Zilengezo
◼ Cogaŵila ca mu November ndi December: Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya? January ndi February: Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu kapena kamodzi ka tumabuku totsatilatu twa masamba 32: Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalila, kapena Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!, Mvetselani kwa Mulungu ndi kakuti Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya.