Ndandanda ya Mlungu wa December 9
MLUNGU WA DECEMBER 9
Nyimbo 84 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibo la Mpingo:
jr mutu 1 ndime 15-21 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibo: 1 Yohane 1 mpaka Yuda (Mph. 10)
Na. 1: 1 Yohane 5:1-21 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Kodi Tiyenela Kumukumbukila Bwanji Yesu Kristu?—Luka 1:32, 33; Yoh. 17:3 (Mph. 5)
Na. 3: Cipembedzo Coona Cimacita Zinthu Zosonyeza Kuti Cimakhulupilila Yesu Kristu—rs tsa. 89 ndime 5 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 5
Mph. 15: Sukulu ya Ulaliki ya 2014. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anila sukulu. Kambitsilanani mfundo zimene zingapindulitse mpingo wanu mwa kugwilitsila nchito malangizo a Sukulu ya Ulaliki ya 2014. Fotokozani kuti ngati nkhani Na. 2 ndi 3 ndime zake zacokela m’buku la Kukambitsilana, ndime zokhazo zimene zachulidwa ndi zimene muyenela kugwilitsila nchito. Limbikitsani onse kuyesetsa kukwanilitsa mbali zao, kutengako mbali pa mfundo zazikulu, ndi kugwilitsila nchito malingalilo a m’buku la Sukulu ya Utumiki opelekedwa mlungu uliwonse.
Mph. 15: “Mmene Tingakonzekelele Mau Oyamba Ogwila Mtima.” Mafunso ndi mayankho. Citani zitsanzo ziŵili za mmene mungagaŵilile buku la Baibo Imaphunzitsa. Citsanzo coyamba cikhale ndi mau osagwila mtima, koma caciŵili cikhale ndi mau ogwila mtima.
Nyimbo 60 ndi Pemphelo