Ndandanda ya Mlungu wa May 6
MLUNGU WA MAY 6
Nyimbo 26 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 22 ndime 15-21 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Yohane 1–4 (Mph. 10)
Na. 1: Yohane 3:22-36 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi “Kuyenda mwa Mzimu” Kumatanthauza Ciani?—Agal. 5: 16 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Imfa ya Yesu Kristu Imasiyana Bwanji Ndi Imfa ya Anthu Ena Amene Anaphedwa Cifukwa ca Cikhulupililo Cao?—rs tsa. 122 ndime 1-4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 57
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu May. Kukambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, pa nkhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Olonda, pemphani omvela kuti achule funso lodzutsa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano, ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani! komanso ngati nthawi ilola, citaninso cimodzi-modzi ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Yehova Akapanda Kumanga Nyumba, Omanga Nyumbayo Amagwila Nchito Pacabe. (Sal. 127:1) Nkhani yokambilana yocokela mu Yearbook ya 2013, patsamba 149, ndime 1, mpaka tsamba 151, ndime 1. Pemphani omvela kunenapo maphunzilo amene apeza.
Nyimbo 47 ndi Pemphelo