LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 3/13 tsa. 8
  • Zilengezo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zilengezo
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 3/13 tsa. 8

Zilengezo

March ndi April: Gaŵilani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pamaulendo obwelelako, gaŵilani buku lakuti Baibo Imaphunzitsa. Ngati kungakhale koyenela kwa munthuyo, m’gaŵileni kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Kenako, yambitsani phunzilo la Baibo. May ndi June: Gaŵilani kalikonse ka tumapepala twa uthenga utu: Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Kodi Ndani Kweni-kweni Akulamulila Dziko? kapena kakuti Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya? Ngati munthuyo ali ndi cidwi, gwilitsilani nchito buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa kumuonetsa mmene timacitila Phunzilo la Baibo. Kapena gwilitsilani nchito kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya.

◼ Cikumbutso cidzacitika Paciŵili, pa 26 March 2013. Ngati mpingo wanu umasonkhana Paciŵili, muyenela kupanga makonzedwe akuti mukasonkhane tsiku lina mlungu umenewo pa Nyumba ya Ufumu ngati ena sadzaigwilitsila nchito. Ngati Msonkhano wa Nchito sudzacitika, mgwilizanitsi wa bungwe la akulu ayenela kupanga makonzedwe akuti mbali zimene munali kufunikila kuphunzila pa msonkhano wa nchito mukaziphunzile tsiku lina limene mudzakasonkhana mkati mwa mwezi. Mipingo imene idzakhala ndi woyang’anila dela mlungu wa Cikumbutso, iyenela kupanga makonzedwe akuti misonkhano imene imacitika pa Ciŵili ikacitike pa tsiku lina mu mlungu wapadela umenewo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani