Ndandanda ya Mlungu wa July 15
MLUNGU WA JULY 15
Nyimbo 48 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
bt mutu 26 ndime 1-8, bokosi patsamba 204 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Machitidwe 18–21 (Mph. 10)
Na. 1: Machitidwe 20:17-38 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Anthu Adzaona Kristu Akubwela M’mitambo Kudzatenga Akristu Okhulupilika Kupita Nao Kumwamba?—rs mutu womalizila pa tsa. 213 mpaka tsa. 214 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timaika Maganizo Athu pa Zinthu za Mzimu?—Aroma 8:6 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 92
Mph. 10: M’fikeni Pamtima Wophunzila Wanu. (Luka 24:32) Nkhani yokambilana yocokela pa mafunso awa: (1) Potsogoza phunzilo la Baibo, n’cifukwa ciani n’kofunika kugogomezela (a) cikondi ca Yehova ndi nzelu zake? (b) kufunika kogwilitsila nchito mfundo za m’Baibo? (c) kufunika kotsatila citsogozo ca Yehova nthawi zonse tisanapange cosankha? (2) Kodi kufunsa phunzilo lanu mafunso otsatilawa kungakuthandizeni bwanji kudziŵa ngati mukum’fika pamtima? (a) Kodi zimenezi zikuoneka kukhala zothandiza kwa inu? (b) Kodi mukuona kuti zimenezi zikugwilizana ndi cikondi ca Mulungu? (c) Kodi mungapeze mapindu otani mukagwilitsila nchito uphungu umenewu?
Mph. 20: “Abale Acinyamata, Kodi Mukukalamila?” Mafunso ndi mayankho. Mwacidule funsani mkulu kapena mtumiki wothandiza amene anakalamila ali wacinyamata. Kodi anapatsidwa nchito ziti komanso anaphunzitsidwa motani asanaikidwe kukhala mtumiki wothandiza? Kodi ena mumpingo anamuthandiza bwanji kupita patsogolo mwa kuuzimu? Kodi apeza madalitso otani kaamba ka kukalamila?
Nyimbo 85 ndi Pemphelo