Ndandanda ya Mlungu wa April 15
MLUNGU WA APRIL 15
Nyimbo 6 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 21 ndime 14-22 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Luka 13–17 (Mph. 10)
Na 1: Luka 16:16-31 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Mulungu Amationa kuti Ndife Osafunika Cifukwa Cakuti Ndife Opanda Ungwilo?—Sal. 103:8, 9 14; Agal. 6:9 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Anthu Onse Ndi Ana a Mulungu?—rs tsa. 237 ndime 2-6 (Mph. 5)
Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 95
Mph. 10: Danga la Mafunso. Kukambilana.
Mph. 10: Njila Zoonjezela Utumiki Wanu—Gawo 2. Nkhani yocokela m’buku la Gulu, tsamba 112, ndime 3, mpaka tsamba 114, ndime 1. Funsani mpainiya mmodzi kapena aŵili kuti afotokoze zimene anasintha kuti akwanitse kucita upainiya.
Mph. 10: Kodi Mumalalikila Kunchito? Nkhani yokambilana yozikidwa pa mafunso otsatila. (1) N’cifukwa ciani ndi bwino kudziŵitsa amene mumagwila nao nchito kuti ndinu mmodzi wa Mboni za Yehova? (2) Nanga mungawadziŵitse bwanji? (3) Ndi zocitika ziti zimene zingakupatseni mpata wolalikila kunchito? (4) N’cifukwa ninji ndi bwino kukhala ndi Baibo ndi mabuku ena kunchito ngati n’kotheka? (5) N’cifukwa ninji n’kofunika kupewa kulalikila kwa nthawi yaitali pamene mugwila nchito? (6) Kodi ndi zotsatilapo zabwino zotani zimene mwapeza cifukwa colalikila kunchito? Ngati nkhaniyi siikhudza dela lanu, mungakambilane nkhani ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 2003, masamba 3 mpaka 4.
Nyimbo 45 ndi Pemphelo