Ndandanda ya Mlungu wa December 2
MLUNGU WA DECEMBER 2
Nyimbo 123 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 1 ndime 8 mpaka 14 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: 1 Petulo 1 mpaka 2 Petulo 3 (Mph. 10)
Na. 1: 1 Petulo 2:18 mpaka 25 ndi 3:1-7 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cipembedzo Coona Cimaphunzitsa Zimene Baibo imanena Komanso Cimadziŵitsa Anthu Dzina la Mulungu—rs tsa. 89 ndime 3-4 (Mph. 5)
Na. 3: N’cifukwa Ciani Timakhulupilila Kuti Yesu Ndi Mesiya?—Luka 24:44; Agal. 4:4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 116
Mph. 5: Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu Coyamba. Nkhani. Limbikitsani onse kutengako mbali mukuyambitsa maphunzilo a Baibo pa Ciŵelu coyamba mu December. Mwacidule citani citsanzo coonetsa mmene tingacitile zimenezi mwakugwilitsila nchito nkhani ili kucikuto cakumapeto kwa Nsanja ya Mlonda.
Mph. 15: Kodi munaziyesapo? Kukambilana. Mwacidule fotokozani mfundo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu m’nkhani za posacedwapa izi: “Colinga ca Webusaiti Yathu Ndi Kuthandiza Ife ndi Anthu Ena” (km 12/12), ndi yakuti “Ndani Angacite Nazo Cidwi Izi?” (km 5/13). Pemphani omvela kuti afotokoze mmene aphindulila ndi mfundo zili m’nkhani zimenezi.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Nyimbo 12 ndi Pemphelo