Ndandanda ya Mlungu wa July 8
MLUNGU WA JULY 8
Nyimbo 43 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 25 ndime 14-21 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Machitidwe 15–17 (Mph. 10)
Na. 1: Machitidwe 16:16-34 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: N’cifukwa Ciani Mkristu Ayenela Kusangalala Akamazunzidwa?—Mat. 5:11, 12 (Mph. 5)
Na. 3: Pomwe Mtumwi Paulo Ananena Kuti Akristu ‘Adzatengedwa’ Kukakhala ndi Ambuye, Kodi Ankafotokoza Nkhani Yanji?—rs tsa. 213 ndime 1-2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 75
Mph. 10: Njila Zolalikilila Uthenga Wabwino—Kutsogolela Anthu Acidwi ku Gulu la Yehova. Nkhani yocokela m’buku la Gulu, patsamba 99, ndime 2, mpaka tsamba 100, ndime 1. Pemphani omvela kuti afotokoze mmene agwilitsilila nchito kabuku ka Cifunilo ca Yehova kuti atsogolele amene amaphunzila nao Baibo ku gulu.
Mph. 10: Muyeseni Yehova, ndi Kulandila Dalitso cakuti Mudzasoŵa Polilandilila (Mal. 3:10) Funsani mafunso apainiya anthawi zonse aŵili kapena atatu. N’ciani cimawasangalatsa kwambili pautumiki wao waupainiya? Kodi upainiya waŵathandiza bwanji kuyandikila Yehova? Apempheni kuti afotokoze cocitika ca muutumiki ciliconse cosangalatsa. Malizani nkhani yanu mwa kulimbikitsa ofalitsa onse kuti aganizile za kukhala apainiya anthawi zonse mu September.
Mph. 10: “Nchito Yapadela Imene Imakhala ndi Zotulukapo Zabwino.” Nkhani yokambilana. Patsani onse m’gulu kapepala ngati kalipo ndipo kambilanani zimene zilipo. Dziŵitsani mpingo za deti imene mudzayamba nchito yapadela, ndipo adziŵitseni makonzedwe a mpingo amene mwakonza akuti mukagaŵile anthu a m’gawo lanu. Citani citsanzo cacidule.
Nyimbo 54 ndi Pemphelo