Ndandanda ya Mlungu wa July 1
MLUNGU WA JULY 1
Nyimbo 69 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 25 ndime 8 mpaka 15 ndi bokosi patsamba 201 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Machitidwe 11 mpaka 14 (Mph. 10)
Na. 1: Machitidwe 11:1-18 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Dipo Liyenela Kukhudza Bwanji Mmene Timagwilitsila Nchito Miyoyo Yathu?—rs tsa. 127 ndime 4-6 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mumaceza Ndi Anthu Otani?—Sal. 119:63 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 70
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu July. Kukambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, mwa kugwilitsila nchito mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Olonda, pemphani omvela kuti achule funso lodzutsa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano, ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani! komanso ngati nthawi ilola, citaninso cimodzi-modzi ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Citani citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Tiphunzilapo Ciani? Ŵelengani Luka 12:16-31 ndipo kambilanani mmene lembali lingatithandizile mu utumiki.
Nyimbo 35 ndi Pemphelo