amalangidwa Cifukwa ca Macimo Ake?—rs tsa. 344 ndime 5-tsa 345 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa Ciani Munthu Amene Wadzipeleka Kwa Mulungu Amakhala Wacimwemwe?—Mac. 20:35 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 7
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini M’mwezi wa March. Kambilanani mafunso otsatilawa:Tikamagawila tumapepala kumapeto kwa mlungu uliwonse, n’ciani cidzatithandiza kuona ngati tingagawilenso magazini? Kodi tidzakamba ciani pogawila magazini tikamaliza kugawila kapepala? Ngakhale kuti zitsanzo za mmene tingagawile kapepala zimaphatikizapo kufunsa funso ndi kuwelenga lemba, kodi tingakagawile bwanji mwacidule? Citani citsanzo ca mmene mungagaŵile magazini iliyonse limodzi ndi kapepala.
Mph. 10: Pindulani ndi kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku ka 2013. Nkhani yokambilana. Mwacidule fotokozani lemba la caka limene lili pa masamba 3-4 ndipo muonenso pa tsamba 5 pali mutu wakuti “Mmene Mungagwilitsile Nchito Buku Limeneli.” Ndiyeno funsani omvela kuti afotokoze nthawi imene anakonza kuti azisanthula malemba ndi mmene apindulila. Malizani mwa kulimbikitsa onse kuti azisanthula malemba tsiku lililonse.
Mph. 10: Zosoŵa za Mpingo.
Nyimbo 119 ndi Pemphelo