Zilengezo
◼Cogaŵila ca April: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pamaulendo obwelelako, gaŵilani buku lakuti Baibo Imaphunzitsa, kapena malinga ndi mikhalidwe ya munthuyo, mungagaŵile kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. Kenako, yesani kuyambitsa phunzilo la Baibo. May ndi June: Gaŵilani kalikonse ka tumapepala twa uthenga utu: Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Kodi Ndani Kweni-kweni Akulamulila Dziko? kapena kakuti Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya? Ngati munthuyo ali ndi cidwi, gwilitsilani nchito buku lakuti Baibo Imaphunzitsa kumuonetsa mmene timacitila Phunzilo la Baibo. Kapena gwilitsilani nchito kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya.
◼Ngati mukonzekela zakuti mukapezeke pa msonkhano wacigawo m’dziko lina, mudzapeza malangizo othandiza pa Webusaiti ya www.pr2711.com mwa kusankha kamutu kakuti “Misonkhano ya Cigawo” m’cigawo cakuti “About Us”
◼Nsanja ya Olonda yokhala ndi nkhani zophunzila ndi zongoŵelenga idzayamba kupezeka m’Cinyanja mwezi uliwonse kuyambila ndi ya July 1, 2013.