Ndandanda ya Mlungu wa November 25
MLUNGU WA NOVEMBER 25
Nyimbo 122 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 1 ndime 1 mpaka 7 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: Yakobo 1 mpaka 5 (Mph. 10)
Na. 1: Yakobo 1:22 mpaka 27 ndi 2:1-13 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Cikondi Cimathandiza Bwanji Munthu Kuti Asakhale Ndi Mantha?—1 Yoh. 4:16-18 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa Ciani Kuŵelenga Baibo Kokha Sikokwanila?—rs tsa. 89 ndime 1-2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 95
Mph. 10: Zimene Mungakambe Pogaŵila Magazini mu December. Kukambilana. Fotokozani cifukwa cake magazini awa adzakhala okopa anthu a m’gawo lanu. Citani zimenezi kwa tumphindi 30 mpaka 60. Ndiyeno, pankhani zoyambilila zogwilizana ndi mutu wa pacikuto ca Nsanja ya Mlonda, pemphani omvela kuti achule funso lodzutsa cidwi limene angafunse poyambitsa makambilano, ndi lemba limene angaŵelenge. Citani cimodzi-modzi ndi Galamukani! komanso ngati nthawi ilola, citaninso cimodzi-modzi ndi nkhani ina imodzi ya mu Nsanja ya Mlonda kapena Galamukani! Citani zitsanzo ziŵili za mmene mungagaŵilile magazini iliyonse.
Mph. 10: Kodi Mungayankhe Bwanji? Nkhani yocokela m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 69, ndime 1 mpaka 5. Citani citsanzo coonetsa wofalitsa amene apeleka yankho kwa wophunzila Baibo amene afuna kupanga cosankha caumwini. Wophunzila am’funsa kuti: “Mukanakhala inu, kodi mukanacita ciani?”
Mph. 10: “Nkhani Zothandiza mu Ulaliki.” Mafunso ndi mayankho. Mwa kugwilitsila nchito nkhani yakuti, “Kuceza ndi Mnzathu,” yocokela mu Nsanja ya Mlonda ya posacedwa, citani citsanzo cacidule mogwilitsila nchito malangizo ali mu ndime 3.
Nyimbo 45 ndi Pemphelo