Zilengezo
◼ Cogaŵila ca mu June: Gaŵilani kalikonse ka tumapepala twa uthenga utu: Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Kodi Ndani Kweni-kweni Akulamulila Dziko? Cifukwa Cake Mungadalile Baibo, kapena kakuti Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya? Ngati munthuyo ali ndi cidwi, gwilitsilani nchito buku lakuti Baibo Imaphunzitsa kumuonetsa mmene timacitila Phunzilo la Baibo. Kapena gwilitsilani nchito kabuku kakuti Mvetselani kwa Mulungu, kapena kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. July ndi August: Mungagwilitsile nchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu! kapena kalikonse ka masamba 32 mwa tumabuku utu: Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!, Mvetselani kwa Mulungu ndi kakuti Mvetselani kwa Mulungu kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya. September: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Kumapeto kwa mwezi wa March, abale ndi alongo okwana 24 amene anali m’kalasi loyamba muno m’Zambia la Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Akristu Okwatilana anamaliza maphunzilo ao. Asanabwele ku sukulu imeneyi, okwatilana amenewa anali kutumikila m’maiko osiyana-siyana awa: Botswana, Namibia, South Africa, Zambia ndi Zimbabwe. Onse analandila utumiki umene udzawathandiza kugwilitsila nchito zimene aphunzila pothandiza ndi kulimbitsa mipingo ndi madela. Tikuyamikila kwambili kuti ambili akuika patsogolo Ufumu, mwa kukhala opanda ana ndi kulinganiza umoyo wao kuti atumikile kumene kufunika olengeza uthenga ambili.