“Ndabwela pano kuti . . .”
Eninyumba akatsegula citseko ndi kutipeza taima pakhomo pao, io angafune kudziŵa kuti ndife ndani ndi kuti tabwela kudzatani. Kodi tingadzidziŵikitse bwanji kuti tiŵakhazike mtima pansi? Pambuyo popeleka moni ofalitsa ena amayamba ndi mau akuti “tabwela pano kuti,” ndiyeno amayamba kufotokoza. Mwacitsanzo, anganene kuti: “Tabwela pano kuti ticezeko nanu popeza anthu ambili amadela nkhawa zaupandu. Kodi inu muganiza kuti . . .” Kapena anganene kuti “Ndabwela pano kuti tiziphunzila Baibo kwaulele.” Ngati kuciyambi kwa makambitsilano tamuuza mwininyumba cifukwa cake tam’cezela, angakhale wofunitsitsa kumvetsela zimene tifuna kunena.