LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 3/13 tsa. 8
  • Maulaliki Acitsanzo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Maulaliki Acitsanzo
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Maulaliki Acitsanzo
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
Onaninso Zina
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 3/13 tsa. 8

Maulaliki Acitsanzo

Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba mu April

“Tikulimbikitsa anansi athu kuŵelenga Baibo. Koma anthu ambili amaona kuti Baibo ndi yovuta kumvetsa. Kodi inunso mumaona conco? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene magazini iyi ikamba.” Muonetseni nkhani ili patsamba lothela kucikuto ca Nsanja ya Olonda ya April 1. Ndiyeno kambilanani naye nkhani ili pansi pa funso loyamba ndi kuŵelenga lemba limodzi. Kenako, m’gaŵileni magazini ndi kupangana naye kuti mukabwelenso kudzakambilana funso lotsatila.

Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova April 1

“Aliyense amene tikamba naye akunena kuti ali ndi mavuto. Izi zimacititsa kuti anthu ambili azikaikila ngati moyo uli ndi phindu. Kodi inu muona kuti n’ciani cimene cimacititsa anthu ambili kusakhala ndi cimwemwe masiku ano? [Yembekezani ayankhe.] Baibo imatilonjeza kuti posacedwapa Mulungu adzacotsapo mavuto amene timakumana nao masiku ano. [Ŵelengani Chivumbulutso 21:4.] Magazini iyi ifotokoza madalitso amene tidzalandila m’tsogolo komanso mmene tingakhalile ndi moyo waphindu tsopano lino.”

Galamukani! April

“Kuzungulila dziko lonse lapansi m’mabanja ambili muli ciwawa. Ena amakamba kuti cimene cimapangitsa ciwawa ndi kusiyana kwa cikhalidwe, mmene munthu anakulila ndi mafilimu aciwawa. Nanga inu mumaona kuti n’ciani cimene cimacititsa ciwawa m’mabanja? [Yembekezani ayankhe.] Baibo imakamba za ubwenzi umene uyenela kukhalapo pakati pa mwamuna ndi mkazi. [Ŵelengani Aefeso 5:33.] Magazini iyi ifotokoza mmene mabanja ena akhalila ndi mtendele kaamba kogwilitsila nchito mfundo za m’Baibo.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani